Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ubale Wathu Wapadziko Lonse Wandilimbikitsa

Ubale Wathu Wapadziko Lonse Wandilimbikitsa

Mbiri ya Moyo Wanga

Ubale Wathu Wapadziko Lonse Wandilimbikitsa

YOSIMBIDWA NDI THOMSON KANGALE

Pa April 24, 1993, anandiitana kukakhala nawo pamwambo wopatulira maofesi a nthambi yatsopano ku Lusaka, Zambia. Mwa zina, panthambiyi pali nyumba 13. Popeza ndinkavutika kuyenda, mlongo wachikristu amene ankationetsa malo anandifunsa mokoma mtima kuti, “Kodi mungakonde kuti ndikunyamulireni mpando kuti muzipumula mukatopa?” Zoti ine ndine munthu wakuda ndipo iye ndi mzungu analibe nazo ntchito. Ndinachita chidwi kwambiri ndipo ndinam’thokoza chifukwa kukoma mtima kwake kunachititsa kuti ndione nthambi yonseyo.

KWA zaka zambiri, zochitika ngati zimenezi zandisangalatsa ndiponso zalimbitsa chikhulupiriro changa chakuti gulu lachikristu la Mboni za Yehova ndilo lili ndi chikondi chomwe Yesu ananena kuti chidzakhala chizindikiro cha otsatira ake oona. (Yohane 13:35; 1 Petro 2:17) Imani ndikuuzeni mmene ndinadziŵirana ndi Akristu ameneŵa kale mu 1931, chaka chomwe iwo analengeza kuti akufuna kumadziŵika ndi dzina la m’Baibulo lakuti Mboni za Yehova.​—Yesaya 43:12.

Utumiki M’masiku Oyambirira mu Africa

Mu November 1931, ndinali ndi zaka 22 ndipo ndinkakhala ku Kitwe, m’chigawo cha Copperbelt ku Northern Rhodesia (komwe tsopano ndi ku Zambia). Ndinadziŵana ndi Mboni chifukwa cha mnzanga amene ndinkaseŵera naye mpira wamiyendo. Ndinkachita nawo misonkhano yawo ina ndipo ndinalembera kalata ku ofesi ya nthambi ku Cape Town, South Africa, yoitanitsa buku lothandiza kuphunzira Baibulo lakuti The Harp of God. * Bukulo linali lachingelezi ndipo linkandivuta kumva chifukwa chinenerochi sindinkachidziŵa bwino.

Chigawo cha Copperbelt chili pa mtunda wa makilomita 240 kumwera chakumadzulo kwa nyanja ya Bangweulu, kufupi ndi kumene ndinakulira ine. Anthu ambiri ochokera m’zigawo zina ankabwera m’chigawochi kudzagwira ntchito m’migodi ya kopa. Magulu ambiri a Mboni ankasonkhana nthaŵi zonse kuti aphunzire Baibulo. Mosakhalitsa, ndinasamuka ku Kitwe kupita ku Ndola. Kumeneko, ndinayamba kusonkhana ndi gulu la Mboni. Panthaŵiyo, ndinali kaputeni wa timu yampira ya Prince of Wales. Ndinkagwiranso ntchito m’nyumba ya mzungu amene anali mkulu wa kampani ya African Lakes Corporation yomwe inali ndi masitolo ambiri m’mayiko apakati pa Africa.

Sukulu sindinaphunzire kwenikweni moti chingelezi chopereŵera chomwe ndinkadziŵa ndinaphunzira kwa azungu amene ndinkagwirako ntchito. Komabe, ndinkafunitsitsa kuwonjezera maphunziro anga moti ndinafunsira malo pa sukulu ina ku Plumtree, ku Southern Rhodesia (komwe tsopano ndi ku Zimbabwe). Komabe panthaŵiyi, ndinalemba kalata ina ku ofesi ya nthambi ku Cape Town yowadziŵitsa kuti ndalandira buku lakuti The Harp of God ndiponso kuti ndikufuna kutumikira Yehova nthaŵi zonse.

Ndinadabwa kwambiri kulandira yankho lawo lomwe linali lakuti: “Tikuthokoza kwambiri kuti ukufuna kutumikira Yehova. Limbikira kupempherera zomwe ukufunazo ndipo Yehova adzakuthandiza kuti udziŵe choonadi kwambiri ndiponso adzakupezera malo oti um’tumikire.” N’taŵerenga kalatayo maulendo angapo, ndinafunsa a Mboni angapo zomwe ndiyenera kuchita. Iwo anati: “Ngatidi ukufuna kutumikira Yehova, yamba kum’tumikira.”

Ndinapemphera za nkhaniyi mlungu wonse ndipo kenako ndinaganiza zosiya kupita kusukulu, n’kupitiriza kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Chaka chotsatira, mu January 1932, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa kubatizidwa. N’tasamuka ku Ndola kupita ku Luanshya, ndinakumana ndi Jeanette, wokhulupirira mnzanga, ndipo tinakwatirana mu September 1934. Pamene tinkakwatirana n’kuti Jeanette ali kale ndi ana aŵiri, wamwamuna ndi wamkazi.

Pang’ono ndi pang’ono, ndinapita patsogolo mwauzimu, ndipo mu 1937, ndinayamba utumiki wanthaŵi zonse. Patangopita nthaŵi yochepa, anandiika kukhala mtumiki woyendayenda, tsopano amati woyang’anira dera. Oyang’anira oyendayenda amachezera mipingo ya Mboni za Yehova kuti ailimbikitse mwauzimu.

Kulalikira M’zaka Zoyambirira

Mu January 1938, anandiuza kuti ndikaonane ndi mfumu ina yachikuda dzina lake Sokontwe. Mfumuyi inapempha kuti Mboni za Yehova zikacheze nayo. Ndinayenda pa njinga kwa masiku atatu kuti ndikafike m’dera la mfumuyi. N’taiuza kuti anditumiza kudzaonana nayo malinga ndi kalata yomwe inalemba ku ofesi yathu ya nthambi ku Cape Town, mfumuyi inathokoza kwambiri.

Mfumuyi inayenda nyumba ndi nyumba kuitana anthu ake kuti asonkhane ku insaka (bwalo la mfumu). Anthuwo atasonkhana, ndinawalankhula. Zotsatira zake zinali zakuti, maphunziro a Baibulo ambiri anayambika. Mfumuyo ndi mlembi wake ndiwo anali oyamba kukhala oyang’anira a mipingo kumeneko. M’derali lomwe tsopano amalitcha kuti chigawo cha Samfya muli mipingo yopitirira 50.

Kuchokera mu 1942 mpaka 1947, ndinkatumikira m’chigawo chozungulira nyanja ya Bangweulu. Ndinkakhala masiku khumi pa mpingo uliwonse. Popeza ogwira ntchito yotuta mwauzimu anali oŵerengeka, tinkaona monga momwe Mbuye wathu, Yesu Kristu, anaonera pomwe anati: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:36-38) Masiku amenewo mayendedwe anali ovuta kwambiri. Choncho, nthaŵi zambiri ndikamayendera mipingo, Jeanette ankatsala ndi ana ku Luanshya. Panthaŵiyo, n’kuti ine ndi Jeanette tili ndi ana ena aŵiri. Koma kenako mwana mmodzi anamwalira ali ndi miyezi khumi.

Magalimoto komanso misewu zinali zochepa masiku amenewo. Tsiku lina ndinanyamuka ulendo wamakilomita oposa 200 panjinga ya Jeanette. Nthaŵi zina powoloka mtsinje waung’ono, ndinkanyamula njinga pamapewa, n’kuigwira ndi dzanja limodzi, kwinaku n’kumasambira ndi dzanja linali. Mosayembekezereka, Mboni zinachuluka kwambiri ku Luanshya, ndipo mu 1946, anthu 1,850 anafika pa Chikumbutso cha Imfa ya Kristu.

Kulimbana ndi Adani a Ntchito Yathu

Tsiku lina, nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse ili m’kati, woimira boma wa ku Kawambwa anandiitana n’kundiuza kuti: “Ndikufuna kuti usiye kugwiritsa ntchito mabuku a Watch Tower Society chifukwa tsopano ndi oletsedwa. Koma ndikhoza kukupatsa mabuku ena amene angakuthandize kulemba mabuku atsopano oti uzigwiritsa ntchito.”

Ndinayankha kuti: “Mabuku amene ndili nawo ndi okwanira ndipo sindikufuna ena.”

Iye anati: “Azungu a ku America suwadziŵa bwino eti!” (panthaŵiyo mabuku athu onse ankasindikizidwa ku United States). “Akupusitsa.”

Ndinayankha kuti: “Ayi, amene ndimagwirizana nawo ine, sangandipusitse.”

Kenako anandifunsa kuti: “Kodi sungalimbikitse anthu a m’mipingo yanu kuti asonkhe ndalama zothandizira pa nkhondo monga akuchitira a zipembedzo zina?”

Ndinayankha kuti: “Imeneyo ndi ntchito ya atumiki a boma.”

Iye anati: “Bwanji upite kaye kunyumba ukaganize bwino za nkhaniyi?”

Ndinayankha kuti: “Pa Eksodo 20:13 ndiponso pa 2 Timoteo 2:24, Baibulo limatiletsa kuti usaphe komanso usachite ndewu.”

Ngakhale anandilola kupita kunyumba, woimira boma wa ku Foot Rosebery, tauni yomwe tsopano ndi Mansa, anandiitanitsanso. Iye anati: “Ndakuitana kuti ndikuuze kuti boma laletsa mabuku anu.”

Ndinati: “Inde, ndamva kale zimenezo.”

Iye anati: “Choncho, pita m’mipingo yanu yonse ndipo uwauze anthu amene umapemphera nawo kuti abweretse mabuku awo onse kuno. Wamva?”

Ndinayankha kuti: “Imeneyi si ntchito yanga koma ya atumiki a boma.”

Kukumana Kosayembekezereka Kunabala Zipatso

Nkhondoyo itatha, tinapitiriza kulalikira. Tsiku lina mu 1947, ndinali n’tangomaliza kutumikira mpingo wina m’mudzi wa Mwanza pamene ndinafunsa komwe ndingagule tiyi. Anandilozera kunyumba ya bambo Nkonde komwe ankagulitsako tiyi. Bambo Nkonde ndi mkazi wawo, anandilandira ndi manja aŵiri. Ndinawapempha bambo Nkonde ngati panthaŵi yomwe ndikumwa tiyi, angaŵerenge mutu wakuti ‘Helo, Malo Achiyembekezo,’ m’buku lakuti “Mulungu Akhale Woona.”

Ndiyeno n’tamaliza kumwa tiyi ndinawafunsa kuti, “Kodi inuyo Helo m’mati n’chiyani?” Anachita chidwi kwambiri ndi zomwe anaŵerenga, ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Kenako anabatizidwa pamodzi ndi akazi awo. Ngakhale kuti a Nkonde sanapitirize choonadi, mkazi wawo ndi ana awo anapitiriza. Ndipotu tikunena pano, mwana wawo wina wamkazi, Pilney, akutumikirabe pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Zambia. Ngakhale kuti mayi a Pilney tsopano ndi okalamba kwambiri, iwo akadali Mboni yokhulupirika.

Kukakhala Kummaŵa kwa Africa Kwanthaŵi Yochepa

Ofesi yathu ya nthambi ku Northern Rhodesia yomwe anaikhazikitsa kumayambiriro a mu 1948 ku Lusaka, inanditumiza ku Tanganyika (komwe tsopano ndi ku Tanzania). Ine ndi mkazi wanga tinanyamuka motsagana ndi Mboni ina paulendo wathu womwe unali wapansi ndiponso wodutsa m’mapiri. Tinayenda masiku atatu ndipo unali ulendo wotopetsa. Ine ndinanyamula mabuku, mkazi wanga ananyamula zovala, ndipo Mboni inayo inanyamula zofunda.

Titafika ku Mbeya mu March 1948, panali ntchito yaikulu yothandiza abale kuti asinthe zina ndi zina pa moyo wawo kuti agwirizane ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa. Anthu m’deralo ankangotitchula kuti anthu a Watchtower. Ngakhale kuti abale anali atavomereza dzina lakuti Mboni za Yehova, dzinali sankalitchula pagulu. Komanso, Mboni zina zinafunika kusiya miyambo ina yokhudza kulemekeza anthu akufa. Koma kwa anthu ambiri, chomwe chinali chovuta kwambiri chinali kulembetsa maukwati awo ku boma, kuti achitidwe ulemu ndi onse.​—Ahebri 13:4.

Kenako, ndinali ndi mwayi wokatumikira m’madera ena a Kummaŵa kwa Africa, monga m’dziko la Uganda. Kwa milungu isanu ndi umodzi ndinakhalapo ku Entebbe ndi ku Kampala komwe ndinathandiza anthu ambiri kudziŵa choonadi cha m’Baibulo.

Kundiitana Kupita ku New York City

N’tatumikira ku Uganda kwanthaŵi yaitali ndithu, chakumayambiriro a mu 1956, ndinafika mumzinda wa Dar es Salaam womwe ndi likulu la dziko la Tanganyika. Kumeneko, kalata yochokera ku likulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova inali kundidikira. M’kalatayo munali malangizo oti ndiyambe kukonzekera ulendo wopita ku New York kukachita nawo msonkhano wamayiko womwe unali kudzayamba pa July 27 mpaka pa August 3, 1958. N’zosachita kufunsa, kuti ndinali ndi chimwemwe chodzaza tsaya.

Nthaŵi yonyamuka itakwana, ine pamodzi ndi Luka Mwango, woyang’anira woyendayenda wina yemwenso anali nawo paulendowu tinakwera ndege kuchoka ku Ndola kupita ku Salisbury (komwe tsopano ndi ku Harare) ku Southern Rhodesia ndipo kenako tinapita ku Nairobi, Kenya. Kuchoka ku Kenya tinakwera ndege kupita ku London, England, komwe anatilandira ndi manja aŵiri. Titapita kukagona tsiku lomwe tinafika ku England, tinali osangalala kwambiri moti tinkangokambirana mmene azungu atilandirira bwino ife anthu akuda. Izi zinatilimbikitsa kwambiri.

Kenako, tinafika ku New York komwe kunachitikira msonkhanowo. Tsiku limodzi la msonkhanowo, ndinapereka lipoti la mmene ntchito ya Mboni za Yehova ikuyendera ku Northern Rhodesia. Patsikulo kunafika anthu pafupifupi 200,000 omwe anasonkhana ku Polo Grounds ndi Yankee Stadium mumzinda wa New York. Sindinagone tsiku limenelo chifukwa choganizira mwayi womwe anandipatsawo.

Mosakhalitsa msonkhano unatha ndipo tinabwerera kumudzi. Paulendo wathu wobwerera kumudzi, abale ndi alongo athu a ku England anatisamaliranso bwino kwambiri. Kugwirizana kwa anthu a Yehova, kaya akhale osiyana mtundu kapena dziko lomwe akuchokera, kunaoneka bwino kwambiri kwa ife paulendowu moti sitidzaiŵala.

Kupitiriza Kutumikira Komanso Mayesero

Mu 1967, anandiika kukhala woyang’anira chigawo​—mtumiki amene amayendera madera. Panthaŵiyo Mboni ku Zambia zinali zitawonjezeka kupitirira pa 35,000. Kenako chifukwa cha umoyo wovutirapo anandiika kukhala woyang’anira dera la Copperbelt. M’kupita kwanthaŵi, Jeanette anadwala ndipo mu December 1984 anamwalira ali wokhulupirika kwa Yehova.

Jeanette atamwalira, achibale ake omwe si a Mboni anandivutitsa kwambiri. Iwo ankandiimba mlandu woti ndamulodza Jeanette ndine. Koma ena amene ankadziŵa za matenda a Jeanette ndiponso kuti analankhulanapo ndi dokotala wake anawafotokozera achibale a Jeanette zoona zake za nkhaniyi. Kenako panabukanso chiyeso china. Achibale ena a Jeanette ankafuna kuti ndiloŵe ukupyanika (chokolo). M’dera lakwathu, mwambo umenewu umafuna kuti mkazi kapena mwamuna akamwalira, wotsalayo akwatire kapena kukwatiwa ndi mbale wa womwalirayo. Ine zimenezo ndinakana.

M’kupita kwanthaŵi, anthuwo anasiya kundivutitsa. Ndinathokoza kwambiri kuti Yehova anandithandiza kuti ndisagonje pa ziyesozi. Patapita mwezi umodzi titaika maliro a mkazi wanga, mbale wina anabwera kwa ine nati: “Mbale Kangale, munatilimbikitsa kwambiri pamaliro a mkazi wanu chifukwa simunalole mwambo uliwonse wosakondweretsa Mulungu kuchitika. Tikukuthokozani kwambiri.”

Zotuta Zochititsa Chidwi

Zaka 65 zatha tsopano kuchokera pamene ndinayamba utumiki wanthaŵi zonse monga wa Mboni za Yehova. N’zosangalatsa kwambiri kuti m’zaka zimenezi ndaona mipingo mazanamazana ikupangidwa ndiponso Nyumba za Ufumu zambirimbiri zikumangidwa m’madera amene ndinatumikiramo monga woyang’anira woyendayenda. Kuchokera pa Mboni 2,800 mu 1943, tsopano olengeza Ufumu kuno ku Zambia tawonjezereka kupitirira 122,000. Inde, chaka chatha, anthu opitirira 514,000 anafika pa Chikumbutso m’dziko lino lomwe lili ndi anthu osakwana 11,000,000.

Pakalipano, Yehova akundisamalira bwino kwambiri. Ndikafuna chithandizo chamankhwala, mbale wachikristu amapita nane kuchipatala. Mipingo imandipemphabe kukakamba nkhani za onse ndipo zimenezi zimandipatsa mwayi wokhala ndi macheza olimbikitsa. Mpingo umene ndimasonkhana umakonza zoti alongo achikristu azisinthana kukandikonzera m’nyumba mwanga. Abale nawonso amadzipereka kunditengera kumisonkhano mlungu uliwonse. Ndikudziŵa kuti si bwenzi ndikusamalidwa mwachikondi chonchi n’kanakhala kuti sindikutumikira Yehova. Ndikumuthokoza kwambiri chifukwa chopitiriza kundigwiritsira ntchito mu utumiki wanthaŵi zonse ndiponso chifukwa cha maudindo ambiri amene ndakhala nawo mpaka lero.

Maso anga saona bwinobwino tsopano, ndipo ndikamapita ku Nyumba ya Ufumu, ndimayenera kupumula kambirimbiri m’njira. Chikwama changa cha mabuku chimalemera kwambiri masiku ano, moti ndimachotsa buku lililonse lomwe sindikaligwiritsa ntchito kumisonkhano. Utumiki wanga wakumunda umangokhala wochititsa maphunziro a Baibulo ndi anthu amene amabwera kunyumba kwanga. Komabe, ndimasangalala kwambiri ndikamaganizira zaka zakumbuyo ndi kuona kuwonjezereka kochititsa chidwi komwe kwachitika. Ndatumikira m’dziko lomwe mawu a Yehova a pa Yesaya 60:22 akwaniritsidwa mochititsa chidwi. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Wang’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” Inde, ndaona ndi maso anga zimenezi zikuchitika osati ku Zambia kokha kuno komanso padziko lonse. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano sakulisindikizanso.

^ ndime 50 N’zachisoni kuti Mbale Kangale anamwalira ali wokhulupirika pamene nkhani ino ankaikonza kuti itulutsidwe.

[Zithunzi patsamba 24]

Thomson komanso nthambi ya ku Zambia kumbuyoko

[Chithunzi patsamba 26]

Mmene nthambi ya ku Zambia ilili masiku ano