Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zilembo Zinayi Zoimira Dzina la Mulungu mu Baibulo la Septuagint

Zilembo Zinayi Zoimira Dzina la Mulungu mu Baibulo la Septuagint

Zilembo Zinayi Zoimira Dzina la Mulungu mu Baibulo la Septuagint

DZINA la Mulungu lakuti Yehova, limaimiridwa ndi zilembo zinayi zachihebri izi יהוה (YHWH). Kwa nthaŵi yaitali, anthu anali kukhulupirira kuti m’Baibulo la Septuagint munalibe zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu. Motero, iwo anali kunena kuti amene analemba Malemba Achigiriki Achikristu sakanagwiritsa ntchito dzina la Mulunguli pogwira mawu Malemba Achihebri.

Zimene anthu atulukira m’zaka 100 zapitazo zinavumbula kuti dzina la Mulungu linali kupezeka mu Septuagint. Buku lina limati: “Anthu anali kufuna kusungabe dzina lopatulika la Mulungu moti Ayuda achihelene potembenuzira m’Chigiriki Baibulo la Chihebri, anakopera zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu n’kuziika m’malemba achigirikiwo.”

Chidutswa cha mpukutu chimene tikuchiona kumanzereku ndi chimodzi mwa zitsanzo za mipukutu imene yakhalapo mpaka lerolino. Chidutswa chimenechi anachipeza ku Oxyrhynchus, ku Egypt, ndipo nambala yake ndi 3522. Chinalembedwa m’kati mwa zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. * N’cha masentimita 10.5 mlitali ndi masentimita 7 mlifupi ndipo chili ndi ndime ya pa Yobu 42:11, 12. Zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu, zimene tazizunguliza pachithunzipo, zili m’zilembo za Chihebri chakale. *

Nangano, kodi dzina la Mulungu linali kupezeka m’mabuku oyambirira a Malemba Achigiriki Achikristu? Katswiri wina wa maphunziro, George Howard, anati: “Popeza zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu anali kuzilembabe m’mabaibulo a Chigiriki [Septuagint], Malemba amene tchalitchi choyambirira chinali kugwiritsa ntchito, m’pake kukhulupirira kuti amene analemba Chipangano Chatsopano, anakopera zilembozo m’mawu a m’Baibulo pogwira mawu Malemba.” Zikuoneka kuti patangopita nthaŵi pang’ono, okopera Baibulo anachotsa dzina la Mulungu ndipo m’malo mwake anaika mawu akuti Kyʹri·os (Ambuye) ndi The·osʹ (Mulungu).

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kuti mudziŵe zambiri za mipukutu imene anaipeza ku Oxyrhynchus, onani Nsanja ya Olonda, ya February 15, 1992, masamba 26-8.

^ ndime 4 Onani mu zowonjezera 1C m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures−With References. M’menemo muli zitsanzo zina za dzina la Mulungu m’mabaibulo akale a Chigiriki.

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Mwachilolezo cha a Egypt Exploration Society