Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulemerero wa Yehova Umawalira Anthu Ake

Ulemerero wa Yehova Umawalira Anthu Ake

Ulemerero wa Yehova Umawalira Anthu Ake

“Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha.”​—YESAYA 60:20.

1. Kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu ake okhulupirika?

“YEHOVA akondwera nawo anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.” (Salmo 149:4) Wamasalmo wakale ndi amene ananena zimenezi, ndipo zochitika za m’mbiri zatsimikizira kuti mawu akeŵa ndi oona. Anthu a Yehova akakhulupirika, iye amawasamala, kuwachulukitsa, ndiponso kuwateteza. Kale, iye anathandiza anthu ake kugonjetsa adani awo. Lerolino amathandiza anthu ake kukhala olimba mwauzimu ndipo amawatsimikizira kuti adzawapulumutsa pamaziko a nsembe ya Yesu. (Aroma 5:9) Amachita zimenezi chifukwa chakuti amawaona kukhala okongola.

2. Ngakhale kuti anthu a Mulungu akutsutsidwa, kodi angakhale ndi chikhulupiriro chotani?

2 Komabe, m’dziko lino limene lili mumdima wandiweyani, amene ‘amakhala opembedza [“odzipatulira kwa Mulungu,” NW]’ anthu adzawatsutsa. (2 Timoteo 3:12) Komabe, Yehova amawaona adaniwo, ndipo akuwachenjeza kuti: “Mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzawonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.” (Yesaya 60:12) Masiku ano, anthu akutsutsa m’njira zosiyanasiyana. M’mayiko ena, adani salola Akristu oona kulambira Yehova momasuka kapena amawaletsa kumene. Ndipo m’mayiko ena, adaniŵa amamenya olambira Yehova ndi kutentha katundu wawo. Komabe, kumbukirani kuti Yehova waneneratu zimene zidzachitikira omwe akutsutsa kukwaniritsidwa kwa chifuniro chake. Adani adzalephera. Onse olimbana ndi Ziyoni, yemwe akuimiridwa ndi ana ake pa dziko lapansi, adzalephera. Kodi amenewo si mawu olimbikitsa kwambiri ochokera kwa Mulungu wathu wamkulu, Yehova?

Wawadalitsa Kuposa Mmene Iwo Ankayembekezera

3. Kodi n’chiyani chikuimira kukongola ndi kuchulukana kwa olambira Yehova?

3 Zoona zake n’zakuti m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipa lino, Yehova wadalitsa anthu ake kuposa mmene iwo ankayembekezera. Iye makamaka wakongoletsa pang’onopang’ono malo ake olambirira ndi anthu amene amalambiramo amene ali ndi dzina lake. Ulosi wa Yesaya ukunena kuti iye anauza Ziyoni kuti: “Ulemerero wa Lebano udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.” (Yesaya 60:13) Mapiri amene ali ndi nkhalango yabwino, amasangalatsa kuwaona. Motero, mitengo yabwino ikuimira moyenerera kukongola ndi kuchulukana kwa olambira Yehova.​—Yesaya 41:19; 55:13.

4. Kodi “kachisi” ndi “malo a mapazi [a Yehova]” n’chiyani, ndipo zimenezi zakometseredwa motani?

4 Kodi “kachisi” ndi “malo a mapazi [a Yehova]” amene awatchula pa Yesaya 60:13 n’chiyani? Mawu ameneŵa akuimira mabwalo a kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova, omwe ndi makonzedwe olambira Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu. (Ahebri 8:1-5; 9:2-10, 23) Yehova wafotokoza kuti ali ndi cholinga chopatsa ulemerero kachisi wauzimu ameneyo mwa kusonkhanitsa anthu amitundu yonse kuti abwere ndi kudzalambira kumeneko. (Hagai 2:7) Yesaya m’mbuyomo anaona makamu a anthu amitundu akukhamukira ku phiri lokwezeka lolambirira la Yehova. (Yesaya 2:1-4) Patapita zaka zambiri, mtumwi Yohane anaona m’masomphenya “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Khamu limeneli linaima ‘ku mpando wachifumu wa Mulungu; kum’tumikira Iye usana ndi usiku m’Kachisi mwake.’ (Chivumbulutso 7:9, 15) Maulosi onseŵa akwaniritsidwa m’nthaŵi yathu ino, ndipo tadzionera tokha kuti nyumba ya Yehova yakometseredwa.

5. Kodi n’kusintha kwakukulu kwabwino zedi kuti kumene kwachitikira ana a Ziyoni?

5 Konsekutu n’kusintha kwakukulu kwa Ziyoni kwabwino zedi! Yehova akuti: “Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro [“chinthu chonyaditsa,” NW] chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.” (Yesaya 60:15) Nkhondo yoyamba yapadziko lonse ikuyandikira kutha, “Israyeli wa Mulungu” analidi m’nthaŵi ya chisoni. (Agalatiya 6:16) Anamvadi kuti ‘anasiyidwa,’ chifukwa ana ake padziko lapansi sanazindikire bwinobwino zimene Mulungu ankafuna kwa iwo. Ndiyeno, mu 1919, Yehova anapatsanso mphamvu atumiki ake odzozedwa, ndipo kuchokera nthaŵi imeneyo wawadalitsa ndi kupita patsogolo kwauzimu kochititsa kaso. Ndiponso, kodi lonjezo la m’vesi limeneli si losangalatsa? Yehova adzamuona Ziyoni kukhala “chinthu chonyaditsa.” Inde, ana a Ziyoni ndi Yehova yemwe, adzanyadira naye Ziyoniyo. Iye adzakhala “chokondweretsa,” chimene chidzachititsa anthu kukhala ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Ndipotu, zimenezi sizidzangokhala kwa nthaŵi yochepa chabe ayi. Ziyoni, yemwe akuimiridwa ndi ana ake padziko lapansi, Mulungu adzamuyanja kwa “mibadwo yambiri.” Sadzasiya kumuyanja.

6. Kodi Akristu oona agwiritsa ntchito bwanji zinthu za amitundu?

6 Tsopano tamverani lonjezo lina la Mulungu. Yehova akuuza Ziyoni kuti: “Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziŵa kuti Ine Yehova ndine mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.” (Yesaya 60:16) Kodi Ziyoni wayamwa bwanji “mkaka wa amitundu” ndi kuyamwanso “bere la mafumu”? Akristu odzozedwa ndi anzawo a “nkhosa zina” amagwiritsa ntchito zinthu zina zaphindu za amitundu pofuna kupititsa patsogolo kulambira koyera. (Yohane 10:16) Ndalama zimene anthu amapereka mwaufulu zathandiza kuti ntchito yaikulu yolalikira ndi kuphunzitsa padziko lonse itheke. Kugwiritsa ntchito mwanzeru umisiri wamakono, kwafeŵetsa ntchito yosindikiza mabaibulo ndi mabuku othandiza kuphunzira Baibulo m’zinenero zambiri. Lerolino, anthu ochuluka kwambiri kuposa kale lonse akupeza choonadi cha m’Baibulo. Anthu a m’mayiko ambirimbiri akuphunzira kuti Yehova amene anawombola atumiki ake odzozedwa ku ukapolo wauzimu, alidi Mpulumutsi.

Kupita Patsogolo kwa Kayendetsedwe ka Gulu

7. Kodi ana a Ziyoni aona kupita patsogolo kotani?

7 Yehova wakometseranso anthu ake m’njira ina. Wawadalitsa ndi kupita patsogolo kwa kayendetsedwe ka gulu. Pa Yesaya 60:17 timaŵerenga kuti: “M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” Ngati golidi aloŵa m’malo mwa mkuwa ndiye kuti zinthu zikuyenda bwino, chimodzimodzinso ndi zinthu zina zomwe azitchulazo. Mogwirizana ndi zimenezi, Israyeli wa Mulungu waona kupita patsogolo kwa kayendetsedwe ka gulu m’masiku onse otsiriza. Taonani zitsanzo izi.

8-10. Fotokozani kupita patsogolo kwa kayendetsedwe ka gulu kumene kwachitika kuyambira 1919.

8 Chaka cha 1919 chisanafike, mipingo ya anthu a Mulungu inali kuyang’aniridwa ndi akulu ndi adikoni omwe mpingo unali kuwasankha mowavotera. Kuyambira chaka chimenecho, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anali kusankha wotsogolera utumiki mu mpingo uliwonse kuti aziyang’anira ntchito ya utumiki wakumunda. (Mateyu 24:45-47) Komabe, zimenezi sizinali kuyenda bwino m’mipingo yambiri chifukwa chakuti akulu ena amene ankawasankha mowavoterawo sankathandiza mokwanira ntchito yolalikira. Motero, mu 1932, mipingo anailangiza kuti ileke kusankha akulu ndi adikoni. M’malo mwake, ankafunika kusankha mwa voti amuna a m’komiti ya utumiki yomwe inali yoti izigwira ntchito limodzi ndi wotsogolera utumiki. Zimenezi zinali ngati kutenga “mkuwa” m’malo mwa “mtengo,” komwe kunali kusintha kwakukulu.

9 Mu 1938 mipingo padziko lonse inalandira dongosolo latsopano, limene linali logwirizana kwambiri ndi zitsanzo za m’Malemba. Anaika mtumiki wa gulu kuti aziyang’anira mpingo pamodzi ndi atumiki ena, ndipo onse anali kuwaika motsogozedwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Panalibenso kusankha mwa mavoti. Motero, otsogolera mumpingo anali kuwaika mwa teokalase. Zimenezi zinali ngati “chitsulo” m’malo mwa “miyala” kapena “golidi” m’malo mwa “mkuwa.”

10 Kuyambira nthaŵi imeneyo, kayendetsedwe ka gulu kapitabe patsogolo. Mwachitsanzo, mu 1972 kunaoneka kuti kukhala ndi bungwe la akulu loikidwa mwa teokalase limene lingamayang’anire mpingo, osati mkulu m’modzi azilamulira ena onse, kunali kofanana kwambiri ndi mmene anali kuyendetsera mpingo wachikristu wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Ndiponso pafupifupi zaka ziŵiri zapitazo, kuwongolera kwina kunachitika. Panali kusintha pankhani ya oyendetsa ntchito za mabungwe ena oona za malamulo, zomwe zinapatsa mpata Bungwe Lolamulira kusamalira mokwanira zofunika zauzimu za anthu a Mulungu m’malo motanganidwa ndi nkhani zamalamulo za tsiku ndi tsiku.

11. Kodi ndani wachititsa kuti pakhale kupita patsogolo pa kayendetsedwe ka gulu la anthu a Yehova, ndipo n’chiyani chachitika chifukwa cha zimenezi?

11 Kodi ndani amene akuchititsa kuti pakhale kupita patsogolo kumeneku kwa kayendetsedwe ka gulu? Palibenso wina koma Yehova Mulungu. Ndiye amene akuti: “Ndidzatenga golidi.” Ndiponso ndiye amene akupitiriza kuti: “Ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” Inde, Yehova ndi amene amayang’anira anthu ake. Kupita patsogolo kwa kayendetsedwe ka gulu kumene analoseraku, ndi njira ina imene iye akukometsera anthu ake. Ndipo chifukwa cha zimenezi, Mboni za Yehova zadalitsidwa m’njira zambiri. Pa Yesaya 60:18 timaŵerenga kuti: “Chiwawa sichidzamvekanso m’dziko mwako, kupulumutsa pena kupasula m’malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando.” Mawu okomatu aŵa! Koma kodi mawu ameneŵa akwaniritsidwa bwanji?

12. Kodi zatheka bwanji kuti Akristu oona akhale ndi mtendere?

12 Akristu oona amadalira Yehova yekha basi kuti awalangize ndi kuwatsogolera, ndipo zotsatira zake zili monga mmene Yesaya analosera kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Ndiponso, mzimu wa Yehova ukugwira ntchito pa anthu ake, ndipo mbali ina ya chipatso cha mzimu umenewo ndiyo mtendere. (Agalatiya 5:22, 23) Mtendere wa anthu a Yehova umenewu umawapangitsa kukhala malo othaŵirako otsitsimula m’dziko lachiwawali. Mtendere wawo, umene watheka chifukwa cha chikondi chimene Akristu ali nacho kwa wina ndi mnzake, ndiwo chithunzithunzi cha mmene anthu adzakhalira m’dziko latsopano. (Yohane 15:17; Akolose 3:14) Mosakayika, tonsefe tikusangalala kuti tili nawo ndiponso timalimbikitsa mtendere umenewu womwe umatamanda ndi kulemekeza Mulungu wathu ndipo ndiwo uli chinthu chachikulu m’paradaiso wathu wauzimu.​—Yesaya 11:9.

Kuunika kwa Yehova Kudzapitirizabe Kuwala

13. N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti kuunika kwa Yehova sikudzaleka kuwalira anthu ake?

13 Kodi kuunika kwa Yehova kudzapitirizabe kuwalira anthu ake? Inde! Pa Yesaya 60:19, 20 timaŵerenga kuti: “Dzuŵa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako. Dzuŵa lako silidzaloŵanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha.” “Masiku a kulira maliro” kwa omwe anali mu ukapolo wauzimu atangotha mu 1919, kuunika kwa Yehova kunayamba kuwawalira. Yehova akuwayanjabe pamene kuunika kwake kukupitirizabe kuwala patatha zaka zopitirira 80 kuchokera nthaŵi imeneyo. Ndipo kuwalako sikudzatha. Kwa olambira ake, Mulungu wathu ‘sadzaloŵa’ ngati dzuŵa kapena ‘kumka kumidima’ ngati mwezi. M’malo mwake, iye adzawalitsa kuunika kwake pa iwo mpaka muyaya. Amenewotu ndi mawu okhazika mtima pansi kwambiri kwa ife pamene tikukhala m’masiku otsiriza a dziko lamdimali!

14, 15. (a) Kodi anthu a Mulungu onse ndi “olungama” motani? (b) Malinga ndi Yesaya 60:21, kodi ndi kukwaniritsidwa kofunika kuti kumene a nkhosa zina akuyembekezera?

14 Tsopano tamverani lonjezo lina la Yehova kwa oimira Ziyoni padziko lapansi, Israyeli wa Mulungu. Yesaya 60:21 akuti: “Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala choloŵa chawo ku nthaŵi zonse, nthambi yowoka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.” Mu 1919 pamene Akristu odzozedwa anayambiranso kugwira ntchito, iwo anali gulu lapadera. Iwo “ayesedwa olungama” m’dziko lochimwa lino chifukwa cha chikhulupiriro chawo chosagwedera mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. (Aroma 3:24; 5:1) Ndiyeno, mofanana ndi Aisrayeli amene anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo, iwo ali ndi “dziko,” dziko lauzimu, kapena malo a ntchito, kumene angasangalale ndi paradaiso wauzimu. (Yesaya 66:8) Kukongola konga paradaiso kwa dziko limenelo sikudzatha chifukwa, mosiyana ndi Israyeli wakale, Israyeli wa Mulungu monga mtundu sudzakhala wosakhulupirika. Chikhulupiriro chawo, kupirira kwawo ndi changu chawo sizidzasiya kulemekezetsa dzina Mulungu.

15 Anthu onse a mu mtundu wauzimu umenewo aloŵa m’pangano latsopano. Lamulo la Yehova lalembedwa m’mitima ya iwo onse, ndipo Yehova wawakhululukira machimo awo pamaziko a nsembe ya dipo ya Yesu. (Yeremiya 31:31-34) Amawayesa olungama monga “ana” ndipo amachita nawo zinthu ngati kuti ndi angwiro. (Aroma 8:15, 16, 29, 30) Yehova wakhululukiranso machimo a anzawo a nkhosa zina pamaziko a nsembe ya Yesu ndipo, monga Abrahamu, wawayesa olungama monga mabwenzi a Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro. Iwo ‘atsuka zovala zawo naziyeretsa m’mwazi wa mwanawankhosa.’ Ndipo anzawo a nkhosa zina ameneŵa akuyembekezera madalitso ena aakulu. Akadzapulumuka “chisautso chachikulu” kapena akadzawaukitsa adzaona kukwaniritsidwa kwenikweni kwa mawu a pa Yesaya 60:21 pamene dziko lonse lapansi lidzasanduka paradaiso. (Chivumbulutso 7:14; Aroma 4:1-3) Panthaŵi imeneyo, “ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:11, 29.

Anthu Akuwonjezekabe

16. Kodi ndi lonjezo lochititsa chidwi liti limene Yehova anapereka, ndipo lakwaniritsidwa bwanji?

16 M’vesi lomaliza la Yesaya chaputala 60, timaŵerenga lonjezo la Yehova lomaliza m’chaputala chimenechi. Iye akuuza Ziyoni kuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.” (Yesaya 60:22) Yehova wakwaniritsadi zimenezi m’nthaŵi yathu ino. Pamene odzozedwa anayambiranso kugwira ntchito mu 1919, analipo ochepa, analidi “wamng’ono.” Iwo anayamba kuchuluka pamene Aisrayeli ena auzimu anali kusonkhanitsidwa. Ndiyeno a nkhosa zina anayamba kukhamukira kwa iwo m’chigulu chimene chinali kuwonjezekawonjezekabe. Mtendere wa anthu a Mulungu, paradaiso wauzimu amene ali ‘m’dziko’ lawo, wakopa anthu oona mitima ochuluka kotero kuti “wochepa” wasandukadi “mtundu wamphamvu.” Pakalipano ‘mtunduwu,’ womwe wapangidwa ndi Israyeli wa Mulungu ndi “alendo” odzipatulira oposa sikisi miliyoni, uli ndi anthu ambiri kuposa amene ali m’mayiko ambiri odzilamulira a dziko lapansili. (Yesaya 60:10) Nzika zake zonse zimawalitsa nawo kuunika kwa Yehova, ndipo zimenezi zimawapangitsa onse kukhala okoma m’maso mwake.

17. Kodi kukambirana Yesaya chaputala 60 kumeneku kwakukhudzani motani?

17 Kunena zoona, kukambirana mfundo zazikulu za Yesaya chaputala 60 kwalimbikitsa chikhulupiriro chathu. N’zolimbikitsa kuona kuti Yehova anadziŵiratu kuti anthu ake adzapita ku ukapolo wauzimu ndiyeno n’kuwabwezeretsa. N’zodabwitsa kuti Yehova anaoneratu kuti olambira oona adzawonjezereka m’nthaŵi yathu ino. Ndiponso, n’zolimbikitsa kwambiri kukumbukira kuti Yehova sadzatisiya. N’zosangalatsa kwambiri kuti zipata za “mzinda” zidzakhala zotseguka nthaŵi zonse pofuna kulandira ndi manja aŵiri anthu amene “anaikidwiratu ku moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48) Yehova adzapitiriza kuwalira anthu ake. Ziyoni adzapitirizabe kukhala chinthu chonyaditsa pamene ana ake akulola kuunika kwawo kuwalirawalira. (Mateyu 5:16) Inde, ndife otsimikiza mtima kwambiri kuposa kale kuti tidzayendabe limodzi ndi Israyeli wa Mulungu ndi kunyadira mwayi wamtengo wapatali wowalitsa kuunika kwa Yehova.

Kodi Mungafotokoze?

• Pa nkhani ya chitsutso, kodi tili ndi chikhulupiriro chotani?

• Kodi ana a Ziyoni ‘ayamwa mkaka wa amitundu’ motani?

• Kodi Yehova ‘wabweretsa’ motani ‘mkuwa m’malo mwa mtengo’?

• Kodi ndi makhalidwe aŵiri ati amene awafotokoza pa Yesaya 60:17, 21?

• Kodi “wochepa” wasanduka bwanji “mtundu wamphamvu”?

[Mafunso]

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 18]

ULOSI WA YESAYA​—Muuni wa Anthu Onse

Mfundo zambiri zimene takambirana m’nkhani zimenezi anazifotokoza m’nkhani imene anakamba pa Msonkhano Wachigawo wa 2001/02 wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.” Pamapeto pa nkhaniyo, m’madera ambiri wokamba nkhaniyo anatulutsa buku latsopano lakuti Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse, Gawo 2. M’chaka cha 2000, buku lakuti Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse, Gawo 1 linatuluka. Tsopano pamene buku latsopanoli latuluka, munthu angathe kupeza mmene pafupifupi vesi lililonse la buku la Yesaya alifotokozera mwamakono. Magawo aŵiri ameneŵa ndi othandiza kwambiri kuti timve mozama ndi kuyamikira buku la ulosi wolimbitsa chikhulupiriro wa Yesaya.

[Zithunzi patsamba 15]

‘Yehova amakometsera anthu ake ndi chipulumutso’ pamene akukumana ndi chitsutso

[Zithunzi patsamba 16]

Anthu a Mulungu amagwiritsa ntchito zinthu zaphindu za amitundu popititsa patsogolo kulambira koyera

[Chithunzi patsamba 17]

Yehova wadalitsa anthu ake ndi kupita patsogolo kwa kayendetsedwe ka gulu ndiponso mtendere