Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupindula Chifukwa Chodzipereka Kutumikira Mulungu

Kupindula Chifukwa Chodzipereka Kutumikira Mulungu

Mbiri ya Moyo Wanga

Kupindula Chifukwa Chodzipereka Kutumikira Mulungu

YOSIMBIDWA NDI WILLIAM AIHINORIA

Ndinadzuka pakati pausiku chifukwa cha kulira kwa bambo; ankalira nthaŵi zambiri. Iwo anali kugubuduzika pansi atagwira pamimba. Mayi, mlongo wanga wamkulu, ndi ine tinawazungulira. M’mimbamo mutalekako pang’ono kupweteka, anakhala tsonga, anadzuma, kenako anati: “Mboni za Yehova zokha ndizo zili ndi mtendere padziko lapansi pano.” Mawu ameneŵa anali odabwitsa, koma anandikhudza kwambiri chifukwa ndinali ndisanamvepo za Mboni za Yehova. Ndinafunitsitsa kudziŵa zomwe ankatanthauza.

ZIMENEZI zinachitika mu 1953 ndili ndi zaka zisanu ndi chimodzi. Bambo anga anali ndi mitala. Mudzi wathu wa Ewossa, womwe unkadalira ulimi, unali kumadzulo chapakati pa dziko la Nigeria. Ndinali mwana wachiŵiri, koma mnyamata woyamba m’banja lathu lomwe m’kupita kwa nthaŵi linakula chifukwa bambo anali ndi akazi atatu ndiponso ana khumi ndi atatu. Tonse tinali kukhala m’nyumba yomata ya agogo, yofolera ndi udzu, ya zipinda zinayi. Enanso omwe ankakhala m’nyumbayo anali agogo aakazi komanso abale awo atatu a bambo anga pamodzi ndi mabanja awo.

Moyo wanga woyambirira unali womvetsa chisoni kwambiri. Kudwala kwa bambo anga ndiko makamaka kunachititsa zimenezi. Anali kumva kupweteka m’mimba ndipo matendawo anatenga zaka zambiri mpaka kenako anamwalira. Matenda osadziŵikawo sanali kumva mankhwala omwe banja lathu losauka likanatha kugula kaya azitsamba kapena achizungu. Nthaŵi zambiri tinali kulira pamodzi ndi bambo usiku wonse, kwinaku iwo akugubuduzika pansi ndi ululu mpaka atambala kulira m’mbandakucha. Nthaŵi zambiri bambo ndi mayi pofunafuna mankhwala anali kuchoka kundisiya ine ndi abale anga m’manja mwa agogo aakazi.

Banja lathu linkapeza zofunika pa moyo mwa kulima ndi kugulitsa chilazi, chinangwa, ndi mtedza wa kola. Tinalinso kugulitsa manthova opangira mphira kuti tiwonjezere pa ndalama zochepa zomwe tinkapeza. Chakudya chathu chenicheni chinali chilazi. M’maŵa tinkadya chilazi chongophika, nsima ya chilazi masana, ndi chilazi chophika madzulo. Mwa apo ndi apo tinali kusintha mwa kudya nthochi zowotcha.

Mbali yofunika kwambiri pa moyo wathu inali kulambira makolo omwe anamwalira. Banja lathu linkapereka chakudya kwa makolowo mwa kuchiika patsogolo pa timitengo tomwe anamangirirako zigoba zonyezimira za nkhono zosiyanasiyana za m’nyanja. Bambo analinso kulambira fano linalake eti kuti achotse mizimu yoipa komanso kuthamangitsa mfiti.

Ndili ndi zaka zisanu, tinasamuka kumudzi kwathu kwanthaŵi yochepa chabe kupita kumsasa wa zaulimi womwe unali pamtunda wamakilomita khumi ndi limodzi kuchokera kumudzi kwathu. Kumeneko, bambo anadwala matenda a njoka za m’mimba ndipo zimenezi zinawonjezera vuto la m’mimba lomwe anali nalo kale. Sankagwira ntchito masana, ndipo usiku m’mimba munali kuwapweteka kwambiri. Inenso matekenya anandigwira. Zitatero, banja lathu linkangodalira thandizo kuchokera kwa achibale athu ena. Pokana kungodzifera pa msasa, tinabwerera kumudzi kwathu ku Ewossa. Bambo anga ankafuna kuti ine, mwana wawo woyamba wamwamuna, ndisadzakhale mlimi wamba. Choncho, anaona kuti maphunziro abwino adzandithandiza kutukula moyo wa banja lathu komanso kulera abale anga.

Kudziŵa Zipembedzo Zosiyanasiyana

Titabwerera kumudzi, ndinayamba sukulu. Izi zinandichititsa kudziŵa zipembedzo zachikristu. M’ma 1950, maphunziro a Azungu anali ogwirizana kwambiri ndi chipembedzo cha olamulira achizunguwo. Popeza ndinali kupita kusukulu ya pulayimale ya chikatolika ndiye kuti ndinayenera kukhala wa Roma Katolika.

Mu 1966, chaka chomwe ndinakwanitsa zaka 19, anandisankhira ku sukulu ya sekondale ya Pilgrim Baptist m’tauni ya Ewohinmi, makilomita asanu ndi atatu kuchokera ku Ewossa. Kumeneko zimene ndinkaphunzira pankhani yachipembedzo zinasintha. Popeza tsopano ndinali pasukulu yachipulotesitanti, ansembe achikatolika anandiletsa kudya nawo Misa ya Lamlungu.

Ndili pasukulu ya Baptist imeneyi m’pamene ndinaŵerenga Baibulo kwanthaŵi yanga yoyamba. Ngakhale kuti ndinkapitabe kutchalitchi cha Katolika, ndinkaŵerenga Baibulo Lamlungu lililonse ndikabwerako kutchalitchiko. Zomwe Yesu Kristu ankaphunzitsa zinkandisangalatsa kwambiri, ndipo zinandichititsa kukhala ndi chilakolako chofuna kukhala ndi moyo waphindu wodzipereka kutumikira Mulungu. N’taŵerenga kwambiri Baibulo, chinyengo cha atsogoleri ena amatchalitchi komanso kupanda khalidwe kwa anthu wamba a m’matchalitchiwo kunkandinyansa kwambiri. Zimene ankachita omwe ankati ndi Akristu zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe Yesu ndi ophunzira ake ankaphunzitsa ndi kuchita.

Zomwe zinachitika nthaŵi ina zinandikhumudwitsa kwambiri. Tsiku lina n’tapita ku kasitolo ka mishoni kuti ndikagule kolona, ndinaona chithumwa atachikoloŵeka pakhomo la kasitoloko. Tsiku linanso, mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya Baptist imeneyo anafuna kundigwirira. Ndinadziŵa pambuyo pake kuti iye amagona amuna anzake ndipo kuti anagonapo kale ena. Ndinaganizira zinthu zimenezi ndipo ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amavomereza chipembedzo chomwe anthu ake ngakhale atsogoleri ake salangidwa chifukwa cha machimo aakulu?

Kusintha Chipembedzo

Komabe zomwe ndinkaŵerenga m’Baibulo ndinkazikonda kwambiri moti ndinaganiza zopitiriza kuliŵerenga. Inali nthaŵi imeneyi pamene ndinayamba kukumbukira mawu omwe bambo anga ananena zaka 15 m’mbuyomo. Anati: “Mboni za Yehova zokha ndizo zili ndi mtendere padziko lapansi pano.” Koma ndinkaopa chifukwa ana a Mboni pasukulu yathu anali kuwaseka ndiponso nthaŵi zina kuwalanga chifukwa chakuti sanali kuchita nawo mapemphero a m’maŵa. Komanso zikhulupiriro zawo zina zinkaoneka zachilendo kwambiri. Mwachitsanzo, zinkandivuta kukhulupirira kuti anthu 144,000 okha ndiwo opita kumwamba. (Chivumbulutso 14:3) Popeza ndinkafuna kudzapita kumwamba, ndinadzifunsa ngati anthu ameneŵa anakwana kale ine ndisanabadwe.

Zinali zoonekeratu kuti makhalidwe ndi maganizo a Mboni anali osiyana ndi a ena. Iwo sankachita nawo zinthu zopanda mkhalidwe komanso zachiwawa zomwe ana ena ankachita pasukulupo. Kwa ine, iwo analidi olekana ndi dziko lapansi monga momwe ndinaŵerengera m’Baibulo kuti otsatira chipembedzo choona ayenera kutero.​—Yohane 17:14-16; Yakobo 1:27.

Ndinaganiza zoti ndifufuze zambiri. Mu September 1969, ndinapeza buku lakuti “Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya.” Mwezi wotsatira, mpainiya wina, dzina la mtumiki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, anayamba kuphunzira nane. Phunziro loyambalo linandilimbikitsa kwambiri moti Loŵeruka madzulo ndinayamba kuŵerenga buku lakuti Coonadi ndipo ndinalimaliza tsiku lotsatira masana. Nthaŵi yomweyo, ndinayamba kuuza ophunzira anzanga zinthu zabwino kwambiri zomwe ndaŵerenga. Ophunzira anzanga ndi aphunzitsi ankaganiza kuti chipembedzo chatsopano chomwe ndayamba chandichititsa misala. Koma ndinkadziŵa kuti sinali misala.​—Machitidwe 26:24.

Makolo anga anamva zoti ndikulalikira chipembedzo chatsopano. Nthaŵi yomweyo anandiitanitsa kupita kunyumba kuti akamve vuto langa. Panalibe aliyense amene ndikanafunsirako nzeru, chifukwa chakuti a Mboni onse anali atapita kumsonkhano wawo wachigawo m’tauni ya Ilesha. N’tapita kunyumba, mayi ndi achibale ena anandipanikiza ndi mafunso komanso anandidzudzula kwambiri. Ndinayesetsa kwambiri kuteteza zomwe ndinkaphunzira m’Baibulo.​—1 Petro 3:15.

Amalume atalephera kupereka umboni wotsimikizira kuti Mboni za Yehova ndi aphunzitsi onyenga, iwo anayesa njira ina. Anandipempha, amvekere: “Usaiŵale kuti unapita kusukulu kuti ukaphunzire. Ndiye ngati umasiya kuŵerenga n’kupita kokalalikira ndiye kuti sukulu suimaliza. Chotero, bwanji umalize kaye sukulu usanayambe chipembedzo chako chatsopanocho.” Panthaŵiyo zimenezi zinaoneka ngati zanzeru moti ndinasiya kuphunzira ndi Mboni.

N’tangomaliza maphunziro anga mu December 1970, ndinapita ku Nyumba ya Ufumu ndipo ndakhala ndikupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova mpaka lero. Pa August 30, 1971, ndinabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwanga kwa Mulungu. Izi zinawavutitsa maganizo kwambiri makolo anga komanso anthu ena onse m’mudzimo. Iwo anati ndawakhumudwitsa chifukwa chakuti ndinali woyamba m’mudzi wa Ewossa kuti boma lindilipirire sukulu. Anthu ochuluka anali kuyembekezera zambiri kuchokera kwa ine. Ankaganiza kuti ndidzagwiritsa ntchito maphunziro angawo kutukula deralo.

Zotsatira za Kusintha Kwanga

Banja langa ndi akuluakulu ena a m’mudzimo anatumiza anthu kuti andinyengerere kuti ndisiye chipembedzo changa. Pofuna kuti ndichite zimenezo iwo ananditemberera. Anati: “Ngati susiya chipembedzo chimenechi ndiye kuti wawononga tsogolo lako. Ntchito sudzaipeza. Sudzamanga nyumba yakoyako. Sudzakwatira ndi kukhala ndi ana.”

Mosiyana ndi zimene ananenazo, patangotha miyezi khumi n’tamaliza sukulu, ndinapeza ntchito yauphunzitsi. Mu October 1972, ndinakwatira Veronica mkazi wanga wokondedwa. Kenako boma linandiphunzitsa kukhala mlangizi wa zaulimi. Ndinagula galimoto langa loyamba ndipo ndinayamba kumanga nyumba yathu. Pa November 5, 1973, mwana wathu wamkazi woyamba Victory anabadwa, ndipo zaka zotsatira tinakhalanso ndi ana ena, Lydia, Wilfred, ndi Joan. Mu 1986 mwana wathu womaliza, Micah, anabadwa. Onseŵa ndi ana abwino kwambiri, cholandira chamtengodi wapatali kuchokera kwa Yehova.​—Salmo 127:3.

Ndikaganiza za moyo wakumbuyo, ndinganene kuti matemberero onse a anthu akumudzi kwathu asanduka madalitso. N’chifukwa chake ndinatchula mwana wanga woyamba dzina lakuti Victory (Chipambano). Posachedwapa anthu akumudzi anandilembera kalata ndipo anati: “Chonde bwererani kumudzi tsopano mudzathandize kutukula dera lanu popeza Mulungu akukudalitsani.”

Kulera Ana Motsatira Njira za Mulungu

Ine ndi mkazi wanga tinadziŵa kuti sitingachite zinthu ziŵiri nthaŵi imodzi, kusenza udindo wathu womwe Mulungu anatipatsa wolera ana komanso kufunafuna chuma. Choncho, tinaphunzira kukhutira ndi moyo wosalira zambiri. Tinasankha kukhala ndi moyo woterowo m’malo mokumana ndi zotsatira zoonekeratu za moyo winawo.

M’dziko lathu lino n’zofala kwambiri kuti mabanja angapo azikhala m’nyumba imodzi, kumagwiritsa ntchito bafa limodzi, ziwiya za ku khichini, ndi zina zotero. Tinkasangalala kuchita lendi nyumba yokwanira banja lathu lokha m’tauni iliyonse yomwe anali kunditumiza monga wogwira ntchito za boma. N’zoona kuti nyumba zoterozo zinali zodula, koma kukhala m’nyumba yaing’ono kunathandiza kuti anthu ena asawononge maganizo a ana athu. Ndikuthokoza Yehova kuti kwa zaka zambiri ana athu tinawalerera m’malo abwino mwauzimu.

Komanso, mkazi wanga amakhala pakhomo nthaŵi zonse kusamalira ana athu. Ndikamaliza kugwira ntchito, timayesetsa kuchitira zinthu pamodzi monga banja. Timachita chilichonse pamodzi. Izi zikuphatikizapo kuphunzira Baibulo ndi banja, kukonzekera ndiponso kupita ku misonkhano ya mpingo, kuloŵa mu utumiki wachikristu, komanso zochitika zina zongofuna kusangalala.

Tayesetsa kutsatira uphungu wa pa Deuteronomo 6:6, 7, womwe umalimbikitsa makolo kuphunzitsa ana awo osati kunyumba kokha komanso nthaŵi iliyonse yomwe apeza mpata. Izi zathandiza ana athu kuti azicheza ndi a Mboni anzawo osati anthu ena. Iwo amakhala osamala ndi anthu amene akucheza nawo; aphunzira kwa ife chifukwa Veronica ndi ine siticheza nthaŵi yaitali ndi anthu amene si achipembedzo chathu.​—Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33.

Kuwonjezera pa malangizo athu ndi zomwe timawaphunzitsa palinso zina zomwe zathandiza kwambiri pa moyo wa ana athu. Nthaŵi zambiri Akristu achangu omwe ambiri mwa iwo ndi atumiki oyendayenda a Mboni za Yehova amabwera kunyumba kwathu. Nthaŵi imene Akristu okhwima mwauzimu ameneŵa amakhala ndi banja lathu yathandiza kwambiri ana athu kuona ndi kuphunzira moyo wawo wodzimana. Zimenezi zawonjezera mphamvu ya zomwe timawaphunzitsa ndipo apanga choonadi kukhala chawochawo.

Kupindula Chifukwa Chodzipereka kwa Mulungu

Tsopano, ine ndi mkazi wanga pamodzi ndi ana athu anayi tikuchita utumiki wanthaŵi zonse. Ndinayamba upainiya mu 1973. Kwa zaka zonsezi, ndinali kulekeza utumiki wanga wanthaŵi zonse mwa apo ndi apo chifukwa cha mavuto azachuma. Nthaŵi zina ndakhalanso ndi mwayi wophunzitsa nawo Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, yomwe imaphunzitsa oyang’anira achikristu a Mboni za Yehova. Panopa ndikutumikira m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala komanso monga woyang’anira mzinda wa Uhonmora.

Ana anga aakazi aŵiri oyamba, Victory ndi Lydia, anakwatiwa ndi akulu achikristu abwino kwambiri ndipo akusangalala m’mabanja mwawo. Iwowa pamodzi ndi azimuna awo akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Igieduma, Nigeria. Mwana wathu wamwamuna wamkulu Wilfred, ndi mtumiki wotumikira ndipo wamng’ono kwambiri Micah amachita upainiya wothandiza nthaŵi ndi nthaŵi. Mu 1997, Joan anamaliza maphunziro ake ku sekondale ndipo anayamba upainiya wanthaŵi zonse.

Chimodzi mwa zinthu zosangalatsa pa moyo wanga ndicho kuthandiza anthu ena kutumikira Yehova Mulungu. Ena mwa anthu ameneŵa ndi achibale anga. Bambo anga anayesetsa kufuna kutumikira Yehova, koma mitala ndiyo inawalepheretsa kupita patsogolo. Kuyambira ndili wamng’ono mpaka pano ndimakonda anthu kwambiri. Ndikaona anthu ena akuvutika, ndimaona ngati mavuto anga ndi osafunika kwenikweni. Ndikuganiza kuti mwina anthu amaona kuti ndikufunadi kuwathandiza ndipo zimenezi zimawachititsa kukhala omasuka kulankhula nane.

Mmodzi mwa anthu omwe ndawathandizapo kudziŵa zolinga za Mulungu ndi mwamuna wina yemwe sankachoka pa bedi lake. Iye ankagwira ntchito ku kampani yamagetsi ndipo ali ku ntchito yakeyo shoko inamugwira n’kupheratu thupi lake kuyambira pachifuwa mpaka kumiyendo. Iye anavomera kuphunzira naye Baibulo ndipo pang’ono ndi pang’ono anayamba kugwiritsa ntchito zomwe anali kuphunzira. Anabatizidwa pa October 14, 1995, mumtsinje wa pafupi ndi nyumba yathu ndipo imeneyi ndiyo inali nthaŵi yoyamba kuchoka pa bedi lake patapita zaka 15. Iye anati limenelo ndilo linali tsiku losangalatsa kwambiri pa moyo wake. Tsopano ndi mtumiki wotumikira mumpingo.

Kunena zoona, sindikudandaula m’pang’ono pomwe ndi zomwe ndinachita zaka 30 zapitazo, kusankha kutumikira Yehova pamodzi ndi anthu ake ogwirizana ndi odzipereka. Ndaona chikondi chenicheni chikugwiradi ntchito pakati pawo. Ngakhale pakanakhala kuti chiyembekezo cha moyo wosatha palibe pa mphoto zomwe Yehova adzapereke kwa atumiki ake okhulupirika, n’kanakondabe moyo wodzipereka kutumikira Mulungu. (1 Timoteo 6:6; Ahebri 11:6) Moyo umenewu ndiwo wachititsa ine ndi banja langa kukhala anthu achimwemwe, okhutira, ndiponso osangalala.

[Chithunzi patsamba 25]

Ine, mkazi wanga, ndi ana athu mu 1990

[Chithunzi patsamba 26]

Ine, mkazi wanga, ana athu, ndi azimuna a ana athu aakazi aŵiri