Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Utsogoleri Wabwino Tingaupeze Kuti?

Kodi Utsogoleri Wabwino Tingaupeze Kuti?

Kodi Utsogoleri Wabwino Tingaupeze Kuti?

BAIBULO limati: “Nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4; Chivumbulutso 4:11) Popeza Mulungu woona, Yehova, ndiye Mlengi wathu, ‘amadziŵa mapangidwe athu.’ (Salmo 103:14) Amadziŵa kwambiri zofooka ndi zosoŵa zathu. Ndipo popeza ndi Mulungu wachikondi, amafuna kutipatsa zosoŵa zathuzo. (Salmo 145:16; 1 Yohane 4:8) Zimenezi zikuphatikizapo utsogoleri wabwino.

Yehova kudzera mwa mneneri Yesaya anati: “Tawonani, ndam’pereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.” (Yesaya 55:4) Njira yothetsera vuto lalikulu la utsogoleri limene lilipo pakalipano ikuphatikizapo kudziŵa Mtsogoleri amene wasankhidwa ndi Wamphamvuyonse komanso kuvomereza kuti atitsogolere. Nangano, kodi Wotsogolera ndi Wolamulira amene analoseredwayu ndi ndani? Kodi ali ndi ziyeneretso zotani monga mtsogoleri? Kodi adzatitsogolera kuti? Kodi titani kuti tipindule ndi utsogoleri wake?

Kufika kwa Mtsogoleri Woloseredwayo

Zaka pafupifupi 2,500 zapitazo, mngelo Gabrieli anaonekera kwa mneneri Danieli ndi kumuuza kuti: “Dziŵa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kum’manga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi aŵiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri makwalala ndi chemba zidzamangidwanso, koma mu nthaŵi za mavuto.”​—Danieli 9:25.

Inde, mngeloyo anali kum’dziŵitsa Danieli nthaŵi yeniyeni imene Mtsogoleri amene Yehova anamusankha adzafika. “Wodzozedwayo, ndiye kalonga,” kapena Mtsogoleri, anali kudzaonekera pamapeto pa milungu 69, kapena kuti zaka 483, kuŵerenga kuyambira mu 455 B.C.E., pamene lamulo la kumanganso Yerusalemu linatuluka. * (Nehemiya 2:1-8) Kodi n’chiyani chinachitika kumapeto kwa nthaŵi imeneyo? Luka, yemwe analemba uthenga wabwino, anasimba kuti: “Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya [29 C.E.], . . . panadza mawu a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m’chipululu. Ndipo iye anadza kudziko lonse la m’mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo.” Pa nthaŵi imeneyo, “anthu anali kuyembekezera” Mtsogoleri Wodzozedwayo. (Luka 3:1-3, 15) Ngakhale kuti anthu ambiri anapita kwa Yohane, iye sanali Mtsogoleriyo.

Ndiyeno cha mu October mu 29 C.E., Yesu wa ku Nazarete anapita kwa Yohane kuti amubatize. Ndipo Yohane anachitira umboni, anati: “Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye. Ndipo sindinam’dziŵa Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.” (Yohane 1:32-34) Pa ubatizo wake, Yesu anakhala Mtsogoleri wodzozedwa kutanthauza kuti Mesiya kapena Kristu.

Inde, “wotsogolera ndi wolamulira anthu” woloseredwayo anali Yesu Kristu. Ndipo tikapenda makhalidwe ake monga mtsogoleri, timazindikira mosavuta kuti utsogoleri wake ukuposa kwambiri ziyeneretso za masiku ano za mtsogoleri wabwino.

Mesiya Ndiye Mtsogoleri Wabwino

Mtsogoleri wabwino amapereka malangizo omveka ndipo amathandiza anthu amene akuwatsogolera kukhala odzidalira ndi anzeru kuti athane bwinobwino ndi mavuto awo. ‘Zimenezi n’zofunika kwa mtsogoleri wopambana wa m’zaka za m’ma 2000,’ likutero buku lakuti 21st Century Leadership: Dialogues With 100 Top Leaders. Yesu anathandiza bwino omvera ake momwe angathetsere mavuto a tsiku ndi tsiku. Tangoganizani nkhani yake yotchuka​—Ulaliki wa pa Phiri. M’buku la Mateyu machaputala 5 mpaka 7 timapeza malangizo othandiza kwambiri.

Mwachitsanzo, taganizani langizo la Yesu pankhani yothetsa kusemphana maganizo. Iye anati: “Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.” (Mateyu 5:23, 24) Kuyanjana kaye ndi anthu ena kuli pamalo oyamba ndipo n’kofunika kwambiri kuposa kuchita ntchito zachipembedzo, monga kupereka mtulo pa guwa la kachisi ku Yerusalemu malinga ndi mmene zinkafunikira m’Chilamulo cha Mose. Kupanda kutero ndiye kuti kulambira kwako sikungakhale kolandirika kwa Mulungu. Langizo la Yesu limeneli likugwiranso ntchito lerolino monga mmene linachitira zaka zambiri zapitazo.

Yesu analangizanso omvera ake kupeŵa msampha wa chiwerewere. Anawalangiza kuti: “Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:27, 28) Ndi langizo loyenereratu limenelo. N’kuyambiranji kuganizira za chigololo, zinthu zimene zingatipangitse kuchita zimenezo? Yesu ananena kuti chiwerewere ndi chigololo zimachokera mu mtima. (Mateyu 15:18, 19) N’kwanzeru kutchinjiriza mtima wathu.​—Miyambo 4:23.

Ulaliki wa pa Phiri ulinso ndi malangizo abwino pankhani yokonda adani athu, yooloŵa manja, yoona zinthu zakuthupi ndi zauzimu moyenera, ndi zina zotero. (Mateyu 5:43-47; 6:1-4, 19-21, 24-34) Yesu anasonyezanso omvera ake mmene angapemphere thandizo la Mulungu mwa kuwaphunzitsa mmene angapempherere. (Mateyu 6:9-13) Mesiya Mtsogoleri amalimbikitsa ndi kukonzekeretsa otsatira ake kuti athane ndi mavuto amene ndi ofala pakati pa anthu.

Mu Ulaliki wa pa Phiri, Yesu kasanu ndi kamodzi anayamba kulankhula ndi mawu akuti “munamva kuti kunanenedwa,” kapena “kunanenedwanso,” koma kenako anali kupereka mfundo ina, kuti “koma ine ndinena kwa inu.” (Mateyu 5:21, 22, 27, 28, 31-34, 38, 39, 43, 44) Zimenezi zikusonyeza kuti omvera ake anazoloŵera kuchita zinthu mwa njira inayake, malinga ndi miyambo ya pakamwa ya Afarisi. Koma tsopano Yesu anali kuwasonyeza njira ina imene inasonyeza tanthauzo lenileni la Chilamulo cha Mose. Motero, Yesu anali kusintha zinthu, ndipo anachita zimenezi mwa njira imene inali yosavuta kwa omvera ake kutsatira. Inde, Yesu anachititsa anthu kusintha kwambiri miyoyo yawo, mwauzimu ndi mwamakhalidwe. Chimenechi n’chizindikiro cha mtsogoleri wabwino.

Buku lina lofotokoza za kutsogolera ena linafotokoza mmene kulili kovuta kuwasintha anthu motero. Linati: “[Mtsogoleri] amene angasinthe anthu motero afunika kukhala wachifundo ngati wantchito yothandiza anthu, wozindikira ngati katswiri wa zamaganizo, wamphamvu ngati katswiri wothamanga, wakhama ngati galu, wodzidalira ngati munthu wodzipatula n’kukakhala kwayekha, ndiponso woleza mtima ngati munthu wodzipereka kwambiri pa kulambira. Ndipo ngakhale atakhala ndi makhalidwe ameneŵa, sikuti n’zotsimikizika kuti adzapambana, ayi.”

Nkhani ina ya mutu wakuti, “Leadership: Do Traits Matter?,” (“Kodi Makhalidwe Ndi Ofunika kwa Mtsogoleri?”) inati: “Atsogoleri afunika kuchita zinthu zofanana ndi zimene amafuna kuti otsatira awo azichita.” Inde, mtsogoleri wabwino amachita zimene amauza ena kuti azichita. Zimenezitu n’zimene Yesu Kristu anachita. Inde, iye anaphunzitsa anthu amene anali naye kuti akhale odzichepetsa, koma anawapatsanso chitsanzo mwa kusambitsa mapazi awo. (Yohane 13:5-15) Iye sanangotumiza ophunzira ake kuti akalalikire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, m’malo mwake iye mwiniyo anaigwira mwamphamvu ntchito imeneyi. (Mateyu 4:18-25; Luka 8:1-3; 9:1-6; 10:1-24; Yohane 10:40-42) Ndiponso pankhani yomvera otsogolera, Yesu anapereka chitsanzo. Iye anadzinena yekha kuti: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho.”​—Yohane 5:19.

Zonena ndi zochita za Yesu zimene tapendazi zikusonyeza kuti iye ndi Mtsogoleri wabwino. Ndipotu, iye akuposa miyezo yonse ya anthu ya mtsogoleri wabwino. Yesu ndi wangwiro. Popeza analandira moyo wosafa pambuyo pa kumwalira ndi kuukitsidwa, iye adzakhala ndi moyo kwamuyaya. (1 Petro 3:18; Chivumbulutso 1:13-18) Kodi pali wolamulira waumunthu amene angakhale ndi ziyeneretso ngati zimenezi?

Kodi Tichite Chiyani?

‘Wodzozedwa Mtsogoleri,’ monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzadalitsa anthu omvera. Pankhani imeneyi, Malemba amalonjeza kuti: “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.” (Mika 4:4) “Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Dziko lerolino likusoŵa utsogoleri wabwino. Koma Yesu Kristu akutsogolera anthu ofatsa ku dziko latsopano la mtendere, kumene anthu omvera adzagwirizana polambira Yehova Mulungu ndipo azidzasintha pang’onopang’ono kuti akhale angwiro. Ndiyetu n’kofunika kupatula nthaŵi kuti tiphunzire za Mulungu woona ndi Mtsogoleri amene anamusankha ndi kutsatira zimene taphunzirazo.​—Yohane 17:3.

Chinthu chabwino kuposa china chilichonse chimene tingachitire munthu posonyeza kumuyamikira ndicho kumutsanzira. Motero, kodi sitingatsanzire Yesu Kristu, Mtsogoleri wamkulu kuposa wina aliyense m’mbiri ya anthu? Kodi tingachite motani zimenezo? Kodi kuvomereza utsogoleri wake kudzakhudza motani miyoyo yathu? Mafunso ameneŵa pamodzi ndi enanso ayankhidwa m’nkhani ziŵiri zotsatirazi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani masamba 186-92 m’buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli!, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 4]

Danieli analosera za kubwera kwa Mtsogoleri amene Mulungu anamusankha

[Zithunzi patsamba 7]

Zimene Yesu anaphunzitsa zinathandiza anthu kuthana ndi mavuto amene anali kukumana nawo

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu adzatsogolera anthu omvera kuloŵa m’dziko latsopano la mtendere