Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akristu Angaumitse Mtembo?

Kodi Akristu Angaumitse Mtembo?

Kodi Akristu Angaumitse Mtembo?

Yakobo, kholo lakale lokhulupirika, atatsala pang’ono kumwalira anapempha chinthu chomaliza kuti: “Mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m’phanga lili m’munda wa Efroni Mhiti, m’phanga lili m’munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamre, m’dziko la Kanani.”​—Genesis 49:29-31.

YOSEFE analemekeza pempho la atate wake mwa kuchita mwambo umene unali wofala mu Igupto nthaŵi imeneyo. Anauza “akapolo ake asing’anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi.” Nkhani imene ili mu Genesis chaputala 50 imanena kuti asing’angawo anakonza thupilo kwa masiku 40 malinga ndi mwambo wawo. Kuumitsa mtembo wa Yakobo kunathandiza kuti gulu lalikulu la anthu a m’banja la Yakobo pamodzi ndi akuluakulu a dziko la Igupto omwe anali kuyenda pang’onopang’ono ayende mtunda wa makilomita pafupifupi 400 pokaika m’manda mtembowo ku Hebroni.​—Genesis 50:1-14.

Kodi mtembo wa Yakobo umene unaumitsidwawo n’kutheka kudzaupeza tsiku lina? N’zokayikitsa kwambiri. Dziko la Israyeli linali dera la madzi ambiri, zimene zachititsa kuti mitundu ina ya zinthu zofukulidwa m’mabwinja isapezeke kumeneko. (Eksodo 3:8) Kumapezeka zinthu zakale zachitsulo ndi zamiyala zambiri, koma zinthu zambiri zosachedwa kuwonongeka, monga nsalu, zikopa, ndi mitembo youmitsidwa, sizipezeka chifukwa cha chinyezi ndiponso kusintha kwa zinthu m’chilengedwe.

Koma kodi kuumitsa mtembo n’kutani? N’chifukwa chiyani anthu amaumitsa mitembo? Kodi n’koyenera Akristu?

Kodi Mwambowu Unayambira Kuti?

Kuumitsa mtembo ndiko kukonza mtembo wa munthu kapena wa nyama kuti usawonongeke. Olemba mbiri amati kuumitsa mitembo kunayambira ku Igupto koma Asuri, Aperisi, ndi Asikuti akale anali kuchitanso zimenezi. Mwina anthu anayamba kuchita nako chidwi ndiponso kuyesera kuumitsa mitembo pamene anatulukira mitembo imene anaikwirira mu mchenga wa m’chipululu ndipo inasungika popanda anthu kuikonza. Madzi ndi mpweya sizikanatha kuloŵa m’malo amene mitemboyo anaikwirira, motero siikanawola. Ena amati kuumitsa mitembo kunayamba atapeza kuti mitembo inasungika mu mtundu wina wa soda wofala ku Igupto ndi madera oyandikana nawo.

Cholinga cha munthu woumitsa mtembo ndicho kulepheretsa tizilombo towoletsa zinthu kugwira ntchito yawo imene imayamba patangopita nthaŵi pang’ono munthu akamwalira zimene zimachititsa mtembowo kuwonongeka. Ntchito imeneyi ikalepheretsedwa, mtembowo sumawola kapena ungawole mwapang’onopang’ono zedi. Pali zinthu zitatu zimene amafuna: kusunga mtembowo mooneka ngati munthuyo ali moyo, kuti usawole, ndiponso kuuteteza ku tizilombo towononga zinthu.

Aigupto akale anali kuumitsa mitembo makamaka pa zifukwa za chipembedzo. Chikhulupiriro chawo chakuti munthu akamwalira amakhalanso ndi moyo kwinakwake anachigwirizanitsa ndi kuti munthu womwalirayo amafuna kuyenderana ndi anthu amoyo. Ankakhulupirira kuti matupi awo adzagwiritsidwa ntchito mpaka kalekale ndipo adzapatsidwanso moyo. Ngakhale kuti kuumitsa mitembo kunali kofala, mpaka pano sipanapezeke nkhani ya Aigupto yofotokoza mmene anali kuchitira zimenezi. Nkhani yabwino kwambiri yofotokoza zimenezi ndi imene analemba wolemba mbiri wachigiriki Herodotus m’zaka za m’ma 400 B.C.E. Komabe akuti kuumitsa mitembo potsatira malangizo a Herodotus zinthu siziyenda bwino kwenikweni.

Kodi N’koyenera Akristu?

Mtembo wa Yakobo unaumitsidwa ndi anthu amene anali osiyana naye zikhulupiriro zachipembedzo. Komabe Yosefe popereka thupi la atate wake kwa asing’anga sanapemphe kuti achite mapemphero ndi miyambo imene inkachitika poumitsa mitembo ku Igupto nthaŵi imeneyo. Yakobo ndi Yosefe anali ndi chikhulupiriro cholimba. (Ahebri 11:21, 22) Ngakhale kuti si Yehova amene analamula kuti aumitse mtembo wa Yakobo, Malemba sanena kuti analakwa pochita zimenezi. Kuumitsa mtembo wa Yakobo sikunali chitsanzo ku mtundu wa Israyeli kapena mpingo wachikristu. Ndipotu, m’Mawu a Mulungu mulibe malangizo enieni a nkhani imeneyi. Mtembo wa Yosefe utaumitsidwa ku Igupto, palibenso pena m’Malemba pamene akutchula za kuumitsa mtembo.​—Genesis 50:26.

Mitembo yowonongeka imene inapezeka m’manda a ku Palesitina imasonyeza kuti Ahebri sanali kuchita mwambo woumitsa mitembo kuti isungike kwa nthaŵi yaitali. Mwachitsanzo, mtembo wa Lazaro sunaumitsidwe. Ngakhale kuti anaukuta ndi nsalu, anthu amene analipo anali ndi nkhaŵa pamene anafuna kuti achotse mwala wotseka pa manda ake. Popeza panali patapita masiku anayi Lazaro atamwalira, mlongo wake anadziŵa kuti pamveka fungo mandawo akatsegulidwa.​—Yohane 11:38-44.

Kodi mtembo wa Yesu Kristu unauumitsa? Mauthenga Abwino samanena kuti anatero. Nthaŵi imeneyo, Ayuda anali ndi mwambo wokonza mtembo ndi mankhwala onunkhira asanakauike m’manda. Mwachitsanzo, pokonza thupi la Yesu, Nikodemo anapereka mankhwala onunkhira ochuluka kuti agwiritse ntchito. (Yohane 19:38-42) N’chifukwa chiyani anapereka mankhwala onunkhira ochuluka motero? Anapereka mooloŵa manja chonchi chifukwa chakuti anali kum’konda ndi kum’lemekeza Yesu kwambiri. Tisaganize kuti kugwiritsa ntchito mankhwala onunkhira koteroko cholinga chake chinali chakuti mtembowo usawonongeke.

Kodi Mkristu angatsutse mwambo woumitsa mtembo? Kunena mosapita m’mbali, kuumitsa mtembo n’kungochedwetsa chinthu chimene chidzachitikabe. Tinachokera kufumbi ndipo tikamwalira timabwerera kufumbi komweko. (Genesis 3:19) Koma kodi padzapita nthaŵi yaitali motani kuchokera pamene munthuyo wamwalira mpaka pa mwambo wa maliro? Ngati anthu ena a m’banjalo ndi mabwenzi akuchokera kutali ndipo akufuna kuona thupilo, mosakayika mtembowo udzafunika kuumitsa.

Motero, malinga ndi Malemba, palibe chifukwa chodera nkhaŵa ngati pakufunika kuti mtembowo uumitsidwe mogwirizana ndi malamulo a kumaloko kapena ngati ena m’banjamo akufuna kuti zimenezi zichitike. Akufa “sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Ngati ali m’chikumbukiro cha Mulungu, adzaukitsidwa m’dziko latsopano limene iye walonjeza.​—Yobu 14:13-15; Machitidwe 24:15; 2 Petro 3:13.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 31]

KUUMITSA MTEMBO​—KALE NDI MASIKU ANO

Kale ku Igupto, kaumitsidwe ka mtembo kamadalira ndi kupeza kwa banjalo. Mabanja olemera nthaŵi zambiri ankasankha kaumitsidwe kotsatiraka:

Ankachotsa ubongo kudzera m’mphuno pogwiritsa ntchito chipangizo chachitsulo. Akatero, anali kukonza chibadecho ndi mankhwala oyenerera. Kenako anali kuchotsa ziwalo zonse za mkati kupatulapo mtima ndi impso. Kuti achotse ziwalo zimenezi, ankang’amba pamimba, koma kuchita zimenezi ankakuona ngati tchimo. Pofuna kupeŵa mfundo yovuta imeneyi, oumitsa mitembo a ku Igupto ankasankha munthu amene ankamutcha kuti wodula kuti ang’ambe thupilo. Wodulayo anali kuthaŵa akangochita zimenezi chifukwa chilango cha limene ankati tchimoli chinali kutembereredwa ndi kuponyedwa miyala.

Akachotsa zinthu zonse m’mimba, anali kutsukamo bwinobwino. Wolemba mbiri Herodotus analemba kuti: “M’mimbamo anali kuikamo mure weniweni woperapera, pamodzi ndi kasya, ndi mitundu ina ya mankhwala onunkhira kupatulapo libano, ndipo akatero anali kusoka pamene anang’ambapo.”

Kenako, thupilo anali kuliumitsa polinyika mu soda kwa masiku 70. Akatero, mtembowo anali kuutsuka ndi kuukuta mu nsalu mwaluso. Ndiyeno nsaluyo anali kuipaka utomoni kapena mitundu ina ya zomatira zimene zinkagwira ntchito ngati gluu. Akatero, mtembo woumitsidwawo anali kuuika m’bokosi lamatabwa limene anali kulikongoletsa kwambiri ndiponso anali kulikonza mogwirizana ndi thupi la munthu.

Masiku ano, mtembo ungaumitsidwe m’nthaŵi yochepa chabe. Nthaŵi zambiri amachita zimenezi mwa kuika mlingo wabwino wa mankhwala oumitsira m’mitsempha pamodzi ndi m’mimba ndi m’chifuwa. M’zaka zambiri zapitazi, mitundu yosiyanasiyana ya mankhwala yapangidwa ndi kugwiritsidwa ntchito. Komabe, mankhwala otchedwa formaldehyde ndi amene akugwiritsidwa ntchito kwambiri chifukwa cha mtengo wake ndiponso kuti ndi otetezeka.

[Chithunzi]

Bokosi lagolide la Mfumu Tutankhamen