Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Adzapulumuka Tsiku la Yehova?

Kodi Ndani Adzapulumuka Tsiku la Yehova?

Kodi Ndani Adzapulumuka Tsiku la Yehova?

“Likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo.”​—MALAKI 4:1.

1. Kodi Malaki akufotokoza motani mapeto a dziko loipali?

MULUNGU anauzira mneneri Malaki kuti alembe ulosi wa zinthu zochititsa mantha zomwe zichitike posachedwapa. Zochitika zimenezi zidzakhudza munthu aliyense padziko lapansi lino. Malaki 4:1 analosera kuti: “Taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.” Kodi kuwonongeka kwa dziko loipa lino kudzakhala kwakukulu bwanji? Kudzakhala ngati mtengo umene mizu yake yawonongeka moti sungaphukenso.

2. Kodi Malemba ena amalifotokoza bwanji tsiku la Yehova?

2 Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi mneneri Malaki analosera za “tsiku” liti?’ Tsikuli n’limenenso pa Yesaya 13:9 analifotokoza kuti: “Tawonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzawonongamo akuchimwa psiti.” Zefaniya 1:15 amalifotokoza motere tsikuli: “Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la masauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii.”

‘Chisautso Chachikulu’

3. Kodi “tsiku la Yehova” n’chiyani?

3 Pa kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi wa Malaki, “tsiku la Yehova” lidzakhala nthaŵi ya ‘chisautso chachikulu’. Yesu analosera kuti: “Pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” (Mateyu 24:21) Taganizani za masautso omwe dzikoli lakumana nawo kale makamaka kuyambira 1914. (Mateyu 24:7-12) Pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse yokha anthu oposa 50 miliyoni anaphedwa! Komatu, pa ‘chisautso chachikulu’ padzakhala zoopsa zoposa mavuto amenewo. Chisautso chachikulu chimenecho, chomwe n’chimodzimodzi ndi tsiku la Yehova, chidzathera pa Armagedo. Ameneŵa adzakhala mapeto a masiku otsiriza a dziko loipa lino.​—2 Timoteo 3:1-5, 13; Chivumbulutso 7:14; 16:14, 16.

4. Kodi n’chiyani chidzakhala chitachitika pofika pamapeto pa tsiku la Yehova?

4 Pamapeto pa tsiku la Yehova limenelo, dziko la Satana pamodzi ndi amene ali ku mbali yake adzakhala atawawononga. Adzayamba kuwononga zipembedzo zonyenga zonse. Kenako, Yehova adzaweruza dongosolo lamalonda ndi landale la Satana. (Chivumbulutso 17:12-14; 19:17, 18) Ezekieli analosera kuti: “Adzataya siliva wawo kumakwalala, nadzayesa golidi wawo chinthu chodetsedwa; siliva wawo ndi golidi wawo sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Ezekieli 7:19) Posimba za tsikulo, Zefaniya 1:14 amati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi, lifulumira kudza.” Poona zimene Baibulo likunena za tsiku la Yehova, tiyenera kutsimikiza mtima kutsatira malamulo olungama a Mulungu.

5. Kodi n’chiyani chikuwachitikira amene akuopa dzina la Yehova?

5 Atalosera zomwe tsiku la Yehova lidzachitire dziko la Satana, Malaki 4:2, akufotokoza mawu a Yehova akuti: “Inu akuopa dzina langa, dzuŵa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m’mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng’ombe onenepa.” “Dzuŵa la chilungamo” ndiye Yesu Kristu. Iye ndiye “kuunika [kwauzimu] kwa dziko lapansi.” (Yohane 8:12) Yesu akuŵala mwa kuchiritsa. Choyamba, akuchiritsa mwauzimu, zomwe zikutichitikira pakalipano, ndipo kenako m’dziko lapansi latsopano adzachiritsa matenda enieni. Monga mmene Yehova akunenera, ochiritsidwawo “adzatuluka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng’ombe onenepa” osangalala chifukwa choti wawatulutsa m’ndende.

6. Kodi atumiki a Yehova adzakondwerera kupambana kotani?

6 Nanga bwanji za anthu onyalanyaza zimene Yehova amafuna? Malaki 4:3, akuti: “[Inu atumiki a Mulungu] mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa ku mapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.” Anthu amene amalambira Mulungu sadzawononga nawo dziko la Satana. M’malo mwake, iwo mophiphiritsira ‘adzapondereza oipa’ pokondwerera kupambana kwakukulu komwe kudzachitike pambuyo pa tsiku la Yehova. Ankhondo a Farao atawawononga m’Nyanja Yofiira, panachitika chikondwerero chachikulu. (Eksodo 15:1-21) Satana ndi dziko lake akadzawachotsa pa chisautso chachikulu, padzakhalanso kukondwerera kupambana kumeneku. Anthu okhulupirika amene adzapulumuke tsiku la Yehova adzafuula kuti: “Tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.” (Yesaya 25:9) Padzakhalatu chisangalalo chachikulu Yehova akadzatsimikizira kuti ndiye woyenera kulamulira ndiponso akadzayeretsa dziko kuti anthu akhalemo mwamtendere.

Matchalitchi Achikristu Amatsanzira Israyeli

7, 8. Fotokozani mmene moyo wauzimu wa Aisrayeli unalili m’nthaŵi ya Malaki.

7 Anthu amene Yehova amawakonda ndi okhawo amene amamutumikira. Iye sakonda amene sam’tumikira. Zinalinso chimodzimodzi pamene Malaki analemba buku lake. M’chaka cha 537 B.C.E, otsalira a Israyeli anabwerera kwawo atatha zaka 70 ali mu ukapolo ku Babulo. Komabe, m’kati mwa zaka 100 zotsatira, mtunduwo unayamba kukhala wampatuko ndi kuchita zoipa. Anthu ambiri sankalemekeza dzina la Yehova; ankanyalanyaza malamulo ake olungama; ankaipitsa kachisi wake mwa kubweretsa nyama zakhungu, zotsimphina, ndi zodwala kuti azipereke nsembe; ndiponso ankasudzula akazi a ubwana wawo.

8 N’chifukwa chake Yehova anawauza kuti: “Ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa ine, . . . pakuti ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:5, 6) Komabe, Yehova anaitana onse amene akanasiya njira zawo zoipa kuti: “Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.”​—Malaki 3:7.

9. Kodi maulosi a Malaki anakwaniritsidwa bwanji koyamba?

9 Mawu amenewo anakwaniritsidwanso m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Ayuda ena anatumikira Yehova ndipo anakhala m’gulu la anthu a “mtundu” watsopano wa Akristu odzozedwa ndi mzimu, womwe kenako munaloŵanso Amitundu. Koma Aisrayeli ambiri anakana Yesu. Motero Yesu anauza Aisrayeliwo kuti: “Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:38; 1 Akorinto 16:22) Mu 70 C.E., monga momwe Malaki 4:1 analoserera, “tsiku lotentha ngati ng’anjo” linadza pa mtundu wa Israyeli. Aroma anapasula Yerusalemu ndi kachisi wake, ndipo mbiri imati anthu oposa wani miliyoni anafa chifukwa cha chilala, kulimbirana ulamuliro, ndiponso kuukira kwa asilikali a Roma. Komabe, amene ankatumikira Yehova anapulumuka chisautso chimenecho.​—Marko 13:14-20.

10. Kodi anthu pamodzi ndi atsogoleri a zipembedzo akutsanzira bwanji Aisrayeli a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino?

10 Anthu, ndipo makamaka Matchalitchi Achikristu, atsanzira mtundu wa Israyeli wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Atsogoleri ndi anthu ena onse a m’Matchalitchi Achikristu amakonda ziphunzitso zawo za chipembedzo zonyenga m’malo mokonda choonadi chonena za Mulungu chomwe Yesu anaphunzitsa. Makamaka atsogoleri achipembedzo ndiwo ali ndi mlandu waukulu. Amakana kugwiritsa ntchito dzina la Yehova, ndipo afika ngakhale polichotsa m’mabaibulo awo. Amanyoza Yehova mwa kuphunzitsa zinthu zomwe si za m’malemba, monga ziphunzitso zachikunja za chizunzo chosatha m’helo, Utatu, kusafa kwa mzimu, ndi chisinthiko. Motero, iwo salemekeza Yehova, monganso mmene ansembe a m’nthaŵi ya Malaki sanam’lemekezere.

11. Kodi zipembedzo za dziko lapansi zaonetsa bwanji amene izo zimamutumikira?

11 Mu 1914, pamene masiku otsiriza anayamba, zipembedzo za dziko lino, motsogoleredwa ndi amene amati ndi Akristu, zinaonetsa kuti ndi ndani amene zikumutumikira. Pa nkhondo zonse ziŵiri za padziko lonse, izo zinalimbikitsa anthu awo kupita ku nkhondo chifukwa cha kusagwirizana kwa mayiko awo, ngakhale kuti zimenezo zinatanthauza kupha anthu achipembedzo chawo chomwecho. Mawu a Mulungu amasiyanitsa bwinobwino anthu amene amamvera Yehova ndi amene samvera. Amati: “Mmenemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdyerekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake.”​—1 Yohane 3:10-12.

Kukwaniritsa Ulosi

12, 13. Kodi ndi maulosi ati amene atumiki a Mulungu akwaniritsa m’nthaŵi zathu zino?

12 Pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inali kutha m’chaka cha 1918, atumiki a Yehova anatha kuona kuti Mulungu waweruza Matchalitchi Achikristu ndi zipembedzo zonse zonyenga. Kuyambira nthaŵi imeneyo, anthu oongoka mtima akhala akuitanidwa kuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.” (Chivumbulutso 18:4, 5) Amene anafuna kutumikira Yehova anayamba kuwayeretsa ku zinthu zonse zokhudzana ndi chipembedzo chonyenga. Ndiyeno, anayamba kulalikira padziko lonse uthenga wabwino wa Ufumu umene Mulungu anaukhazikitsa, ntchito imene ifunikira kuimaliza mapeto a dziko lino asanafike.​—Mateyu 24:14.

13 Kumeneku kunali kukwaniritsa ulosi wa pa Malaki 4:5 pamene Yehova anati: “Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.” Ulosi umenewo unakwaniritsidwa koyamba ndi ntchito ya Yohane Mbatizi, yemwe anaimira Eliya. Yohane anachita ntchito yofanana ndi ya Eliya pamene anabatiza Ayuda omwe analapa machimo awo ochimwira pangano la Chilamulo. Chofunika kwambiri n’chakuti Yohane anali kalambulabwalo wa Mesiya. Komabe, zimene Yohane anachita kunali kukwaniritsa ulosi wa Malaki koyamba chabe. Yesu, ngakhale kuti anati Yohane anali Eliya wachiŵiri, anasonyeza kuti m’tsogolo mudzachitikanso ntchito ya “Eliya.”​—Mateyu 17:11, 12.

14. Kodi ndi ntchito yofunika iti imene iyenera kuchitika mapeto a dzikoli asanafike?

14 Ulosi wa Malaki unasonyeza kuti ntchito yaikulu ya Eliya imeneyi idzachitika lisanadze “tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.” Tsikulo lidzatha ndi nkhondo yomwe ikuyandikira mofulumira kwambiri ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse, pa Armagedo. Zimenezi zikutanthauza kuti mapeto a dziko loipali asanafike ndiponso Ulamuliro wa Zaka 1000 wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu womwe anaupereka m’manja mwa Yesu Kristu usanayambe, ntchito yofanana ndi ya Eliya iyenera kuchitika. Monga mmene anafotokozera mu ulosiwo, Yehova asanawononge dziko loipali, gulu lamakono la Eliya, mothandizidwa ndi miyandamiyanda ya Akristu anzawo amene akuyembekeza kudzakhala padziko lapansi, akugwira mwachangu ntchito yobwezeretsa kulambira koyera, kulemekeza dzina la Yehova, ndi kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo kwa anthu onga nkhosa.

Yehova Amadalitsa Atumiki Ake

15. Kodi Yehova amakumbukira bwanji atumiki ake?

15 Yehova amadalitsa amene amamutumikira. Malaki 3:16 akuti: “Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” Kuyambira pa Abele kufika masiku ano, tinganene kuti Mulungu wakhala akulemba m’buku maina a anthu amene adzawakumbukira mwa kuwapatsa moyo wosatha. Kwa anthu ameneŵa, Yehova akuti: “Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono . . . ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.”​—Malaki 3:10.

16, 17. Kodi Yehova wadalitsa motani anthu akefe ndi ntchito yathu?

16 Yehova wadalitsadi anthu amene akumutumikira. Motani? Njira yoyamba imene wawadalitsira ndiyo kumvetsa bwino zolinga zake. (Miyambo 4:18; Danieli 12:10) Njira ina ndiyo kuwapatsa zotsatira zabwino za ntchito yawo yolalikira. Anthu ambiri oona mtima agwirizana nawo m’kulambira koona, ndipo onsewa pamodzi akupanga “khamu lalikulu, . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, . . . ndipo akufuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 10) Khamu lalikulu limeneli laonekera mochititsa chidwi, ndipo amene akutumikira Yehova pakalipano akuposa 6,000,000 m’mipingo yoposa 93,000 padziko lonse lapansi.

17 Njira ina imene Yehova wadalitsira atumiki ake ndiyo mabuku ophunzirira Baibulo amene Mboni za Yehova zimafalitsa. Mabuku athu ndiwo afalitsidwa kwambiri kuposa ena alionse. Pakalipano, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amatuluka okwana 90 miliyoni mwezi uliwonse, Nsanja ya Olonda m’zinenero 144, ndipo Galamukani! m’zinenero 87. Tinagaŵira mabuku okwana 107 miliyoni a buku lothandizira kuphunzira Baibulo lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya limene linatuluka mu 1968 m’zinenero 117. Buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, limene linatuluka mu 1982 tinalifalitsa mabuku oposa 81 miliyoni m’zinenero 131. Buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, limene linatuluka mu 1995, talifalitsa mabuku oposa 85 miliyoni m’zinenero 154. Bulosha lomwe linatuluka mu 1996 lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? talifalitsa mabulosha okwana 150 miliyoni m’zinenero 244 tsopano.

18. N’chifukwa chiyani zinthu zikutiyendera bwino mwauzimu ngakhale kuti dzikoli likutitsutsa?

18 Kuyenda bwino kwa zinthu zauzimu kumeneku kwachitika ngakhale kuti dziko la Satana likutitsutsa modetsa nkhaŵa. Zimenezi zikungosonyeza kuti mawu amene ali pa Yesaya 54:17 ndi oona. Mawuwo amati: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi choloŵa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chawo chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.” Atumiki a Yehova zimawalimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti kukwaniritsidwa kwakukulu kwa mawu a pa Malaki 3:17 kukuchitikira pa iwo. Lemba limenelo limati: “Adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo.”

Kutumikira Yehova Mosangalala

19. Kodi amene amatumikira Yehova akusiyana motani ndi amene sam’tumikira?

19 Kusiyana kwa atumiki okhulupirika a Yehova ndi anthu a dziko la Satanali kukuonekera mosavuta tsiku ndi tsiku. Malaki 3:18 analosera kuti: “Adzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.” Njira ina imene akusiyanira ndiyo yakuti amene akutumikira Yehova amachita zimenezo mosangalala kwambiri. Amasangalala potumikira chifukwa chakuti akuyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Amakhulupirira kwambiri zimene Yehova ananena kuti: “Taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.”​—Yesaya 65:17, 18; Salmo 37:10, 11, 29; Chivumbulutso 21:4, 5.

20. N’chifukwa chiyani ndife anthu osangalala kwambiri?

20 Timakhulupirira lonjezo la Yehova lakuti anthu ake okhulupirika adzapulumuka tsiku lake lalikulu ndi kuloŵa m’dziko latsopano. (Zefaniya 2:3; Chivumbulutso 7:13, 14) Ndipo, ngakhale kuti ena angamwalire chifukwa cha kukalamba, kudwala, kapena ngozi dziko latsopano lisanafike, Yehova amatiuza kuti adzawaukitsa anthu amenewo ndi kuwapatsa moyo wosatha. (Yohane 5:28, 29; Tito 1:2) Motero, ngakhale kuti tonsefe tili ndi mavuto athu ndiponso zopinga, pamene tikuyandikira tsiku limeneli la Yehova, tili ndi zifukwa zokwanira zokhalira anthu osangalala kwambiri padziko lonse lapansi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi “tsiku la Yehova” n’chiyani?

• Kodi zipembedzo za m’dzikoli zikutsanzira motani Aisrayeli akale?

• Kodi atumiki a Yehova akukwaniritsa maulosi otani?

• Kodi Yehova wadalitsa bwanji anthu ake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Yerusalemu wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino ‘anatentha ngati ng’anjo’

[Zithunzi patsamba 23]

Yehova amapatsa anthu amene akumutumikira zimene iwo akufuna

[Zithunzi patsamba 24]

Atumiki a Yehova ndi osangalala kwambiri chifukwa cha zabwino zimene akuyembekeza