Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amakometsera Anthu Ake ndi Kuunika

Yehova Amakometsera Anthu Ake ndi Kuunika

Yehova Amakometsera Anthu Ake ndi Kuunika

“Nyamuka, [mkazi iwe, NW] wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.”​—YESAYA 60:1.

1, 2. (a) Kodi anthu akutidwa ndi chiyani? (b) Kodi ndani akuchititsa mdima umene anthu alimo?

“TIKANAKONDA anthu akanakhala ndi makhalidwe abwino ngati Yesaya kapena Paulo Woyera!” Uku kunali kudandaula kwa Pulezidenti Harry Truman wa ku United States kalelo m’ma 1940. N’chifukwa chiyani analankhula mawu amenewo? Chifukwa chakuti panthaŵiyo, iye anaona kuti dziko linafunikira atsogoleri a makhalidwe abwino kwambiri. Anthu anali atangochoka kumene m’nyengo yamdima wandiweyani kuposa ina iliyonse m’zaka za m’ma 1900, nyengo ya nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse. Ngakhale kuti nkhondoyo inali itatha, dziko silinali pamtendere ayi. Mdima unapitirizabe. Inde, dzikoli likadali mumdima ngakhale kuti patha zaka 57 kuchokera pamene nkhondoyo inatha. Pulezidenti Truman akanakhala kuti ali moyo lerolino, mosakayika akanaonabe kuti tikufunika atsogoleri a makhalidwe abwino monga Yesaya kapena mtumwi Paulo.

2 Sitikudziŵa ngati Pulezidenti Truman anali kudziŵa kapena ayi kuti mtumwi Paulo ananenapo za mdima umene ukuvutitsa anthu ndipo anachenjeza za mdima umenewu m’zimene iye analemba. Mwachitsanzo, iye anachenjeza okhulupirira anzake kuti: ‘Kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a choipa m’zakumwamba.’ (Aefeso 6:12) Paulo ndi mawu ameneŵa anasonyeza kuti ankadziŵa za mdima wauzimu womwe wakuta dziko lonse ndiponso kuti ziwanda zamphamvu zomwe anazitchula kuti “akuchita zolimbika a dziko lapansi” n’zimene zimauchititsa. Popeza mizimu yoipa ndi imene yachititsa mdima umene uli m’dzikoli, kodi anthu angatani kuti auchotse?

3. Ngakhale kuti anthu ali mumdima, kodi Yesaya analosera chiyani chimene chidzachitike kwa anthu okhulupirira?

3 Yesaya nayenso ananena za mdima umene ukuvutitsa anthu. (Yesaya 8:22; 59:9) Komabe, iye mouziridwa analosera za m’nthaŵi yathu ino kuti ngakhale mdima uli chonchi, Yehova adzawalitsa maganizo a anthu amene amakonda kuunika. Inde, ngakhale kuti Paulo ndi Yesaya sali nafe lerolino, tili ndi zimene analemba kuti zititsogolere. Pofuna kuona mmene anthu okonda Yehova amapindulira ndi zimenezi, tiyeni tikambirane mawu aulosi a Yesaya amene ali m’chaputala 60 cha buku lake.

Mkazi Waulosi Awala

4, 5. (a) Kodi Yehova akulamula mkazi kuchita chiyani, ndipo akum’lonjeza chiyani? (b) Kodi ndi uthenga wosangalatsa uti umene uli mu Yesaya chaputala 60?

4 Mawu oyamba a Yesaya chaputala 60 akumuuza mkazi amene akumvetsa chisoni kwambiri. Iye wagona pansi mumdima. Mwadzidzidzi, pamdimapo pakuwala, ndipo Yehova akuitana kuti: “Nyamuka, [mkazi iwe, NW] wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.” (Yesaya 60:1) Nthaŵi yakwana yoti mkaziyu aimirire ndi kusonyeza kuunika kwa Mulungu, ulemerero Wake. Chifukwa chiyani? Yankho tikulipeza m’vesi lotsatira limene likuti: “Taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.” (Yesaya 60:2) Mkaziyu akumutsimikizira kuti akamvera lamulo la Yehova, zotsatira zake zidzakhala zabwino. Yehova akuti: “Amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.”​—Yesaya 60:3.

5 Mawu osangalatsa a m’mavesi atatu ameneŵa ndiwo mawu otsegulira Yesaya chaputala 60 komanso akutipatsa chithunzithunzi cha zimene zili m’chaputala chonsecho. Akulosera zimene zidzachitikire mkazi waulosi ndiponso akufotokoza mmene tingakhalire mu kuunika kwa Yehova ngakhale kuti anthu ali mumdima. Koma kodi mawu ophiphiritsa amene ali m’mavesi atatu ameneŵa akutanthauzanji?

6. Kodi mkazi amene amutchula pa Yesaya chaputala 60 ndani, ndipo ndani akuimira mkazi ameneyo padziko lapansi?

6 Mkazi amene amutchula pa Yesaya 60:1-3 ndi Ziyoni, gulu la kumwamba la Yehova la zolengedwa zauzimu. Lerolino Ziyoni akuimiridwa pa dziko lapansi ndi otsalira a “Israyeli wa Mulungu,” gulu lapadziko lonse la Akristu odzozedwa ndi mzimu, omwe ali ndi chiyembekezo chokalamulira ndi Kristu kumwamba. (Agalatiya 6:16) Mtundu wauzimu umenewu uli ndi anthu 144,000, ndipo kukwaniritsidwa kwamakono kwa Yesaya chaputala 60 kwagona pa amene ali ndi moyo padziko lapansi mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1; Chivumbulutso 14:1) Ulosiwu ukunenanso zambiri za anzawo a Akristu odzozedwawa, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.”​—Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16.

7. Kodi Ziyoni anali bwanji mu 1918, ndipo zimenezi anazilosera motani?

7 Kodi panali nthaŵi ina pamene “Israyeli wa Mulungu” anagona mu mdima, monga anasonyezera mkazi waulosiyo? Inde, zimenezi zinachita zaka zoposa 80 zapitazo. Panthaŵi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, Akristu odzozedwa anavutika kwambiri kuti ntchito yolalikira ipitirize. Koma mu 1918, chaka chomaliza cha nkhondoyo, ntchito yolalikira yolinganizika bwino inatsala pang’ono kuimiratu. Joseph F. Rutherford amene anali kuyang’anira ntchito yolalikira padziko lonse ndi Akristu ena otsogolera anawalamula kukhala m’ndende kwa zaka zambiri pa milandu yabodza. M’buku la Chivumbulutso, Akristu odzozedwa omwe anali pa dziko lapansi panthaŵiyo anawafotokoza mwaulosi kuti anali mitembo yomwe inali gone ‘pa khwalala la mudzi waukulu, umene utchedwa mwauzimu, Sodoma ndi Aigupto.’ (Chivumbulutso 11:8) Imeneyo inalidi nthaŵi yamdima kwa Ziyoni, woimiridwa ndi ana ake odzozedwa padziko lapansi!

8. Kodi zinthu zinasintha kwambiri motani mu 1919, ndipo n’chiyani chinachitika chifukwa cha kusinthaku?

8 Komabe, zinthu zinasintha kwambiri m’chaka cha 1919. Yehova anawalitsa kuunika pa Ziyoni. Opulumuka a Israyeli wa Mulungu anadzuka kuti awalitse kuunika kwa Mulungu, kuyambanso kulengeza uthenga wabwino mopanda mantha. (Mateyu 5:14-16) Chifukwa chakuti Akristu ameneŵa anakhalanso achangu, anakokera ena ku kuunika kwa Yehova. Oyamba mwa anthu atsopanoŵa anali odzozedwa, omwe analoŵa m’gulu la Israyeli wa Mulungu. Pa Yesaya 60:3 akuwatcha mafumu chifukwa chakuti adzalamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 20:6) Kenako, khamu lalikulu la nkhosa zina anayamba kulibweretsa m’kuunika kwa Yehova. Ameneŵa ndiwo “amitundu” amene awatchula mu ulosiwu.

Ana a Mkaziyo Abwera Kunyumba!

9, 10. (a) Kodi ndi zinthu ziti zosangalatsa zimene mkaziyo anaona, ndipo zimenezi zikuimira chiyani? (b) Kodi Ziyoni angakondwere chifukwa chiyani?

9 Tsopano Yehova akuyamba kufotokoza mwatsatanetsatane zimene zili pa Yesaya 60:1-3. Akulamula mkaziyu kuchita chinthu chinanso. Tamverani zimene akumuuza. Akuti: “Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona.” Mkaziyu akumvera, ndipo akuonatu zosangalatsa kwambiri! Ana ake akubwera kunyumba. Lembali likupitiriza kuti: “Iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.” (Yesaya 60:4) Kulengeza Ufumu padziko lonse kumene kunayamba mu 1919 kunabweretsa anthu atsopano zikwizikwi kuti atumikire Yehova. Ameneŵanso anakhala ‘ana aamuna’ ndi ‘ana aakazi’ a Ziyoni, odzozedwa a m’gulu la Israyeli wa Mulungu. Motero Yehova anakometsera Ziyoni pamene anabweretsa omalizira a gulu la 144,000 ku kuunika.

10 Kodi mungaone m’maganizo mwanu mmene Ziyoni akukondwera pokhala limodzi ndi ana ake? Yehova akupatsa Ziyoni zifukwa zina zokondwerera. Timaŵerenga kuti: “Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.” (Yesaya 60:5) Mogwirizana ndi mawu aulosi amenewo, kuyambira m’ma 1930, Akristu miyandamiyanda oyembekeza kudzakhala padziko lapansi kosatha akhamukira ku Ziyoni. Atuluka mu “nyanja” ya anthu opatuka kwa Mulungu ndipo akuimira chuma cha amitundu. Iwo ndiwo “zofunika za amitundu.” (Hagai 2:7; Yesaya 57:20) Onaninso kuti ‘zofunikazi’ sizikutumikira Yehova aliyense m’njira yakeyake. M’malo mwake, iwo akuwonjezera kukometsa Ziyoni mwa kudzalambira pamodzi ndi abale awo odzozedwa, ndipo onse akukhala “gulu limodzi, mbusa mmodzi.”​—Yohane 10:16.

Amalonda ndi Abusa Abwera ku Ziyoni

11, 12. Fotokozani za khamu la anthu limene likuoneka likupita ku Ziyoni.

11 Kusonkhanitsa kumene analoserako kwachititsa anthu otamanda Yehova kuchuluka kwambiri. Zimenezi anazilosera m’mawu otsatira aulosiwu. Tayerekezani kuti mwaima paphiri la Ziyoni ndi mkazi waulosiyu. Ndiyeno ponyani maso kum’maŵa, kodi mukuona chiyani? “Gulu la ngamila lidzakukuta, ngamila zazing’ono za Midyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Seba adzabwera nazo golidi ndi zonunkhira; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.” (Yesaya 60:6) Makamu a amalonda akutsogolera gulu lawo la ngamila m’njira zopita ku Yerusalemu. Ngamila zangokhala ngati madzi omwe asefukira dziko lonselo! Amalondawo ali ndi mphatso za mtengo wapatali, “golidi ndi zonunkhira.” Amalonda onseŵa akubwera ku kuunika kwa Mulungu n’cholinga chodzamutamanda pamaso pa anthu, ‘kulalikira matamando a Yehova.’

12 Si amalonda okha amene ali paulendo. Abusanso akukhamukira ku Ziyoni. Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Zoŵeta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebaioti zidzakutumikira.” (Yesaya 60:7a) Mitundu ya anthu oŵeta ziŵeto ikubwera ku mzinda wopatulika kukapereka zoŵeta zawo zabwino kwambiri kwa Yehova. Akudzipereka ngakhale iwo eni kutumikira Ziyoni! Kodi Yehova awalandira motani alendo ameneŵa? Mulungu akuyankha kuti: “Izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.” (Yesaya 60:7b) Yehova akulandira mwachisomo nsembe ndi utumiki wa alendo ameneŵa. Iwo akukometsera kachisi wake.

13, 14. Kodi n’chiyani chikuonekera kumadzulo?

13 Tsopano tembenukani ndi kumwaza maso anu chakumadzulo. Kodi mukuona chiyani? Chapatali apo, pakuoneka ngati mtambo woyera umene wafutukuka pamwamba pa nyanja. Yehova akufunsa funso limene lili m’maganizo mwanu, kuti: “Ndani aŵa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera awo?” (Yesaya 60:8) Yehova akuyankha funso lakelo kuti: “Zisumbu zidzandilandira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisi kutenga ana ako amuna kutali, golidi wawo ndi siliva wawo pamodzi nawo, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israyeli, popeza Iye wakukometsa iwe.”​—Yesaya 60:9.

14 Kodi mukutha kuziona zimenezi m’maganizo mwanu? Mtambo woyera uja wayandikira ndipo tsopano ukuoneka ngati madontho ambiri amene asonkhana pamodzi, kutali chakumadzulo. Ukuoneka ngati mbalame zimene zikuyenda pamwamba pa mafunde. Koma pamene akuyandikirabe, mukuona kuti ndi ngalawa, matanga ake atafunyululidwa bwino kuti azitenga mphepo. Pali ngalawa zambirimbiri zomwe zikupita ku Yerusalemu moti zangoti mbuu ngati gulu la nkhunda. Ngalawazi zanyamula okhulupirira omwe akuthamangira ku Yerusalemu kukalambira Yehova kuchokera ku madoko akutali.

Gulu la Yehova Likukula

15. (a) Kodi mawu a pa Yesaya 60:4-9 analosera kuti padzakhala kuwonjezeka kotani? (b) Kodi Akristu oona amasonyeza mzimu wotani?

15 Ndi chithunzi chaulosi choonekatu bwino kwambiri chomwe mavesi 4 mpaka 9 akuonetsa cha kufutukuka kwa padziko lonse kumene kwachitika kuyambira mu 1919! N’chifukwa chiyani Yehova anadalitsa Ziyoni kuti achuluke moteremu? Chifukwa chakuti kuyambira mu 1919, Israyeli wa Mulungu wawalitsa kuunika kwa Yehova momvera. Komano, kodi munaona kuti vesi 7 inati anthu amene akungofika kumenewo ‘akufika pa guwa la nsembe’ la Mulungu? Pa guwa la nsembe m’pamene amaperekerapo nsembe, ndipo zimenezi zikutikumbutsa kuti kutumikira Yehova kumafuna kupereka nsembe. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndikupemphani inu . . . kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.” (Aroma 12:1) Mogwirizana ndi mawu a Paulo ameneŵa, Akristu oona samangopita kumisonkhano yachipembedzo kamodzi pa mlungu ayi. Amagwiritsa ntchito nthaŵi yawo, nyonga zawo, ndi chuma chawo kupititsa patsogolo kulambira koyera. Kodi kukhala ndi olambira odzipereka oterowo sikukometsera nyumba ya Yehova? Ulosi wa Yesaya unanena kuti kumakometsadi. Ndiponso, tikutsimikiza kuti chifukwa cha kukometsera nyumba yake, Yehova amawaona olambira achangu amenewo kukhala okongola.

16. Kodi ndani anathandiza ntchito yomanga m’nthaŵi zakale, ndipo ndani achita zimenezo masiku ano?

16 Anthu atsopanowa akufuna kugwira ntchito. Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu awo adzakutumikira.” (Yesaya 60:10) Pokwaniritsa koyamba mawu ameneŵa m’nthaŵi imene Ayuda otsalira anabwerera kuchokera ku ukapolo ku Babulo, mafumu ndi anthu ena amitundu anathandizadi kumanganso kachisi ndi mzinda wa Yerusalemu. (Ezara 3:7; Nehemiya 3:26) Pokwaniritsa ulosi umenewu masiku ano, khamu lalikulu lathandiza otsalira odzozedwa kumanga kulambira koona. Athandiza kumanga mipingo yachikristu ndipo motero amalimbitsa “malinga” a gulu la Yehova longa mzinda. Amathandizanso ntchito yomanga yeniyeni, monga kumanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano, ndi nyumba za Beteli. M’njira zonsezi, amathandiza abale awo odzozedwa kusamalira zofunika za gulu la Yehova lomwe likukulirakulira!

17. Kodi njira ina imene Yehova amakometsera anthu ake ndi iti?

17 Mawu omaliza a Yesaya 60:10 ndi olimbikitsa kwambiri. Yehova akuti: “M’kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakuchitira iwe chifundo.” Inde, kale mu 1918 ndi 1919, Yehova analangadi anthu ake. Koma limenelo ndi kale. Tsopano ino ndi nthaŵi yoti Yehova achitire chifundo atumiki ake odzozedwa ndi anzawo a nkhosa zina. Umboni woti zimenezi n’zoona ndiwakuti iye wawachulukitsa modabwitsa, motero tingati ‘wawakometsera.’

18, 19. (a) Kodi Yehova akulonjeza chiyani za anthu atsopano amene akubwera m’gulu lake? (b) Kodi mavesi otsala a Yesaya chaputala 60 adzatiuza chiyani?

18 Chaka chilichonse, “alendo” ena atsopano zikwi mazana ambiri amagwirizana ndi gulu la Yehova, ndipo khomo ndi lotsegukabe kwa enanso ambiri. Yehova akuuza Ziyoni kuti: “Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere nacho kwa iwe chuma cha amitundu, ndi mafumu awo otsogozedwa nawo pamodzi.” (Yesaya 60:11) Adani amayesa kutseka ‘zipatazo,’ koma tikudziŵa kuti sangathe kutero. Yehova wanena kuti zipata zikhalabe zotsegula m’njira zosiyanasiyana. Anthu apitirizabe kuwonjezeka.

19 Palinso njira zina zimene Yehova wadalitsira anthu ake, kuwakometsera m’masiku otsiriza ano. Mavesi otsala a Yesaya chaputala 60 akuvumbula mwaulosi njira zimenezo.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi “mkazi” wa Mulungu ndani, ndipo akumuimira ndani padziko lapansi?

• Kodi ndi liti pamene ana a Ziyoni anagona, ndipo ndi liti pamene ‘anaimirira,’ nanga anaimirira motani?

• Kodi Yehova pogwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa osiyanasiyana analosera motani kuwonjezeka kwa olalikira Ufumu lerolino?

• Kodi Yehova wawalitsa kuunika kwake pa anthu ake m’njira zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

“Mkazi” wa Yehova akumulamula kuimirira

[Chithunzi patsamba 12]

Gulu la ngalawa likuoneka ngati nkhunda chapatali