Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dikirani, Pitani Patsogolo Molimba Mtima!

Dikirani, Pitani Patsogolo Molimba Mtima!

Dikirani, Pitani Patsogolo Molimba Mtima!

Lipoti la Misonkhano Yapadera

KODI alipo amene angakane kuti tikukhala ‘m’nthaŵi zoŵaŵitsa’? Ife monga Mboni za Yehova, timakumananso ndi mavuto a ‘m’masiku otsiriza’ ano. (2 Timoteo 3:1-5) Komabe timazindikira kuti anthu akufuna thandizo. Sakudziŵa tanthauzo la zimene zikuchitika m’dzikoli. Akufuna kuwalimbikitsa ndiponso kuwapatsa chiyembekezo. Kodi ntchito yathu yaikulu ndi yotani pothandiza anthu anzathu?

Mulungu watipatsa ntchito youza anthu uthenga wabwino wa Ufumu wake umene waukhazikitsa. (Mateyu 24:14) Anthu afunika kudziŵa kuti Ufumu wakumwamba umenewu ndiwokhawo umene anthu onse angayembekezere. Komabe, nthaŵi zambiri anthu salandira uthenga wathu. M’madera ena ntchito yathu ailetsa ndipo abale athu awazunza. Komabe, sititaya mtima. Mwa kukhulupirira Yehova kotheratu, timatsimikiza mtima kukhala tcheru ndi kupitabe patsogolo molimba mtima, kulengeza uthenga wabwino mosabwerera mmbuyo.​—Machitidwe 5:42.

Kutsimikiza mtima kolimba kumeneku kunaonekera pa msonkhano wapadera umene unachitika mu October 2001. Loŵeruka pa October 6, msonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania unachitika pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ku Jersey City, New Jersey, ku United States. * Tsiku lotsatira, misonkhano yowonjezera inachitika m’malo anayi, atatu ku United States ndi amodzi ku Canada. *

M’mawu ake oyamba pa msonkhano wapachakawu, tcheyamani, Samuel F. Herd wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anagwiritsa ntchito Salmo 92:1, 4 ndiyeno anati: “Tikufuna kuyamikira.” Inde, zifukwa zoyamikirira anazipereka m’malipoti asanu a padziko lonse.

Malipoti Ochokera Kumadera Osiyanasiyana

Mbale Alfred Kwakye anapereka lipoti la kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira ku Ghana, dziko lomwe kale linkatchedwa Gold Coast. Ntchito yathu kumeneko anailetsa kwa zaka zambiri. Anthu ankafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani anakuletsani? Munachita chiyani?” Zimenezi zinapereka mipata yolalikira, anafotokoza motero Mbale Kwakye. Mu 1991 pamene anachotsa chiletso, m’dziko la Ghana munali Mboni za Yehova zokwana 34,421. Mu August 2001, m’dzikoli munali Mboni zokwana 68,152​—kuwonjezeka ndi 98 peresenti. Pakalipano akukonza zomanga Nyumba ya Msonkhano yokwana kuloŵa anthu 10,000. N’zoonekeratu kuti abale athu auzimu ku Ghana akugwiritsa ntchito mokwanira ufulu wawo wa chipembedzo.

Ngakhale kuti ku Ireland kuli mavuto a zandale, abale athu kumeneko akuchita utumiki mwachangu, ndipo anthu akuwasirira chifukwa cha kusaloŵerera kwawo mu ndale. Wotsogolera m’Komiti ya Nthambi kumeneko, Peter Andrews anati ku Ireland kuli mipingo yokwana 115 m’madera 6. Mbale Andrews anasimba zimene anachita mnyamata wina wa zaka khumi dzina lake Liam amene saopa kulalikira kusukulu. Iye anagaŵira buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova kwa anzake a m’kalasi okwana 25 ndiponso kwa aphunzitsi ake. Liam anafuna kubatizidwa koma munthu wina anamufunsa ngati anayenerera kubatizidwa popeza anali wamng’ono kwambiri. Liam anayankha kuti: “Chimene chingandiyeneretse kubatizidwa ndicho kukonda kwanga Yehova osati usinkhu wanga. Kubatizidwa kwanga kudzasonyeza mmene ndimamukondera.” Cholinga cha Liam n’chakuti adzakhale mmishonale.

Ku Venezuela kunali ofalitsa uthenga wabwino okwana 5,400 m’chaka cha 1968. Koma pakalipano aliko oposa 88,000, anatero Stefan Johansson, wotsogolera m’Komiti ya Nthambi. Ndipo zikuoneka kuti chiŵerengerochi chidzapitirira pamenepa chifukwa anthu oposa 296, 000 anapezeka pa Chikumbutso m’chaka cha 2001. Mu December 1999, mvula ya mkuntho inapanga matope okokolola zinthu amene anapha anthu pafupifupi 50,000 kuphatikizapo Mboni zingapo. Nyumba ina ya Ufumu inadzala ndi matope amene anatsala pang’ono kugunda denga. Munthu wina atanena kuti nyumbayo angoisiya, abale anayankha kuti: “Ayi! Iyi ndi Nyumba yathu ya Ufumu, ndipo sitifuna kuisiya.” Anayamba kugwira ntchito pa Nyumba ya Ufumuyo, kuchotsa matope, miyala, ndi zinyalala zambirimbiri. Nyumbayo anaikonzanso ndipo abalewo akuti tsopano ndi yokongola kwambiri kuposa mmene inalili mvula ya mkunthoyo isanagwe.

Ku Philippines kuli zinenero zokwana 87, anatero Mbale Denton Hopkinson, wotsogolera m’Komiti ya Nthambi kumeneko. M’chaka chautumiki chapita, Baibulo lonse lathunthu la New World Translation of the Holy Scriptures analitulutsa m’zinenero zitatu zazikulu za m’dzikolo zomwe ndi Cebuano, Iloko, ndi Tagalog. Mbale Hopkinson anasimba zimene anachita mnyamata wina wa zaka zisanu ndi zinayi amene anaŵerenga buku lakuti Mbiri Yabwino Yokusangalatsani lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Anaitanitsa mabuku ena ku nthambi amene anawaŵerenganso, koma achibale ake anali kum’tsutsa. Patapita zaka, pamene anali ku sukulu yophunzitsa udokotala, analankhula ndi a kunthambi ndi kupempha kuti aphunzire Baibulo. Anabatizidwa mu 1996 ndipo posakhalitsa anayamba utumiki wa nthaŵi zonse. Tsopano akutumikira ku ofesi ya nthambi pamodzi ndi mkazi wake.

‘Chilumba cha Puerto Rico “chimatumiza Mboni kunja,”’ anatero wotsogolera m’Komiti ya Nthambi, Ronald Parkin. Pa chilumbachi pali ofalitsa pafupifupi 25,000 ndipo kwa zaka zambiri chiŵerengerochi sichinakwere kuposa pamenepa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti chilumba cha Puerto Rico “chimatumiza” ku United States ofalitsa pafupifupi 1,000 chaka chilichonse, omwe ambiri mwa iwo amapita kumeneko pa zifukwa zachuma. Mbale Parkin anasimba za chiweruzo chimene chinasintha zinthu chokhudza Mboni ya zaka 17, Luis, amene anadwala matenda a m’magazi. Popeza Luis anakana kumuika magazi, nkhani yake anaitengera ku khoti. Woweruza wa khotilo anafuna kulankhula naye maso ndi maso, motero anapita ku chipatala komweko. Luis anamufunsa woweruzayo kuti: “Ndikanapalamula mlandu waukulu, mukanandiweruza ngati wamkulu, koma n’chifukwa chiyani pamene ndikufuna kumvera Mulungu, mukundiona ngati mwana?” Woweruzayo anakhutira kuti Luis anali wokhwima maganizo ndipo ankatha kusankha yekha chochita.

Atatha malipoti ochokera ku madera osiyanasiyana, Harold Corkern, wa m’Komiti ya Nthambi ku U.S. anafunsa atumiki a Yehova anayi omwe atumikira kwa nthaŵi yaitali. Arthur Bonno wakhala akuchita utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka 51 ndipo tsopano akutumikira m’Komiti ya Nthambi ku Ecuador. Angelo Catanzaro wachita utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka 59, ndipo zambiri mwa zaka zimenezi anatumikira monga woyang’anira woyendayenda. Richard Abrahamson anamaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi mu 1953, ndipo analandira mwayi woyang’anira ntchito ku Denmark kwa zaka 26 asanabwerere ku Beteli ya ku Brooklyn. Pomaliza, anthu onse anasangalala kumva kwa Carey W. Barber wa zaka 96. Mbale Barber anabatizidwa mu 1921, wachita utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka 78 ndipo wakhala ali m’Bungwe Lolamulira kuyambira 1978.

Nkhani Zokhudza Mtima

Pa msonkhano wapaderawu panali nkhani zotsatizana zochititsa munthu kuganiza. Mbale Robert W. Wallen anakamba nkhani yakuti “Anthu a Dzina Lake.” Ndife anthu a dzina la Mulungu, ndipo tikupezeka m’mayiko oposa 230. Yehova watipatsa “tsogolo ndi chiyembekezo.” (Yeremiya 29:11, NW) Tiyenera kupitiriza kulengeza Ufumu wa Mulungu, kuuza anthu ena uthenga wabwino wopatsa chiyembekezo ndi kuchepetsa nkhaŵa. (Yesaya 61:1) Mbale Wallen anamaliza ndi mawu akuti: “Tiyenitu tsiku lilionse tipitirize kukhala mogwirizana ndi dzina limene tikutchedwa nalo lakuti, Mboni za Yehova.”​—Yesaya 43:10.

Chigawo chomaliza cha pulogalamuyi chinali nkhani yosiyirana imene anakamba a m’Bungwe Lolamulira. Inali ndi mutu wakuti “Tsopano Ndiyo Nthaŵi Yodikira, Kuchirimika, ndi Kulimbika.”​—1 Akorinto 16:13.

Woyamba anali mbale Stephen Lett amene anakamba nkhani yakuti “Dikirani Nthaŵi Yomaliza Ino.” Mbale Lett anafotokoza kuti tulo teniteni ndi mphatso. Tikagona timapeza mphamvu. Koma tulo tauzimu n’toipa. (1 Atesalonika 5:6) Nangano kodi tingakhale bwanji ogalamuka mwauzimu? Mbale Lett anafotokoza “mankhwala” atatu auzimu: (1) Kukhala ndi zambiri zochita mu ntchito ya Ambuye. (1 Akorinto 15:58) (2) Kuzindikira zosoŵa zanu zauzimu. (Mateyu 5:3) (3) Kutsatira uphungu wa m’Baibulo kuti muchite zinthu mwanzeru.​—Miyambo 13:20.

Mbale Theodore Jaracz anakamba nkhani yokhudza mtima yakuti “Chirimikani Poyesedwa.” Mbale Jaracz pogwira mawu Chivumbulutso 3:10 anafunsa kuti: “Kodi ‘nthaŵi ya kuyesedwa’ ndi iti?” Kuyesedwako kukudza ‘m’tsiku la Ambuye,’ nthaŵi imene tikukhalayi. (Chivumbulutso 1:10) Mayeserowa ndi okhudza nkhani yaikulu yakuti kodi tili kumbali ya Ufumu wa Mulungu umene waukhazikitsa kapena tili kumbali ya dongosolo la zinthu loipa la Satanali? Tidzakumanabe ndi mayesero kapena mavuto mpaka nthaŵi ya kuyesedwayo itatha. Kodi tidzakhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake? ‘Tiyenera kusonyeza kukhulupirika koteroko aliyense payekha,’ anatero Mbale Jaracz.

Pomaliza, Mbale John E. Barr anakamba nkhani yakuti “Limbikani Monga Munthu Wauzimu.” Pogwira mawu Luka 13:23-25, iye ananena kuti tiyenera kuyesetsa “kuloŵa pa khomo lopapatiza.” Ambiri amalephera kuloŵa chifukwa sakuchita khama kwambiri kuti akhale olimbika. Kuti tikhale Akristu okhwima mwauzimu, tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo m’mbali zonse za moyo wathu. Mbale Barr analimbikitsa kuti: “Mungavomereze kuti ino ndiyo nthaŵi (1) yoika Yehova patsogolo; (2) yolimbika; ndiponso (3) yodzipereka kuchita chifuniro cha Yehova. Mwa kuchita zimenezi tidzatha kuloŵa pa khomo lopapatiza loloŵera ku moyo wosangalatsa wopanda mapeto.”

Pamene msonkhano wapachakawu unkafika kumapeto, panali funso limodzi limene anali asanaliyankhe: Kodi lemba la chaka chautumiki cha 2002 ndi liti? Funso limeneli analiyankha tsiku lotsatira.

Msonkhano Wowonjezera

Anthu anali kuyembekezera mwachidwi Lamlungu m’mawa pamene pulogalamu ya msonkhano wowonjezera inayamba. Inayamba ndi chidule cha phunziro la Nsanja ya Olonda, ndipo kenako panatsatira mfundo zazikulu zachidule za msonkhano wapachaka. Kenako, anthu anasangalala kumvetsera nkhani ya lemba la chaka cha 2002 lakuti: “Idzani kuno kwa Ine . . . ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11:28) Nkhaniyi inachokera pa nkhani yophunzira imene kenako anaifalitsa mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 2001.

Itatha nkhani imeneyi, ena amene anali nthumwi kumisonkhano yaikulu yapadera yakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” ku France ndi ku Italy mu August 2001 anafotokoza mmene misonkhanoyo inawalimbikitsira. * Pomaliza, alendo ochokera ku Beteli ya ku Brooklyn anakamba nkhani ziŵiri zomaliza, monga mfundo zazikulu za pulogalamu ya tsikulo.

Nkhani yoyamba inali ndi mutu wakuti “Kukhulupirira Yehova Molimba Mtima m’Nthaŵi Zowawitsa Zino.” Wokambayo anafokoza mfundo zazikulu zotsatirazi: (1) Kukhulupirira Yehova molimba mtima kwakhala kofunika kwambiri kwa anthu a Mulungu kuyambira kale. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anasonyeza kulimba mtima ndi chikhulupiriro atakumana ndi chitsutso. (Ahebri 11:1–12:3) (2) Yehova wapereka zifukwa zoti timukhulupirire ndi mtima wonse. Ntchito zake ndi Mawu ake zikupereka umboni wakuti amasamala atumiki ake ndiponso kuti sadzawaiwala. (Ahebri 6:10) (3) Kulimba mtima ndi kukhulupirira n’zofunika makamaka masiku ano. Anthu ‘akudana nafe’ monga mmene Yesu ananeneratu. (Mateyu 24:9) Kuti tipirire, tifunika kudalira Mawu a Mulungu, kukhulupirira kuti mzimu wake uli nafe, ndi kulimba mtima kupitirizabe kulengeza uthenga wabwino. (4) Zitsanzo zikusonyeza kuti tikukumana ndi chitsutso pakalipano. Anthu onse anakhudzidwa mtima pamene wokambayo anasimba zimene abale athu akumana nazo ku Armenia, France, Georgia, Kazakhstan, Russia, ndi ku Turkmenistan. N’zoonadi kuti ino ndi nthaŵi yosonyeza kulimba mtima ndi kukhulupirira Yehova.

Wokamba nkhani womaliza anakamba nkhani yakuti “Kupita Patsogolo Mogwirizana ndi Gulu la Yehova.” Nkhaniyi inafotokoza mfundo zingapo zapanthaŵi yake. (1) Anthu kulikonse akuona kupita patsogolo kwa gulu la Yehova. Ntchito yathu yolalikira ndi misonkhano yathu yaikulu imachititsa anthu ambiri kutidziŵa. (2) Yehova wakhazikitsa gulu logwirizana. Mu 29 C.E., Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera n’cholinga choti asonkhanitse “zonse”​—amene akuyembekezera kupita kumwamba ndiponso amene akuyembekeza kudzakhala pa dziko lapansi​—kukhala banja la Mulungu logwirizana. (Aefeso 1:8-10) (3) Misonkhano yaikulu imasonyeza bwino kugwirizana kwathu kwa padziko lonse. Zimenezi zinaonekera bwino pa misonkhano yachigawo imene inachitikira ku France ndi ku Italy mu August. (4) Anthu anapanga chigamulo chokhudza mtima ku France ndi ku Italy. Wokamba nkhaniyo anafotokoza mfundo zochepa chabe za m’chigamulo chokhudza mtimacho. Mfundo zonse za m’chigamulocho zili m’munsimu.

Pamapeto pa nkhani yomaliza, mlendo amene anakamba nkhaniyo anaŵerenga chilengezo chokhudza mtima chochokera ku Bungwe Lolamulira. Mawu ena a chilengezocho anali akuti: “Tsopano ndiyo nthaŵi yodikira ndi kukhala tcheru, kuzindikira mmene zinthu pa dziko lapansi zikuchitikira. . . . Tikufuna kukudziŵitsani kuti Bungwe Lolamulira limakukondani kwambiri pamodzinso ndi anthu a Mulungu onse. Tikupempha Mulungu kuti akudalitseni kwambiri pochita chifuniro chake ndi mtima wonse.” Anthu a Yehova kulikonse ndi otsimikiza mtima kudikira m’nthaŵi zowawitsa zino ndi kupitabe patsogolo molimba mtima limodzi ndi gulu la Yehova logwirizana.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Pulogalamu ya msonkhano wapachakayi anailumikiza pa wailesi za kanema ku malo osiyanasiyana zimene zinachititsa kuti omvera akwane 13,757.

^ ndime 5 Misonkhano yowonjezera inachitikira ku Long Beach, California; Pontiac, Michigan; Uniondale, New York; ndi ku Hamilton, Ontario. Anthu onse amene anamvera kuphatikiza omwe anamvera pa wailesi za kanema m’malo ena anakwana 117, 885.

^ ndime 23 Ku France kunachitika misonkhano yaikulu yapadera itatu imene inachitikira m’mizinda ya Paris, Bordeaux, ndi Lyons. Ku Italy, nthumwi zochokera ku United States anazitumiza ku Rome ndi ku Milan, ngakhale kuti misonkhano yaikulu yokwana isanu ndi inayi inachitika panthaŵi imodzi.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 9-31]

Chigamulo

Mu August 2001, misonkhano yaikulu yapadera ya “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” inachitika ku France ndi ku Italy. Pa misonkhano imeneyo, anapereka chigamulo chokhudza mtima. Chigamulocho chinali motere:

“MONGA MBONI ZA YEHOVA, tonse amene tapezeka pa msonkhano waukuluwu wa ‘Aphunzitsi a Mawu a Mulungu’ talangizidwa ndi maphunziro opindulitsa kwambiri. Gwero la maphunziro ameneŵa talidziŵa bwinobwino. Maphunzirowa sanachokere kwa anthu. Achokera kwa amene mneneri Yesaya anam’nena kuti ndi “Mlangizi Wamkulu.” (Yesaya 30:20, NW) Onani zimene Yehova akutikumbutsa pa Yesaya 48:17. Akuti: ‘Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.’ Kodi amachita zimenezi motani? Njira yaikulu ndiyo kudzera m’Baibulo, buku limene latembenuzidwa ndiponso kufalitsidwa kuposa buku lina lililonse, mmene akutiuza mosapita m’mbali kuti: ‘Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.’​—2 Timoteo 3:16.

“Lerolino, anthu akufunikira kwambiri chiphunzitso chopindulitsa chimenechi. N’chifukwa chiyani tikutero? Poona kusintha kodabwitsa kwa zochitika m’dziko lino, kodi anthu anzeru akuzindikira chiyani? Palibenso china choposa mfundo iyi: Ngakhale kuti anthu ambirimbiri aphunzira maphunziro a m’dzikoli, makhalidwe abwino akusoŵeka momvetsa chisoni ndipo anthu satha kusiyanitsa chabwino ndi choipa. (Yesaya 5:20, 21) Anthu sadziŵa zimene zili m’Baibulo. Ngakhale kuti luso la umisiri lachititsa anthu kudziŵa zambiri pogwiritsa ntchito makompyuta, iwo sakupeza mayankho a mafunso monga akuti, Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Kodi zimene zikuchitika m’nthaŵi yathu ino zikutanthauza chiyani? Kodi tingayembekeze zinthu zabwino m’tsogolo? Kodi zidzatheka anthu kukhala mwamtendere ndiponso motetezeka? Ndiponso, m’malaibulale mumapezeka mabuku ambirimbiri ofotokoza nkhani zokhudza zochita zonse za anthu. Komabe, anthu akubwereza zolakwika zimene zinachitika kale. Upandu ukuwonjezeka. Matenda amene anthu ankaganiza kuti anawathetsa akuyambiranso, pamene matenda ena monga AIDS, akufalikira mochititsa mantha. Mabanja akusweka modetsa nkhaŵa. Malo okhala akuipitsidwa. Uchigaŵenga ndi zida za nkhondo zowononga kwambiri zikusokoneza mtendere ndi chitetezo. Mavuto osoŵa njira zowathetsera akuwonjezeka. Kodi ntchito yathu yoyenerera pothandiza anthu anzathu m’nthaŵi zowawitsa zino ndi yotani? Kodi pali maphunziro amene akufotokoza chifukwa chake anthu akukumana ndi mavuto oterewa ndiponso kusonyeza mmene tingakhalire ndi moyo wabwinopo pakalipano komanso kutipatsa chiyembekezo chodalirika cha zinthu zabwino m’tsogolo?

“Ntchito yathu imene Malemba akutiuza kuti tiichite ndiyo yakuti ‘timuke tiphunzitse anthu amitundu yonse, ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene Kristu anatilamulira.’ (Mateyu 28:19, 20) Yesu Kristu anapereka ntchito imeneyi ataukitsidwa, pamene analandira ulamuliro wonse kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ntchito imeneyi ndi yoposa ntchito zonse za anthu. Kwa Mulungu, ntchito yathuyi, yomwe imayang’ana zosoŵa zauzimu za anthu amene ali ndi njala yachilungamo, ili pa nambala wani. Pali zifukwa za m’Malemba zomveka zimene zingatichititse kusaiona ntchito imeneyi mwachibwanabwana.

“Zimenezi zimafuna kuti tiike patsogolo ntchito imeneyi m’moyo wathu. Mothandizidwa ndi Mulungu komanso ndi dalitso lake, ntchitoyi ichitika ngakhale kuti pali zosokoneza zambiri monga mavuto ndi kutsutsa kwa anthu achipembedzo ndi a ndale omwe cholinga chawo ndicho kulepheretsa pulogalamu yophunzitsa ya padziko lonseyi kuti isapite patsogolo. Tili ndi chidaliro ndiponso chikhulupiriro chakuti ntchitoyi idzachitikabe ndi kufika pamapeto ake oyenera. N’chifukwa chiyani tikutsimikiza zimenezi? Chifukwa chakuti Ambuye Yesu Kristu analonjeza kuti adzakhala nafe pa utumiki umene Mulungu watipatsa mpaka pamapeto a dongosolo la zinthu lino.

“Kuvutika kwa anthu kwatsala pang’ono kutha. Ntchito imene tili nayo pakalipano tiyenera kuimaliza mapeto asanafike. Motero, ife monga Mboni za Yehova, tikutsimikiza mtima kuchita izi:

“Choyamba: Monga atumiki odzipatulira, tikutsimikiza mtima kuika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wathu ndi kupitiriza kukula mwauzimu. Pofuna kukwaniritsa zimenezi, pemphero lathu n’logwirizana ndi mawu amene ali pa Salmo 143:10: ‘Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga.’ Zimenezi zimafuna kuphunzira kwambiri, kuyesetsa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kuchita phunziro laumwini ndi kufufuza nkhani. Kuti kupita kwathu patsogolo kuonekere kwa anthu onse, tidzachita zonse zimene tingathe kukonzekera ndiponso kupindula mokwanira ndi maphunziro a Mulungu amene timalandira pa misonkhano ya mpingo, yapadera ndi yadera, yachigawo ndiponso ya mayiko.​—1 Timoteo 4:15; Ahebri 10:23-25.

“Chachiŵiri: Pofuna kuti Mulungu atiphunzitse, tidzadya pa gome lake nthaŵi zonse ndipo tidzamvera chenjezo la Baibulo la ziphunzitso zonyenga za ziwanda. (1 Akorinto 10:21; 1 Timoteo 4:1) Tidzasamala kwambiri kupeŵa zinthu zovulaza monga chipembedzo chonyenga, ziphunzitso zachabe, chiwerewere, mliri wa zolaula, zosangalatsa zoipa, ndi zina zonse zimene ‘sizivomerezana nawo mawu a moyo.’ (Aroma 1:26, 27; 1 Akorinto 3:20; 1 Timoteo 6:3; 2 Timoteo 1:13) Pofuna kulemekeza ‘mphatso mwa amuna,’ amene ayeneretsedwa kuphunzitsa zinthu zabwino, tidzalemekeza kwambiri ntchito yawo ndipo tidzagwirizana nawo ndi mtima wonse posunga miyezo yoyera ndi yolungama ya makhalidwe abwino ndi yauzimu ya m’Mawu a Mulungu.​—Aefeso 4:7, 8, 11, 12, NW; 1 Atesalonika 5:12, 13; Tito 1:9.

“Chachitatu: Monga makolo achikristu, tidzalangiza ana athu ndi mtima wonse mwa mawu ndi chitsanzo chathu. Cholinga chathu chachikulu ndicho kuwathandiza kuyambira ali makanda kuti ‘aphunzire malembo opatulika okhoza kuwapatsa nzeru kufikira chipulumutso.’ (2 Timoteo 3:15) Sitidzaiŵala kuti kuwalera kwathu m’maleredwe ndi m’chilangizo cha Ambuye kudzawapatsa mpata waukulu woti ziwachitikire zimene Mulungu analonjeza kuti ‘zidzakhala bwino ndi iwo ndi kuti adzakhala nthaŵi yaikulu padziko’.​—Aefeso 6:1-4.

“Chachinayi: Tikakhala ndi nkhaŵa kapena kukumana ndi mavuto aakulu, choyamba ‘tidzadziŵitsa Mulungu zopempha zathu,’ tili ndi chikhulupiriro kuti ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse cha anthu’ udzatiteteza. (Afilipi 4:6, 7) Popeza tili m’goli la Kristu, tidzapeza mpumulo. Sitidzazengereza kutula nkhaŵa yathu kwa Mulungu podziŵa kuti amatisamalira.​—Mateyu 11:28-30; 1 Petro 5:6, 7.

“Chachisanu: Posonyeza kuthokoza Yehova chifukwa cha mwayi wokhala aphunzitsi a Mawu ake, tidzakonzanso zochita zathu kuti ‘tilunjike nawo bwino mawu a choonadi’ ndi ‘kukwaniritsa utumiki wathu.’ (2 Timoteo 2:15; 4:5) Popeza tikudziŵa bwinobwino zimene zimafunika, tikufuna ndi mtima wonse kufunafuna anthu oyenerera ndi kusamalira mbewu zimene tabzala. Ndiponso tidzapititsa patsogolo chiphunzitso chathu mwa kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba ambiri mogwira mtima. Zimenezi zidzatigwirizanitsa kwambiri ndi chifuniro cha Mulungu chakuti ‘anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.’​—1 Timoteo 2:3, 4.

“Chachisanu ndi chimodzi: M’zaka zonse za m’ma 1900 mpaka kufika m’zaka zino za m’ma 2000, anthu m’mayiko ambiri atsutsa Mboni za Yehova ndi kuzizunza m’njira zosiyanasiyana. Koma Yehova wakhala nafe. (Aroma 8:31) Mawu ake odalirika amatitsimikizira kuti ‘palibe chida chosulidwira ife’ kuti chidodometse, kuchepetsa, kapena kuimitsa ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu chidzapindula. (Yesaya 54:17) Sitingasiye kulankhula choonadi kaya m’nthaŵi zabwino kapena m’nthaŵi zovuta. Tatsimikiza mtima kugwira ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa mwachangu. (2 Timoteo 4:1, 2) Cholinga chathu ndicho kuuza anthu a mitundu yonse uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mokwanira monga momwe tingathere. Mwakuchita zimenezi, anthuwo adzakhalabe ndi mwayi wophunzira njira yodzapezera moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama. Monga khamu logwirizana la aphunzitsi a Mawu a Mulungu, tatsimikiza mtima kupitiriza kutsatira chitsanzo cha Mphunzitsi Wamkulu, Yesu Kristu, ndi kusonyeza makhalidwe a Mulungu omwe iye anali nawo. Tidzachita zonsezi n’cholinga choti tilemekeze ndi kutamanda Mlangizi wathu Wamkulu ndi Wopereka Moyo, Yehova Mulungu.

“Chonde, tiyeni tonse amene tili pa msonkhano uno amene tikugwirizana ndi chigamulochi tiyankhe kuti INDE!”

Pamene anthu okwana 160,000 amene anali pa misonkhano itatu ya ku France ndi 289,000 amene anali m’malo a misonkhano asanu ndi anayi ku Italy anafunsidwa funso lomaliza chigamulochi, anayankha mwamkokomo m’zilankhulo zosiyanasiyana kuti “Indee!”