Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yendani Motsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Mulungu

Yendani Motsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Mulungu

Yendani Motsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Mulungu

‘Yehova akukuphunzitsani kupindula.’​—YESAYA 48:17.

1. Kodi Mlengi amatsogolera motani anthu?

PAMENE asayansi akuyesetsa kuti adziŵe zambiri zomwe Mulungu analenga, amachita kakasi poona mphamvu zambiri zimene zili m’zinthu zimenezi. Dzuŵa lathuli, lomwe ndi nyenyezi yocheperapo kusiyana ndi nyenyezi zina, limatulutsa mphamvu zofanana ndi “mabomba amphamvu kwambiri okwana 100 biliyoni ophulika pa sekondi iliyonse.” Mlengi amalamulira ndi kutsogolera zinthu zakumwamba zamphamvu kwambiri zimenezo pogwiritsa ntchito mphamvu zake zopanda malire. (Yobu 38:32; Yesaya 40:26) Nanga bwanji ife anthu, amene anatipatsa ufulu wodzisankhira, amene tingathe kukhala ndi makhalidwe abwino, kuganiza mwanzeru ndiponso kumvetsa zinthu zauzimu? Kodi Mlengi wathu wasankha kutitsogolera m’njira zotani? Amatitsogolera pogwiritsa ntchito malamulo ndi mfundo za makhalidwe abwino zapamwamba, pamodzi ndi chikumbumtima chathu chophunzitsidwa bwino.​—2 Samueli 22:31; Aroma 2:14, 15.

2, 3. Kodi Mulungu amasangalala ndi kumvera kotani?

2 Mulungu amasangalala ndi zolengedwa zanzeru zimene zimasankha kumumvera. (Miyambo 27:11) Yehova, m’malo motikonza kuti tizingomvera popanda kuganiza monga maloboti omwe alibe nzeru, anatipatsa ufulu wodzisankhira kuti tisankhe kuchita zoyenera titadziŵa bwinobwino kufunika kwake ndi zotsatira zake.​—Ahebri 5:14.

3 Yesu, amene anasonyeza bwino mmene Atate wake alili, anauza ophunzira ake kuti: “Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu. Sinditchanso inu akapolo.” (Yohane 15:14, 15) Kale, kapolo analibe ufulu wosankha zochita. Anayenera kumvera zimene mbuye wake wamulamula kuchita. Koma, ubwenzi umapangika mwa kusonyezana makhalidwe osangalatsa. Tingakhale mabwenzi a Yehova. (Yakobo 2:23) Ubwenzi umenewu umalimba mwa kukondana nonse aŵiri. Yesu anagwirizanitsa kumvera Mulungu ndi chikondi pamene anati: “Ngati wina akonda Ine, adzasunga mawu anga; ndipo Atate wanga adzam’konda.” (Yohane 14:23) Popeza Yehova, Atate wathu, amatikonda ndipo amafuna kutitsogolera bwino, akutipempha kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino.

Mfundo za Makhalidwe Abwino za Mulungu

4. Kodi mfundo zamakhalidwe abwino n’chiyani?

4 Kodi mfundo za makhalidwe abwino n’chiyani? Mfundo ya makhalidwe abwino imatanthauza “choonadi chachikulu kapena chofunika kwambiri: lamulo, chiphunzitso, kapena mfundo zofunika kwambiri ndiponso zokhudza mbali zosiyanasiyana zomwe ndi maziko kapena pamene pamachokera malamulo ndi ziphunzitso zina.” (Webster’s Third New International Dictionary) Kulifufuza mosamala Baibulo kukuvumbula kuti Atate wathu wakumwamba amapereka malangizo ofunika kwambiri amene amakhudza zochitika ndiponso mbali za moyo zosiyanasiyana. Amachita zimenezi n’cholinga choti tipindule mpaka kalekale. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Tamvera mwananga, nulandire mawu anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa m’njira ya nzeru, ndakuyendetsa m’mayendedwe olungama.” (Miyambo 4:10, 11) Mfundo zofunika kwambiri zimene Yehova wapereka zimakhudza ubwenzi wathu ndi iye komanso ndi anthu anzathu, kulambira kwathu, ndiponso moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. (Salmo 1:1) Tiyeni tione zina mwa mfundo zamakhalidwe abwino zofunika kwambiri zimenezo.

5. Perekani zitsanzo za mfundo zina za makhalidwe abwino zofunika kwambiri.

5 Yesu pa za ubwenzi wathu ndi Yehova, anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Ndiponso, Mulungu amapereka mfundo zokhudza mmene tingachitire ndi anthu anzathu, monga Mfundo Yaikulu ya Makhalidwe Abwino imene imati: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12; Agalatiya 6:10; Tito 3:2) Pankhani ya kulambira, amatilangiza kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi.” (Ahebri 10:24, 25) Pa za moyo wa tsiku ndi tsiku, mtumwi Paulo ananena kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) M’Mawu a Mulungu muli mfundo zina za makhalidwe abwino zambirimbiri.

6. Kodi mfundo za makhalidwe abwino zimasiyana bwanji ndi malamulo?

6 Mfundo za makhalidwe abwino n’zothandiza. Ndizo mfundo zoona zofunika kwambiri, ndipo Akristu anzeru amaphunzira kuzikonda. Yehova anauzira Solomo kulemba kuti: “Tamvera mawu anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke ku maso ako; uwasunge m’kati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lawo lonse.” (Miyambo 4:20-22) Kodi mfundo za makhalidwe abwino zimasiyana bwanji ndi malamulo? Mfundo za makhalidwe abwino ndizo maziko a malamulo. Malamulo, amene nthaŵi zambiri amakhala achindunji, angagwire ntchito pa nthaŵi inayake kapena pa zochitika zinazake, koma mfundo za makhalidwe abwino zilibe nthaŵi. (Salmo 119:111) Mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu sizitha ntchito. Mawu amene mneneri Yesaya anamuuzira ndi oona. Amati: “Udzu unyala, duŵa lifota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.”​—Yesaya 40:8.

Ganizani ndi Kuchita Zinthu Motsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino

7. Kodi Mawu a Mulungu akutilimbikitsa bwanji kuganiza ndi kuchita zinthu motsatira mfundo za makhalidwe abwino?

7 “Mawu a Mulungu wathu” amatilimbikitsa mobwerezabwereza kuganiza ndi kuchita zinthu motsatira mfundo za makhalidwe abwino. Yesu atamufunsa kuti afotokoze Chilamulo mwachidule, anatchula mfundo ziŵiri zomveka. Ina inatsindika kukonda Yehova ndipo inayo inatsindika kukonda anthu anzathu. (Mateyu 22:37-40) Pochita zimenezi, Yesu anagwira mawu pang’ono mfundo zomwe zinali maziko a Chilamulo cha Mose zimene anazifotokoza mwachidule pa Deuteronomo 6:4, 5 kuti: “Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi; ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” Mwachionekere, Yesu anali kukumbukiranso malangizo a Mulungu amene ali pa Levitiko 19:18. Mawu a Mfumu Solomo omveka bwino, aafupi ndiponso a mphamvu amene anamaliza nawo buku la Mlaliki, anafotokoza mwachidule malamulo ambirimbiri a Mulungu. Anati: “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.”​—Mlaliki 12:13, 14; Mika 6:8.

8. N’chifukwa chiyani n’kothandiza kumvetsa bwino mfundo za makhalidwe abwino zofunika kwambiri za m’Baibulo?

8 Kumvetsa bwino mfundo zofunika kwambiri zimenezo kungatithandize kudziŵa ndi kugwiritsa ntchito malangizo ambiri osapita m’mbali. Ndiponso, ngati sitimvetsa bwinobwino ndi kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zofunika kwambiri, mwina sitingathe kusankha zochita mwanzeru ndipo chikhulupiriro chathu chingagwedere mosavuta. (Aefeso 4:14) Ngati mfundo za makhalidwe abwino zimenezo tiziika mumtima ndi m’maganizo athu, tidzakhala okonzeka kuzigwiritsa ntchito posankha zochita. Tikazigwiritsa ntchito mozindikira, zidzatipindulitsa.​—Yoswa 1:8; Miyambo 4:1-9.

9. N’chifukwa chiyani nthaŵi zina n’kovuta kuzindikira ndi kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo?

9 Kuzindikira ndi kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo n’kovutirapo kusiyana ndi kutsatira mpambo wa malamulo. Monga anthu opanda ungwiro, tingapewe kuganiza motsatira mfundo za makhalidwe abwino. Tingakonde atatipatsa lamulo losapita m’mbali pakafika poti tisankhe chochita kapena tikakumana ndi vuto lalikulu. Nthaŵi zina tingapemphe malangizo kwa Mkristu wokhwima, mwinamwake mkulu mumpingo, tikuyembekeza kuti atipatsa lamulo latchutchutchu lomwe likukhudza vuto lathulo. Komabe, Baibulo kapena mabuku othandiza kuphunzira Baibulo mwina sangapereke lamulo latchutchutchu, ndipo ngakhale atatipatsa lamulolo, mwina silingathandize m’mbali zonse. Mwina mungakumbukire kuti mwamuna wina anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, uzani mbale wanga agaŵane ndi ine chuma chamasiye.” Yesu anamuuza mwamunayo mfundo ya makhalidwe abwino yokhudza mbali zambiri m’malo mofulumira kupereka lamulo lothetsera kusiyana maganizo kwawo ndi mbale wakeyo. Anati: “Yang’anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse.” Motero Yesu anapereka langizo limene linkathandiza nthaŵi imeneyo ndipo n’lothandizabe lerolino.​—Luka 12:13-15.

10. Kodi kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo za makhalidwe abwino kumavumbula bwanji zolinga za mtima wathu?

10 Mwina mwaonapo anthu amene amamvera malamulo mokakamizika, poopa chilango. Kutsatira mfundo za makhalidwe abwino sikufuna kuti munthu atero mokakamizika. Mfundo za makhalidwe abwino zimalimbikitsa munthu amene akuzitsatirayo kuchita zimenezo kuchokera pansi pa mtima. Ndipotu, mfundo zambiri n’zoti munthu amene sazitsatira salandira chilango nthaŵi yomweyo. Zimenezi zimatipatsa mpata wosonyeza chifukwa chake timamvera Yehova, ndipo motero timasonyeza zolinga za mtima wathu. Chitsanzo n’cha Yosefe amene anakana kunyengerera kwa mkazi wa Potifara koti agone naye. Yosefe ankadziŵa mfundo ya kukhulupirika m’banja imene Mulungu anaika ngakhale kuti nthaŵi imeneyo Yehova anali asanapereke lamulo lochita kulemba loletsa kuchita chigololo ndiponso anali asanaike chilango chimene munthu angalandire ngati agona ndi mkazi wa mwini. (Genesis 2:24; 12:18-20) Tingaone m’yankho lake kuti mfundo zimenezo zinazika mizu m’maganizo mwake. Anati: “Nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?”​—Genesis 39:9.

11. Kodi mfundo za makhalidwe abwino za Yehova zifunika kutsogolera Akristu m’mbali ziti?

11 Lerolino, mfundo za makhalidwe abwino za Yehova zifunika kutsogolera Akristu pankhani za munthu payekha, monga ngati kusankha ocheza nawo, zosangalatsa, nyimbo, ndi mabuku amene timaŵerenga. (1 Akorinto 15:33; Afilipi 4:8) Chikumbumtima chathu ndi kuzindikira kwathu za makhalidwe abwino zidzatithandiza kugwiritsa ntchito mfundo za Mulungu pa zochitika zilizonse zimene tingakumane nazo, ngakhale pa nkhani za ife patokha. Koma tingachite zimenezi ngati tipitiriza kudziŵa zambiri, kumvetsa bwino, ndi kukonda Yehova ndi miyezo yake. Ngati tilola mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo kutitsogolera, sitidzafuna kuchita chinthu chosayenera chabe chifukwa choti lamulo la Mulungu silinatchule mwatchutchutchu. Ndiponso sitidzatsanzira anthu amene amayesa kuona kuti angafike pati asanaswe lamulo linalake. Tikuzindikira kuti kuchita zimenezi n’kovulaza.​—Yakobo 1:22-25.

12. Kodi chofunika kwambiri n’chiyani kuti mfundo za makhalidwe abwino zititsogolere?

12 Akristu okhwima mwauzimu amazindikira kuti chofunika kwambiri kuti titsatire mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu ndicho kudziŵa mmene Yehova amaionera nkhaniyo. Wamasalmo analangiza kuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.” (Salmo 97:10) Lemba la Miyambo 6:16-19 likutchula zinthu zina zimene Mulungu amadana nazo. Ilo likuti: “Ziripo zinthu zisanu ndi chimodzi Mulungu azida; ngakhale zisanu ndi ziŵiri zim’nyansa: maso akunyada, lilime lonama ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu mmangummangu; mboni yonama yonong’ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.” Tingapitirizebe kutsatira mfundo za makhalidwe abwino ngati kufuna kusonyeza mmene Yehova amaonera zinthu zimenezi kukutitsogolera.​—Yeremiya 22:16.

Zolinga Zabwino N’zofunika

13. Kodi Yesu anatsindika maganizo otani pa Ulaliki wake wa pa Phiri?

13 Kudziŵa ndi kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino kumathandizanso kuti tisamangolambira mwachiphamaso. Pali kusiyana pakati pa kutsatira mfundo za makhalidwe abwino ndi kuumirira malamulo mopitirira muyeso. Yesu anasonyeza bwino zimenezi pa Ulaliki wake wa pa Phiri. (Mateyu 5:17-48) Kumbukirani kuti omwe anali kumumvetsera Yesu anali Ayuda, motero Chilamulo cha Mose chinayenera kutsogolera makhalidwe awo. Komatu kunena zoona, Chilamulocho ankachiona molakwika. Anali kuumirira kuti munthu azitsatira zimene Lamulo linanena ngakhale atachita mosemphana ndi tanthauzo lenileni la lamulolo. Ndiponso anali kulimbikitsa kwambiri miyambo yawo, n’kuiika patsogolo kuposa ziphunzitso za Mulungu. (Mateyu 12:9-12; 15:1-9) Motero, sanawaphunzitse anthu kuganiza motsatira mfundo za makhalidwe abwino.

14. Kodi Yesu anathandiza bwanji omvera ake kuganiza motsatira mfundo za makhalidwe abwino?

14 Mosiyana ndi Ayuda, Yesu pa Ulaliki wa pa Phiri anafotokoza mfundo m’mbali zisanu za makhalidwe: mkwiyo, ukwati ndi chisudzulo, malonjezo, kubwezera zoipa, ndi chikondi ndi chidani. Anasonyeza phindu lotsatira mfundo za makhalidwe abwino m’mbali zonsezi. Motero, Yesu anaika miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino kwa otsatira ake. Mwachitsanzo, pankhani ya chigololo, iye anapereka mfundo imene imatsogolera zochita zathu komanso maganizo ndi zofuna zathu. Anati: “Yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.”​—Mateyu 5:28.

15. Kodi tingapeŵe bwanji kuumirira malamulo mopitirira muyeso?

15 Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti sitiyenera kuiwala cholinga ndiponso tanthauzo la mfundo za makhalidwe abwino za Yehova. Inde, sitiyenera kuyesa kupeza chiyanjo cha Mulungu mwa kudzionetsera pamaso chabe kuti tili ndi makhalidwe abwino. Yesu anavumbula kulakwika kwa maganizo oterowo mwa kufotokoza chifundo ndi chikondi cha Mulungu. (Mateyu 12:7; Luka 6:1-11) Tikamatsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo, tidzapeŵa kutsatira kapena kuuza ena kuti azitsatira malamulo ambirimbiri ndiponso okhwima amene akupitirira malire a ziphunzitso za m’Baibulo. Tidzaika mtima kwambiri pa mfundo za chikondi ndi kumvera Mulungu osati pa kulambira kongodzionetsera chabe.​—Luka 11:42.

Zotsatira Zabwino

16. Perekani zitsanzo za mfundo za makhalidwe zimene zimabala malamulo ena a m’Baibulo.

16 Pamene tikuyesetsa kumvera Yehova, n’kofunika kuzindikira kuti malamulo ake ndi ozikidwa pa mfundo za makhalidwe abwino zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, Akristu afunika kupeŵa kulambira mafano, chiwerewere, ndi kugwiritsa ntchito magazi molakwika. (Machitidwe 15:28, 29) Kodi n’chiyani makamaka chimachititsa Akristu kupeŵa zinthu zimenezi? Chimene chimawachititsa kupeŵa ndicho mfundo zakuti Mulungu ndi amene tiyenera kum’lambira osati wina aliyense; tiyenera kukhulupirika kwa munthu amene takwatirana naye; ndiponso kuti Yehova ndiye Wopereka Moyo. (Genesis 2:24; Eksodo 20:5; Salmo 36:9) Kumvetsa mfundo zofunika zimenezi kumachititsa kuti kusakhale kovuta kuvomereza ndi kutsatira malamulo amene amagwirizana ndi mfundozi.

17. Kodi ndi zotsatira zabwino ziti zimene zingabwere ngati tidziŵa ndi kugwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo?

17 Pamene tizindikira mfundo zofunika kwambiri ndi kuzigwiritsa ntchito, timazindikira kuti anaziika kuti zitipindulitse. Phindu lauzimu limene anthu a Mulungu amapeza nthaŵi zambiri limatsagana ndi phindu lenileni. Mwachitsanzo, anthu amene amapeŵa kusuta fodya, amene amadzisunga, ndiponso amene amaona mwazi kukhala wopatulika amapeŵa matenda ena. Mofananamo, kutsatira choonadi cha Mulungu kungatipindulitse pankhani ya zachuma, za mmene timakhalira ndi anthu ena, ndiponso m’banja. Mapindu enieni ameneŵa amasonyeza kuti miyezo ya Yehova ndi yofunika ndipo imatithandizadi. Komabe, chifukwa chachikulu chogwiritsira ntchito mfundo za makhalidwe abwino sindicho phindu limene timapeza ayi. Akristu oona amamvera Yehova chifukwa chakuti amamukonda, ndiye woyenera kum’lambira, ndiponso chifukwa chakuti ndicho chinthu choyenera kuchita.​—Chivumbulutso 4:11.

18. Kodi n’chiyani chiyenera kutitsogolera kuti zitiyendere bwino monga Akristu?

18 Kulola kuti mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo zititsogolere kumatichititsa kukhala ndi moyo wapamwamba umene ungachititse ena kukopeka kuti atsatire njira za Mulungu. Chofunika kwambiri n’chakuti zimene timachita zimalemekeza Yehova. Timazindikira kuti Yehova alidi Mulungu wachikondi amene amatifunira zabwino zokhazokha. Timakonda kwambiri Yehova tikamasankha zochita mogwirizana ndi mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ndi kuona mmene iye akutidalitsira. Inde, timakhala pa ubwenzi weniweni ndi Atate wathu wakumwamba.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi mfundo ya makhalidwe abwino n’chiyani?

• Kodi mfundo za makhalidwe abwino zimasiyana bwanji ndi malamulo?

• N’chifukwa chiyani timapindula ngati tiganiza ndi kuchita zinthu motsatira mfundo za makhalidwe abwino?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 20]

Wilson yemwe ndi Mkristu wa ku Ghana anamuuza kuti kwatsala masiku ochepa kuti amuchotse ntchito. Patsiku lake lomaliza kugwira ntchito, anamuuza kuti atsuke galimoto ya bwana wamkulu pa kampaniyo. Wilson atapeza ndalama m’galimotoyo, bwana wake wamng’ono anamuuza kuti Mulungu watumiza ndalamazo chifukwa chakuti ntchito yake inali kutha tsiku limenelo. Komabe, pogwiritsa ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo pankhani ya kuona mtima, Wilson anabweza ndalamazo kwa bwana wamkulu pa kampaniyo. Bwanayo atadabwa ndiponso kuchita chidwi, anauza Wilson nthaŵi yomweyo kuti apitirize kugwira ntchito ndipo anamukweza udindo n’kukhala m’modzi mwa akuluakulu a kampaniyo.​—Aefeso 4:28.

[Bokosi patsamba 21]

A Rukia ndi mayi wa ku Albania wa zaka za m’ma 60. Atayambana ndi achimwene awo, anakhala osalankhulana kwa zaka zoposa 17. Anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anaphunzira kuti Akristu oona ayenera kuyanjana ndi anthu ena, osasunga chakukhosi. Anapemphera usiku wonse, ndipo anapita kunyumba kwa achimwene awo aja mtima ukugunda. Mwana wa achimwene awowo anatsegula chitseko. Mwanayo atadabwa kuwaona a Rukia pakhomopo, anawafunsa kuti: “Ndani wamwalira? Mukudzatani kuno?” A Rukia anapempha kuti aonane ndi achimwene awo. Anafotokoza mofatsa kuti kuphunzira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ndiponso kuphunzira za Yehova kunawachititsa kuti ayanjane ndi achimwene awo. Anagwetsa misozi ndi kukumbatirana ndipo anakondwerera kugwirizananso kwapadera kumeneku.​—Aroma 12:17, 18.

[Chithunzi patsamba 23]

Mateyu 5:27, 28

[Chithunzi patsamba 23]

Mateyu 5:3

[Chithunzi patsamba 23]

Mateyu 5:24

[Chithunzi patsamba 23]

“Ndipo mmene iye anaona makamu, anakwera m’phiri; ndipo mmene iye anakhala pansi, anadza kwa iye ophunzira ake; ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo.”​—MATEYU 5:1, 2.