Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi kupanda ungwiro kwa namwali Mariya kunaipitsa Yesu panthaŵi yotenga pakati pa Iye?

Pa za “kubadwa kwake kwa Yesu,” nkhani youziridwa imati: “Amayi wake Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.” (Mateyu 1:18) Inde, mzimu woyera wa Mulungu unagwira ntchito yaikulu kuti Mariya akhale ndi pakati.

Koma bwanji nanga za Mariyayo? Kodi dzira lake linagwira ntchito iliyonse panthaŵi yotenga pakati pakepo? Malinga ndi zomwe Mulungu analonjeza Abrahamu, Isake, Yakobo, Yuda, ndi Mfumu Davide​—omwe anali makolo akale a Mariya​—mwana wobadwayo anayenera kudzakhala mbadwa yawo yeniyeni. (Genesis 22:18; 26:24; 28:10-14; 49:10; 2 Samueli 7:16) Kodi mwana wa Mariya akanabadwa m’njira inanso iti, kuti akhale woyenerera malonjezo a Mulungu amenewo? Anayenera kukhala mwana wa Mariya weniweni.​—Luka 3:23-34.

Mngelo wa Yehova anali ataonekera kwa namwaliyo Mariya, nati: “Usawope, Mariya; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.” (Luka 1:30, 31) Kuti munthu akhale ndi pakati, dzira lake limafunika kupatsidwa mphamvu ya moyo. Mwachionekere, Yehova Mulungu ndiye anachititsa dzira m’chibelekero cha Mariya kukhala ndi mphamvu ya moyo mwa kusamutsa moyo wa Mwana wake wobadwa yekha kuchokera kumwamba kufika padziko lapansi.​—Agalatiya 4:4.

Kodi mwana wobadwa mwa njira imeneyi kwa mayi wopanda ungwiro akanakhala wangwiro ndi wopanda tchimo m’thupi lake? Kodi lamulo lachibadwa loti ana amatengera makolo awo limagwira ntchito motani pakakhala kugwirizana kwa ungwiro ndi kupanda ungwiro? Kumbukirani kuti mzimu woyera unagwiritsidwa ntchito posamutsa mphamvu ya moyo wangwiro wa Mwana wa Mulungu yomwe inachititsa kuti Mariya akhale ndi pakati. Izi zinachititsa kuti kupanda ungwiro komwe kunali m’dzira la Mariya kukhale kopanda mphamvu kotero kuti majini angwiro anapangika kuchokera pachiyambi pa pakatipo.

Mulimonse mmene zinalili, tingatsimikize kuti mzimu woyera wa Mulungu panthaŵiyo unagwira ntchito kuonetsetsa kuti chifuno cha Mulungu chakwaniritsidwa. Mngelo Gabrieli anali atamuuza Mariya kuti: “Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Inde, tinganene kuti mzimu woyera wa Mulungu unamanga khoma loteteza kuti kupanda ungwiro kapena mphamvu yoipa zisaipitse kukula kwa mwana wosabadwayo kuyambira pamene mayi wake anakhala ndi pakati mpaka m’tsogolo.

Mwachionekere, Yesu anapeza moyo wake waumunthu wangwiro kuchokera kwa Atate wake wakumwamba osati kwa munthu aliyense ayi. Yehova ‘anam’konzera thupi’ Yesu ndipo iye​—kuyambira pamene mayi wake anakhala ndi pakati mpaka m’tsogolo​—analidi “wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa.”​—Ahebri 7:26; 10:5.

[Chithunzi patsamba 19]

“Udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna”