“Anamira”
“Anamira”
“Nyanja inawamiza; anamira mozama ngati mwala.”
MOSE ndi Aisrayeli ananena mawu ameneŵa m’nyimbo yokondwerera chipulumutso chawo pa Nyanja Yofiira komanso kuwonongedwa kwa mdani wawo Farao ndi magulu ake a nkhondo a ku Igupto amene ankawalondola.—Eksodo 15:4, 5.
Phunziro lomwe anatengapo aliyense amene ankaona chochitika chochititsa chidwi chimenecho linali lodziŵikiratu. Palibe amene angatsutsane ndi ulamuliro wa Yehova mpaka kupambana n’kukhala ndi moyo. Komabe, patangopita miyezi yoŵerengeka chabe, Aisrayeli otchuka—Kora, Datani, Abiramu, ndi otsatira awo 250—anatsutsa poyera ulamuliro umene Mulungu anapatsa Mose ndi Aroni.—Numeri 16:1-3.
Yehova atamulangiza, Mose anachenjeza Aisrayeli kuchoka m’mahema a anthu opandukawo. Datani ndi Abiramu pamodzi ndi a m’mabanja awo anakana kusintha maganizo awo. Kenako Mose analengeza kuti Yehova m’njira imene Iye akufuna, adzadziŵitsa Aisrayeliwo kuti anthu ameneŵa “anyoza Mulungu.” Atatero, Yehova anang’amba pansi pomwe iwo anaponda. “Chomwecho iwowa, ndi onse anali nawo, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo.” Nanga Kora ndi opanduka ena zinawayendera bwanji? “Moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana aŵiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.”—Numeri 16:23-35; 26:10.
Farao ndi magulu ake ankhondo, komanso anthu amene anapanduka m’chipululu, onse anawonongeka psiti chifukwa cholephera kuzindikira ulamuliro wa Yehova komanso chidwi chomwe iye ali nacho pankhani zokhudza anthu ake. Choncho, n’kofunika kwambiri kuti onse amene akufuna kuti Yehova aziwateteza m’masiku ovuta ano, aphunzire za Yehova ndiponso kumumvera monga “Wam’mwambamwamba” komanso “Wamphamvuyonse.” Akatero, angatsimikize kuti zivute zitani mawu a Yehova adzakwaniritsidwa. Anati: “Pambali pako padzagwa chikwi, ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako; sichidzakuyandikiza iwe. Koma udzapenya ndi maso ako, nudzaona kubwezera chilango oipa. Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga! Udaika Wam’mwambamwamba chokhalamo chako.”—Salmo 91:1, 7-9.