Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto a Anthu Akutha Posachedwapa!

Mavuto a Anthu Akutha Posachedwapa!

Mavuto a Anthu Akutha Posachedwapa!

“KUTHANDIZA anthu ovutika n’kosapindulitsa kwenikweni ngati sipakupezeka njira zokwanira ndiponso mfundo zandale zomwe zingathandize kuthetsa gwero la nkhondo. Zochitika zasonyeza mobwerezabwereza kuti kuthandiza ovutika pakokha sikungathetse mavuto a ndale.”​—The State of the World’s Refugees 2000.

Ngakhale kuti pachitika ntchito yaikulu yothandiza ovutika, mavuto a anthu akupitirizabe kukula. Kodi n’kutheka kuti mfundo zandale zidzathetseratu mavutoŵa? Kunena zoona, n’zokayikitsa kwambiri. Koma kodi n’kuti kumene tingapeze thandizo? Mtumwi Paulo m’ndime yochititsa chidwi yomwe ili koyambirira kwa kalata yake yopita kwa Akristu a ku Efeso, anafotokoza mmene Mulungu adzathetsere mavuto onse a anthu. Iye anatchula ngakhale bungwe lomwe Mulungu adzagwiritse ntchito. Bungweli lidzachotsa gwero la mavuto onse omwe amatisautsa lerolino. Bwanji tipende zomwe Paulo ananena? Ndimeyi ili pa Aefeso 1:3-10.

‘Kusonkhanitsanso Pamodzi Zonse mwa Kristu’

Paulo ananena kuti Mulungu akufuna zomwe Pauloyo anazitcha “makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti Mulungu waika nthaŵi yomwe adzachitepo kanthu kuti ‘akasonkhanitsenso pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.’ (Aefeso 1:10) Inde, Mulungu wayamba ntchito yosonkhanitsanso chilichonse kumwamba ndi padziko lapansi kuti zikhale m’manja mwake. N’zochititsa chidwi kuti pa mawu omwe anawamasulira pano kuti ‘kusonkhanitsanso pamodzi,’ katswiri wina wamaphunziro a Baibulo, J. H. Thayer, ananena kuti: “Kudzisonkhanitsiranso pamodzi . . . zinthu zonse ndi anthu onse (omwe mpaka lero uchimo unawalekanitsa) kuti akhale m’gulu limodzi logwirizana mwa Kristu.”

Izi zikusonyeza kufunika koti Mulungu ndiye achite zimenezi poganizira mmene chisokonezo chinayambira. Koyambirira kwa mbiri ya anthu, makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anatsatira Satana Mdyerekezi kupandukira Mulungu. Iwo anafuna kukhala odziimira kuti azidzisankhira okha chabwino ndi choipa. (Genesis 3:1-5) Mulungu malinga ndi chilungamo chake, anawachotsa m’banja lake ndipo sanalinso mabwenzi ake. Motero iwo anachititsa anthu onse kukhala opanda ungwiro ndipo zotsatira zake ndizo mavuto osaneneka omwe tikukumana nawo masiku ano.​—Aroma 5:12.

Kulola Zinthu Zoipa kwa Nthaŵi Yokhala ndi Malire

Ena angafunse kuti: ‘N’chifukwa chiyani Mulungu anawalola kuchita zimenezo? Bwanji sanagwiritse ntchito mphamvu zake zazikuluzo ndi kuchita zofuna zake kuti mavuto onse amene tikukumana nawo leroŵa asachitike?’ Kuganiza motero sikwachilendo ayi. Koma kodi kugwiritsa ntchito mphamvu zazikulu koteroko kukanasonyeza chiyani? Kodi mumakonda kapena kugwirizana ndi munthu amene amapha nthaŵi yomweyo onse amene ayamba kum’tsutsa, chabe chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zochitira zimenezo? Simungatero ayi.

Anthu opandukawo sanatsutse zoti Mulungu ndi wamphamvuyonse. Iwo kwenikweni anatsutsa zoti iye ndiye woyenera kulamulira anthu ndiponso kuti ulamuliro wake ndiwo woyenera. Yehova pofuna kuthetseratu nkhani yaikuluyo kuti isadzabukenso m’tsogolo, walola anthu kuti adzilamulire kwanthaŵi yokhala ndi malire popanda iye kuloŵererapo. (Mlaliki 3:1; Luka 21:24) Nthaŵiyo ikatha, iye adzaloŵererapo n’kuyambanso kulamulira dziko lonse lapansi. Podzafika nthaŵiyo, zidzaonekeratu kuti ulamuliro wake ndi wokhawo umene ungabweretsedi mtendere, chimwemwe, ndi ulemerero zokhalitsa kwa anthu padziko lapansi. Kenako onse opondereza anzawo padziko lapansi adzawachotsa kwamuyaya.​—Salmo 72:12-14; Danieli 2:44.

“Lisanakhazikike Dziko Lapansi”

Yehova anafuna kuchotsa anthu oipaŵa kalekale. Paulo anatchula kuti “lisanakhazikike dziko lapansi.” (Aefeso 1:4) Izi sizikutanthauza kuti asanalenge dziko lapansi kapena Adamu ndi Hava ayi. Dziko loyambalo linali ‘labwino ndithu’ ndipo anthu anali asanapanduke. (Genesis 1:31) Ndiyeno, kodi Paulo ankanena za “dziko” lake liti? Ankanena za ana a Adamu ndi Hava, mtundu wa anthu ochimwa ndi opanda ungwiro womwe ukuyembekezera kuwomboledwa. Mwana aliyense wa Adamu asanabadwe, Yehova anali atadziŵa kale mmene adzakonzere zinthu kuti apulumutse mbadwa za Adamu zomwe zingawomboleke.​—Aroma 8:20.

Izi sizikutanthauza kuti Mfumu yachilengedwe chonse iyenera kuchita zinthu monga amachitira anthu. Anthu pozindikira kuti chinachake chitha kuchitika mwadzidzidzi, iwo amakonzeratu njira zosiyanasiyana zothetsera vutolo. Mulungu wamphamvuyonse sachita zimenezo ayi. Iye amangonena zomwe akufuna, n’kuchita zomwezo. Komabe, Paulo anafotokoza njira zimene Yehova anafuna kukonzera zinthu kuti apulumutse anthu kwamuyaya. Kodi njira zimenezo zinali zotani?

Kodi Ndani Adzabweretsa Chipulumutso?

Paulo anafotokoza kuti ophunzira odzozedwa a Kristu ali ndi udindo wapadera pantchito yochotsa mavuto omwe tchimo la Adamu linachititsa. Paulo anati, Yehova “anatisankha ife mwa [Kristu],” kukalamulira pamodzi ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba. Paulo anapitiriza mfundoyi kuti, Yehova “anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Kristu.” (Aefeso 1:4, 5) Komabe, Yehova sanawasankhe kapena kuwaikiratu iwo aliyense payekha ayi. Koma anaikiratu gulu la anthu okhulupirika ndi odzipereka amene adzathandizana ndi Kristu kuchotsa mavuto omwe Satana Mdyerekezi pamodzi ndi Adamu ndi Hava anabweretsa kwa anthu.​—Luka 12:32; Ahebri 2:14-18.

Zodabwitsatu kwambiri zimenezi. Satana m’mawu ake oyambirira otsutsana ndi ulamuliro wa Mulungu, anasonyeza kuti Mulungu analenga anthu okhala ndi nthenya, moti ngati atapanikizika kapena kuwanyengerera mokwanira, onse atha kupandukira ulamuliro wa Mulungu. (Yobu 1:7-12; 2:2-5) Yehova Mulungu posonyeza “ulemerero wa chisomo chake,” anaonetsa panthaŵi yake kuti amakhulupirira anthu omwe anawalenga padziko lapansi mwa kusankha ena a m’banja lochimwalo la Adamu kukhala ana ake auzimu. Gulu lochepali adzalitenga kukatumikira kumwamba. N’cholinga chotani?​—Aefeso 1:3-6; Yohane 14:2, 3; 1 Atesalonika 4:15-17; 1 Petro 1:3, 4.

Mtumwi Paulo ananena kuti ana a Mulungu ameneŵa akakhala “oloŵa anzake a Kristu” mu Ufumu wake wakumwamba. (Aroma 8:14-17) Iwo monga mafumu ndi ansembe, adzagwira nawo ntchito yomasula anthu ku mavuto ndi zowawa zomwe akukumana nazo masiku ano. (Chivumbulutso 5:10) N’zoona kuti “cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.” Koma posachedwapa, ana a Mulungu osankhidwa mwapaderawo pamodzi ndi Yesu Kristu adzakhala pantchito, ndipo anthu onse omvera ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’​—Aroma 8:18-22.

“Kuwomboledwa ndi Dipo”

Zonsezi zatheka chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu Kristu yomwe tingati ndiyo chisomo chachikulu koposa chomwe Mulungu wasonyeza kwa anthu omwe akhoza kuwomboleka. Paulo analemba kuti: “Mwa [Yesu Kristu] tawomboledwa ndi dipo kudzera m’mwazi wake, inde, machimo athu akhululukidwa, malinga ndi kulemera kwa chisomo chake.”​Aefeso 1:7, NW.

Yesu Kristu ndiye wofunika kwambiri kuposa wina aliyense pantchito yokwaniritsa zomwe Mulungu akufuna. (Ahebri 2:10) Nsembe yake ya dipo ndiyo maziko ovomerezeka oti Yehova atenge mbadwa zina za Adamu kukakhala m’banja lake lakumwamba ndiponso kumasula anthu ku mavuto omwe uchimo wa Adamu wadzetsa, popanda kufooketsa chidaliro m’malamulo Ake ndi mfundo zake zamakhalidwe abwino. (Mateyu 20:28; 1 Timoteo 2:6) Yehova wachita izi m’njira imene imalimbikitsa chilungamo chake ndiponso kukwaniritsa zomwe chilungamo changwiro chimafuna.​—Aroma 3:22-26.

“Chinsinsi Chopatulika” cha Mulungu

Mulungu kwa zaka zikwizikwi, sanaulule mwachindunji mmene adzakwaniritsira zolinga zake padziko lapansi. M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino iye ‘anawazindikiritsa [Akristu] chinsinsi [chopatulika, NW] cha chifuniro chake.’ (Aefeso 1:9) Paulo ndi Akristu anzake odzozedwa anamvetsa bwino udindo waukulu wa Yesu Kristu pantchito yokwaniritsa zolinga za Mulungu. Iwo anamvetsanso udindo wawo wapadera monga oloŵa anzake a Kristu mu Ufumu wake wakumwamba. (Aefeso 3:5, 6, 8-11) Inde, boma la Ufumu lomwe lili m’manja mwa Yesu Kristu ndi olamulira anzake ndilo bungwe lomwe Mulungu adzagwiritsa ntchito kubweretsa mtendere wosatha osati kumwamba kokha komanso padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Yehova kudzera m’boma limeneli, adzakonzanso dziko lapansili kuti likhale mmene anafunira poyamba.​—Yesaya 45:18; 65:21-23; Machitidwe 3:21.

Nthaŵi yomwe iye waika kuti achitepo kanthu kuchotsa onse opondereza anzawo komanso chinyengo chonse ili pafupi. Yehova anayamba kale ntchito yokonzanso zinthu pa Pentekoste wa 33 C.E. Kodi anachita bwanji zimenezo? Mwa kuyamba kusonkhanitsa pamodzi “za kumwamba,” okalamulira pamodzi ndi Kristu kumwamba. Akristu a ku Efeso anali m’gulu limeneli. (Aefeso 2:4-7) Yehova m’nthaŵi yathu ino, akusonkhanitsa pamodzi “za padziko.” (Aefeso 1:10) Iye kudzera mu ntchito yolalikira ya padziko lonse, akuuza anthu amitundu yonse uthenga wabwino wa boma la Ufumu wake lomwe lili m’manja mwa Yesu Kristu. Ngakhale panopo, amene akulabadira akuwasonkhanitsira ku malo achitetezo ndi machiritso auzimu. (Yohane 10:16) Iwo posachedwapa adzakhala pa ufulu weniweni m’dziko lapansi lokonzedwanso la paradaiso lopanda chinyengo ndi mavuto.​—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 11:18.

Ntchito yothandiza anthu oponderezedwa “yapita patsogolo modabwitsa kwambiri.” (The State of the World’s Children 2000). Komabe, zodabwitsa kwambiri kuposa pamenepa zidzakhala kuloŵerera komwe kukuyandikira kwa Kristu Yesu pamodzi ndi olamulira anzake a boma la Ufumu wakumwamba. Iwo adzachotseratu zonse zomwe zimachititsa nkhondo ndi mavuto ena onse amene amatisautsaŵa. Iwo adzathetseratu mavuto onse a anthu.​—Chivumbulutso 21:1-4.

[Zithunzi patsamba 4]

Kuthandiza ovutika sikunathetse mavuto a anthu

[Chithunzi patsamba 6]

Nsembe ya dipo ya Kristu inamasula anthu ku uchimo wa Adamu

[Chithunzi patsamba 7]

N’zotheka kupeza chitetezo ndiponso machiritso auzimu lerolino

[Zithunzi patsamba 7]

Posachedwapa, Ufumu Waumesiya udzathetseratu mavuto a anthu