Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Apasitala Aŵiri Omwe Anayamikira Zimene Russell Analemba

Apasitala Aŵiri Omwe Anayamikira Zimene Russell Analemba

Apasitala Aŵiri Omwe Anayamikira Zimene Russell Analemba

MU 1891, Charles Taze Russell, amene anagwira ntchito yaikulu kwambiri pakati pa Akristu oona olambira Yehova, anakacheza ku Ulaya kwa nthaŵi yoyamba. Malinga ndi malipoti ena, ali paulendowo Russell anaima mu mzinda wa Pinerolo, ku Italy. Ali mu mzindawu, iye anakumana ndi Pulofesa Daniele Rivoire yemwe anali pasitala wakale wa gulu lachipembedzo la Awadensi. * Ngakhale kuti Rivoire atasiya upasitala anapitirizabe kugwirizana kwambiri ndi Awadensi, iye anali ndi mtima wofuna kuphunzira ndipo anaŵerenga mabuku ambiri amene C. T. Russell analemba.

Mu 1903, Rivoire anatembenuzira m’Chitaliyana buku la Russell lakuti The Divine Plan of the Ages, ndipo analisindikizitsa ndi ndalama zake. Izi zinachitika padakali zaka zingapo kuti eni bukuli alisindikize m’Chitaliyana. M’mawu oyamba m’bukuli, Rivoire analemba kuti: “Ambuye ateteze buku ili loyamba m’Chitaliyana. Alidalitse kuti, ngakhale lili ndi mwina mophophonya, lithandizire kulemekeza dzina lake lopatulika kwambiri ndiponso lilimbikitse ana ake olankhula Chitaliyana kukhala opembedza kwambiri. Mitima ya onse omwe, chifukwa choŵerenga bukuli, akuzindikira kuti m’cholinga ndiponso m’chikondi cha Mulungu mwagona nzeru, kudziŵa zinthu, ndiponso chuma chakuya, iyamike Mulungu mwiniyo, yemwe chisomo chake chathandiza kuti ntchito yosindikiza bukuli itheke.”

Rivoire anayambanso kutembenuzira m’Chitaliyana magazini ya Zion’s Watchtower and Herald of Christ’s Presence. Magaziniyi, yomwe ndi Nsanja ya Olonda tsopano, inatuluka mu 1903 monga magazini yofalitsidwa kamodzi m’miyezi itatu. Ngakhale kuti Pulofesa Rivoire sanakhalepo Wophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinkadziŵika nalo panthaŵiyo, iye anasonyeza chidwi chachikulu pantchito yofalitsa uthenga wa Baibulo wofotokozedwa m’mabuku a Ophunzira Baibulo.

“Zinali Ngati Kuti Mamba Agwa Kuchoka m’Maso Mwanga”

Pasitala wina wachiwadensi yemwe anayamikira kwambiri mabuku a Russell anali Giuseppe Banchetti. Abambo ake a Giuseppe, omwe anatembenuka kuchoka m’Chikatolika, anaphunzitsa Giuseppe maphunziro a Awadensi. Mu 1894, Giuseppe anakhala pasitala ndipo anatumikira m’magulu osiyanasiyana a Awadensi ku Apulia ndi Abruzzi ndiponso pazilumba za Elba ndi Sicily.

Buku lachitaliyana la Russell lakuti Divine Plan of the Ages litafalitsidwa mu 1905, Banchetti analemba ndemanga yosangalatsa kwambiri ya malingaliro ake pa bukuli. Ndemangayi inasindikizidwa m’magazini yachipulotesitanti yotchedwa La Rivista Cristiana. Banchetti analemba kuti, buku la Russell “kwa ife ndi chikwangwani choŵala kwambiri ndiponso choona chomwe Mkristu aliyense angatsatire pofuna kuti apindule ndiponso akhutire pophunzira Malemba Opatulika . . . Nditangoliŵerenga, zinali ngati kuti mamba agwa kuchoka m’maso mwanga, moti njira yopita kwa Mulungu inali yowongoka ndi yosavuta. Ngakhale zinthu zomwe zinkaoneka kuti ndi zotsutsana nthaŵi zonse zinatheratu. Ziphunzitso zomwe kalelo zinkavuta kumvetsa zinakhala zophweka ndi zosavuta kuzivomereza. Zinthu zomwe m’mbuyomo sindinkazimva m’pang’ono pomwe zinamveka bwino. Sizinandivute m’pang’ono pomwe kuona cholinga chapadera kwambiri chopulumutsa dzikoli kudzera mwa Kristu, ndiye ngati kuti ndifuulire pamodzi ndi Mtumwi, kuti: Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu!”​—Aroma 11:33.

Malinga ndi zimene ananena Remigio Cuminetti mu 1925, Banchetti “anagwirizana kwambiri” ndi ntchito ya Ophunzira Baibulo ndipo ziphunzitso zomwe iwo ankafotokoza ‘zinam’gwira mtima kwambiri.’ Banchetti, ankafunanso kudziŵikitsa ziphunzitso zimenezo, mwanjira yakeyake.

Kuchokera m’zimene Banchetti analemba, n’zoonekeratu kuti mofanana ndi Mboni za Yehova, iye ankakhulupirira kuti anthu adzaukitsidwa padziko lonse, malinga ndi zimene Malemba amaphunzitsa. Anagwirizananso ndi Ophunzira Baibulo pamene anafotokoza kuti chaka chimene Yesu anafa chinali chitaikidwa ndiponso kuululidwa ndi Mulungu mu ulosi wa Danieli wa masabata 70. (Danieli 9:24-27) Pofotokoza kusagwirizana kwake ndi ziphunzitso za tchalitchi chake, iye ananena mobwerezabwereza kuti Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu chiyenera kuchitidwa kamodzi kokha pachaka, “tsiku lenileni limene mwambowu unachitika.” (Luka 22:19, 20) Anakana chiphunzitso cha Darwin chakuti zinthu zimasanduka kuchokera ku zinthu zina, ndipo ankanena motsimikiza kuti Akristu oona sayenera kumenya nawo nkhondo.​—Yesaya 2:4.

Panthaŵi ina yake, Banchetti anali kukambirana ndi mwamuna wina dzina lake J. Campbell Wall za mabuku a Russell. Poyankha mawu a Wall otsutsa mabuku a Russell, Banchetti anati: “Ndikukhulupirira kuti utaŵerenga mavoliyumu asanu ndi imodzi a Russell, ungapeze chimwemwe chachikulu, ndipo ungandithokoze kuchokera mu mtima. Sindikometsa chiphunzitso chilichonse; koma ndinaŵerenga mabuku amenewo zaka khumi ndi chimodzi zapitazo, ndipo ndimathokoza Mulungu tsiku lililonse chifukwa chondipatsa muuni woterowo ndiponso chilimbikitso choterocho mwa ntchito yokhala ndi maziko onse pa Malembo Opatulika.”

“Mvetserani, Mvetserani, Mvetserani”

N’zochititsa chidwi kwambiri kuti apasitala aŵiri achiwadensi​—Daniele Rivoire ndi Giuseppe Banchetti​—anavomereza ndiponso anayamikira mmene Russell anafotokozera Baibulo. Banchetti analemba kuti: “Ndikunena kuti palibe mmodzi wa ife a Evangelical, ngakhale mmodzi wa apasitala athu kapena mapulofesa a za maphunziro apamwamba a zaumulungu, palibe ngakhale mmodzi yemwe amadziŵa zonse. Ndipo tili ndi zambiri, zinthu zina zambiri zoti tiphunzire. . . . [Tiyenera] . . . kuyembekeza ndi kumvetsera, osaganiza kuti tikudziŵa zonse, ndipo osakana zomwe tapatsidwa kuti tiphunzire. Mmalo mwake, mvetserani, mvetserani, mvetserani.”

Chaka ndi chaka, anthu ambiri amamvetsera uthenga wa Ufumu womwe Mboni za Yehova zimapita nawo m’makomo mwawo. Kulikonseko, anthu ofuna kuphunzira, omwe ali ndi ludzu la choonadi cha Baibulo akulabadira pempho la Yesu lakuti: ‘Idza kuno, unditsate Ine.’​—Marko 10:17-21; Chivumbulutso 22:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Ankatchedwa Awadensi chifukwa cha Pierre Vaudès, kapena kuti Peter Waldo, mkulu wina wamalonda wa m’zaka za m’ma 1100 mu mzinda wa Lyons, ku France. Waldo anachotsedwa m’Tchalitchi cha Katolika chifukwa cha zikhulupiriro zake. Kuti mudziŵe zochuluka pankhani ya Awadensi, onani nkhani yakuti “Awadensi​—Gulu la Mpatuko Lomwe Linaloŵa Chipulotesitanti” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2002.

[Chithunzi patsamba 28]

Pulofesa Daniele Rivoire

[Chithunzi patsamba 29]

Giuseppe Banchetti

[Mawu a Chithunzi]

Banchetti: La Luce, April 14, 1926