Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Imfa Mumaiona Bwanji?

Kodi Imfa Mumaiona Bwanji?

Kodi Imfa Mumaiona Bwanji?

IMFA imatidetsa nkhaŵa tsiku ndi tsiku. Kaya ndife a thanzi labwino kapena olemera, titha kufa nthaŵi iliyonse podutsa pamsewu kapena pogona. Masoka monga kuukira kwa zigaŵenga komwe kunachitika pa September 11, 2001, m’mizinda ya New York City ndi Washington, D.C., kumatichititsa kuzindikira kuti “mdani wotsiriza” imfa, akupha anthu alionse komanso a zaka zosiyanasiyana. Nthaŵi zina mdani ameneyu amapha anthu ambirimbiri pa mphindi zoŵerengeka chabe.​—1 Akorinto 15:26.

Ngakhale kuti imfa ndi yoopsa chonchi, anthu akuoneka kuti amachita nayo chidwi. Zikuoneka kuti nkhani za imfa zimachititsa anthu kugula nyuzipepala kwambiri kapena kuonerera wailesi yakanema kuposa nkhani ina iliyonse, makamaka ngati akufotokoza za kufa kwa anthu ambirimbiri pa zochitika zoopsa. Anthu akuoneka kuti sakutopa ndi nkhani za imfa, kaya pankhondo, tsoka lachilengedwe, upandu, kapena matenda. Kuchita chidwi ndi imfa kumeneku kumakula kwambiri makamaka ngati womwalirayo anali munthu wodziŵika kwambiri kapena wotchuka.

Zimenezi n’zoona ndipo palibe angakane. Anthu akupitirizabe kuchita chidwi ena akafa. Koma ikakhala yawo, amaiopa kwambiri. Imfa yathu ndi nkhani imene ambirife sitifuna kuiganizira n’komwe.

Aima Mitu ndi Imfa

Anthufe nthaŵi zonse sitifuna kuganiza za imfa yathu ndipo zidzakhalabe choncho. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Mulungu anaika mwa ife chilakolako chofuna kukhala ndi moyo kosatha. Lemba la Mlaliki 3:11 limati: “Ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo.” Motero, imfa yasokoneza zinthu m’matupi a anthu ndipo siikugwirizanabe ndi thupi. Pofuna kuthetsa kusagwirizana kumeneku ndi kukwaniritsa chilakolako chachibadwa chofuna kukhala ndi moyo kosatha, anthu apeka zikhulupiriro zosiyanasiyana monga kusafa kwa moyo ndiponso kubadwanso munthu akamwalira.

Mulimonsemo, mfundo n’njakuti, kulikonse imfa n’njosautsa ndiponso yoopsa. Choncho, sitiyenera kudabwa kuti ambiri amati ndi yothetsa nzeru. Mwa zina, imaonetsa poyera kuti moyo wokhalira kufunafuna chuma komanso ulamuliro n’ngopanda phindu.

Kodi Kufera ku Chipatala Kumawalekanitsa?

Kale munthu wodwala kapena wovulala mwakayakaya nthaŵi zambiri ankamusiya kuti afere kwawo achibale ake alipo. Izi n’zimene kaŵirikaŵiri zinkachitika m’nthaŵi za m’Baibulo ndipo zikuchitikabe m’madera ena. (Genesis 49:1, 2, 33) Zikatero, banja lonse ndi ana omwe, limakhala pamodzi kukambirana za wodwalayo. Izi zimathandiza kuti aliyense m’banjamo adziŵe kuti sakulira yekha. Zimatonthozanso kwambiri popeza aliyense amakhala ndi udindo komanso chisoni.

Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zomwe zimachitika m’madera amene kukambirana za imfa amati n’kulaula komanso malodza. Ana amawachotsa poganiza kuti “ziwasokoneza maganizo mopitirira muyeso.” Kufa masiku ano n’kosiyana m’njira zambiri. Nthaŵi zambiri munthu amafa ali yekhayekha. Ngakhale kuti ambiri angakonde kuti banja lawo liziwasamalira ndiponso kufa mwamtendere kunyumba kwawo, anthu ambiri amafera kuchipatala. Kumeneko nthaŵi zambiri amakhala okhaokha kwinaku akumva ululu, atawamangilira zinthu zosiyanasiyana za chipangizo choopsa chamagetsi. Mosiyana ndi zimenezo, anthu miyandamiyanda amangofa mosadziŵika bwino, monga amene amafa pa ziwembu zopulula fuko, chilala, AIDS, nkhondo yapachiŵeniŵeni ngakhalenso umphaŵi wadzaoneni.

Nkhani Yofunika Kuiganizira

Baibulo silimaletsa kuganizira za imfa. Lemba la Mlaliki 7:2 limati: “Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse.” Tikaganizira zoti tidzafa, tingachotse nkhaŵa zathu za tsiku ndi tsiku ndi kukumbukira kuti moyo ndi waufupi kwambiri. Zimenezi zingatithandize kukhala ndi cholinga pa moyo m’malo mongodzikhalira popanda cholinga ndiponso kungowononga nthaŵi imene tili ndi moyo.

Kodi imfa mumaiona bwanji? Kodi mwalingalirapo mofatsa zomwe mumaganiza, kukhulupirira, kuyembekezera, kapena kuopa pankhani ya kutha kwa moyo wanu?

Monga mmene moyo ulili, imfa nayonso munthu sangathe kuifotokoza kapena kuimvetsa. Mlengi yekha ndiye anganene motsindika zoona zake pankhaniyi. Iye ndiye ali ndi “chitsime cha moyo,” komanso njira “zopulumutsira kuimfa.” (Salmo 36:9; 68:20) Ngakhale kuti zingaoneke zodabwitsa, kufufuza bwino zina mwa zikhulupiriro zotchuka zokhudza imfa poziyerekezera ndi zomwe Mawu a Mulungu amanena, kutitonthoza ndiponso kutilimbikitsa. Kuvumbula kuti imfa si mapeto a zonse ayi.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Kudziŵa kuti tidzafa kumatithandiza kukhala ndi moyo m’njira yopindulitsa kwambiri