Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikondi cha Mulungu Mumachimvetsa?

Kodi Chikondi cha Mulungu Mumachimvetsa?

Kodi Chikondi cha Mulungu Mumachimvetsa?

PANTHAŴI ina Yobu anagwiritsa ntchito mawu otsatiraŵa pofotokoza munthu wopanda ungwiro. Iye anati: “Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duŵa, nafota; athaŵa ngati mthunzi, osakhalitsa.” (Yobu 14:1, 2) Moyo womwe Yobu anali nawo panthaŵiyo unali wodzala ndi mavuto ndiponso chisoni. Kodi inu munamvapo choncho?

Ngakhale kuti timakumana ndi mavuto ambiri, pali chiyembekezo cholimba chakuti zinthu zidzakhala bwino. Maziko a chiyembekezo chimenecho ndi chifundo ndi chikondi cha Mulungu. Choyamba, Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachifundo wapereka nsembe ya dipo kuti awombole anthu ku uchimo. Malinga ndi Yohane 3:16, 17, Yesu Kristu anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi [anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wake [Yesu] ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.”

Talingaliraninso za kukoma mtima kwa Mulungu pa anthu opanda ungwirofe. Mtumwi Paulo anati: “Ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo; kuti afunefune Mulungu, kapena akamufufuze ndi kumupeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:26, 27) Tangoganizani! Ngakhale kuti tilibe ungwiro, tingakhalebe paubwenzi ndi Yehova Mulungu, Mlengi wathu wachikondi.

Choncho, timalimba mtima tikamaganiza za m’tsogolo podziŵa kuti Mulungu amatisamala ndi kuti wakonza zinthu zomwe tidzapindule nazo kosatha popeza amatikonda. (1 Petro 5:7; 2 Petro 3:13) Chotero tili ndi chifukwa chabwino chofuna kudziŵira zambiri zokhudza Mulungu wathu wachikondi ndipo tingatero mwa kuphunzira Baibulo, Mawu ake.