Kufufuza Bwino Zikhulupiriro Zina Zopeka Zokhudza Imfa
Kufufuza Bwino Zikhulupiriro Zina Zopeka Zokhudza Imfa
KUYAMBIRA kale, anthu amaima mitu ndi imfa ndiponso imawachititsa mantha. Komanso, kuopa imfa kwapitirizabe chifukwa cha ziphunzitso zonyenga za chipembedzo, miyambo yotchuka, ndiponso zikhulupiriro zomwe zinazika mizu mwa anthu. Vuto la kuopa imfa n’lakuti munthu amalephera kusangalala ndi moyo komanso kuona kuti moyo uli ndi cholinga.
Zipembedzo zotchuka ndizo zili ndi mlandu wolimbikitsa zikhulupiriro zopeka zofalazi. Mothandizidwa ndi choonadi cha m’Baibulo, onani ngati mungasinthe maganizo anu okhudza imfa mwa kufufuza zina mwa zikhulupiriro zimenezi.
Chikhulupiriro chopeka choyamba: Imfa ndiyo kutha kwa moyo Komwe Mulungu anaika.
Buku lakuti Death—The Final Stage of Growth limanena kuti: “Imfa . . . ndi mbali ya miyoyo yathu.” Mawu ngati ameneŵa amagwirizana ndi chikhulupiriro chakuti imfa siyachilendo, ndipo kuti mapeto a zamoyo zonse ndi imfa basi. Chotero, chikhulupirirochi chalimbikitsa maganizo akuti moyo ndi wopanda pake ndiponso chachititsa anthu ambiri kukhala opanda khalidwe.
Koma kodi imfa ndi mapeto achibadwa a moyo? Ofufuza zinthu ena sakhulupirira zimenezi. Mwachitsanzo, katswiri wina wa zamoyo, Calvin Harvey, amene akufufuza za kukalamba kwa anthu atamufunsa anati sakukhulupirira kuti anthu “anawapanga kuti azifa.” William Clark yemwe ndi katswiri wasayansi ya mphamvu zathupi zotetezera ku matenda anati: “Imfa simbali ya moyo.” Seymour Benzer wapasukulu ya zaumisiri ya California Institute of Technology, nayenso anati, “tingayembekezere kuti kukalamba kudzatha.”
Asayansi amaima mitu akamafufuza mmene munthu anamupangira. Amaona kuti anthufe anatipatsa mphamvu zambiri kuposa zomwe tingagwiritse ntchito pa zaka 70 kapena 80 zomwe timakhala ndi moyo. Mwachitsanzo, asayansi apeza kuti ubongo wa munthu uli ndi mphamvu yaikulu kwambiri yokumbukira zinthu. Wofufuza wina ananena kuti ubongo wathu ungasunge chidziŵitso chomwe “chingadzaze mabuku mamiliyoni makumi aŵiri, omwe ndi mabuku ochuluka ngati amene amapezeka m’malaibulale akuluakulu a padziko lonse.” Akatswiri ena asayansi ya ubongo amakhulupirira kuti munthu pa moyo wake wonse amagwiritsa ntchito chigawo chimodzi mwa zigawo 10,000 za mphamvu zonse za ubongo wake. M’pake kufunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani tili ndi ubongo wamphamvu motere pamene timangogwiritsa ntchito chigawo chochepa chabe pa moyo wathu?’
Taganiziraninso mmene anthu amachitira wina akafa. Kwa anthu ambiri, imfa ya mkazi wawo, mwamuna wawo, kapena ana, imakhala chochitika chopweteka kwambiri pa moyo wawo. Maganizo a anthu amasokonezeka kwanthaŵi yaitali munthu amene anali kumukonda akamwalira. Ngakhale anthu amene amati imfa ndi
yachibadwa, zimawavuta kuvomereza kuti imfa yawo ndi mapeto a zonse. Magazini ya British Medical Journal inanena za “maganizo ofala a akatswiri akuti, aliyense amafuna kukhala ndi moyo wautali mmene angathere.”Poganizira zomwe anthu amachita wina akafa, mphamvu yawo yodabwitsa yokumbukira ndi kuphunzira zinthu, komanso chilakolako chawo chofuna kukhala ndi moyo kosatha, kodi sizodziŵikiratu kuti anthu anawapanga kuti akhale ndi moyo kosatha? Inde, Mulungu anatilenga anthufe kuti tikhale ndi moyo kosatha, osati kuti tizifa ayi. Dziŵani kuti Mulungu anaika tsogolo la anthu aŵiri oyambawo kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Tsogolotu labwino ndiponso losatha limeneli.
Chikhulupiriro chopeka chachiŵiri: Mulungu amatenga anthu kudzera mu imfa kuti akakhale naye.
Mayi wina wa zaka 27 amene anali kutsirizika ndi kusiya ana ake atatu, anauza mvirigo wachikatolika kuti: “Musaloŵe muno ndi kundiuza kuti imfa yangayi ndi chifuniro cha Mulungu . . . Munthu akamandiuza zimenezi ndimadana nazo kwambiri.” Komabe, mfundo yoti Mulungu amatenga anthu kukakhala pafupi naye ndi imene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa.
Kodi Mlengi ndi wankhanza moti mpaka amachititsa imfa kwinaku akudziŵa kuti zimenezi zimatipweteka mumtima? Ayi. Mulungu amene Baibulo limatchula sangachite zimenezo. Lemba la 1 Yohane 4:8, limati: “Mulungu ndiye chikondi.” Onani kuti lembali silikunena kuti Mulungu ali ndi chikondi kapena kuti Mulungu ndi wachikondi koma likuti Mulungu ndiye chikondi. Chikondi cha Mulungu n’chachikulu, choyera, changwiro, moti khalidwe lake ndi zochita zake zonse n’zachikondi. Chotero, mpake kunena kuti mkhalidwe weniweni wa Mulungu ndiwo chikondi. Ameneyu si Mulungu amene amatenga anthu kudzera mu imfa kuti akhale naye pafupi ayi.
Chipembedzo chonyenga chasokoneza anthu ambiri pankhani ya kumene akufa amapita komanso chimene chimachitika munthu akafa. Zina mwa zikhulupiriro zosiyanasiyana zovuta kumvetsa komanso zochititsa mantha ndi izi: kupita kumwamba, helo, purigatoriyo, Limbo. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limatiuza kuti akufa sadziŵa kanthu, ali ngati munthu amene wagona. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 11:11-14) Chotero, sitifunika kuda nkhaŵa ndi zomwe zimachitika tikamwalira, monga momwe sitidera nkhaŵa tikaona munthu wina akugona. Yesu anatchula za nthaŵi imene ‘onse ali m’manda adzatuluka’ n’kukhala ndi moyo wabwino padziko lapansi la paradaiso.—Yohane 5:28, 29; Luka 23:43.
Chikhulupiriro chopeka chachitatu: Mulungu amatenga ana aang’ono kuti akakhale angelo.
Elisabeth Kübler-Ross yemwe anaphunzira za anthu odwala mwakayakaya, anatchula maganizo ena ofala kwambiri kwa anthu achipembedzo. Posimba zomwe zinachitikadi, iye anati “n’kupanda nzeru kuuza mwana wamng’ono amene mbale wake wamwalira kuti Mulungu amakonda kwambiri ana aang’ono moti wamutenga Johnny kupita naye kumwamba.” Kutero n’kumunamizira Mulungu ndipo mawu ngati ameneŵa sasonyeza umunthu wake ndi khalidwe lake. Dr. Kübler-Ross anapitiriza kuti: “Mwanayo atakula kukhala mayi, mkwiyo wake ndi Mulungu unali ukadalipo ndipo zotsatira zake zinali zakuti patatha zaka makumi atatu iye anadwala ndi maganizo mwana wake wamwamuna atamwalira.”
Kodi Mulungu angatengerenji mwana kuti akhale mngelo, ngati kuti Mulunguyo amafuna ana kwambiri kuposa mmene makolo awo amawafunira? Zikanakhala kuti zimenezi n’zoona, iye akanakhala Mlengi wopanda chikondi, wodzikonda, si choncho kodi? Mosiyana ndi maganizo ameneŵa, Baibulo limati: “Chikondi chichokera kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:7) Kodi Mulungu wachikondi angachite bwanji chinthu chomwe ngakhale anthu omwe amadziŵa zochepa chabe za makhalidwe abwino sangavomereze?
Nangano n’chifukwa chiyani ana amafa? Mbali imodzi ya yankho la m’Baibulo lili pa Mlaliki 9:11. Limati: “Nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimawagwera iwo onse,” (NW). Ndipo lemba la Salmo 51:5 limatiuza kuti tonsefe ndife opanda ungwiro, ochimwa, kuchokera pamene mayi anatenga pakati pathu. Zotsatira zake tsopano n’zakuti anthu onse amafa ndi zinthu zosiyanasiyana. Nthaŵi zina mwana amafa asanabadwe ndipo zikatero mayi amapita padera. Nthaŵi zinanso ana amafa chifukwa cha masoka kapena ngozi. Si Mulungu amene amachititsa zinthu zimenezi ayi.
Chikhulupiriro chopeka chachinayi: Anthu ena amalangika akamwalira.
Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti anthu oipa amapita ku moto wa helo ndipo amakalangika kosatha. Kodi chiphunzitsochi n’choona komanso cha m’Malemba? Anthu amakhala ndi moyo zaka 70 kapena 80 zokha basi. Ngakhale munthuyo atakhala woipitsitsa pa moyo wake wonse, kodi chingakhale chilungamo kumulanga kosatha? Ayi. Kungakhale kupanda chilungamo kwakukulu kulanga munthu kosatha chifukwa cha machimo omwe anachita panthaŵi yochepa ya moyo wake.
Mulungu yekha ndiye angaulule zimene zimachitika munthu akamwalira ndipo wachita kale zimenezi m’Mawu ake Baibulo. Ilo limati: “Monga winayo [munthu] angofa momwemo zinazo [nyama] zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi . . . Onse apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.” (Mlaliki 3:19, 20) Apa sakutchulapo za moto wa helo ayi. Anthu akamwalira amabwerera kufumbi kapena kuti sakhalakonso.
Munthu amene akudziŵa ndiye angalangike. Kodi akufa amadziŵa kalikonse? Apanso, Baibulo limayankha kuti: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphoto; pakuti angoiwalika.” (Mlaliki 9:5) N’zosatheka kuti akufa omwe “sadziŵa kanthu” azizunzika kwinakwake.
Chikhulupiriro chopeka chachisanu: Imfa ndiyo mapeto athu amuyaya.
Timasiya kukhalako tikamwalira, koma zimenezi sizitanthauza kuti zonse zathera pomwepo ayi. Munthu wokhulupirika Yobu ankadziŵa kuti adzapita kumanda, kapena kuti ku Sheol, akamwalira. Koma tamvani pemphero lake kwa Yobu 14:13-15.
Mulungu. Anati: “Ha! mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m’tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? . . . Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani.”—Yobu ankakhulupirira kuti ngati akanakhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake, Mulungu akanam’kumbukira ndipo akanamuukitsa panthaŵi yake. Atumiki a Mulungu onse kalelo ankakhulupirira zimenezi. Yesu anatsimikiza chikhulupiriro chimenechi ndipo anasonyeza kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito iyeyo kuukitsa akufa. Mawu a Kristu amatitsimikizira kuti: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu a [Yesu], nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”—Yohane 5:28, 29.
Posachedwapa Mulungu adzachotsa kuipa konse ndipo adzakhazikitsa dziko latsopano la olamulira akumwamba. (Salmo 37:10, 11; Danieli 2:44; Chivumbulutso 16:14, 16) Zotsatira zake zidzakhala zakuti dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso ndipo anthu amene amatumikira Mulungu ndiwo adzakhale mmenemo. Timaŵerenga m’Baibulo kuti: “Ndinamva mawu aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Musaope
Kudziŵa chiyembekezo cha chiukiriro pamodzi ndi kudziŵa Amene analonjeza zimenezi kungakulimbikitseni kwambiri. Yesu analonjeza kuti: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Zimenezi zimaphatikizapo kutimasula kuti tisaope imfa. Yehova yekha ndiye angasinthe zinthu kuti tisamakalambe ndi kufa komanso ndiye angatipatse moyo wosatha. Kodi mungakhulupirire malonjezo a Mulungu? Inde mungatero, chifukwa chakuti nthaŵi zonse Mawu a Mulungu amachitikadi. (Yesaya 55:11) Tikukulimbikitsani kuphunzira zambiri zokhudza zolinga za Mulungu kwa anthu. Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuthandizani.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Vuto la kuopa imfa n’lakuti munthu amalephera kusangalala ndi moyo
[Tchati patsamba 7]
ZIKHULUPIRIRO ZINA ZOPEKA KODI MALEMBA AMATI
ZOFALA ZOKHUDZA IMFA CHIYANI PANKHANIYI?
● Imfa ndiyo kutha kwa Genesis 1:28; 2:17; Aroma 5:12
moyo komwe Mulungu anaika
● Mulungu amatenga anthu kudzera Yobu 34:15; Salmo 37:11, 29; 115:16
mu imfa kuti akakhale naye
● Mulungu amatenga ana Salmo 51:5; 104:1, 4;
aang’ono kuti akakhale angelo Ahebri 1:7, 14
● Anthu ena amalangika Salmo 146:4; Mlaliki 9:5, 10;
akamwalira Aroma 6:23
● Imfa ndiyo mapeto athu Yobu 14:14, 15; Yohane 3:16; 17:3;
amuyaya Machitidwe 24:15
[Chithunzi patsamba 8]
Kudziŵa zoona zake za imfa kumatimasula kuti tisaope
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
Barrators—Giampolo/The Doré Illustrations For Dante’s Divine Comedy/Dover Publications Inc.