Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Wabwino Mungaupeze Kuti?

Kodi Moyo Wabwino Mungaupeze Kuti?

Kodi Moyo Wabwino Mungaupeze Kuti?

M’mudzi wina waung’ono kumadzulo kwa Africa, mnyamata wina dzina lake Josué anachoka m’mudzimo kusiya abale ake ndi anzake. * Iye anapita m’tauni ina yaikulu kukafuna chuma. Komabe atangofika, zomwe ankayembekeza sanazipeze ndipo anazindikira kuti m’tauni si malo oti munthu angalemere msanga.

JOSUÉ anakhumudwa kwambiri poyesa kuzoloŵera moyo wam’tauni. Moyo wam’tauni womwe ankauganizira unali wosiyana kotheratu ndi womwe anaupeza. Josué analakalaka kubwerera kumudzi kuja komwe anasiya abale ake ndi anzake. Koma anaopa kuti anthu kumudziko akamuseka. Iye anadandaula kuti: ‘Anthu azikanena kuti ndine wolephera chifukwa ndalephera kukhala m’tauni.’

Iye analinso kuvutika maganizo kwambiri chifukwa choganizira kuti makolo ake adzakhumudwa kwabasi. Iwo ankamudalira kuti aziwathandiza. Akulimbana ndi maganizo ameneŵa, Josué anayamba ntchito yochotsa ulemu. Ankagwira ntchitoyo tsiku lonse, ndi kulandira ndalama zochepa kwambiri poyerekeza ndi zomwe ankaganiza. Popeza ankatopa kwambiri ndi ntchito yakeyo, nthaŵi yochita zinthu zachikristu zomwe ankaziona kukhala zofunika kwambiri, inkachepa mlungu uliwonse. Anali wokhumudwa ndi wosungulumwa chifukwa ankakhala kutali ndi abale ake ndiponso anzake apamtima. Tauni sinam’patse moyo wabwino womwe ankaufuna kwambiri.

Ngakhale kuti zochita ndiponso malo zimasiyana, zomwe zinachitikira Josué zimachitika kaŵirikaŵiri. Sikuti Josué zinamuchitikira zimenezi chifukwa choti anali ndi zolinga zadyera pochoka kumudzi ayi. Iye ankangofuna kupeza moyo wabwinopo basi. Ankaganiza moona mtima, kuti m’tauni ndi mmene akanapeza moyo woterowo osati kumudzi. N’zoona kuti nthaŵi zina munthu angapezedi chuma koma zimenezo sizimabweretsa moyo wabwino weniweni. Kwa Josué mwachionekere sunapezeke, ndipo n’kutheka kuti sungapezeke kwa ena ambiri omwe akufuna moyo wabwino. Izi zimatichititsa kufunsa kuti: ‘Kodi moyo wabwino n’chiyani?’

Anthu amaona moyo wabwino mosiyanasiyana. Buku lina lotanthauzira mawu limati, moyo wabwino ndiwo “kukhala wotetezeka” kapena “kukhala wopanda mantha kapena nkhaŵa.” Anthu ambiri akuona kuti “kukhala wotetezeka” kotheratu n’kosatheka lerolino. Iwo amakhala okhutira ndi moyo malinga ngati akukhala bwino ngakhale pali zinthu zomwe zingawaopse.

Nanga bwanji inuyo? Kodi mumaganiza kuti moyo wabwino mungaupeze kuti? Kodi mungaupeze m’tauni osati kumudzi monga ankaganizira Josué? Kodi kapena mungaupeze mutakhala ndi ndalama, mosaganizira kumene munazipeza ndalamazo kapena mmene munazipezera? Kapena kodi mungaupeze ngati mutakhala munthu wapamwamba? Kaya mumaganiza kuti moyo wabwino mungaupeze kuti, funso n’lakuti, kodi moyo umenewo udzakhala kwa nthaŵi yaitali bwanji kwa inu ndi banja lanu?

Tiyeni tikambirane mbali zitatu zomwe anthu ambiri amaganiza kuti ndizo zimadzetsa moyo wabwino. Mbali zake ndizo, malo okhala, ndalama, ndiponso udindo wapamwamba. Kenako tiona komwe tingapeze moyo wabwino weniweni.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha dzina.