Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Chitsanzo cha Mfumu

Tsanzirani Chitsanzo cha Mfumu

Tsanzirani Chitsanzo cha Mfumu

“Adzilembere chofanana cha chilamulo ichi m’buku . . . ndipo azikhala nacho, naŵerengemo masiku onse a moyo wake.”​—DEUTERONOMO 17:18, 19.

1. Kodi Mkristu ayenera kufanana ndi yani?

INU mwina simungadziyerekezere ndi mfumu kapena mfumukazi. Kodi alipo Mkristu wokhulupirika yemwe amaphunzira Baibulo amene angadziyerekezere kuchita zinthu ngati mmene ankachitira mafumu okhulupirika monga Davide, Yosiya, Hezekiya, kapena Yehosafati? Komatu, mungafanane nawo ndipo muyeneradi kufanana nawo m’njira ina yapadera. Kodi ndi njira iti imeneyo? Ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kufanana nawo m’njira imeneyo?

2, 3. Kodi Yehova anadziŵiratu chiyani zokhudza mfumu yaumunthu, ndipo mfumuyo inayenera kuchita chiyani?

2 M’nthaŵi ya Mose, Mulungu asanavomereze Aisrayeli kukhala ndi mfumu, anadziŵiratu kuti anthu Ake adzafuna kukhala ndi mfumu yaumunthu. Motero, anauzira Mose kulemba malangizo okhudza nkhani imeneyi m’pangano la Chilamulo. Ameneŵa anali malangizo a mfumu.

3 Mulungu anati: “Mutakaloŵa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, . . . ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga; mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha. . . . Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilembere chofanana cha chilamulo ichi m’buku, . . . ndipo azikhala nacho, naŵerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mawu onse a chilamulo ichi ndi malemba awa, kuwachita.”​—Deuteronomo 17:14-19.

4. Kodi malangizo a Mulungu anafuna kuti mfumu izitani?

4 Inde, mfumu imene Yehova akanasankhira olambira ake inayenera kukopera m’buku lake mawu a m’Baibulo. Ndiyeno mfumuyo inafunika kuŵerenga bukulo tsiku ndi tsiku kapena kuti mobwerezabwereza. Kumenekotu sikunali kubwerezabwereza kongoti azikumbukira msanga ayi. Kunali kuphunzira, ndipo cholinga chinali choti apindule. Mfumu imene Yehova akanaikonda inafunika kuchita zimenezi kuti ikhale ndi mtima wabwino. Inafunikanso kuphunzira mawu ouziridwawo kuti zinthu zimuyendere bwino ndi kukhala mfumu yozindikira.​—2 Mafumu 22:8-13; Miyambo 1:1-4.

Phunzirani Ngati Mfumu

5. Kodi panali mabuku ati a m’Baibulo amene Mfumu Davide inafunika kukopera ndi kuwaŵerenga, ndipo iye anaona bwanji zimenezi?

5 Kodi mukuganiza kuti zimenezi zinafuna kuti Davide achite chiyani pamene anakhala mfumu ya Israyeli? Ee, anafunika kukopera m’buku lake mabuku a Pentatuke (Genesis, Eksodo, Levitiko, Numeri, Deuteronomo). Tangoganizani mmene zimenezi ziyenera kuti zinakhudzira mtima ndi maganizo a Davide pamene anagwiritsa ntchito maso ndi manja ake kukopera Chilamulo! Mwachionekere, Mose analembanso buku la Yobu ndiponso Masalmo 90 ndi 91. Kodi Davide anakoperanso mabuku ameneŵa? Ayenera kuti anatero. Ndiponso, mwina panthaŵi imeneyo mabuku a Yoswa, Oweruza, ndi Rute n’kuti alipo. Choncho, mungaone kuti panali mabuku ochulukirapo a m’Baibulo amene Mfumu Davide anafunikira kuŵerenga ndi kuwamvetsa. Ndipo pali zifukwa zokwanira kukhulupirira kuti anachitadi zimenezo, poona zimene anafotokoza pankhani ya Chilamulo cha Mulungu pa Salmo 19:7-11.

6. Kodi tingatsimikize bwanji kuti Yesu ankakonda Malemba monga mmene ankachitira atate ake Davide?

6 Davide Wamkulu, yemwe ali Yesu, Mwana wa Davide, anatsanzira zomwezo. Iye ankakonda kupita ku sunagoge wa m’deralo mlungu uliwonse. Ku sunagogeko iye anali kumva Malemba akuwaŵerenga ndi kuwafotokoza. Ndipo nthaŵi ina yake, Yesu anaŵerenga Mawu a Mulungu pagulu mokweza ndi kufotokoza tanthauzo lake. (Luka 4:16-21) Mutha kuona kuti iye ankadziŵa bwino Malemba. Tangoŵerengani nkhani za m’Mauthenga Abwino ndi kuona nthaŵi zimene Yesu anati “kwalembedwa” kapena pamene anatchula ndime zina za m’Malemba. Mwachitsanzo, pa Ulaliki wake wa pa Phiri umene Mateyu analemba, Yesu anagwira mawu Malemba Achihebri maulendo 21.​—Mateyu 4:4-10; 7:29; 11:10; 21:13; 26:24, 31; Yohane 6:31, 45; 8:17.

7. Kodi Yesu anasiyana bwanji ndi atsogoleri achipembedzo?

7 Yesu anatsatira malangizo amene ali pa Salmo 1:1-3 akuti: “Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, . . . komatu m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. . . . Zonse azichita apindula nazo.” Iye anasiyana kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo a m’nthaŵi yake, omwe ‘anakhala pa mpando wa Mose’ koma n’kumanyalanyaza “chilamulo cha Yehova.”​—Mateyu 23:2-4.

8. N’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo achiyuda amene anali kuŵerenga Baibulo sanapindule?

8 Komabe, mwina ena angazunguzike mitu chifukwa cha ndime ina imene anthu angaitanthauzire kuti Yesu anali kuletsa kuphunzira Baibulo. Pa Yohane 5:39, 40, timaŵerenga zimene Yesu anauza anthu ena a m’nthaŵi yake kuti: “Musanthula m’malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nawo moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo; ndipo simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nawo moyo.” Yesu polankhula mawu ameneŵa sanali kuuza Ayuda amene anali kumumvera kuti asamaŵerenge Malemba. M’malo mwake, iye anali kuvumbula kusaona mtima kwawo kapena kusatsatira kwawo zimene anali kuŵerenga. Ayudawo ankadziŵa kuti Malemba akanawathandiza kupeza moyo wosatha, koma Malemba omwewo amene anali kusanthula anayeneranso kuwatsogolera kwa Mesiya, Yesu. Komabe, iwo anamukana. Motero, kuŵerenga kwawo Malemba kunali kopanda phindu chifukwa sanali oona mtima, kapena kuti ophunzitsika.​—Deuteronomo 18:15; Luka 11:52; Yohane 7:47, 48.

9. Kodi atumwi ndi aneneri amene anakhalako m’mbuyomo anapereka chitsanzo chabwino chotani?

9 Anthu ameneŵa anasiyana kwambiri ndi ophunzira a Yesu kuphatikizapo atumwi. Ophunzira a Yesu anali kuŵerenga “malembo opatulika, okhoza kupatsa [munthu] nzeru kufikira chipulumutso.” (2 Timoteo 3:15) Pochita zimenezi, iwo anafanana ndi aneneri amene anakhalako m’mbuyomo amene “anafunafuna nasanthula.” Aneneri amenewo sanaone kusanthula kumeneko kungokhala nthaŵi yochepa chabe yophunzira kwambiri kwa miyezi ingapo kapena chaka. Mtumwi Petro anati iwo “[anapitiriza, NW] kusanthula,” makamaka za Kristu ndi ulemerero umene unalipo pa ntchito yake yopulumutsa anthu. M’kalata yake yoyamba, Petro anagwira mawu mabuku khumi a m’Baibulo maulendo 34.​—1 Petro 1:10, 11.

10. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kukonda kuphunzira Baibulo?

10 Motero, mafumu a Israyeli wakale anali ndi ntchito yophunzira Mawu a Mulungu mosamala. Yesu anatsanzira zomwezo. Ndiponso anthu amene anali oti adzalamulira pamodzi ndi Kristu monga mafumu kumwamba anafunikira kuchita zomwezo. (Luka 22:28-30; Aroma 8:17; 2 Timoteo 2:12; Chivumbulutso 5:10; 20:6) Chitsanzo cha mafumuchi n’chofunikanso kwambiri kwa onse amene lerolino akuyembekezera kudzalandira madalitso padziko lapansi lolamulidwa ndi Ufumu.​—Mateyu 25:34, 46.

Ntchito ya Mafumu Ndiponso Yanu

11. (a) Kodi Akristu afunika kupeŵa chiyani pankhani yophunzira Baibulo? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso otani?

11 Tinganene motsindika komanso mosapita m’mbali kuti Mkristu woona aliyense ayenera kumasanthula Baibulo payekha. Zimenezi sikuti zimangofunika pamene mukuphunzira Baibulo koyamba ndi Mboni za Yehova ayi. Tonsefe tifunika kuonetsetsa kuti tikupeŵa kukhala ngati anthu ena a m’nthaŵi ya mtumwi Paulo amene patapita nthaŵi ananyalanyaza phunziro lawo laumwini. Iwo anaphunzira “zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu,” monga ngati “mawu a chiyambidwe cha Kristu.” Komabe, sanapitirize kuphunzira ndipo chifukwa cha zimenezo ‘sanapitirire kutsata ukulu msinkhu.’ (Ahebri 5:12–6:3) Ifenso tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaona bwanji kuphunzira Mawu a Mulungu, kaya ndakhala mumpingo wachikristu kwa nthaŵi yochepa kapena kwa zaka zambiri? Paulo anapemphera kuti Akristu a m’nthaŵi yake apitirize “kukula m’chizindikiritso cha Mulungu.” Kodi ndimasonyeza kuti ndimafunanso kuchita chimodzimodzi?’​—Akolose 1:9, 10.

12. N’chifukwa chiyani kupitiriza kukonda Mawu a Mulungu n’kofunika kwambiri?

12 Chinsinsi choti mukhale ndi chizoloŵezi chabwino cha kuphunzira ndicho kukonda Mawu a Mulungu. Pa Salmo 119:14-16 amafotokoza kuti mungakonde Mawu a Mulungu ngati muwasinkhasinkha nthaŵi zonse ndiponso n’cholinga. Muyeneranso kuchita zimenezi kaya mwakhala muli Mkristu kwa zaka zambiri motani. Potsindika mfundo imeneyi, kumbukirani chitsanzo cha Timoteo. Ngakhale kuti mkulu wachikristu ameneyu anali kale “msilikali wabwino wa Kristu Yesu,” Paulo anamulangiza kuti achite changu ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:3, 15; 1 Timoteo 4:15) N’zoonekeratu kuti ‘kuchita changu’ kumafuna kuti muziphunzira nthaŵi zonse.

13. (a) Kodi mungapeze bwanji nthaŵi yokulirapo yophunzira Baibulo? (b) Kodi mungathe kusintha zinthu ziti kuti mupeze nthaŵi yophunzira?

13 Kuti mukhale ndi chizoloŵezi chabwino chophunzira, mufunika nthaŵi zonse kupatula nthaŵi yophunzira Baibulo. Kodi mukuchita bwanji pa nkhani imeneyi? Kaya yankho lanu loona mtima n’lotani, kodi mukuganiza kuti mungapindule mwa kupatula nthaŵi yokulirapo ya phunziro laumwini? Mwina mungafunse kuti, ‘Ndingapeze kuti nthaŵi imeneyo?’ Eya, ena awonjezera nthaŵi yawo yophunzira Baibulo mogwira mtima mwa kudzuka mofulumirirapo m’maŵa. Angaŵerenge Baibulo kwa mphindi 15 kapena kuchita phunziro laumwini. Bwanji mutasintha pang’ono zochita zanu za mlungu ndi mlungu monga njira ina yopezera nthaŵi? Mwachitsanzo, ngati masiku ambiri mumakonda kuŵerenga nyuzipepala kapena kuonera nkhani zamadzulo pa wailesi ya kanema, kodi zingatheke osachita zimenezi tsiku limodzi lokha pa mlungu? Mungagwiritse ntchito tsiku limenelo kuwonjezera kuphunzira Baibulo. Ngati nthaŵi ya tsiku limodzi imene mumaŵerenga kapena kumvera nkhani, yomwe ingakhale mphindi pafupifupi 30, muigwiritsa ntchito kuchita phunziro laumwini, ndiye kuti nthaŵi yanu yophunzira mudzaiwonjezera ndi maola 25 pachaka. Tangoganizani phindu limene mungapeze ngati muŵerenga ndi kuphunzira Baibulo kwa maola ena 25! Njira ina ndi iyi: Mlungu wamaŵa, pofika madzulo a tsiku lililonse, tayesani kuona zinthu zimene mwachita tsikulo. Onani ngati mungapeze chinachake chimene mungasiye kuchita kapena kuchichepetsa kuti mupeze nthaŵi yokulirapo yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo.​—Aefeso 5:15, 16.

14, 15. (a) N’chifukwa chiyani kukhala ndi zolinga n’kofunika pankhani ya phunziro laumwini? (b) Kodi pangakhale zolinga zotani pankhani yoŵerenga Baibulo?

14 Kodi n’chiyani chingathandize kuti kuphunzira kusakuvuteni ndiponso kuti kukhale kosangalatsa? Zolinga. Kodi mungakhale ndi zolinga zotheka ziti? Cholinga choyamba chimene anthu ambiri amakonda ndicho kuŵerenga Baibulo lonse. Mwina pofika lero, mwaŵerenga zigawo zina za Baibulo nthaŵi zosiyanasiyana ndipo mwapindula nazo. Kodi mungakonze tsopano zoti muŵerenge Baibulo lonse? Cholinga choyamba pofuna kuŵerenga Baibulo lonse chingakhale kuŵerenga Mauthenga Abwino anayi, ndiyeno mungafike pa cholinga chachiŵiri chomwe chingakhale kuŵerenga Malemba Achigiriki Achikristu ena otsala. Mutakhutira kuti mwaŵerenga ndi kupindula nawo, cholinga chanu chotsatira chingakhale kuŵerenga mabuku a Mose ndi mabuku osimba zomwe zinachitika, limodzilimodzi mpaka kufika pa buku la Estere. Mukafika pamenepa, mudzaona kuti n’kotheka kumaliza Baibulo lonse. Mkazi wina amene anali ndi zaka pafupifupi 65 pamene anakhala Mkristu, ankalemba kuchikuto kwa Baibulo lake deti limene anayamba kuŵerenga Baibulo ndipo kenako deti limene anamaliza kuliŵerenga lonse. Pakalipano waŵerenga Baibulo lonse kasanu. (Deuteronomo 32:45-47) Ndipo m’malo moŵerengera pa kompyuta kapena pa mapepala olemba pa kompyuta, iye anali ndi Baibulo m’manja poŵerenga.

15 Ena amene aŵerenga kale Baibulo lonse amatsatira njira zina kuti kuŵerenga Baibulo kwawo kwa nthaŵi ndi nthaŵi kukhale kopindulitsa kwambiri. Njira ina ndiyo kuŵerenga buku lothandiza kuphunzira Baibulo limene mungasankhe musanaŵerenge mabuku a m’Baibulo limodzi ndi limodzi. Mabuku akuti “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial” ndi Insight on the Scriptures, ali ndi mfundo zabwino kwambiri zokhudza buku lililonse la m’Baibulo, ndiponso phindu limene munthu angapeze poŵerenga bukulo. *

16. Kodi tiyenera kupeŵa kutsanzira chitsanzo chiti pophunzira Baibulo?

16 Pamene mukuphunzira, peŵani maganizo a anthu ambiri amene amati ndi akatswiri a maphunziro a Baibulo. Iwo amaika mtima kwambiri pa kufufuza nkhaniyo ngati kuti zimene zili m’Baibulo ndi maganizo a munthu. Ena mwa iwo amachita kugaŵira buku lililonse gulu la anthu amene akuganiza kuti anawalembera. Kapenanso kuyerekeza zolinga ndi maganizo amene munthu amene analemba bukulo amati anali nawo. Zotsatira za maganizo aumunthu amenewo zingakhale zakuti amaliona Baibulo ngati buku longosimba zochitika za m’mbiri basi kapena ngati buku longolimbikitsa kapembedzedwe. Akatswiri ena amatanganidwa ndi kufufuza mawu a m’Baibulo. Amatanganidwa ndi kufufuza kumene mawuwo anachokera ndi kutchula matanthauzo a Chihebri ndi Chigiriki osati tanthauzo la uthenga wa Mulungu. Kodi mukuganiza kuti kuchita zimenezi kungathandize munthu kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso chimene chingam’pangitse kuchitapo kanthu?​—1 Atesalonika 2:13.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona uthenga wa Baibulo monga wa anthu onse?

17 Kodi zimene akatswiri a maphunzirowo amanena n’zoona? Kodi n’zoona kuti buku lililonse lili ndi mfundo yaikulu imodzi kapena kuti analilembera gulu la anthu limodzi basi? (1 Akorinto 1:19-21) Mfundo ndi yakuti mabuku a Mawu a Mulungu ali ndi phindu lokhalitsa kwa anthu onse ndiponso a chikhalidwe chilichonse. Ngakhale kuti bukulo poyamba analilembera munthu mmodzi, monga ngati Timoteo kapena Tito, kapena kwa gulu linalake, monga Agalatiya kapena Afilipi, tonse tingaphunzire ndipo tiyenera kuphunzira mabukuwo. Mabukuwo ndi ofunika kwambiri kwa tonsefe, ndipo buku limodzi lingafotokoze mfundo zambiri ndi kupindulitsa anthu osiyanasiyana. Inde, uthenga wa Baibulo umagwira ntchito padziko lonse, ndipo n’chifukwa chake alimasulira m’zilankhulo za anthu padziko lonse.​—Aroma 15:4.

Mungapindule ndi Kupindulitsanso Anthu Ena

18. Kodi muyenera kusinkhasinkha chiyani pamene mukuŵerenga Mawu a Mulungu?

18 Pamene mukuphunzira, kungakhale kopindulitsa kufuna kumvetsa Baibulo ndiponso kuona mmene mfundo zina zikugwirizanira ndi zinzake. (Miyambo 2:3-5; 4:7) Zimene Yehova wavumbula kudzera m’Mawu ake n’zogwirizana kwambiri ndi cholinga chake. Motero poŵerenga, gwirizanitsani mfundo ndi malangizowo ndi zolinga zake. Mungasinkhesinkhe mmene zochitika, mfundo, kapena ulosi zikugwirizanira ndi cholinga cha Yehova. Dzifunseni kuti: ‘Kodi pamenepa ndikuphunzirapo chiyani za Yehova? Kodi zikugwirizana bwanji ndi zolinga za Mulungu zimene akuzikwaniritsa kudzera mu Ufumu wake?’ Mwinanso mungadzifunse kuti: ‘Kodi zimene ndaŵerengazi ndingazigwiritse ntchito bwanji? Kodi ndingazigwiritse ntchito pophunzitsa kapena kulangiza ena kuchokera m’Malemba?’​—Yoswa 1:8.

19. Kodi ndani amapindula pamene muuza ena zimene mwaphunzira? Fotokozani.

19 Kuganizira anthu ena n’kopindulitsanso kwambiri. Poŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, mudzaphunzira ndi kuzindikira zinthu zina zatsopano. Yesani kugwiritsa ntchito zimenezi pokambirana molimbikitsa ndi achibale anu kapena anthu ena. Ngati muchita zimenezi panthaŵi yoyenera ndiponso modzichepetsa, makambirano anuwo mosakayikira adzakhala opindulitsa. Ngati mufotokoza ndi mtima wonse zimene mwaphunzira kapena mbali zimene zakusangalatsani, mosakayika zidzalimbikitsa ena. Ndiponso, inuyo mudzapindula. Motani? Akatswiri amanena kuti munthu angakumbukire kwa nthaŵi yaitali zimene waphunzira kapena kuŵerenga ngati pamene wangoŵerenga kumene azigwiritsa ntchito kapena kuzibwereza, monga pouza ena. *

20. N’chifukwa chiyani n’kopindulitsa kuŵerenga Baibulo mobwerezabwereza?

20 Mosakayika, nthaŵi iliyonse pamene muŵerenga ndi kumaliza buku la m’Baibulo, mudzaphunzira zatsopano. Mudzachita chidwi ndi ndime zimene poyamba simunachite nazo chidwi kwambiri. Mudzazimvetsa bwino kwambiri ndime zimenezo. Zimenezi zikutsindika mfundo yakuti mabuku a m’Baibulo si mawu a munthu, m’malo mwake ndiwo chuma chimene inuyo mufunikira kuchiphunzira mobwerezabwereza ndi kupindula nacho. Kumbukirani kuti mfumu, monga Davide, inafunika ‘kuŵerengamo masiku onse a moyo wake.’

21. Kodi mungapindule chiyani ngati muwonjezera kuphunzira Mawu a Mulungu?

21 Inde, amene amapatula nthaŵi kuphunzira Baibulo ali ndi cholinga amapindula kwambiri. Amapeza chuma ndi luntha lauzimu. Amakhala bwenzi lenileni la Mulungu. Amapindulitsanso achibale awo, abale ndi alongo mumpingo wachikristu, ndiponso kwa amene akufuna kudzakhala olambira Yehova.​—Aroma 10:9-14; 1 Timoteo 4:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Mboni za Yehova n’zimene zimafalitsa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo ameneŵa ndipo akupezeka m’zilankhulo zambiri.

^ ndime 19 Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1993, masamba 13-14.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi mafumu a Israyeli anafunika kuchita chiyani?

• Kodi Yesu ndi atumwi anapereka chitsanzo chotani pankhani yoŵerenga Baibulo?

• Kodi mungasinthe zinthu ziti kuti muwonjezere nthaŵi ya phunziro lanu laumwini?

• Kodi muyenera kuphunzira Mawu a Mulungu muli ndi maganizo otani?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 15]

“M’manja Mwathu”

“Ngati tikufuna . . . m’ndandanda wa mawu a m’Baibulo, chida chabwino kwambiri chimene tingagwiritse ntchito ndi Intaneti. Koma ngati tikufuna kuŵerenga Baibulo, kuliphunzira, kulisinkhasinkha, tiyenera kukhala nalo m’manja mwathu, chifukwa imeneyi ndi njira yokhayo imene ingatithandize kuti zimene zili m’Baibulo zikhazikike m’maganizo ndi mumtima mwathu.”​—Anatero Gertrude Himmelfarb, pulofesa wotchuka pa City University, New York, amene anapuma pantchito.