Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndiwe Mkazi Waulemu”

“Ndiwe Mkazi Waulemu”

“Ndiwe Mkazi Waulemu”

Mkazi wachimoabu ndi amene ankamuyamikira chonchiyu. Anali mkazi wamasiye dzina lake Rute, mpongozi wake wa Naomi yemwe anali mkazi wachiisrayeli. Rute anakhala mu Israyeli zaka pafupifupi 3000 zapitazo, nthaŵi imene oweruza anali kulamulira, ndipo anadziŵika kuti anali mkazi waulemu. (Rute 3:11) Kodi mbiri yabwinoyi anaipeza bwanji? Kodi ndani angapindule ndi chitsanzo chake?

Rute sanali ‘kudya zakudya za ulesi,’ ankagwira ntchito yotola khunkha m’minda nthaŵi yaitali ndiponso molimbika, ndipo chifukwa cha zimenezo anthu ankamuyamikira. Ngakhale pamene anam’chepetsera ntchito yake, ankagwirabe ntchito molimbika ndipo ankagwira kuposa imene ankafunika kugwira. Choncho, anayeneradi zimene Baibulo limafotokoza za mkazi wotamandika, waluso, wa zintchito.​—Miyambo 31:10-31; Rute 2:7, 15-17.

Chifukwa chachikulu chimene chinapangitsa Rute kupeza mbiri yabwinoyi ndi makhalidwe ake auzimu monga kudzichepetsa, kudzimana ndiponso chikondi chokhulupirika. Iye anam’kakamira Naomi, kusiya makolo ake ndi dziko lakwawo, alibe chiyembekezo chenicheni chodzakhala ndi moyo wabwino umene umapezeka m’banja. Komanso, Rute anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kutumikira Yehova, yemwe anali Mulungu wa apongozi ake. Posonyeza kuti Rute anali wofunika, nkhani ya m’Malemba imanena kuti, ‘kwa [Naomi] anaposa ana aamuna asanu ndi aŵiri.’​—Rute 1:16, 17; 2:11, 12; 4:15.

Ngakhale kuti Rute ankatamandidwa ndi anthu anzake kuti anali waulemu, chabwino kwambiri n’chakuti Mulungu anakonda makhalidwe ake ndipo anam’dalitsa kukhala kholo la Yesu Kristu. (Mateyu 1:5; 1 Petro 3:4) Rute n’chitsanzo chabwino kwa akazi achikristu komanso kwa onse amene amati amalambira Yehova!