Kuphunzira Kulibe Msinkhu
Kuphunzira Kulibe Msinkhu
AKSENIYA, omwe ndi mayi okalamba, anabadwa m’chaka cha 1897. Anali ndi ana aakazi atatu, wamwamuna mmodzi, zidzukulu 15, ndi zidzukulutudzi 25. Nthaŵi zonse ankachita zimene makolo awo anawaphunzitsa. Ngakhale kuti a Kseniya anabwera ku Moscow chifukwa chothaŵa nkhondo ku lipabuliki la Abkhaz, limene lili pakati pa Black Sea ndi Caucasus, ankasangalala ndi moyo, makamaka ndi chipembedzo cha makolo awo.
M’chaka cha 1993, Meri, mwana wamkazi wa a Kseniya anakhala m’modzi wa Mboni za Yehova. Meri anayamba kuwauza a Kseniya za Yehova Mulungu ndi Baibulo, koma sankamvetsera. A Kseniya ankakonda kumuuza mwana wawoyo kuti, “Ndakalamba kwambiri, sindingaphunzirenso zinthu zatsopano.”
Ngakhale zinali choncho, mwana wawoyo, Meri; mkazi wa mdzukulu wawo dzina lake Londa; ndiponso zidzukulutudzi zawo, Nana ndi Zaza, omwe ndi Mboni za Yehova, anapitiriza kuwauza za Baibulo. Tsiku lina usiku m’chaka cha 1999, anawaŵerengera a Kseniya lemba limene linawafika pamtima. Linali ndi mawu olimbikitsa amene Yesu ananena kwa atumwi ake okhulupirika pamene anali kukhazikitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. (Luka 22:19, 20) A Kseniya ali ndi zaka 102, anaganiza usiku umenewo kuti ayambe kuphunzira Baibulo.
A Kseniya akuti: “Ndamvetsa cholinga cha moyo ndili ndi zaka 102. Tsopano ndadziŵa kuti palibe chinthu chabwino choposa kutumikira Yehova, Mulungu wathu wabwino ndi wachikondi. Ndidakali wanyonga ndi wanthanzi. Ndimatha kuŵerenga wopanda magalasi ndiponso kucheza bwinobwino ndi banja langa.”
A Kseniya anabatizidwa pa November 5, 2000. Iwo akuti: “Tsopano ndapereka moyo wanga kwa Yehova kuti ndim’tumikire mwachikondi. Ndimagaŵira magazini ndi mathirakiti n’takhala pansi pa siteji ya basi yapafupi ndi kunyumba kwanga. Nthaŵi zambiri achibale amabwera kudzandiona, ndipo ndimawauza mosangalala choonadi cha Yehova.”
A Kseniya akudikirira nthaŵi imene ‘mnofu wawo udzakhala se, woposa wa mwana, ndi kubwerera ku masiku a ubwana wawo.’ (Yobu 33:25) Ngati munthu wa zaka zoposa 100 akuona kuti kuphunzira Baibulo kuti udziŵe cholinga cha moyo kulibe msinkhu, nanga inu?