Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mufunika Kuganiza Musanakhulupirire?

Kodi Mufunika Kuganiza Musanakhulupirire?

Kodi Mufunika Kuganiza Musanakhulupirire?

“Pali anthu ochuluka kwambiri ‘opembedza’ omwe amangotsata miyambo ya chipembedzo popanda kuganiza,” analemba motero mkulu wa seminale ina yophunzitsa za Mulungu ku United States. Anapitiriza ndi kuti: “Amangofuna kukhulupirira zilizonse ‘popanda kufunsa umboni wotsimikizira zimenezo.’”

MFUNDO yomwe anali kunena apa n’njakuti anthu ambiri omwe amati amakhulupirira zimene chipembedzo chawo chimaphunzitsa saganiza kuti aone chifukwa chomwe amakhulupirira zinthu zimenezo kapena ngati zomwe amakhulupirirazo zili ndi maziko enieni. N’chifukwa chake ambiri amakana kukambirana za chipembedzo.

N’zomvetsa chisoni kuti miyambo inanso monga kupembedza mafano ndiponso kulakatula mapemphero mobwerezabwereza siilimbikitsa anthu kuganiza. Miyambo imeneyi limodzi ndi nyumba zomangidwa mochititsa kaso, mawindo okhala ndi magalasi opentapenta ndiponso nyimbo zachikoka, ndi zinthu zokhazo zomwe anthu ambiri opembedza amadziŵa. Ngakhale kuti matchalitchi ena amati zimene amakhulupirira zili m’Baibulo, uthenga wawo wakuti, ‘khulupirira Yesu ndipo udzapulumuka’ sulimbikitsa anthu kuti aphunzire Baibulo mozama. Ena amalalikira uthenga woti Chikristu chifunika kuthandiza kukonza zinthu pa mavuto a chikhalidwe cha anthu ndi zachuma kapena m’ndale. Kodi chachitika n’chiyani chifukwa cha zonsezi?

Ponenapo za mmene zinthu zilili ku North America, mwamuna wina wolemba nkhani zachipembedzo anati: “Chikristu . . . langokhala dzina chabe, [ndipo] anthu ake saphunzitsidwa bwino za chikhulupiriro chawo.” Mwamuna wina wochita kafukufuku anafika mpaka ponena kuti dziko la United States ndi “dziko la anthu osadziŵa Baibulo.” Kunena chilungamo, ndemanga zimenezi zikukhudzanso mayiko ena kumene amati chipembedzo chawo ndi Chikristu. Nazonso zipembedzo zochuluka zomwe si zachikristu sizilimbikitsa anthu kuganiza. M’malo mwake zimalimbikitsa kulakatula mavesi, kupemphera mwamwambo, ndiponso mitundu yosiyanasiyana ya kusinkhasinkha kofuna kudziŵa zinsinsi za Mulungu. Sizilimbikitsa anthu kuganiza mwanzeru ndiponso zaphindu.

Ngakhale zili choncho, anthu omwewo amene saganiza kwambiri kuti aone ngati zimene amakhulupirira pa chipembedzo chawo zili zolondola kapena zoona, amakonda kuganiza kwambiri pa nkhani zina m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Munthu amati akafuna kugula galimoto, amachita kafukufuku woopsa ngakhale kuti tsiku lina adzakaitaya. Kodi sizikukudabwitsani kuti munthu ngati ameneyu amati akam’funsa za chipembedzo chake amangoti, ‘Makolo anga ankakonda chipembedzo chimenechi, ndiye inenso ndimakonda chomwechi’?

Ngati tikufunitsitsa kusangalatsa Mulungu, kodi zomwe timakhulupirira ponena za iye sitiyenera kuzilingalira mozama kuti tione ngati zili zolondola? Mtumwi Paulo ananena za anthu ena opembedza m’masiku ake omwe anali “ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso [cholondola, NW].” (Aroma 10:2) Tingayerekeze anthu oterowo ndi mmisiri wopaka penti amene wapatsidwa ntchito yopenta nyumba. Mmisiriyo akugwira ntchitoyo mwakhama kwambiri koma akugwiritsa ntchito mitundu yolakwika ya penti chifukwa chosamvera malangizo a mwininyumbayo. Iye angasangalale ndi zimene wachita, koma kodi mwininyumbayo adzasangalala nazo?

Pankhani ya kulambira koona, kodi n’chiyani chimene chimasangalatsa Mulungu? Baibulo limayankha kuti: “Ichi n’chokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; amene afuna anthu onse apulumuke nafike, pozindikira choonadi [“pa chidziŵitso cholondola cha choonadi,” NW].” (1 Timoteo 2:3, 4) Ena angaganize kuti n’zosatheka kupeza chidziŵitso choterocho chifukwa cha kuchuluka kwa zipembedzo masiku ano. Koma taganizani​—ngati Mulungu akufuna kuti anthu afike pa chidziŵitso cholondola cha choonadi, kodi iye angachite zachinyengo mwa kuwabisira choonadicho? Malingana ndi Baibulo, sangatero, chifukwa limati: “Ukam’funafuna [Mulungu] udzam’peza.”​—1 Mbiri 28:9.

Kodi Mulungu amadzidziŵikitsa motani kwa anthu amene akumufunitsitsa? Nkhani yotsatirayi ipereka yankho lake.