Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyenda M’njira za Yehova Kumapindulitsa Kwambiri

Kuyenda M’njira za Yehova Kumapindulitsa Kwambiri

Kuyenda M’njira za Yehova Kumapindulitsa Kwambiri

KODI munayendapo ulendo wautali m’mapiri n’cholinga chongofuna kusangalala kapena kuwongola miyendo? Ngati munayendapo, mosakayikira munasangalala kwambiri. Bwanji kusangalatsa kwake pamene munali kupuma kam’mpweya kayeziyezi, kuona malo akutali, ndiponso kuona kukongola kwa chilengedwe! Mwinatu mpaka munaiŵala mavuto anu a tsiku ndi tsiku.

Anthu ambiri sayenda maulendo osangalatsa ngati ameneŵa, koma ngati inu ndinu Mkristu wodzipatulira, mwina mwakhala mukuyenda mophiphiritsa m’phiri lauzimu kwanthaŵi yaitali ndithu. Monga anachitira wamasalmo wakale, mosakayikira inunso mwapemphera kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.” (Salmo 25:4) Kodi mukukumbukira mmene munkamvera pamene munakwera pa phiri la nyumba ya Yehova kwanthaŵi yoyamba n’kuyamba kuyenda pamwamba pake? (Mika 4:2; Habakuku 3:19) Mosakayikira, simunatenge nthaŵi yaitali kuzindikira kuti ndinu wotetezeka ndiponso wachimwemwe chifukwa choyenda m’njira zapamwamba za kulambira koyera. Munayamba kuona kuti mawu a wamasalmo ndi oona. Anati: “Odala anthu odziŵa liwu la lipenga; ayenda m’kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.”​—Salmo 89:15.

Komabe, nthaŵi zina, anthu amene amayenda ulendo wautali m’mapiri amavutika ndi zigwembe. Miyendo yawo imayamba kuwawa ndipo amafooka. Ifenso tingakumane ndi mavuto potumikira Mulungu. Mwina posachedwapa tayamba kuyenda mokhwekhwereza miyendo. Kodi tingatani kuti tipezenso mphamvu zathu ndi chimwemwe chathu? Choyamba tiyenera kuzindikira kuti njira za Yehova n’zapamwamba kuposa njira zina zonse.

Malamulo Apamwamba a Yehova

Njira za Yehova n’zapamwamba kuposa njira za anthu, komanso kulambira kwake ‘kwakhazikika pamwamba pa mapiri ndiponso kwakwezeka pamwamba pa zitunda.’ (Yesaya 55:9; Mika 4:1) Nzeru ya Yehova ndi nzeru “yochokera kumwamba.” (Yakobo 3:17) Malamulo ake ndi apamwamba kuposa ena onse. Mwachitsanzo, pamene Akanani ankapereka ana nsembe mwankhanza, Yehova anapatsa Aisrayeli malamulo apamwamba ndiponso osonyeza chifundo. Anawauza kuti: “Usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka . . . Mlendo . . . mumuyese pakati pa inu monga wa m’dziko momwemo; um’konde monga udzikonda wekha.”​—Levitiko 19:15, 34.

Kenako patapita zaka 1400, Yesu anapereka zitsanzo zina zambiri za ‘chilamulo chokuzika’ cha Yehova. (Yesaya 42:21) Paulaliki wake wa pa Phiri, iye anauza ophunzira ake kuti: “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa kumwamba.” (Mateyu 5:44, 45) Yesu anawonjezera kuti: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.”​—Mateyu 7:12.

Malamulo apamwamba ameneŵa amasintha mitima ya anthu amene amatsatira malamuloŵa ndipo amawalimbikitsa anthuwo kutsanzira Mulungu amene amamulambira. (Aefeso 5:1; 1 Atesalonika 2:13) Taganizirani mmene Paulo anasinthira. Nthaŵi yoyamba imene timamva za Paulo m’Baibulo m’pamene “anali kuvomerezana nawo pa imfa” ya Stefano ndiponso pamene “anapasula Mpingo.” Kenako patangopita zaka zoŵerengeka, iye anali kusamalira Akristu a ku Tesalonika “monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha.” Maphunziro ochokera kwa Mulungu omwe Paulo analandira anamusintha kuchoka pa munthu wozunza kufika pa Mkristu wosamala ena. (Machitidwe 8:1, 3; 1 Atesalonika 2:7) Iye mosakayikira anayamikira kwambiri kuti zomwe Kristu anaphunzitsa zinasintha makhalidwe ake. (1 Timoteo 1:12, 13) Kodi mtima woyamikira ngati umenewu ungatithandize bwanji kuyendabe m’njira zapamwamba za Mulungu?

Kuyenda Moyamikira

Anthu amene ali paulendo wautali wa m’mapiri amasangalala kuona zinthu zochititsa chidwi. Amasangalala kuonanso zinthu zina zing’onozing’ono zokongola m’mphepete mwa njira, monga miyala yachilendo, maluŵa okongola, ndiponso kuderuka kwa nyama zakutchire. Mwauzimunso, tiyenera kuzindikira zinthu zosangalatsa, kaya zazikulu kapena zazing’ono, zomwe timapeza chifukwa choyenda ndi Mulungu. Kuzindikira zimenezi kungatichititse kuyenda ndi mphamvu zatsopano ndipo kungapangitse ulendo wotopetsa kukhala wolimbikitsa kwambiri. Tikatero tidzanena mawu a Davide akuti: “Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: mundidziŵitse njira ndiyendemo.”​—Salmo 143:8.

Mary, yemwe wayenda m’njira za Yehova kwa zaka zambiri anati: “Ndikamayang’ana zomwe Yehova analenga, ndimaona osati luso lodabwitsa lokha la mmene zinthuzo anazipangira komanso makhalidwe abwino a Mulungu. Kaya ndikuyang’ana nyama, mbalame, kapena nyerere, chilichonse n’chosangalatsa pachokha. Ndimasangalalanso chimodzimodzi ndikamaona choonadi chauzimu chomwe m’kupita kwanthaŵi chikuwalirawalira.”

Kodi tingatani kuti tisonyeze kuti timayamikira kwambiri zimenezi? Mwa zina, sitiyenera kuona mwachibwanabwana zimene Yehova amatichitira. Paulo analemba kuti: “Pempherani kosaleka; M’zonse yamikani.”​—1 Atesalonika 5:17, 18; Salmo 119:62.

Phunziro laumwini limatithandiza kukhala ndi mtima woyamikira. Paulo analimbikitsa Akristu a ku Kolose kuti: ‘Yendani mwa Kristu Yesu, okhazikika m’chikhulupiriro, ndi kuchulukitsa chiyamiko.’ (Akolose 2:6, 7) Kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha pa zimene taŵerenga kumalimbitsa chikhulupiriro chathu ndipo kumatithandiza kukhala bwenzi lapamtima la Mlembi Wamkulu wa Baibulo. M’masamba ake onse muli chuma chomwe chingatilimbikitse “kuchulukitsa chiyamiko.”

Kutumikira Yehova pamodzi ndi abale athu kumachititsanso ulendo wathu kukhala wosavuta. Wamasalmo ananena za iye mwini kuti: “Ine ndine wakuyanjana nawo onse akukuopani, ndi iwo akusamalira malangizo anu.” (Salmo 119:63) Timasangalala kwambiri pamisonkhano ikuluikulu ndiponso pa zochitika zina zomwe timakhala pamodzi ndi abale athu. Timadziŵa kuti tili ndi banja lathu lachikristu la padziko lonse chifukwa cha Yehova ndiponso njira zake zapamwamba.​—Salmo 144:15b.

Kuwonjezera pa kuyamikira, kudziŵa kuti tili ndi udindo kudzatilimbikitsa kupitirizabe kuyenda m’njira zapamwamba za Yehova.

Kuyenda Mosamala Udindo

Anthu amene amayenda m’mapiri amadziŵa kufunika koyenda mosamala kuti asasochere kapena kuti asayandikire ku phompho lakuya. Monga anthu amene tili ndi ufulu wodzisankhira zochita, Yehova amatipatsa ufulu wokwanira woti tichite zomwe tikufuna. Koma ufulu umenewu umafuna kuti tikhale osamala pamene tikuchita ntchito yathu yachikristu.

Mwachitsanzo, Yehova amakhulupirira atumiki ake kuti agwira ntchito zawo mosamala. Iye sachita kutiuza kuchuluka kwa mphamvu ndi nthaŵi yomwe tingathere pantchito yachikristu kapena kuchuluka kwa ndalama kapena zinthu zina zomwe tingapereke. M’malo mwake, mawu a Paulo kwa Akorinto amagwiranso ntchito kwa tonsefe. Amati: “Yense achite monga anatsimikiza mtima.”​—2 Akorinto 9:7; Ahebri 13:15, 16.

Kulalikira uthenga wabwino kwa ena ndi chimodzi mwa zopereka za Akristu omwe amadziŵa kuti ali ndi udindo. Timasonyezanso kuti timadziŵa za udindo wathu mwa kupereka ndalama zothandizira pantchito yolalikira Ufumu ya padziko lonse. Gerhardt, yemwe ndi mkulu, anafotokoza kuti iye ndi mkazi wake anawonjezera kwambiri ndalama zomwe amapereka atapita kumsonkhano waukulu kummaŵa kwa Ulaya. Iye anati: “Tinaona kuti abale athu kumeneko ndi osauka kwambiri; koma amayamikira kwambiri mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Choncho, tinaganiza zothandiza mmene tingathere abale athu osoŵa m’mayiko ena.”

Kuwonjezera Kupirira Kwathu

Munthu afunika kukhala ndi mphamvu kuti athe kuyenda m’mapiri. Anthu oyenda maulendo ataliatali amakonzekera mwa kuchita maseŵero olimbitsa thupi nthaŵi iliyonse yomwe angathe kutero ndiponso ambiri amayenda maulendo afupiafupi. Mofananamo, Paulo analangiza kuti tizikhala otanganidwa mu ntchito za Ambuye kuti tikhalebe olimba mwauzimu. Paulo anati, amene akufuna ‘kuyenda koyenera Ambuye’ ndi kuti awapatse “mphamvu,” ayenera “kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino.”​—Akolose 1:10, 11.

Kuganizira komwe akupita kumathandiza munthu wapaulendo kupirira. Motani? Kuika mtima pa cholinga chake chofuna kukafika komwe akupita, chomwe chingakhale ngati phiri lomwe layamba kuonekera, kungalimbikitse munthu wapaulendoyo. Ndipo wapaulendoyo akafika pa malo ena omwe akuwadziŵa, atha kuona mtunda womwe watsala kuti akafike komwe akupitako. Ndipo akayang’ana mtunda womwe wayenda kale, iye amatsimikiza kuti akafikadi.

Mofananamo, chiyembekezo chathu cha moyo wosatha chimatilimbikitsa ndiponso chimatithandiza kupirira. (Aroma 12:12) Pakalipano, pamene tikuyenda m’njira za Yehova, timaona kuti zinthu zatiyendera bwino tikaika ndi kukwaniritsa zolinga zachikristu. Timakhalatu ndi chimwemwe kwambiri tikaganizira zaka zambiri zomwe tatumikira mokhulupirika mmbuyomu kapenanso tikaona mmene tasinthira makhalidwe athu.​—Salmo 16:11.

Kuti anthu ayende mtunda wautali ndi kukhalabe ndi mphamvu, iwo sasinthasintha kayendedwe kawo. Mofananamo, chizoloŵezi chabwino chomwe mwa zina chimaphatikizapo kupita kumisonkhano ndi mu utumiki wakumunda nthaŵi zonse, chidzatithandiza kuyenda molunjika cholinga chathu. Chotero, Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Tipitirizebe kuyenda molongosoka ndi chizoloŵezi chomwechi.”​—Afilipi 3:16, NW.

N’zoona kuti si ife tokha amene tikuyenda m’njira za Yehova. Paulo analemba kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24) Kuyanjana ndi anthu okhwima mwauzimu kudzatithandiza kuyendabe mosasintha pamodzi ndi okhulupirira anzathu.​—Miyambo 13:20.

Chinthu chomaliza ndiponso chofunika kwambiri n’chakuti sitiyenera kuiŵala mphamvu yomwe Yehova amapereka. Amene amadalira mphamvu ya Yehova adzayenda “mwamphamvu naonjezapo mphamvu.” (Salmo 84:5, 7) Ngakhale kuti nthaŵi zina timakumana ndi mavuto, tidzapitirizabe chifukwa cha thandizo la Yehova.