Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Vuto la Utsogoleri Wabwino Lili Padziko Lonse

Vuto la Utsogoleri Wabwino Lili Padziko Lonse

Vuto la Utsogoleri Wabwino Lili Padziko Lonse

Munthuyo anali wolemba mabuku ndi ndakatulo. Ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino kwa anthu onse. Zaka 90 zapitazo, iye anayerekezera m’maganizo malo “kumene anthu alibe mantha ndipo akungoyembekezera zabwino zokhazokha; kumene akuphunzira zinthu kwaulere; kumene dziko silinagawanike kukhala mayiko ang’onoang’ono okhala ndi malire chifukwa cha udani; kumene anthu akulankhula zoona zokhazokha; [ndiponso] kumene mwa kuyesetsa kwambiri anthu atsala pang’ono kukhala angwiro m’zochita zawo.”

NDIYENO wolemba ameneyu anafotokoza chiyembekezo chake choti tsiku lina anthu a m’dziko lake komanso anthu ena onse padziko lapansi adzakhala malo ngati amenewo. Wandakatulo amene anapeza mphoto ya Nobel ameneyu akanakhala kuti alipo, akanakhumudwa kwambiri. Ngakhale kuti dziko lapita patsogolo potulukira zinthu zatsopano, n’logawanika kwambiri kuposa kale. Ndiponso tsogolo la anthu lidakali losasangalatsa.

Mlimi wina atafunsidwa chifukwa chake ziwawa zinabuka mwadzidzidzi pakati pa magulu ena m’dziko lake, iye anafotokoza chimene anaona kuti n’china mwa zimene zinayambitsa. Anati: “N’chifukwa cha atsogoleri oipa.” Wolemba mbiri wina, Jonathan Glover, anafotokoza maganizo ofanana ndi ameneŵa m’buku lake lakuti Humanity​—A Moral History of the Twentieth Century. Iye anati: “Kupulula anthu [a m’dziko lomwelo] sikunachitike chifukwa cha kudana kwa mafuko kongoyambika kokha. Anthu ofuna kulamulira anachita kukonza zimenezi.”

Nkhondo itayambika pakati pa mayiko aŵiri a lipabuliki m’dziko limene kale linali Yugoslavia kuchiyambi kwa m’ma 1990, mtolankhani wina analemba kuti: “Takhala tikukhalira limodzi bwinobwino kwa zaka zambiri koma tsopano zaipiratu kufika popherana ana. N’chifukwa chiyani tikuchita zimenezi?”

Makilomita ambirimbiri kuchokera ku Ulaya ndi ku Africa timapeza dziko la India, kumene kunabadwira wolemba ndakatulo amene tam’tchula kuchiyambi kwa nkhani ino. Mlembi wina, Pranay Gupte, m’nkhani yake yakuti “Can India Survive as One Nation?,” [“Kodi India Lidzakhalabe Dziko Limodzi?”], anati: ‘Anthu pafupifupi 70 mwa anthu 100 alionse ku India ndi a zaka zosakwana 30, koma kulibe atsogoleri amene angawapatse chitsanzo chabwino.’

M’mayiko ena, atsogoleri atula pansi maudindo awo chifukwa cha milandu ya katangale. Ndiyetu mwachionekere, pa zifukwa zosiyanasiyana, dziko lili ndi vuto lalikulu la utsogoleri. Zimene zikuchitikazi, zikuchitira umboni kuti zimene mneneri wina amene anakhalako zaka pafupifupi 2,600 zapitazo ananena, n’zoona. Iye anati: “Njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”​—Yeremiya 10:23.

Kodi pali njira yothetsera vuto la padziko lonse limeneli? Kodi ndani amene angatsogolere anthu kuloŵa m’dziko limene anthu sadzachita nkhondo kapena kukhala mwamantha, kumene anthu adzaphunzira zinthu zoona zambiri koma kwaulere, ndiponso kumene anthu azisintha pang’onopang’ono kuti akhale angwiro?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Fatmir Boshnjaku