Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musanyengedwe

Musanyengedwe

Musanyengedwe

CHINYENGO chinayamba kalekale. Chinyengo ndi chimodzi mwa zochitika zoyambirira kulembedwa m’mbiri ya anthu. Izi zinachitika pamene Satana ananyenga Hava m’munda wa Edene.​—Genesis 3:13; 1 Timoteo 2:14.

Ngakhale kuti nthaŵi zonse kuyambira pamenepo chinyengo chakhala chofala padziko lapansi, masiku ano chafala kwambiri kuposa nthaŵi ina iliyonse. Pooneratu zomwe zidzachitike m’masiku athu ano, Baibulo linachenjeza kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.”​—2 Timoteo 3:13.

Anthu amanyengedwa pazifukwa zosiyanasiyana. Akamberembere ndi akathyali amanyenga anthu kuti awabere ndalama. Andale ena amanyenga anthu a m’dera lawo n’cholinga chofuna kupeza udindo ndipo amalolera kuluza chilichonse kuti apeze zimenezo. Anthu afika mpaka podzinyenga okha. M’malo movomereza kuti makhalidwe ena ndi oopsa, iwo amati palibe choopsa kutsatira makhalidwe ovulaza monga kusuta fodya, kugwiritsa ntchito molakwa mankhwala, kapena chiwerewere.

Ndiyeno anthu amanyengedwanso pankhani za chipembedzo. Atsogoleri achipembedzo a m’nthaŵi ya Yesu ankanyenga anthu. Yesu ananena za onyengawo kuti: “Ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu am’tsogolera wakhungu, onse aŵiri adzagwa m’mbuna.” (Mateyu 15:14) Komanso, anthu amadzinyenga okha pankhani za chipembedzo. Miyambo 14:12 amati: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.”

Anthu ambiri masiku ano amanyengedwa pankhani za chipembedzo monga ankanyengedwera anthu a m’nthaŵi ya Yesu ndipo izi n’zosadabwitsa. Mtumwi Paulo ananena kuti Satana ‘wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.’​—2 Akorinto 4:4.

Kamberembere akatinyenga timaluza ndalama. Wandale akatinyenga, potsirizira pake timakhala opanda ufulu winawake. Koma Satana akatinyenga mpaka kukana choonadi cha Yesu Kristu ndiye kuti sitidzapeza moyo wosatha. Choncho, tisanyengedwe. Phunzirani Baibulo moona mtima popeza ndilo gwero lodalirika la choonadi pa nkhani za chipembedzo. Apo ayi, tidzataya phindu lalikulu.​—Yohane 17:3.