Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Funani Mulungu ndi Mtima ndi Maganizo Anu

Funani Mulungu ndi Mtima ndi Maganizo Anu

Funani Mulungu ndi Mtima ndi Maganizo Anu

Chikristu choona chimalimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito maganizo ndi mtima kuti akhale ndi chikhulupiriro chosangalatsa Mulungu.

NGAKHALENSO woyambitsa Chikristu, Yesu Kristu, anaphunzitsa kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi ‘nzeru zathu zonse,’ kuwonjezera pa ‘mtima wathu wonse’ ndi ‘moyo wathu wonse.’ (Mateyu 22:37) Inde, maganizo ayenera kugwira ntchito yaikulu pa kulambira kwathu.

Popempha omvetsera ake kuti asinkhesinkhe pa zophunzitsa zake, Yesu kaŵirikaŵiri ankati: ‘Mukuganiza bwanji?’ (Mateyu 17:25; 18:12; 21:28; 22:42) Mofanana ndi zimenezi, mtumwi Petro analembera okhulupirira anzake pofuna ‘kuwadzutsa kuti alingalire moona.’ (2 Petro 3:1, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Mmishonale wakale amene anayenda kwambiri, mtumwi Paulo, analimbikitsa Akristu kugwiritsa ntchito “mphamvu . . . ya kulingalira” ndiponso ‘kuzindikira [okha] chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.’ (Aroma 12:1, 2, NW) Akristu angakhale ndi chikhulupiriro chokondweretsa Mulungu kokha mwa kulingalira mwakuya ndi mofatsa pa zimene amakhulupirira. Chikhulupiriro chimenecho chimawathandizanso kupirira mayesero.​—Ahebri 11:1, 6.

Pothandiza ena kuti akhale ndi chikhulupiriro choterocho, alaliki akale achikristu ‘ankathandizana nawo kuganiza pa Malemba, mwa kufotokoza ndi kutsimikizira mwa maumboni’ zomwe anaphunzitsazo. (Machitidwe 17:1-3, NW) Kuchita zinthu mwanzeru koteroko kunakopa anthu oona mitima. Mwachitsanzo, anthu angapo a mu mzinda wa Bereya, ku Makedoniya “analandira mawu [a Mulungu] ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu [zomwe Paulo ndi anzake anawafotokozera] zinali zotero.” (Machitidwe 17:11) M’lembali muli zinthu ziŵiri zofunika kuzidziŵa. Choyamba, Abereya anali ofunitsitsa kumvetsera Mawu a Mulungu; chachiŵiri, sanangovomereza mwachimbulimbuli kuti zinthu zomwe amva n’zolondola, koma anazitsimikizira mwa kuonanso m’Malemba. Mmishonale wachikristu, Luka, anadzichepetsa, nayamikira Abereya chifukwa cha zimenezi mwa kuwatcha kuti “mfulu, [“okonda kuphunzira,” NW].” Kodi inuyo mumakhala ndi maganizo okonda kuphunzira oterowo pankhani zauzimu?

Maganizo ndi Mtima Zimagwirira Ntchito Pamodzi

Monga tanena kale, kulambira koona kumakhudza maganizo ndiponso mtima wa munthu. (Marko 12:30) Taganizani mofatsa za fanizo tapereka m’nkhani yapita ija la mmisiri wopaka penti amene wapatsidwa ntchito. Iye wagwiritsa ntchito mitundu yolakwika popenta nyumba. Akanatsatira bwinobwino malangizo a bwana wake, akanaikapo mtima wake wonse pantchitoyo akanakhala wotsimikiza kuti mwininyumbayo adzasangalala ndi ntchito yakeyo. Ndi mmenenso zilili ndi kulambira kwathu.

Yesu anati: ‘Olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi.’ (Yohane 4:23) Motero mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa ichi ifenso . . . sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso [“chidziŵitso cholondola,” NW] cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti mukayende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo.” (Akolose 1:9, 10) “Chidziŵitso cholondola” chimenecho chimathandiza anthu oona mtima kuika mitima ndi miyoyo yawo mwachidaliro pa kulambira kwawo chifukwa ‘amalambira chimene akuchidziŵa.’​—Yohane 4:22.

Malinga ndi zifukwa zimenezi, Mboni za Yehova sizibatiza makanda kapena anthu amene angoyamba kumene kusonyeza chidwi chophunzira Baibulo, omwe sanaphunzire Malemba mozama. Yesu analamula otsatira ake kuti: “Phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Ophunzira Baibulo oona mtima angasankhe mwanzeru zoti achite pankhani ya kulambira, kokha ngati apeza chidziŵitso cholondola cha chifuniro cha Mulungu. Kodi inu mukuyesetsa kuti mupeze chidziŵitso cholondola chimenecho?

Kumvetsa Pemphero la Ambuye

Kuti tione kusiyana pakati pa kukhala ndi chidziŵitso cholondola cha Baibulo ndi kungodziŵa pang’ono chabe zimene Baibulo limanena, tiyeni tione pemphero lija limene ambiri amalitcha kuti Pemphero la Atate Wathu, kapena Pemphero la Ambuye, lolembedwa pa Mateyu 6:9-13.

Anthu ambiri amalakatula nthaŵi ndi nthaŵi kutchalitchi pemphero lachitsanzo limeneli la Yesu. Koma kodi ndi angati omwe aphunzira tanthauzo lake, makamaka mbali yoyambirira ya pempheroli yonena za dzina la Mulungu ndiponso Ufumu wake? Nkhanizi ndi zofunika kwambiri moti Yesu anaziika koyambirira kwa pempheroli.

Limayamba motere: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe,” kutanthauza kuti lichotsedwe chodetsa. Onani kuti Yesu ananena za kupempherera dzina la Mulungu kuti liyeretsedwe. Anthu ambiri, mfundoyi imawapangitsa kufunsa mafunso aŵiri. Loyamba, kodi dzina la Mulungu ndi ndani? Ndipo lachiŵiri, n’chifukwa chiyani likufunika kuyeretsedwa?

Yankho la funso loyambali lingapezeke m’malo oposa 7,000 m’Baibulo m’zinenero zake zoyambirira. Amodzi mwa malowo ndi Salmo 83:18. Pamenepo pamati: ‘Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.’ Ponena za dzina la Mulungu, lakuti Yehova, Eksodo 3:15 amati: “Ili ndi dzina langa nthaŵi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwomibadwo.” * Komano kodi n’chifukwa chiyani dzina la Mulungu, lomwe ndi chizindikiro chenicheni cha udongo ndi chiyero, lifunika kuyeretsedwa? Chifukwa chakuti ena alitonza ndi kulisinjirira kungoyambira pachiyambi penipeni pa mbiri ya anthu.

Mu Edene, Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti adzafa akadya chipatso choletsedwa. (Genesis 2:17) Satana mopanda mantha anatsutsana ndi Mulungu, pamene anauza Hava kuti: “Kufa simudzafayi.” Mwa kunena mawuŵa, Satana anaimba mlandu Mulungu kuti ndi wonama. Komatu, sanasiyire pompo. Anapitiriza kutonza dzina la Mulungu, nauza Hava kuti popanda chifukwa chomveka Mulungu anali kumana mkaziyo nzeru yofunika kwambiri. “Chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya [zipatso za mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa], adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” Ati kum’namiza kwake!​—Genesis 3:4, 5.

Mwa kudya chipatso choletsedwacho, Adamu ndi Hava anakhala kumbali ya Satana. Kuchokera nthaŵi imeneyo anthu ambiri, modziŵa kapena mosadziŵa, awonjezera pa chitonzo choyambirira chimenecho mwa kukana miyezo yolungama ya Mulungu. (1 Yohane 5:19) Anthu akusinjirirabe Mulungu mwa kumuimba mlandu chifukwa cha mavuto awo​—ngakhale mavutowo atadza chifukwa cha njira zawo zoipa. “Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova.” (Miyambo 19:3) Kodi mukuona chifukwa chake Yesu, yemwe anali kukondadi Atate wake, anapemphera kuti dzina Lake liyeretsedwe?

“Ufumu Wanu Udze”

Atapempherera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, Yesu anati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Pamawu ameneŵa, tingafunse kuti: ‘Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Ndipo kubwera kwake kukukhudzana bwanji ndi kuchitika kwa chifuno cha Mulungu pansi pano?’

M’Baibulo, liwu lakuti “ufumu” makamaka limatanthauza “ulamuliro wa mfumu.” Chotero, ndi zoonekeratu kuti Ufumu wa Mulungu ndi ulamuliro, kapena boma, la Mulungu, lokhala ndi mfumu yosankhidwa ndi iye. Mfumu imeneyi sangakhale winanso koma Yesu Kristu amene anaukitsidwa​—“Mfumu ya Mafumu, ndi Mbuye wa Ambuye.” (Chivumbulutso 19:16; Danieli 7:13, 14) Ponena za Ufumu wa Mulungu Waumesiya wolamulidwa ndi Yesu Kristu, mneneri Danieli analemba kuti: “Masiku a mafumu aja [maboma a anthu omwe akulamulira masiku ano] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire,” kutanthauza kuti, kosatha.​—Danieli 2:44.

Inde, Ufumu wa Mulungu udzakhala ndi mphamvu zonse padziko lapansi lino, n’kuchotsapo kuipa konse ndi kulamulira “chikhalire,” kutanthauza kuti, kosatha. Chotero, Ufumu wa Mulungu ndiwo njira yomwe Yehova adzayeretsera dzina lake, kulichotsa chitonzo chonse chochitidwa ndi Satana ndi anthu oipa.​—Ezekieli 36:23.

Mofanana ndi maboma onse, Ufumu wa Mulungu uli ndi anthu omwe udzalamulire. Kodi ameneŵa ndi ndani? Baibulo limayankha kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Mofanana ndi mawuŵa, Yesu anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” Ndithudi, ameneŵa ali ndi chidziŵitso cholondola ponena za Mulungu, chomwe ndi chofunika kuti apeze moyo.​—Mateyu 5:5; Yohane 17:3.

Kodi mutha kuona m’maganizo mwanumo dziko lonse lapansi litadzaza ndi anthu ofatsa, oleza mtima omwe amakondadi Mulungu ndiponso amakondanadi wina ndi mnzake? (1 Yohane 4:7, 8) Ndi zimene Yesu anapempherera pamene ananena kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” Kodi mukumvetsa chifukwa chake Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera motero? Chofunika kuposa zimenezi, kodi mukuona mmene kukwaniritsidwa kwa pemphero limenelo kukukukhudzirani inuyo panokha?

Anthu Ambiri Tsopano Akuthandizidwa Kuganiza pa Malemba

Yesu ananeneratu za ntchito ya padziko lonse ya maphunziro auzimu yolengeza za Ufumu wa Mulungu womwe ukubwerawo. Iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro [cha dziko, kapena dongosolo lamakonoli].”​—Mateyu 24:14.

Padziko lonse lapansi anthu ngati sikisi miliyoni a Mboni za Yehova akuuza anansi awo uthenga wabwino umenewo. Akukupemphani kuti muphunzire zambiri ponena za Mulungu ndi Ufumu wake mwa ‘kusanthula m’malembo’ pogwiritsa ntchito mphamvu yanu ya kulingalira. Kuchita zimenezo kudzalimbitsa chikhulupiriro chanu ndipo mudzasangalala chifukwa cha chiyembekezo chodzakhala m’paradaiso padziko lapansi, amene ‘adzadzale ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’​—Yesaya 11:6-9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Akatswiri ena amakonda kugwiritsa ntchito dzina lakuti “Yahweh” m’malo mwa “Yehova.” Ngakhale zili choncho, otembenuza mabaibulo amakono ambiri achotsa dzina la Mulungu m’mabaibulo awo, ndi kuikamo mayina aulemu omwe angaperekedwe kwa aliyense monga “Ambuye” kapena “Mulungu.” Kuti mudziŵe zambiri zokhudza dzina la Mulungu, onani buku lakuti Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 8]

TSANZIRANI MPHUNZITSI WAMKULU

Yesu kaŵirikaŵiri ankaphunzitsa mwa kulongosola nkhani zinazake za m’Baibulo. Mwachitsanzo, ataukitsidwa analongosolera ophunzira ake aŵiri omwe anaima mutu ndi imfa yake za udindo wake pa chifuno cha Mulungu. Luka 24:27 amati: “Anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za Iye yekha.”

Onani kuti Yesu anasankha nkhani yoti akambirane nawo, nkhani yonena za “Iye yekha,” Mesiya. Onaninso kuti m’nkhani yakeyo, anagwira mawu “m’malembo onse.” Kwenikweni, Yesu anaphatikiza maumboni amphamvu kwambiri a m’Baibulo onga zidutswa zomwazikana za chithunzi, zomwe zinathandiza ophunzira kutha kuona bwino choonadi chauzimu. (2 Timoteo 1:13) Chifukwa cha zimenezi, ophunzirawo sanangodziŵa zinthu koma anakhudzidwanso mtima kwambiri. Nkhaniyo imati: “Anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m’kati mwathu nanga mmene analankhula nafe m’njira, mmene anatitsegulira malembo?”​—Luka 24:32.

Mboni za Yehova zimayesetsa kutsanzira njira za Yesu mu utumiki wawo. Zipangizo zawo zabwino kwambiri zothandiza pophunzira ndizo buku lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndi lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Mabuku ameneŵa amafotokoza nkhani zambiri zochititsa chidwi za m’Baibulo, monga: “Kodi Mulungu Ndani?,” “Kodi Mulungu Waloleranji Kuvutika?,” “Kodi Mungachipeze Motani Chipembedzo Choona?,” “Ano Ndiwo Masiku Otsiriza!,” ndi “Kumanga Banja Lolemekeza Mulungu.” Phunziro lililonse lili ndi malemba ankhaninkhani.

Masukani kulankhula ndi Mboni za Yehova m’dera lanu kapena kulembera kalata ku adiresi yomwe ili patsamba 2 la magazini ino kuti muphunzire nkhanizi ndiponso zina pa phunziro la Baibulo la panyumba laulere.

[Chithunzi]

M’fikeni pamtima wophunzira wanu mwa kukambirana naye mfundo zinazake za m’Baibulo

[Zithunzi patsamba 7]

Kodi mukuzindikira tanthauzo la pemphero lachitsanzo la Yesu?

“Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe . . . ”

“Ufumu wanu [Waumesiya] udze . . . ”

“Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano”