“Ndinkafuna Kutumikira Mulungu”
Olengeza Ufumu Akusimba
“Ndinkafuna Kutumikira Mulungu”
“TULUKANI mmenemo, anthu anga.” Amenewo anali mawu a mngelo omwe mtumwi Yohane anamva m’zaka za zana loyamba C.E. Lerolino anthu miyandamiyanda oona mtima alabadira mawuŵa ndi kuthaŵa mu ‘Babulo Wamkulu,’ ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:1-4) Mwa anthu ameneŵa pali mwamuna wina dzina lake Wilner wa ku Haiti, yemwe akusimba zimene zinam’chitikira.
“Ndinabadwa mu 1956, m’banja lachikatolika lokonda kupembedza kwambiri, lomwe linkakhala m’tauni ina yaing’ono ya St. Marc, ku Haiti. Banja lathu linali ndi chimwemwe chodzala tsaya pamene anandisankha, pamodzi ndi anthu ena aŵiri a m’tauni yomwe tinkakhala, kupita ku seminale ku St. Michel de l’Atalaye, m’Haiti momwemo. Kenako, mu 1980, anatitumiza ku Stavelot, ku Belgium, kuti tikaphunzire zambiri. Kumeneko tinakaphunziranso pa yunivesite ya Chikatolika.
“Poyamba ndinali ndi chidwi chachikulu chofuna kukhala wansembe. Tsiku lina m’chipinda chodyera, wansembe yemwe ankayang’anira gulu lathu anandipempha kuti nditsalire mphindi zingapo chifukwa choti anali ndi nkhani yoti andiuze. Ndinachita mantha kwambiri pamene ananena mosapita m’mbali kuti akufuna atachita nane zachiwerewere! Ndinamukanira zimenezo koma zinandikhumudwitsa kwambiri. Ndinalembera kalata kunyumba yofotokoza nkhaniyo ndipo pambuyo pa miyezi ingapo, ndinachoka pa seminaleyo, ngakhale kuti iwo sizinawasangalatse. Ndinakakhala kumudzi n’kumaphunzira ntchito ina.
“Nditabwerera ku St. Marc, sindinkakhulupiriranso Tchalitchi cha Katolika. Komabe, ndinkafuna kutumikira Mulungu, koma sindinadziŵe chochita. Ndinapita ku tchalitchi cha Adventist, tchalitchi cha Ebenezer, ndiponso ku tchalitchi cha Mormon. Ndinali kungopupulikapupulika mwauzimu.
“Kenako ndinakumbukira kuti nthaŵi yomwe ndinali kuseminale ku Belgium, ndinkaŵerenga Baibulo la Crampon. M’Baibulo limenelo ndinapeza kuti Mulungu ali ndi dzina. Choncho, pogwiritsa ntchito dzina lakelo, ndinapemphera kuchokera pansi pa mtima kuti Mulungu andithandize kupeza chipembedzo choona.
“Patapita nthaŵi pang’ono, anthu aŵiri a Mboni za Yehova anasamukira komwe ine ndimakhala. Anali ofatsa, aulemu, ndiponso olemekezeka. Khalidwe lawo linandichititsa kaso kwambiri. Tsiku lina mmodzi wa a Mboniwo, anandiitana kuti ndikakhale nawo pa Chikumbutso chapachaka cha imfa ya Kristu. Ndinasangalala kwambiri ndi msonkhanowo ndipo ndinavomera kuchita phunziro la Baibulo nthaŵi zonse ndi a Mboniwo. Miyezi isanu ndi umodzi, ndinakhutira kuti ndapeza njira yoona yotumikirira Mulungu. Ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa pa November 20, 1988.”
Patapita nthaŵi, Wilner anayamba utumiki wa nthaŵi zonse. Panopo ndi mkulu mu mpingo. Iye ndi mkazi wake, ndi ana awo aŵiri, akutumikira mosangalala mu mpingo.
[Chithunzi patsamba 9]
Chifukwa choŵerenga Baibulo, Wilner anapeza kuti dzina la Mulungu ndi Yehova