Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulumala N’kosiyanasiyana

Kulumala N’kosiyanasiyana

Kulumala N’kosiyanasiyana

CHRISTIAN yemwe akukhala m’dziko lina la ku Africa, asilikali anam’dula mwendo. Iwo ankamuumiriza kuloŵa usilikali, koma iye anakana chifukwa cha chikumbumtima chake chomwe anachiphunzitsa Baibulo. Asilikaliwo anamutengera ku kampu yawo komwe atam’menya kwa masiku anayi, m’modzi wa asilikaliwo anamuwombera mwendo. Christian anapita ku chipatala komwe sakanachitira mwina, koma kungoduliratu mwendowo pafupi ndi bondo. M’dziko linanso ku Africa, zigaŵenga zadula manja kapena miyendo ya ana ngakhale aang’ono. M’mayiko ambiri monga ku Cambodia, Balkans, Afghanistan, Angola, mabomba okwirira pansi akupitirizabe kupundula ana ndi achikulire omwe.

Anthu akuvutikanso ndi kulumala komwe ngozi ndi matenda monga nthenda ya shuga zikuchititsa. Anthu angalumale chifukwanso cha mankhwala a poizoni m’dera lomwe akukhala. Mwachitsanzo, m’madera oyandikana ndi mzinda wina kummaŵa kwa Ulaya, ana ambiri akhala akubadwa opanda mkono wonse wakumanja. Amangokhala ndi mkono waufupi wobulungira pafupi ndi kasukusuku. Umboni ukusonyeza kuti zimenezi zikuchitika chifukwa cha kuipitsa malo ndi mankhwala apoizoni omwe anawononga majini a m’thupi. Anthu ena ambirimbiri ali ndi manja ndiponso miyendo, koma ndi olumala mwina chifukwa cha matenda oumitsa ziŵalo kapena matenda ena. Inde, kulumala n’kosiyanasiyana.

Kaya munthu alumale ndi chiyani, mfundo n’njakuti kulumala n’kopweteka kwambiri. Junior anaduka mwendo wamanzere ali ndi zaka 20. Kenako iye anati: “Ndinali kuvutika maganizo kwambiri. Ndinalira kwabasi chifukwa ndinadziŵa kuti mwendo wangawo sindidzakhala nawonso. Ndinangokhala kakasi kusoŵa chochita. Mutu wanga unaima.” Komabe, patapita nthaŵi maganizo a Junior anasintha kwambiri. Anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anaphunzira zinthu zimene zinamulimbikitsa kupirira vuto lakelo. Komanso zomwe anaphunzirazo zinam’patsa chiyembekezo chabwino kwambiri cha zinthu zosangalatsa m’tsogolo pompano padziko lapansi. Ngati ndinu wolumala, kodi mungakonde kukhala ndi chiyembekezo choterocho?

Ngati ndi choncho, chonde ŵerengani nkhani yotsatirayi. Mungachite bwino kuŵerenga Malemba omwe ali m’nkhaniyi pogwiritsa ntchito Baibulo lanu kuti mudzionere nokha zimene Mlengi wasungira anthu amene amaphunzira zolinga zake ndi kuzitsatira pa moyo wawo.