Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kristu Amatsogolera Mpingo Wake

Kristu Amatsogolera Mpingo Wake

Kristu Amatsogolera Mpingo Wake

“Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”​—MATEYU 28:20.

1, 2. (a) Kodi Yesu woukitsidwayo polamula otsatira ake kuti apange ophunzira, anawalonjeza chiyani? (b) Kodi Yesu anachita zotani potsogolera mpingo woyambirira wachikristu?

YESU KRISTU, Mtsogoleri wathu amene anaukitsidwa asanakwere kumwamba, anaonekera kwa ophunzira ake ndipo anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”​—Mateyu 23:10; 28:18-20.

2 Yesu sanangopatsa ophunzira ake ntchito yopulumutsa moyo yopanga ophunzira ena koma anawalonjezanso kuti akhala nawo. Mbiri ya Chikristu choyambirira, yolembedwa m’Baibulo m’buku la Machitidwe, ikutsimikizira kuti Kristu anagwiritsa ntchito ulamuliro umene anapatsidwa kutsogolera mpingo umene unangoyamba kumenewo. Anatumiza “nkhoswe” imene analonjeza, mzimu woyera, kuti ulimbitse otsatira ake ndi kuwatsogolera pa ntchito yawo. (Yohane 16:7; Machitidwe 2:4, 33; 13:2-4; 16:6-10) Yesu woukitsidwayo anagwiritsa ntchito angelo amene amam’tumikira kuti athandize ophunzira ake. (Machitidwe 5:19; 8:26; 10:3-8, 22; 12:7-11; 27:23, 24; 1 Petro 3:22) Ndiponso, Mtsogoleri wathu anapereka malangizo ku mipingo mwa kukonza kuti amuna oyenerera atumikire monga bungwe lolamulira.​—Machitidwe 1:20, 24-26; 6:1-6; 8:5, 14-17.

3. Kodi m’nkhani ino tikambirana mafunso ati?

3 Nanga bwanji za nthaŵi yathu ino, “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano”? Kodi Yesu Kristu akutsogolera motani mpingo wachikristu masiku ano? Ndipo tingasonyeze motani kuti timavomereza utsogoleri umenewu?

Mbuyeyo Ali ndi Kapolo Wokhulupirika

4. (a) Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi ndani? (b) Kodi Mbuye wapatsa kapoloyo chiyani kuti ayang’anire?

4 Polosera za chizindikiro cha kukhalapo kwake, Yesu anati: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anam’khazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya panthaŵi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzam’peza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzam’khazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:45-47) ‘Mbuyeyo’ ndiye Mtsogoleri wathu, Yesu Kristu, ndipo waika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” amene ndi gulu la Akristu odzozedwa padziko lapansi, kuti ayang’anire zinthu zake zonse za padziko lapansi.

5, 6. (a) M’masomphenya amene mtumwi Yohane anaona, kodi “zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri” ndi “nyenyezi zisanu ndi ziŵiri” zikuimira chiyani? (b) Kodi zikutanthauzanji kuti “nyenyezi zisanu ndi ziŵiri” zili m’dzanja lamanja la Yesu?

5 Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limasonyeza kuti Yesu Kristu akulamulira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru mwachindunji. Mtumwi Yohane m’masomphenya a “tsiku la Ambuye,” anaona “zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri zagolidi; ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga Mwana wa munthu” amene “m’dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziŵiri.” Yesu pofotokozera Yohane masomphenyawo, anati: “Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zimene unaziona pa dzanja langa lamanja, ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri zagolidi: nyenyezi zisanu ndi ziŵiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iŵiri; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri ndizo Mipingo isanu ndi iŵiri.”​—Chivumbulutso 1:1, 10-20.

6 “Zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri” zikuimira mipingo yonse yoona yachikristu ya mu “tsiku la Ambuye,” limene linayamba mu 1914. Koma bwanji za “nyenyezi zisanu ndi ziŵiri”? Poyambirira, zimenezi zinaimira oyang’anira onse odzozedwa, obadwa ndi mzimu amene anali kusamalira mipingo ya m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. * Oyang’anira anali m’dzanja lamanja la Yesu kutanthauza kuti anali kuwalamulira ndi kuwatsogolera. Inde, Kristu Yesu anali kutsogolera gulu lonse la kapolo. Komabe, oyang’anira odzozedwa ndi ochepa masiku ano. Kodi utsogoleri wa Kristu umafika motani m’mipingo yoposa 93,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse?

7. (a) Kodi Yesu akugwiritsa ntchito motani Bungwe Lolamulira kutsogolera mipingo padziko lonse? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti oyang’anira achikristu amaikidwa ndi mzimu woyera?

7 Monga mmene zinalili m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, kagulu kochepa ka amuna oyenerera mwa oyang’anira odzozedwa tsopano akutumikira monga Bungwe Lolamulira, kuimira gulu lonse la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Mtsogoleri wathu amagwiritsa ntchito Bungwe Lolamulira limeneli kuika amuna oyenerera, kaya odzozedwa ndi mzimu kapena ayi, kukhala akulu m’mipingo. Pamenepa, mzimu woyera umagwira ntchito yofunika kwambiri chifukwa chakuti Yehova wapatsa Yesu ulamuliro wougwiritsa ntchito. (Machitidwe 2:32, 33) Choyamba, oyang’anira ameneŵa ayenera kukwaniritsa ziyeneretso zimene zili m’Mawu a Mulungu, amene anauziridwa ndi mzimu woyera. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9; 2 Petro 1:20, 21) Kuvomereza ndi kuika oyang’aniraŵa kumachitika atapemphera ndiponso motsogozedwa ndi mzimu woyera. Ndiponso, munthu amene waikidwayo amapereka umboni woti ali ndi zipatso za mzimuwo. (Agalatiya 5:22, 23) Motero, uphungu wa Paulo umagwira ntchito mofanana kwa akulu onse, kaya odzozedwa kapena ayi. Uphunguwo umati: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira.” (Machitidwe 20:28) Amuna oikidwa ameneŵa amalandira malangizo kuchokera ku Bungwe Lolamulira ndipo amakonda kubusa mpingo. Mwa njira imeneyi, Kristu ali nafe lerolino ndipo akutsogolera mpingo.

8. Kodi Kristu amagwiritsa ntchito motani angelo kutsogolera otsatira ake?

8 Yesu amagwiritsanso ntchito angelo enieni kutsogolera otsatira ake lerolino. Malinga ndi fanizo la tirigu ndi namsongole, nthaŵi yotuta idzafika pa “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Kodi Mbuyeyo adzagwiritsa ntchito ndani kututa? Kristu anati: “Otutawo ndiwo angelo.” Anawonjezeranso kuti: “Mwana wa munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 13:37-41) Ndiponso, monga mmene mngelo anatsogolera Filipo kuti akapeze mdindo wa ku Etiopia, palinso umboni waukulu lerolino wakuti Kristu akugwiritsa ntchito angelo ake kutsogolera ntchito ya Akristu oona kuti apeze anthu oona mtima.​—Machitidwe 8:26, 27; Chivumbulutso 14:6.

9. (a) Kodi Kristu amagwiritsa ntchito chiyani kutsogolera mpingo wachikristu lerolino? (b) Kodi tiyenera kupenda funso liti ngati tikufuna kupindula ndi utsogoleri wa Kristu?

9 Ndi zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti Yesu Kristu akutsogolera ophunzira ake masiku ano kudzera mwa Bungwe Lolamulira, mzimu woyera ndi angelo! Ngakhale ena olambira Yehova atasiyana ndi Bungwe Lolamulira kwakanthaŵi chifukwa cha chizunzo kapena zifukwa zina, Kristu adzawatsogolerabe pogwiritsa ntchito mzimu woyera ndi thandizo la angelo. Kuti tipindule ndi utsogoleri wake, chofunika si china ayi koma kuuvomereza. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timavomereza utsogoleri wa Kristu?

‘Mverani . . . Gonjerani’

10. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira ndi kulemekeza akulu oikidwa mumpingo?

10 Mtsogoleri wathu wapatsa mipingo “mphatso mwa amuna” (NW)​—“ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi.” (Aefeso 4:8, 11, 12,) Zimene zimavumbula kuti timavomereza utsogoleri wa Kristu kapena kuukana ndi mmene timawaonera amuna ameneŵa komanso zimene timawachitira. Tifunika ‘kukhala oyamika’ chifukwa cha amuna oyenerera mwauzimu amene Kristu wapereka. (Akolose 3:15) Tifunikanso kuwalemekeza. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu woŵirikiza.” (1 Timoteo 5:17) Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira ndi kulemekeza akulu kapena kuti oyang’anira mumpingo? Paulo akuyankha kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere.” (Ahebri 13:17) Inde, tifunika kuwamvera ndi kuwagonjera, kapena kuti kulolera.

11. N’chifukwa chiyani kulemekeza akulu ili mbali ina ya kuchita mogwirizana ndi ubatizo wathu?

11 Mtsogoleri wathu ndi wangwiro. Amuna amene watipatsa monga mphatso ndi opanda ungwiro. Motero, iwo nthaŵi zina angalakwe. Komabe, n’kofunika kwambiri kukhulupirikabe ku makonzedwe a Kristu. Ndipotu, kuchita mogwirizana ndi kudzipatulira ndi ubatizo wathu kumatanthauza kuti tikuvomereza kuti ulamuliro woikidwa ndi mzimu ndi woyenerera ndipo timagonjera ndi mtima wonse. Kubatizidwa kwathu ‘m’dzina la mzimu woyera,’ ndiko kulengeza poyera kuti tikudziŵa kuti mzimu woyera n’chiyani ndiponso tikudziŵa ntchito imene umagwira pa zolinga za Yehova. (Mateyu 28:19) Ubatizo wotero umasonyeza kuti tikugwirizana ndi mzimu ndipo timapeŵa kuchita zinthu zimene zingaulepheretse kugwira ntchito pa otsatira a Kristu. Popeza mzimu woyera umagwira ntchito yofunika kwambiri povomereza ndi kuika akulu, kodi tingakhale okhulupirikadi pa kudzipatulira kwathu ngati sitikugwirizana ndi akulu mumpingo?

12. Kodi ndi zitsanzo ziti za kusalemekeza ulamuliro zimene Yuda anatchula, ndipo zikutiphunzitsa chiyani?

12 M’Malemba muli zitsanzo zambiri zimene zimatiphunzitsa kuti kumvera ndi kugonjera n’kofunika. Wophunzira Yuda, ponena za anthu amene ankachitira mwano amuna oikidwa mumpingo, anatchula zitsanzo zitatu zochenjeza. Anati: “Tsoka kwa iwo! pakuti anayenda m’njira ya Kaini, ndipo anadziwononga m’chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m’chitsutsano cha Kora.” (Yuda 11) Kaini ananyalanyaza uphungu wachikondi umene Yehova anam’patsa ndipo mwadala anapitirizabe ndi udani wake wanjiru. (Genesis 4:4-8) Ngakhale kuti Balamu analandira machenjezo a Mulungu mobwerezabwereza, anayesa kutemberera anthu a Mulungu chifukwa cha ndalama. (Numeri 22:5-28, 32-34; Deuteronomo 23:5) Kora anali ndi udindo wabwino mu Israyeli, koma sanakhutire nawo. Anakonza zopandukira mtumiki wa Mulungu, Mose, munthu wofatsa woposa anthu onse padziko lapansi. (Numeri 12:3; 16:1-3, 32, 33) Kaini, Balamu ndi Kora anaona masoka. Zitsanzo zimenezi zikutiphunzitsa bwino kumvera uphungu wa anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito pa maudindo ndiponso kuwalemekeza.

13. Malinga ndi ulosi wa mneneri Yesaya, kodi amene amagonjera makonzedwe a akulu adzapeza phindu lotani?

13 Ndani amene sangafune kupindula ndi makonzedwe aakulu a uyang’aniro amene Mtsogoleri wathu waika mumpingo wachikristu? Mneneri Yesaya analosera mapindu a makonzedwe ameneŵa kuti: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo. Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:1, 2) Mkulu aliyense ndi woti akhale “pobisalira” ndi “pousira,” kutanthauza malo a chitetezo. Ngakhale kuti kugonjera ulamuliro kumativuta, tiyeni tiyesetse mwapemphero kumvera ndi kugonjera ulamuliro umene Mulungu waika mumpingo.

Mmene Akulu Amagonjera Utsogoleri wa Kristu

14, 15. Kodi amene amatsogolera mumpingo amasonyeza motani kuti amagonjera utsogoleri wa Kristu?

14 Akristu onse, makamaka akulu, ayenera kutsatira utsogoleri wa Kristu. Oyang’anira, kapena akulu, ali ndi mlingo wina wake wa ulamuliro mumpingo. Koma sayenera ‘kuchita ufumu pa chikhulupiriro cha okhulupirira anzawo’ mwa kulamulira miyoyo yawo. (2 Akorinto 1:24) Akulu amamvera mawu a Yesu akuti: “Mudziŵa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi.” (Mateyu 20:25-27) Pamene akulu akukwaniritsa udindo wawo, amayesetsa kutumikira ena ndi mtima wonse.

15 Akristufe amatilimbikitsa kuti: “Kumbukirani atsogoleri anu, . . . ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” (Ahebri 13:7) Sikuti Akristu afunika kutsanzira akulu chifukwa choti ndi atsogoleri ayi. Yesu anati: “Alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.” (Mateyu 23:10) Chimene afunika kutsanzira ndi chikhulupiriro cha akuluwo chifukwa chakuti akuluwo amatsanzira Mtsogoleri wathu weniweni, Kristu. (1 Akorinto 11:1) Taonani njira zina zimene akulu amayesetsa kukhala monga Kristu pochita zinthu ndi ena mumpingo.

16. Ngakhale kuti Yesu anali ndi ulamuliro, kodi ankatani pochita zinthu ndi otsatira ake?

16 Ngakhale kuti Yesu anaposa anthu opanda ungwiro m’zonse ndipo analandira ulamuliro woposa wina uliwonse kuchokera kwa Atate ake, anali wofatsa pochita zinthu ndi ophunzira ake. Sanadodometse omvera ake mwa kuwasonyeza mwamatama kuti anali wanzeru. Yesu anawakomera mtima ndi kuwachitira chifundo otsatira ake. Anaganizira zosoŵa zawo monga anthu. (Mateyu 15:32; 26:40, 41; Marko 6:31) Sanafune kuti ophunzira apereke zimene sakanatha, ndipo sanawauze kuchita zinthu zimene sakanakwanitsa. (Yohane 16:12) Yesu anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” Motero, sitingadabwe kuti ambiri anali kupeza chitsitsimutso kwa iye.​—Mateyu 11:28-30.

17. Kodi akulu angasonyeze motani kudzichepetsa ngati kwa Kristu akamachita zinthu ndi ena mumpingo?

17 Ngati Kristu, Mtsogoleri wathu anali wofatsa, kuli bwanji nanga amene akutsogolera mumpingo! Ayenera kukhala ofatsa kwambiri. Inde, amasamala kuti asagwiritse ntchito mosayenera ulamuliro umene apatsidwa. Ndiponso ‘sadza ndi mawu oposa,’ kuti adabwitse ena. (1 Akorinto 2:1, 2) M’malo mwake, amayesetsa kulankhula mawu a choonadi cha m’Malemba mosavuta ndiponso kuchokera pansi pa mtima. Ndiponso, akulu amayesetsa kusayembekezera ena kuchita zimene sangathe ndipo amawaganizira zosoŵa zawo. (Afilipi 4:5) Podziŵa kuti aliyense ali ndi zofooka zake, iwo amakumbukira zimenezi pochita zinthu ndi abale awo. Amatero chifukwa chowakonda. (1 Petro 4:8) Ndipo kodi akulu odzichepetsa ndi ofatsa sali otsitsimula? Kumene!

18. Kodi akulu angaphunzire chiyani ndi mmene Yesu anachitira ndi ana?

18 Ngakhale ana anali kumasuka kupita kwa Yesu. Taonani mmene anayankhira pamene ophunzira ake anadzudzula anthu chifukwa cha ‘kudza nato tiana kwa Iye.’ Anati: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.” Kenako, “anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito.” (Marko 10:13-16) Yesu anali waubwenzi ndi wokoma mtima, ndipo anthu anakopeka naye. Anthu sanali kumuopa. Ngakhale ana anali kumasuka akakhala naye. Ndi mmenenso akulu alili, ndipo akakhala aubwenzi ndi okoma mtima, ena ndi ana omwe amakhala omasuka kukhala nawo.

19. Kodi kukhala ndi “mtima wa Kristu” kumatanthauza chiyani, ndipo zimenezi zimafuna kuchitanji?

19 Mmene akulu angatsanzirire Kristu Yesu, zimadalira mmene akumudziŵira bwino. Paulo anafunsa kuti: “Wadziŵa ndani mtima wa Ambuye, kuti akam’langize Iye?” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Koma ife tili nawo mtima wa Kristu.” (1 Akorinto 2:16) Kukhala ndi mtima wa Kristu kumatanthauza kudziŵa mmene amaganizira ndi kudziŵa mbali zonse za mtima wake moti n’kudziŵa zimene angachite pa nkhani ina yake. Tangoganizani kumudziŵa bwino motero Mtsogoleri wathu! Inde, zimenezi zimafuna kuika mtima kwambiri pa nkhani za m’Mauthenga Abwino ndi kuyesetsa kumvetsa nthaŵi zonse moyo wa Yesu ndi chitsanzo chake. Akulu akamayesetsa kutsatira utsogoleri wa Kristu mpaka pamenepo, anthu mumpingo amafuna kutsanzira chikhulupiriro chawo. Ndipo akulu amasangalala kuona ena akutsatira mapazi a Mtsogoleri wathu mokondwera.

Pitirizani Kutsata Utsogoleri wa Kristu

20, 21. Kodi tifunika kulimbikira kuchita chiyani pamene tikuyembekeza dziko latsopano lolonjezedwa?

20 Tonsefe tifunika kupitiriza kutsata utsogoleri wa Kristu. Pamene tikuyandikira mapeto a dongosolo lino la zinthu, sitikusiyana ndi Aisrayeli pamene anali m’Chigwa cha Moabu m’chaka cha 1473 B.C.E. Anatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, ndipo Mulungu anati kudzera mwa mneneri Mose: “[Yoswa] udzaloŵa nawo anthu aŵa m’dziko limene Yehova analumbirira makolo awo kuwapatsa ilo.” (Deuteronomo 31:7, 8) Yoswa anali mtsogoleri amene anaikidwa. Kuti Aisrayeli aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, anafunika kugonjera utsogoleri wa Yoswa.

21 Ifeyo Baibulo limatiuza kuti: “Alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.” Kristu yekha adzatitsogolera kuloŵa m’dziko latsopano lolonjezedwa mmene mudzakhalitsa chilungamo. (2 Petro 3:13) Motero, tiyenitu tilimbikire kutsata utsogoleri wake m’mbali zonse za moyo wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 “Nyenyezi” panopa sizikuimira angelo enieni. Yesu sangagwiritse ntchito munthu kulembera uthenga zolengedwa zauzimu zosaoneka. Motero, “nyenyezi” zikuimira oyang’anira aumunthu, kapena akulu, m’mipingo, amene ali monga amithenga a Yesu. Chiŵerengero chawocho, asanu ndi aŵiri, chikutanthauza kukwanira malinga ndi muyezo wa Mulungu.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Kristu anautsogolera motani mpingo woyambirira?

• Kodi Kristu akuutsogolera motani mpingo wake lerolino?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kugonjera amene akutsogolera mumpingo?

• Kodi akulu angasonyeze motani kuti Kristu ndiye Mtsogoleri wawo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Kristu amatsogolera mpingo wake ndipo oyang’anira ali m’dzanja lake lamanja

[Zithunzi patsamba 16]

“Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere”

[Chithunzi patsamba 18]

Yesu anali waubwenzi ndiponso anthu anali omasuka kukhala naye. Akulu amayesetsa kumutsanzira