Kodi Mumaŵerengera Mtengo Wake?
Kodi Mumaŵerengera Mtengo Wake?
YESU KRISTU anapatsa ophunzira ake chiyembekezo cha moyo wosatha, komanso anawalimbikitsa kuŵerengera mtengo wokhala Mkristu. Iye anatsindika mfundoyi mwa kufunsa kuti: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?” (Luka 14:28) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani?
Akristu onse amakumana ndi ziyeso ndipo ziyeso zina zimakhala zovuta kwambiri. (Salmo 34:19; Mateyu 10:36) Choncho, tifunika kukhala okonzeka m’maganizo ndiponso mwauzimu kuti tisadabwe chitsutso kapena mavuto ena akatipeza. Tiyenera kuti tinaŵerengera kale zinthu ngati zimenezo monga mtengo wokhala wophunzira wa Kristu, podziŵa kuti kupulumuka ku uchimo ndi imfa ndi mphoto yaikulu kuposa chilichonse chomwe dzikoli lingapereke. Inde, palibe chilichonse chimene Mulungu amachilola kutichitikira—ngakhale imfa—chomwe chingativulaze kotheratu ngati tipitiriza kumutumikira.—2 Akorinto 4:16-18; Afilipi 3:8.
Kodi tingatani kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba motero? Chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri nthaŵi iliyonse pamene tasankha molondola, kutsatira kwambiri mfundo zachikristu za makhalidwe abwino, kapena kuchita chinachake mogwirizana ndi zomwe Mulungu amafuna, makamaka pamene ena akutikakamiza kuti tichite zina. Tikalandira madalitso a Yehova chifukwa cha kukhulupirika kwathu, chikhulupiriro chathu chimalimba ndiponso chimakula. Mwakuchita zimenezi, timatsatira chitsanzo cha Yesu, ophunzira ake oyambirira, ndiponso amuna ndi akazi onse okhulupirika omwe panthaŵi zosiyanasiyana m’mbuyomu ‘anaŵerengera mtengo’ wotumikira Mulungu molondola.—Marko 1:16-20; Ahebri 11:4, 7, 17, 24, 25, 32-38.