Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’kwanzeru kuti Mkristu akhale nawo pa mwambo wa maliro kapena ukwati wochitikira m’tchalitchi?

Yehova amadana ndi kuchita nawo zinthu zilizonse zokhudza kulambira konyenga ndipo tifunika kupeŵa zimenezi. (2 Akorinto 6:14-17; Chivumbulutso 18:4) Maliro a m’tchalitchi ndi mwambo wa chipembedzo umene mwachionekere amafotokozapo ziphunzitso zosagwirizana ndi malemba, monga zakuti mzimu sufa ndiponso kuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Pangakhalenso zochitika zina monga kupanga chizindikiro cha mtanda ndi kupemphera limodzi ndi wansembe kapena mtumiki. Pamwambo wa ukwati wochitikiranso m’tchalitchi pangakhale mapemphero ndi zochitika zina zachipembedzo zotsutsana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Mkristu zingam’vute kuti asachite nawo miyambo ya chipembedzo chonyenga ngati ali m’gulu la anthu amene akuchita zimenezo. Ndiyetu kungakhale kupanda nzeru kupezeka dala pamalo ngati amenewo.

Nanga bwanji ngati Mkristu akuona kuti akukakamizika kukakhala nawo pa mwambo wa maliro kapena ukwati wochitikira m’tchalitchi? Mwachitsanzo, mwamuna wosakhulupirira angaumirize mkazi wake yemwe ndi Mkristu kuti atsagane naye kumwambo wa maliro kapena ukwati. Kodi angatsagane naye kuti akangokhala duu n’kumangoonerera? Mkaziyo, poganizira zofuna za mwamuna wake, angaganize zotsagana naye, atatsimikiza mtima kuti sakachita nawo miyambo iliyonse ya chipembedzo. Kapena angasankhe kusatsagana naye, poganiza kuti mwina sizikatheka kuti akangokhala duu osachita nawo miyambo ya chipembedzoyo zimene zingam’chititse kuswa mfundo za makhalidwe abwino za Mulungu. Zili kwa iye kusankha chochita. Mosakayika, iye angafune kuti mtima wake usam’vute mwa kukhala ndi chikumbumtima choyera.​—1 Timoteo 1:19.

Kaya asankha kutsagana naye kapena ayi, angachite bwino kum’fotokozera mwamuna wakeyo kuti malinga ndi chikumbumtima chake, sangachite nawo miyambo iliyonse ya chipembedzo kapena kuimba nawo nyimbo kaya kugwetsa nkhope pamene iwo akupemphera. Mwina mwamunayo poona zimene mkaziyo wafotokoza, angaganize kuti ngati mkazi wakeyo atapita naye, pangakachitike zinazake zimene mwamunayo angakachite nazo manyazi. Mwina angaganize zopita yekha posonyeza kukonda mkazi wake, kulemekeza zikhulupiriro zake, kapena pofuna kupeŵa kukachita manyazi. Koma ngati akuumirira kuti atsagane nayebe basi, mkaziyo angapite kuti azikangoonerera.

N’kofunikanso kuganizira mmene kukhala nawo pa miyambo yochitikira m’tchalitchi kungakhudzire okhulupirira anzathu. Kodi sikuvulaza chikumbumtima cha ena? Kodi sikuwachititsa kufooka polimbana ndi kulambira mafano? Mtumwi Paulo analangiza kuti: “Mutsimikizire zinthu zofunika kwambiri, kuti mukhale opanda cholakwa ndi osakhumudwitsa ena kufikira tsiku la Kristu.”​—Afilipi 1:10, NW.

Achibale angaumirizenso Mkristu kuti akapezekepo ngati mwambowo uli wa wachibale wake wina. Mulimonse mmene zingakhalire, Mkristu ayenera kupenda mosamala mbali zonse. Mwina nthaŵi zina angaone kuti sipakakhala chovuta chilichonse atakakhala nawo pa mwambo wa maliro kapena ukwati wochitikira m’tchalitchi n’kumangoonerera. Komabe, mwina zingakhale kuti ngati wakapezekapo, chikumbumtima chake kapena cha ena chingavulale kwambiri kuposa phindu limene angapeze chifukwa chokhala nawo pamwambowo. Mulimonse mmene zinthu zilili, Mkristu ayenera kuonetsetsa kuti zimene wasankha kuchita siziwononga chikumbumtima chake chabwino pamaso pa Mulungu ndi anthu ena.