Kuthandiza Anthu Ovutika ndi Njala Kuli M’kati!
Kuthandiza Anthu Ovutika ndi Njala Kuli M’kati!
MWINA mungafunse kuti, ‘Njala ya chiyani?’ Njala ya chakudya chauzimu! Mneneri wachihebri wakale analosera za njala imeneyi. Anati: “Tawonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Pofuna kuthandiza ovutika ndi njalayi, ophunzira 48 a m’kalasi la 112 la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, yomwe ili ku Patterson, New York, akupita ku mayiko 19 omwe ali m’makontinenti 5 ndi pa zilumba za m’nyanja.
Akupita atatenga chidziŵitso, luso, ndi maphunziro, osati nyama ndi tirigu weniweni. Iwo akhala akuphunzira Baibulo mwakathithi kwa miyezi isanu, kuti alimbitse chikhulupiriro chawo pa ntchito ya umishonale ku mayiko achilendo. Pa March 9, 2002, anthu 5,554 anamvetsera mokondwera pulogalamu yomaliza maphunzirowa.
Stephen Lett, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anatsegulira pulogalamuyi mosangalatsa. Anawalandira mwapadera alendo ambiri amene anachokera m’madera osiyanasiyana a padziko lonse. Ndiyeno anagwiritsa ntchito mawu a Yesu akuti, “Ndinu kuunika kwa dziko lapansi” pa ntchito ya omwe adzakhale amishonaleŵa. (Mateyu 5:14) Anafotokoza kuti: ‘Kumene mukupita, ‘mudzaŵalitsa’ mbali zosiyanasiyana za ntchito zodabwitsa za Yehova, kuthandiza anthu a mtima wabwino kuona kukongola kwa Yehova ndi zolinga zake. Mbale Lett analimbikitsa amishonalewo kuti akagwiritse ntchito Mawu a Mulungu kuvumbula mdima wa ziphunzitso zonyenga ndi kutsogolera anthu ofuna choonadi.
Maganizo Oyenera Ali Ofunika Kuti Zinthu Ziyende Bwino
Tcheyamaniyo atamaliza mawu otsegulira, Baltasar Perla, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku United States, anakamba nkhani yoyamba mwa nkhani zotsatizana zothandiza omaliza maphunzirowo kuti akhale amishonale ogwira mtima pantchito yawo. Nkhani yakeyo inali ndi mutu wakuti, “Limbika, Nulimbe Mtima, Nuchichite.” (1 Mbiri 28:20) Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inalandira ntchito yovuta yomwe inali isanachitepo chibadwire, ntchito yomanga kachisi ku Yerusalemu. Solomo anachitadi zimenezo, ndipo mothandizidwa ndi Yehova, anamaliza kachisiyo. Pogwiritsa ntchito phunziro limene lili pamenepa kwa kalasilo, Mbale Perla anati: ‘Mwalandira ntchito yatsopano, yokhala amishonale, ndipo mufunika kulimbika ndi kulimba mtima.’ Mosakayika, ophunzirawo analimbikitsidwa pamene anawatsimikizira kuti Yehova sadzawasiya ngati iwo apitirizabe kuchita chifuniro chake. Pomaliza, Mbale Perla anakhudza mitima ya omvera mwa kusimba zimene iye anaona. Anati: ‘Mu umishonale mungathe kuchita zabwino zambiri. Amishonale ndi amene anaphunzitsa choonadi makolo anga, mlongo wanga ndi ine amene!’
Samuel Herd yemwenso ndi wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Dalirani Yehova Kuti Zikuyendereni Bwino.” Ophunziraŵa akukayamba ntchito Machitidwe 20:35) Amishonalewo adzakhala ndi mipata yambiri yochitira zimenezi pamene adzadzipereka m’malo mwa ena.—Afilipi 2:17.
ya umishonale, ndipo kuti zinthu zikawayendere bwino, zidzadalira ubwenzi wawo ndi Yehova. Mbale Herd anawalangiza kuti: ‘Mwadziŵa zambiri za m’Baibulo pa zimene mwaphunzira ku Gileadi. Mwakhala mukuphunzira mosangalala. Koma tsopano, kuti mukhale ogwira mtima pantchito yanu, mudzafunika kukayamba kuzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzira.’ (Kodi alangizi a sukuluyi anali ndi malangizo otsazikirana otani kwa ophunzirawo? Mark Noumair anatenga mutu wa nkhani yake pa Rute 3:18, NW, kuti, “Dikira, Mpaka Utaona Mmene Nkhani Ikhalire.” Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha Naomi ndi Rute, wokamba nkhaniyu analimbikitsa omaliza maphunzirowo kukhala ndi chikhulupiriro chonse m’dongosolo limene gulu la padziko lapansi la Mulungu laika ndiponso kulemekeza amene Mulungu wawaika pa ulamuliro. Mbale Noumair anakhudza mitima ya ophunzirawo pamene anati: ‘Zingachitike kuti nthaŵi zina simukumvetsa chifukwa chimene anaganizira kuchita zinthu zinazake zimene zikukhudza inuyo, kapena mungaganize mwamphamvu kuti sanayenere kuchita mmene achitiramo. Kodi mudzatani? Kodi mudzaganiza zongoisamalira nokha nkhaniyo kapena ‘mudzadikira,’ mukumakhulupirira malangizo a Mulungu, kukhala ndi chidaliro chonse kuti panthaŵi yake, iye adzakonza zinthu zonse kuti zidzakhale bwino?’ (Aroma 8:28) Mosakayika, malangizo a ‘kuika mtima pa kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu, kuona zimene gulu la Yehova likuchita m’malo moganizira za kusiyana kwa mitima,’ adzakhala opindulitsa kwambiri kwa omwe adzakhale amishonaleŵa ku mayiko kumene akupita.
Wallace Liverance, amene anali m’mishonale ndipo tsopano ndi mlangizi wa sukulu ya Gileadi, anakamba nkhani yomaliza m’nkhani zotsatizana zoyambirira. Nkhani yake inali ndi mutu wakuti, “Khalani Tcheru, Tumikiranibe Mulungu.” Iye anasonyeza kuti mneneri Danieli anazindikira kuti kumasulidwa kwa Aisrayeli ku ukapolo kunayandikira poona kugwa kwa Babulo ndiponso zimene Yeremiya analosera. (Yeremiya 25:11; Danieli 9:2) Danieli anadziŵa nthaŵi ya Yehova yochitira zinthu, ndipo zimenezo zinam’thandiza kukhalabe tcheru pamene zolinga za Mulungu zinali kuchitika pang’onopang’ono. Koma Aisrayeli a m’nthaŵi ya Hagai sanachite zimenezo. Iwo anati: “Nthaŵi siinafike.” (Hagai 1:2) Sanaganizire za nthaŵi zimene anali kukhalamo, m’malo mwake anaika mtima pa zinthu zimene zinkawasangalatsa ndi kuchita zofuna zawo, ndiponso anasiya kugwira ntchito imene anawamasulira ku Babulo, yomanganso kachisi. Pomaliza Mbale Liverance anati: “Motero khalanibe tcheru mwa kukumbukira cholinga cha Yehova nthaŵi zonse.”
Lawrence Bowen, mlangizi wina wa sukulu ya Gileadi anatsogolera chigawo chimene chinali ndi mutu wakuti “Yehova Amadalitsa Anthu Amene Amagwiritsa Ntchito Mawu a Moyo.” (Ahebri 4:12) M’chigawo chimenechi, a m’kalasilo anasimba zokumana nazo za m’munda zomwe zinatsindika mmene Yehova amadalitsira anthu amene amagwiritsa ntchito Baibulo polalikira ndi kuphunzitsa. Wotsogolerayo anafotokoza kuti Yesu Kristu anapereka chitsanzo chabwino kwa atumiki a Mulungu onse: ‘Yesu ananenadi zoona kuti zimene anali kuphunzitsa sizinali za m’mutu mwake, koma analankhula Mawu a Mulungu.’ Anthu oona mtima anazindikira choonadicho ndipo analabadira. (Yohane 7:16, 17) N’chimodzimodzinso lerolino.
Maphunziro a Sukulu ya Gileadi Amakonzekeretsa Munthu pa Ntchito Iliyonse Yabwino
Kenako, Richard Abrahamson ndi Patrick LaFranca omwe atumikira pa Beteli kwa nthaŵi yaitali anafunsa anthu asanu ndi mmodzi amene anamaliza maphunziro a sukulu ya Gileadi omwe tsopano akuchita mautumiki apadera osiyanasiyana a nthaŵi zonse. Omaliza maphunziro a m’kalasi la 112 analimbikitsidwa pomva kuti patapita zaka zambirimbiri omaliza maphunziro asanu ndi mmodziwo, mosaganizira za mautumiki amene akuchita pakalipano, akupitiriza kugwiritsa ntchito zimene anaphunzira ku sukulu ya Gileadi pochita zinthu monga phunziro la Baibulo, kufufuza, ndi kugwirizana ndi anthu.
Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yaikulu ya pulogalamuyo. Inali ndi mutu wakuti “Zimene Zimachitika Chifukwa Chopirira Udani wa Satana.” M’miyezi isanu yapitayi, ophunzirawo anali pa malo otetezeka ndiponso ophunzirirapo za Mulungu. Komabe, monga mmene anawafotokozera pa maphunziro awo a m’kalasi, tikukhala m’dziko la adani. Anthu a Yehova akudedwa padziko lonse. (Mateyu 24:9) Mwa kugwiritsa ntchito nkhani za m’Baibulo zosiyanasiyana, Mbale Jaracz anafotokoza kuti ‘Mdyerekezi akusakasaka kwambiri ifeyo. Tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndi kuvala zilimbe kuti tithane ndi mayesero.’ (Yobu 1:8; Danieli 6:4; Yohane 15:20; Chivumbulutso 12:12, 17) Pomaliza Mbale Jaracz anati ngakhale kuti anthu akudanabe ndi anthu a Mulungu , ‘palibe chida chosulidwira ife chimene chidzapambana, monga mmene Yesaya 54:17 amanenera. Yehova adzaonetsetsa kuti watilanditsa pa nthaŵi yake ndi m’njira imene iye akufuna.’
Popeza “akonzeka mokwanira,” omaliza maphunziro a m’kalasi la 112 la sukulu ya Gileadi ameneŵa mosakayika adzachita zambiri pothandiza anthu amene akuvutika ndi njala yauzimu m’mayiko amene akukatumikira. (2 Timoteo 3:16, 17) Tikuyembekezera kumva malipoti a mmene akugaŵira uthenga wopatsa thanzi kwa anthu a m’mayiko amenewo.
[Bokosi patsamba 23]
ZIŴERENGERO ZA KALASI
Chiŵerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 6
Chiŵerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 19
Chiŵerengero cha ophunzira: 48
Avareji ya zaka zakubadwa: 33.2
Avareji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 15.7
Avareji ya zaka zimene akhala akuchita utumiki wa nthaŵi zonse: 12.2
[Chithunzi patsamba 24]
Kalasi la 112 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo
M’ndandanda umene uli pansipa, mizera taiiŵerenga kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kumka kumanja mumzera uliwonse.
(1) Parotte, M.; Hooker, E.; Anaya, R.; Reynolds, J.; Gesualdi, K.; Gonzalez, J. (2) Robinson, C.; Phillips, B.; Maidment, K.; Moore, I.; Noakes, J.; Barnett, S. (3) Stires, T.; Palmer, B.; Yang, C.; Groothuis, S.; Groppe, T.; Bach, C. (4) Anaya, R.; Soukore., E.; Stewart, K.; Simozrag, N.; Simottel, C.; Bach, E. (5) Stewart, R.; Yang, H.; Gilfeather, A.; Harris, R.; Barnett, D.; Parotte, S. (6) Maidment, A.; Moore, J.; Groothuis, C.; Gilfeather, C.; Noakes, S.; Stires, T. (7) Gesualdi, D.; Groppe, T.; Soukore., B.; Palmer, G.; Phillips, N.; Simottel, J. (8) Harris, S.; Hooker, P.; Gonzalez, J.; Simozrag, D.; Reynolds, D.; Robinson, M.