Kodi Mulungu Ndani?
Kodi Mulungu Ndani?
“MULUNGU ndi dzina lomwe ambiri amatchulira gwero ndi mphamvu zenizeni za chilengedwe chonse zimenenso anthu amalambira ndi mtima wonse,” limatero buku lamaumboni la The Encyclopedia Americana. Mulungu ndi wamkulu ndiponso wapamwamba kuposa cholengedwa china chilichonse. Kodi iye ndi wotani?
Kodi Mulungu ndi mphamvu chabe kapena ali ndi umunthu wake? Kodi ali ndi dzina? Kodi iye ndi Utatu, ngati mmene anthu ambiri amakhulupiririra? Kodi tingamudziŵe bwanji Mulungu? Baibulo limayankha mafunso ameneŵa molondola komanso mogwira mtima. Ndipo limatilimbikitsa kufunafuna Mulungu. Limati: “Sakhala patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27.
Kodi Ndi Mphamvu Chabe Kapena Ali ndi Umunthu Wake?
Ambiri amene amakhulupirira Mulungu amaganiza kuti iye ndi mphamvu basi, alibe makhalidwe a umunthu. Mwachitsanzo, m’mitundu ina ya anthu, amaona mphamvu za chilengedwe kukhala milungu. Ena omwe apenda maumboni a kafukufuku wa sayansi okhudza chilengedwe ndiponso moyo padziko lapansi pano anena kuti payenera kukhala mphamvu inayake imene inalenga zimenezi. Komabe, safuna kunena kuti mphamvu imeneyo ndi Mlengi amene ali ndi umunthu wake.
Ngakhale zili choncho, kodi kucholowana kwa chilengedwe sikusonyeza kuti mphamvu imene amati inalenga zonse iyenera kuti inali ndi nzeru zochuluka? Nzeru zimafuna kuganiza. Maganizo odabwitsa amene anapanga chilengedwe chonsechi ali m’thupi la Mulungu. Inde, Mulungu ali ndi thupi, osati thupi ngati lathu koma thupi lauzimu. Baibulo limati: “Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.” (1 Akorinto 15:44) Polongosola mmene Mulungu alili, Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Mulungu ndiye mzimu.” (Yohane 4:24) Mzimu umakhala ndi moyo wosiyana kwambiri ndi wathu, ndipo munthu sangauone. (Yohane 1:18) Pali zolengedwa zinanso zauzimu zimene sizioneka. Zolengedwa zimenezi ndi angelo—“ana a Mulungu.”—Yobu 1:6; 2:1.
Popeza kuti Mulungu si munthu wochita kulengedwa ndipo ali ndi thupi lauzimu, ndiye kuti iye ali ndi malo okhala. Ponena za malo a mizimu, Baibulo limatiuza kuti kumwamba ndi “mokhala” mwa Mulungu. (1 Mafumu 8:43) Ndiponso, wolemba Baibulo, Paulo anati: ‘Kristu analoŵa m’Mwamba momwe kukaonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.’—Ahebri 9:24.
M’Baibulo, liwu lakuti “mzimu” limagwiranso ntchito m’njira ina. Polankhula kwa Mulungu m’pemphero, wamasalmo anati: “Potumizira mzimu wanu, zilengedwa.” (Salmo 104:30) Mzimu uwu si Mulungu mwiniyo koma mphamvu imene Mulungu amatumiza, kapena kugwiritsa ntchito, pofuna kuchita zomwe akufuna. Mwa mphamvu imeneyi, Mulungu analenga miyamba yomwe timaionayi, dziko lapansili, ndi zamoyo zonse. (Genesis 1:2; Salmo 33:6) Mzimu wake umatchedwa kuti mzimu woyera. Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kuuzira anthu omwe analemba Baibulo. (2 Petro 1:20, 21) Chotero, mzimu woyera ndi mphamvu yosaoneka imene Mulungu amagwiritsa ntchito pochita zolinga zake.
Mulungu Ali ndi Dzina Lakelake
Wolemba Baibulo, Aguri, anafunsa kuti: ‘Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m’malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwana wake ndani?” (Miyambo 30:4) Mwa mawuŵa, Aguri anali kufunsa kuti, ‘Kodi mukudziŵa dzina kapena banja la munthu aliyense amene anachitapo zimenezi?’ Mulungu yekha ndiye amalamulira mphamvu za chilengedwe. Ngakhale kuti chilengedwe chimapereka umboni wamphamvu wosonyeza kuti Mulungu alipo, sichinena dzina la Mulungu. Ndipo sitikanadziŵa dzina la Mulungu ngati Mulungu akanapanda kutidziŵitsa. Ndipo waterodi. Mlengiyo amati: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli.”—Yesaya 42:8.
Dzina lapadera la Mulungu, Yehova, limapezeka maulendo pafupifupi 7,000 m’Malemba Achihebri. Yesu Kristu anadziŵitsa ena za dzinalo ndipo analilemekeza iwo akumva. (Yohane 17:6, 26) Dzinali limapezeka m’buku lomalizira la Baibulo monga mbali ya mawu akuti “Aleluya,” kutanthauza kuti “tamandani Ya.” Ndipo “Ya” ndi chidule cha “Yehova.” (Chivumbulutso 19:1-6) Ngakhale zili choncho, mabaibulo ambiri amakono saligwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri dzinali. M’zinenero zina, nthaŵi zambiri amagwiritsa ntchito mawu akuti “AMBUYE” kapena “MULUNGU,” omwe amawalemba m’zilembo zikuluzikulu pofuna kuwasiyanitsa ndi mayina ofala aulemu a “Ambuye” ndi “Mulungu.” Akatswiri ena amaganiza kuti dzina la Mulungu linkatchulidwa kuti Yahweh.
N’chifukwa chiyani pali kusiyana malingaliro Eksodo 6:3; Yesaya 26:4.
kotero ponena za dzina la Wolemekezeka kuposa wina aliyense m’chilengedwe chonse. Vuto linayamba zaka mazana ambiri zapitazo pamene Ayuda potsata mwambo anasiya kutchula dzina la Mulungu ndi kuyamba kugwiritsa ntchito liwu la Chihebri la “Ambuye Mfumu” paliponse pamene apeza dzina la Mulungu poŵerenga Malemba. Popeza kuti Chihebri cha m’Baibulo chinalembedwa popanda mavawelo, m’povuta kudziŵa bwinobwino mmene Mose, Davide, ndi anthu ena akale ankatchulira zilembo zomwe zimapanga dzina la Mulungu. Komabe, katchulidwe ka Chicheŵa ka dzinali, kakuti Yehova, kakhala kakugwiritsidwa ntchito kwa zaka zambiri, ndipo zinenero zambiri lerolino zili ndi katchulidwe kawo ka dzina limeneli.—Ngakhale kuti sizikudziŵika bwinobwino kuti dzina la Mulungu linkatchulidwa motani m’Chihebri chakale, tanthauzo lake si chinsinsi. Dzina lake limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Motero Yehova Mulungu amadzidziŵikitsa kuti ndi Wachifuno Wamkulu. Nthaŵi zonse amachititsa kuti zolinga zake ndi malonjezo ake zikwaniritsidwe. Mulungu yekha woona, yemwe ali ndi mphamvu yochita zimenezi, ndiye ayenera dzina limenelo.—Yesaya 55:11.
M’posachita kufunsa kuti dzina lakuti Yehova limasiyanitsa Mulungu Wamphamvuyonse ndi milungu ina yonse. N’chifukwa chake dzinali limapezeka kaŵirikaŵiri m’Baibulo. Ngakhale kuti mabaibulo ambiri sagwiritsa ntchito dzina la Mulungu limeneli, Salmo 83:18 limanena momveka bwino kuti: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.” Pochita utumiki wake, Yesu Kristu anaphunzitsa otsatira ake kuti: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Chotero, tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu popemphera, kulankhula za iye, ndiponso kumutamanda pamaso pa anthu ena.
Kodi Yesu Ndi Mulungu?
Yehova Mulungu mwiniyo amanena momveka kuti Mwana wake ndani? Uthenga Wabwino wa Mateyu umanena kuti Yesu atabatizidwa, panamveka “mawu akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:16, 17) Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu.
Komabe, anthu ena opembedza amati Yesu ndi Mulungu. Ena amati Mulungu ndi Utatu. Malinga ndi chiphunzitso chimenechi, “Atate ndi Mulungu, Mwana ndi Mulungu, ndiponso Mzimu Woyera ndi Mulungu, koma sikuti pali Milungu itatu koma Mulungu mmodzi.” Amati anthu atatuŵa ndi “amuyaya ndiponso ofanana.” (The Catholic Encyclopedia) Kodi malingaliro ameneŵa n’ngolondola?
Ponena za Yehova, Malemba ouziridwa amati: “Kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha, Inu ndinu Mulungu.” (Salmo 90:2) Iye ndi “Mfumu yosatha”—alibe chiyambi kapena mapeto. (1 Timoteo 1:17) Koma Yesu ndi “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse,” “woyamba wa chilengo cha Mulungu.” (Akolose 1:13-15; Chivumbulutso 3:14) Potchula Mulungu monga Atate wake, Yesu anati: “Atate ali wamkulu ndi Ine.” (Yohane 14:28) Yesu anafotokozanso kuti panali zinthu zina zomwe iye ngakhalenso angelo sankazidziŵa koma Mulungu yekha ndiye anali kudziŵa. (Marko 13:32) Komanso, Yesu anapemphera kwa Atate wake, kuti: ‘Kufuna kwanu kuchitike, osati kufuna kwanga ayi.’ (Luka 22:42) Kodi anali kupemphera kwa ndani ngati sanali kupemphera kwa Wolemekezeka kuposa iye? Ndipo ndi Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa, osati Yesu mwiniyo.—Machitidwe 2:32.
Chotero, malinga ndi Malemba, Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse, ndipo Yesu ndi Mwana wake. Aŵiriŵa sanali ofanana Yesu asanabwere padziko lapansi kapena nthaŵi yomwe anali padziko lapansi pano; ngakhalenso ataukitsidwa kupita kumwamba, Yesu sanafanane ndi Atate wake. (1 Akorinto 11:3; 15:28) Monga momwe taoneramu, mzimu woyera, umene anthu amati ndi mbali yachitatu ya Utatu, si munthu. Koma ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito pochita zimene akufuna. Chotero, Malemba saphunzitsa za Utatu. * “Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi,” limatero Baibulo.—Deuteronomo 6:4.
M’dziŵeni Bwino Mulungu
Kuti tikonde Mulungu ndi kumulambira iye yekha popeza amafunikira zimenezi, tifunika timudziŵe kuti iye ndani makamaka. Kodi tingatani kuti tim’dziŵe bwino Mulungu? Baibulo limati: “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” (Aroma 1:20) Njira imodzi yomwe tingadziŵire bwino Mulungu ndiyo kuona ndi kusinkhasinkha moyamikira zinthu zimene iye walenga.
Komabe chilengedwe sichitiuza zonse zomwe timafunikira kudziŵa zokhudza Mulungu. Mwachitsanzo, kuti timvetse kuti iye ndi Munthu weniweni wauzimu ndipo ali ndi dzina lakelake, tifunikira kuona m’Baibulo. Chotero kuphunzira Baibulo ndiyo njira yabwino kwambiri yomudziŵira bwino Mulungu. M’Malemba, Yehova amatiuza zinthu zambiri ponena zakuti iye ndi Mulungu wotani. Amatidziŵitsanso zolinga zake ndipo amatiphunzitsa njira zake. (Amosi 3:7; 2 Timoteo 3:16, 17) Tiyenera kukondwera kwambiri chifukwa Mulungu akufuna kuti tifike podziŵa choonadi molondola kuti tithe kupindula ndi makonzedwe amene wapanga chifukwa cha chikondi chake. (1 Timoteo 2:4) Chotero, tiyeni tiyesetse kuphunzira zomwe tingathe ponena za Yehova.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 19 Kuti mudziŵe zambiri pankhaniyi, onani kabuku kakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Zithunzi patsamba 5]
Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kulenga dziko ndiponso kuuzira anthu kuti alembe Baibulo
[Chithunzi patsamba 5]
Mawu ochokera kumwamba anati: “Uyu ndiye Mwana wanga”
[Chithunzi patsamba 7]
Yesu anapemphera kwa Mulungu—Wolemekezeka kuposa iye
[Chithunzi patsamba 7]
Yesu anadziŵitsa ena dzina la Mulungu
[Zithunzi patsamba 7]
Tingamudziŵe bwino Mulungu