Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Komerani Mtima Anthu Osoŵa Thandizo

Komerani Mtima Anthu Osoŵa Thandizo

Komerani Mtima Anthu Osoŵa Thandizo

‘Chitirani yense mnzake . . . mokoma mtima.’​—ZEKARIYA 7:9.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kusonyeza kukoma mtima? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

MAWU a Yehova Mulungu amatilimbikitsa kuti tikonde “chifundo [kukoma mtima].” (Mika 6:8) Amatiuzanso chifukwa chake tiyenera kuchita zimenezo. Chimodzi mwa zifukwazo ndicho chakuti “wachifundo achitira moyo wake zokoma.” (Miyambo 11:17) N’zoonatu zimenezo! Kukoma mtima kumatithandiza kupanga maubwenzi enieni ndi anthu ena. Motero, timakhala ndi mabwenzi okhulupirika. Kodi si mphoto yamtengo wapatali imeneyo?​—Miyambo 18:24.

2 Ndiponso, Malemba amatiuza kuti: “Wolondola chilungamo ndi chifundo apeza moyo.” (Miyambo 21:21) Inde, Mulungu adzatikonda chifukwa cha kukoma mtima kwathu ndiponso kudzatithandiza kukhala ndi mwayi wolandira madalitso m’tsogolo, kuphatikizapo moyo wosatha. Koma kodi tingasonyeze bwanji kukoma mtima? Kodi ndani amene tifunika kuwakomera mtima? Ndipo kodi kukoma mtima kumene tikukambirana m’nkhani ino kumasiyana bwanji ndi kukoma mtima kwachibadwa?

Kusiyanitsa Kukoma Mtima

3. Kodi kukoma mtima kwa m’nkhani ino kukusiyana bwanji ndi kukoma mtima kwachibadwa?

3 Kukoma mtima kwachibadwa ndi kukoma mtima kwa m’nkhani ino n’kosiyana m’njira zambiri. Mwachitsanzo, amene mwachibadwa amakomera mtima munthu mnzake nthaŵi zambiri amatero ngakhale kuti sakonda munthuyo kapenanso si mabwenzi ndi munthu amene akumukomera mtimayo. Koma posonyeza kukoma mtima kwa m’nkhani ino, timatero chifukwa chom’konda kwambiri munthu amene tikumukomera mtimayo. Malinga ndi Baibulo, anthu amene amasonyezana kukoma mtima kumeneku amatero chifukwa chakuti mwina akudziŵana kale. (Genesis 20:13; 2 Samueli 3:8; 16:17) Kapena angatero chifukwa cha ubwenzi umene unayamba pamene wina anakomera mtima mnzake m’mbuyomo. (Yoswa 2:1, 12-14; 1 Samueli 15:6; 2 Samueli 10:1, 2) Kuti timvetse bwino kusiyana kumeneku, tiyeni tiyerekeze zitsanzo ziŵiri za m’Baibulo, chitsanzo china cha kukoma mtima kwachibadwa ndipo chinacho cha kukoma mtima kwinaku kumene anthu anasonyezana.

4, 5. Kodi zitsanzo ziŵiri za m’Baibulo zimene tazitchulazi zikumveketsa bwanji kusiyana kwa kukoma mtima kwachibadwa ndi kukoma mtima kumene tikukambirana?

4 Chitsanzo chimodzi cha kukoma mtima kwachibadwa chikukhudza gulu la anthu amene ngalawa imene analimo inasweka. Mtumwi Paulo analinso momwemo. Anthuŵa anapulumukira pachilumba cha Melita. (Machitidwe 27:37–28:1) Ngakhale kuti Amelitawo sanali ndi mangawa kapena ubale uliwonse ndi apaulendo ovutikawo, iwo analandira bwino alendowo ndi kuwachitira “zokoma zosachitika pena ponsepo.” (Machitidwe 28:2, 7) Kuchereza kwawoko kunali kukoma mtima, koma kunangochitika mosayembekezera ndipo anachitira alendo. Kumeneku kunali kukoma mtima kwachibadwa.

5 Tsopano yerekezani ndi mmene Mfumu Davide anacherezera mwana wa mnzake Jonatani, Mefiboseti. Iye anauza Mefiboseti kuti: “Udzadya pagome langa chikhalire.” Davide pofotokoza chifukwa chake anachita zimenezi, anamuuza kuti: “Zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Jonatani atate wako.” (2 Samueli 9:6, 7, 13) M’pake kunena kuti Davide, mwa kuchereza kwake kwachikhalire, anasonyeza kukoma mtima kumene tikukambiranaku osati kuja kwachibadwa, chifukwa umenewu unali umboni woti anakhulupirika pa ubale umene unalipo kale. (1 Samueli 18:3; 20:15, 42) N’chimodzimodzinso lerolino. Atumiki a Mulungu mwachibadwa amakomera mtima anthu onse. Komabe, iwo amasonyeza kukoma mtima kosatha kumene tikukambiranaku mokhulupirika kwa anthu amene ali nawo pa ubale umene Mulungu amauyanja.​—Mateyu 5:45; Agalatiya 6:10.

6. Kodi m’Mawu a Mulungu timapeza kuti anthu anasonyezana kukoma mtima kumeneku motani?

6 Kuti tione mbali zina za kukoma mtima kumeneku, tipenda mwachidule nkhani za m’Baibulo zitatu zimene zikusonyeza khalidwe limeneli. Tidzaona m’nkhani zimenezi kuti anthu anasonyeza kukoma mtima kumeneku (1) mwa zimene anachita, (2) mwaufulu, ndiponso (3) kwa anthu osoŵa thandizo. Ndiponso, nkhani zimenezi zikusonyeza mmene tingakomere mtima lerolino.

Tate Anakoma Mtima

7. Kodi mnyamata wa Abrahamu ananena chiyani kwa Betuele ndi Labani, ndipo anadzutsa mfundo yotani?

7 Pa Genesis 24:28-67 akumaliza nkhani yonse ya mnyamata wa Abrahamu amene tam’tchula m’nkhani yoyamba ija. Mnyamatayo atakumana ndi Rabeka, anamuitana kunyumba kwa Betuele, tate wa mkaziyu. (Mavesi 28-32) Atafika kunyumbako, mnyamatayo anafotokoza mwatsatanetsatane zoti akufuna kupezera mkazi mwana wa Abrahamu. (Mavesi 33-47) Popeza zinthu zinam’yendera bwino mpaka kunyumbako, iye anaona zimenezo kukhala chizindikiro chakuti Yehova ali naye, “amene ananditsogolera ine m’njira yakuona, kuti ndikam’tengere mwana wamwamuna wake mwana wamkazi wa mphwake wa mbuyanga”; ndipo anawauza zimenezo motsindika. (Vesi 48) Mosakayika, mnyamatayo anayembekeza kuti kufotokoza kwake nkhaniyo kochokera pansi pa mtima kudzam’chititsa Betuele ndi mwana wake Labani kuona kuti Yehova ndiye amene anali kutsogolera zonsezi. Pomaliza, mnyamatayo anati: “Ngati mudzam’chitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iyayi, mundiuze; kuti ndipatukire kudzanja lamanja kapena kudzanja lamanzere.”​—Vesi 49.

8. Kodi Betuele anatani pankhani yokhudza Rebeka?

8 Yehova anali atakomera kale mtima Abrahamu. (Genesis 24:12, 14, 27) Kodi nayenso Betuele akanachita chimodzimodzi mwa kulola kuti Rebeka apite ndi mnyamata wa Abrahamu? Kodi kukoma mtima kwa munthu kukanagwirizana ndi kukoma mtima kwa Mulungu kuti kukwaniritse cholinga chake? Kapena kodi ulendo wautali wa mnyamatayo ukanangokhala wopanda phindu? Mnyamatayo ayenera kuti anasangalala kumva Labani ndi Betuele akuti: “Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi.” (Vesi 50) Iwo anazindikira kuti Yehova ndi amene anatsogolera zimenezi ndipo anavomereza mwamsanga zimene iye anali atagamula kale. Kenako, Betuele anasonyeza kukoma mtima kwake mwa kuwonjezera kuti: “Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.” (Vesi 51) Rebeka anatsagana ndi mnyamata wa Abrahamu popanda kunyinyirika, ndipo posakhalitsa anakhala mkazi wa Isake amene anam’konda kwambiri.​—Mavesi 49, 52-5867.

Mwana Anakoma Mtima

9, 10. (a) Kodi Yakobo anapempha Yosefe kuti amuchitire chiyani? (b) Kodi Yosefe anawakomera mtima bwanji atate ake?

9 Yakobo, mdzukulu wa Abrahamu, anakomeredwanso mtima. Iye anali kukhala ku Aigupto nthaŵi imeneyo, monga mmene Genesis chaputala 47 chikufotokozera, ndipo “nthaŵi inayandikira kuti [iye] adzafa.” (Mavesi 27-29) Anali ndi nkhaŵa chifukwa anali woti afera m’dziko lina osati limene Mulungu analonjeza Abrahamu. (Genesis 15:18; 35:10, 12; 49:29-32) Komabe, Yakobo sanafune kuti amuike m’manda ku Igupto komweko, choncho anakonza zoti mtembo wake adzautenge kupita nawo ku Kanani. Kodi panalinso wina kupatulapo mwana wake Yosefe waudindo amene akanatha kuonetsetsa kuti zofuna zake zachitikadi?

10 Nkhaniyo ikuti: ‘Ndipo [Yakobo] anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, . . . undichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m’Aigupto; koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m’dziko la Aigupto, ukandiike ine m’manda mwawo.’ (Genesis 47:29, 30) Yosefe analonjeza kuti adzachita zimenezo. Sipanapite nthaŵi ndipo Yakobo anamwalira. Yosefe pamodzi ndi ana ena a Yakobo anatenga mtembo wake “kuloŵa naye m’dziko la Kanani, ndi kumuika iye m’phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula.” (Genesis 50:5-8, 12-14) Umu ndi mmene Yosefe anakomera mtima atate ake.

Kukoma Mtima kwa Mpongozi

11, 12. (a) Kodi Rute anam’komera mtima bwanji Naomi? (b) Kodi kukoma mtima kwa Rute ‘kotsiriza’ kunaposa bwanji ‘koyamba’?

11 Buku la Rute limafotokoza mmene Naomi, mkazi wamasiye, anakomeredwa mtima ndi mpongozi wake wa ku Moabu, Rute, yemwenso anali wamasiye. Naomi ataganiza zobwerera ku Betelehemu ku Yuda, Rute anasonyeza kukoma mtima ndiponso kulimba mtima pamene ananena kuti: “Kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Patapita nthaŵi, Rute anasonyeza kukoma mtima pamene anaonetsa kuti akufuna kukwatiwa ndi Boazi wachikulire amene anali wachibale wa Naomi. * (Deuteronomo 25:5, 6; Rute 3:6-9) Boazi anauza Rute kuti: “Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.”​—Rute 3:10.

12 Kukoma mtima kwa Rute ‘koyamba’ ndi pamene anasiya anthu a kwawo ndi kukangamira Naomi. (Rute 1:14; 2:11) Koma kukoma mtima ‘kotsiriza,’ komwe kunali kuvomera kwake kuti akwatiwa ndi Boazi, kunaposa koyambako. Tsopano Rute akanatha kum’balira Naomi mwana woloŵa nyumba popeza Naomi anapitirira msinkhu wobereka. Ukwati unachitika, ndipo Rute atabala mwana, akazi a m’Betelehemu anafuula kuti: “Kwa Naomi kwam’badwira mwana.” (Rute 4:14, 17) Rute analidi “mkazi waulemu,” ndipo chifukwa cha zimene anachita anakhala ndi mwayi waukulu kwambiri popeza Yehova anam’patsa mphoto yokhala kholo la Yesu Kristu.​—Rute 2:12; 3:11; 4:18-22; Mateyu 1:1, 5, 6.

Mwa Zimene Anachita

13. Kodi Betuele, Yosefe, ndi Rute anasonyeza bwanji kukoma mtima?

13 Kodi mwaona mmene Betuele, Yosefe, ndi Rute anasonyezera kukoma mtima kwawo? Anachita zimenezo osati ndi mawu achifundo okha ayi, koma ntchito zawo. Betuele sanangonena kuti “taonani Rebeka ali pamaso pako” ayi, koma “anam’lola Rebeka . . . amuke.” (Genesis 24:51, 59) Yosefe atanena kuti “ndidzachita monga mwanena,” iye ndi abale ake anam’chitira Yakobo “monga anawalamulira iwo.” (Genesis 47:30; 50:12, 13) Rute sanangonena kuti, “Kumene mumukako ndimuka inenso” ayi, koma anasiyadi anthu a kwawo ndi kutsagana ndi Naomi, “namuka iwo aŵiriwo mpaka anafika ku Betelehemu.” (Rute 1:16, 19) Rute ali ku Yuda, anachitanso “zonse monga umo mpongozi wake adamuuza.” (Rute 3:6) Inde, kukoma mtima kwa Rute, monganso kwa anthu enawo, anakusonyeza ndi zimene anachita.

14. (a) Kodi atumiki a Mulungu masiku ano akusonyeza bwanji kukoma mtima mwa zimene akuchita? (b) Kodi ndi ntchito zotani zimene mukudziŵa za kukoma mtima zimene Akristu m’dera lanu amachita?

14 N’zosangalatsa kuona mmene atumiki a Mulungu lerolino akusonyezerabe kukoma mtima mwa zimene amachita. Mwachitsanzo, taganizani za amene nthaŵi zonse amalimbikitsa okhulupirira anzawo amene akudwala, kuvutika maganizo kapena kutonthoza olira. (Miyambo 12:25) Kapena taganizani za a Mboni za Yehova ambiri amene nthaŵi zonse amatenga okalamba pagalimoto kupita nawo ku Nyumba ya Ufumu kuti akakhale nawo pamisonkhano ya mpingo mlungu ndi mlungu. Agogo ena dzina lawo a Anna a zaka 82 omwe akudwala nyamakazi, analankhula zimene anthu enanso amaganiza. Anati: “Kunditenga pagalimoto kumisonkhano yonse ndi dalitso la Yehova. Ndikum’thokoza ndi mtima wonse pondipatsa abale ndi alongo achikondi otereŵa.” Kodi inunso mukuchita nawo zoterezi mumpingo wanu? (1 Yohane 3:17, 18) Ngati mukutero, dziŵani kuti ena akuyamikira zedi kukoma mtima kwanu.

Mwaufulu

15. Kodi tikuona mbali yotani pa kukoma mtima m’nkhani zitatu za m’Baibulo zimene takambirana zija?

15 Nkhani za m’Baibulo zimene takambiranazi zikuonetsanso kuti munthu amasonyeza kukoma mtima mwaufulu, osati mochita kum’kakamiza. Betuele mwaufulu anachita zimene mnyamata wa Abrahamu anapempha, ndipo Rebeka anachitanso chimodzimodzi. (Genesis 24:51, 58) Yosefe anasonyeza kukoma mtima popanda wina wake kumuumiriza. (Genesis 50:4, 5) Rute “analimbika kumuka naye [Naomi].” (Rute 1:18) Naomi atanena kuti Rute apite kwa Boazi, kukoma mtima kunachititsa mkazi ameneyu Mmoabu kunena kuti: “Zonse muzinena ndidzachita.”​—Rute 3:1-5.

16, 17. N’chiyani chikuchititsa kukoma mtima kwa Betuele, Yosefe, ndi Rute kukhala kwapadera kwambiri, ndipo n’chiyani chinawachititsa kusonyeza khalidwe limeneli?

16 Kukoma mtima kwa Betuele, Yosefe, ndi Rute kunali kwapadera kwambiri chifukwa Abrahamu, Yakobo, ndi Naomi sakanatha kuwaumiriza anthuŵa. Ndipotu, panalibe lamulo limene likanam’chititsa Betuele kulekana ndi mwana wake wamkaziyo. Akanatha kumuuza mnyamata wa Abrahamu kuti: ‘Ayi, sindifuna kuti mwana wanga wogwira ntchito molimbikayu apite kutali.’ (Genesis 24:18-20) N’chimodzimodzi ndi Yosefe. Anali ndi ufulu kuchita kapena kusachita zimene atate ake anamupempha, popeza Yakobo akanakhala atamwalira ndipo sakanamuumiriza kuti achite zimene anamuuza. Akakhala Naomi, iye ndiye anachita kumuuza Rute kuti anali ndi ufulu kutsala ku Moabu. (Rute 1:8) Rute analinso ndi ufulu kukwatiwa ndi mmodzi mwa “anyamata” m’malo mokwatiwa ndi Boazi yemwe anali wachikulire.

17 Betuele, Yosefe, ndi Rute anasonyeza kukoma mtima mwaufulu. Anafuna kuchita zimenezo kuchokera pansi pa mtima. Anaona kuti ndi udindo wawo kusonyeza khalidwe limeneli kwa abale awo, monganso mmene Mfumu Davide kenako anaonera kuti ndi udindo wake kukomera mtima Mefiboseti.

18. (a) Kodi akulu achikristu ‘amaŵeta nkhosa’ ndi mtima wotani? (b) Kodi mkulu wina anati amamva bwanji akamathandiza okhulupirira anzake?

18 Kukoma mtima kukadali chizindikiro cha anthu a Mulungu, kuphatikizapo amuna amene amabusa nkhosa za Mulungu. (Salmo 110:3; 1 Atesalonika 5:12) Akulu ameneŵa, kapena kuti oyang’anira, amaona kuti ndi udindo wawo kugwira ntchito imene anawapatsa mwa kuwaika pa udindo umenewu. (Machitidwe 20:28) Ngakhale zili choncho, ntchito yawo yoŵeta gulu la nkhosa ndiponso ntchito zina zosonyeza kukoma mtima zimene amachitira mpingo, sachita “mokangamiza, koma mwaufulu.” (1 Petro 5:2) Akulu amaŵeta gulu la nkhosa chifukwa chakuti ali ndi udindo umenewo ndiponso amafuna kutero. Amakomera mtima nkhosa za Kristu chifukwa chakuti ayenera kutero ndiponso amafuna kuchita zimenezi. (Yohane 21:15-17) Mkulu wina wachikristu anati: “Ndimasangalala kucheza kunyumba za abale kapena kuwaimbira foni n’cholinga chongofuna kuwasonyeza kuti ndimawaganizira. Kuthandiza abale kumandipatsa chimwemwe ndiponso kumandisangalatsa.” Akulu onse amene amaganizira ena angavomereze ndi mtima wonse kuti zimenezi n’zoona.

Komerani Mtima Anthu Osoŵa Thandizo

19. Kodi ndi mfundo iti yokhudza kukoma mtima imene nkhani za m’Baibulo zimene takambirana m’nkhani ino zikutsindika?

19 Nkhani za m’Baibulo zimene takambirana zikutsindikanso mfundo yosonyeza kukoma mtima kwa anthu osoŵa thandizo limene iwo paokha sangathe kulipeza. Abrahamu anafunikira thandizo la Betuele kuti mzere wa banja lake upitirire. Yakobo anafunikira thandizo la Yosefe kuti mtembo wake akauike ku Kanani. Ndipo Naomi anafunika thandizo la Rute kuti apeze mwana woloŵa nyumba. Abrahamu, Yakobo, ndi Naomi sakanatha kuchita zimenezo popanda thandizo. Mofananamo lerolino, tiyenera kusonyeza kukoma mtima makamaka kwa anthu osoŵa thandizo. (Miyambo 19:17) Tifunika kutsanzira Yobu, kholo lakale, amene anasamala “wozunzika wakufuula; mwana wamasiye yemwe wosoŵa mthandizi” ndiponso ‘iye amene akanatayika.’ Ndiponso, Yobu ‘anakondweretsa mtima wa mkazi wamasiye’ ndipo anali “maso a akhungu ndi mapazi a otsimphina.”​—Yobu 29:12-15.

20, 21. Kodi ndani amene amafuna kuti tiwakomere mtima, ndipo tonsefe tifunika kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

20 Inde, mumpingo uliwonse wachikristu muli ‘ozunzika akufuula.’ Mwina angasoŵe thandizo chifukwa cha kusungulumwa, kugwa ulesi, kudziona ngati wopanda pake, kukhumudwa chifukwa cha ena, matenda akayakaya, kapena kumwalira kwa munthu amene anali kum’konda. Kaya vutolo n’lotani, okondeka onseŵa amafuna thandizo limene ifeyo tingawapatse mwa kuwakomera mtima nthaŵi zonse mwaufulu.​—1 Atesalonika 5:14.

21 Ndiyetu, tiyeni titsanzire Yehova, Mulungu “wa ukoma mtima wochuluka.” (Eksodo 34:6; Aefeso 5:1) Tingatero mwa kuchitapo kanthu mwaufulu, makamaka pothandiza anthu amene akusoŵa thandizo. Ndipo mosakayika, tidzalemekeza Yehova ndi kupeza chimwemwe chachikulu pamene tipitiriza ‘kuchitira yense mnzake . . . kukoma mtima.’​—Zekariya 7:9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Kuti mudziŵe zambiri za ukwati wa mtundu umenewu, onani buku lakuti Insight on the Scriptures Voliyumu 1, tsamba 370. Amene amafalitsa bukuli ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi kukoma mtima kumene takambirana mu nkhani ino kukusiyana bwanji ndi kukoma mtima kwachibadwa?

• Kodi Betuele, Yosefe, ndi Rute anasonyeza bwanji kukoma mtima?

• Kodi tiyenera kusonyeza kukoma mtima ndi maganizo otani?

• Kodi ndani amene amafuna kuti tiwakomere mtima?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi Betuele anasonyeza bwanji kukoma mtima?

[Chithunzi patsamba 21]

Kukoma mtima kwa Rute kunapindulitsa Naomi

[Zithunzi patsamba 23]

Anthu amasonyeza kukoma mtima mwaufulu, mwa kuchitapo kanthu, ndiponso kwa anthu osoŵa thandizo