Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Bzalani Chilungamo, Kololani Kukoma Mtima kwa Mulungu

Bzalani Chilungamo, Kololani Kukoma Mtima kwa Mulungu

Bzalani Chilungamo, Kololani Kukoma Mtima kwa Mulungu

“WOPEREKERA mlendo chikole adzaphwetekwapo; koma wakuda chikole [“kugwirana chanza,” NW] akhala ndi mtendere.” (Miyambo 11:15) Mwambi wosapita m’mbali umenewu ukulimbikitsa kuchita zinthu mosamala. Kukongoza ndalama tambwali n’kuitana mavuto. Peŵani kugwirana chanza​—komwe kunali ngati kusainirana pangano mu Israyeli wakale​—kuti musagwe m’mavuto a ndalama.

Mwachionekere, mfundo yaikulu pamenepa n’njakuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Mneneri Hoseya ananena kuti: “Mudzibzalire m’chilungamo mukolole monga mwa chifundo.” (Hoseya 10:12) Inde, bzalani chilungamo mwa kuchita zinthu motsatira njira za Mulungu ndipo mudzakolola kukoma mtima kwake. Pogwiritsa ntchito mfundoyi mobwerezabwereza, Mfumu Solomo ya Israyeli ikulimbikitsa kuchita zinthu zabwino, kulankhula zabwino, ndiponso khalidwe labwino. Kupenda mosamalitsa mawu ake anzeru ameneŵa kutilimbikitsa kubzala mbewu m’chilungamo.​—Miyambo 11:15-31.

Bzalani ‘Kudekha,’ Kololani “Ulemu”

Mfumu yanzeru ikuti: “Mkazi wodekha agwiritsa ulemu; aukali [“ankhanza,” NW] nagwiritsa chuma.” (Miyambo 11:16) Vesili likusiyanitsa ulemu wokhalitsa umene “mkazi wodekha” angapeze ndi chuma chosakhalitsa chomwe waukali amapeza.

Kodi munthu angatani kuti akhale wodekha ndi kulandira ulemu? Solomo analangiza kuti: ‘Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo khosi lako lidzatengapo chisomo.’ (Miyambo 3:21, 22) Ndipo wamasalmo anatchula za ‘kutsanulira chisomo pa milomo ya mfumu.’ (Salmo 45:1, 2) Inde, nzeru yeniyeni, luso la kulingalira, ndiponso kugwiritsa ntchito bwino lilime kumachititsa munthu kukhala wofunika ndiponso wachisomo. Zimenezi zimakhala choncho kwa mkazi wanzeru. Abigayeli, mkazi wa Nabala wopusayo, ndi mmodzi mwa akazi anzeru oterowo. Iye anali “wanzeru yabwino, ndi wankhope yokongola,” ndipo Mfumu Davide inamutamanda chifukwa cha “kuchenjera” kwake.​—1 Samueli 25:3, 33.

Mkazi wodzipereka kwa Mulungu amene ali wodekha adzapatsidwa ulemu. Anthu adzasimba mbiri yake yabwino. Ngati ndi wokwatiwa, mwamuna wake adzamulemekeza. Ndipotu banja lake lonse lidzalemekezeka chifukwa cha iye. Ndipo ulemu wake si wa kanthaŵi chabe ayi. “Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golidi.” (Miyambo 22:1) Mbiri yabwino imene mkazi wotereyu amakhala nayo kwa Mulungu imakhala ndi phindu lokhalitsa.

Zimenezi n’zosiyana ndi munthu wankhanza, ‘wokakala mtima.’ (Miyambo 11:16, New International Version) Wankhanza ali m’gulu la anthu oipa ndiponso adani a olambira a Yehova. (Yobu 6:23; 27:13) Munthu wotereyu ‘sadziikira Mulungu pamaso pake.’ (Salmo 54:3) Mwa kupondereza ndiponso kudyera masuku pamutu anthu osalakwa, iye ‘angakundike ndalama ngati fumbi.’ (Yobu 27:16) Komabe, nthaŵi ina, angagone osadzuka, ndipo tsiku lina lililonse limene atsegula maso ake lingakhale tsiku lake lomaliza. (Yobu 27:19) Chuma chake chonse ndiponso zonse anazichita zidzakhala zopanda phindu.​—Luka 12:16-21.

Ndi phunzirotu lofunika kwambiri lomwe lili pa Miyambo 11:16. Mwa kutitchulira mosapita m’mbali zimene munthu wodekha ndi wankhanza amakolola, mfumu ya Israyeli ikutilimbikitsa kubzala chilungamo.

Kukoma Mtima’ Kumapindulitsa

Solomo akuphunzitsanso phunziro lina lokhudza ubale wa anthu, iye akuti: “Wachifundo [“wokoma mtima,” NW] achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.” (Miyambo 11:17) Katswiri wina wa maphunziro anati: “Mfundo yaikulu ya mwambiwu n’njakuti, zomwe munthu amachitira anthu ena kaya zabwino kapena zoipa, zimakhala ndi zotsatira zimene munthuyo sakufuna kapena zosayembekezeka.” Talingalirani chitsanzo cha mtsikana wina dzina lake Lisa. * Ngakhale kuti ali ndi zolinga zabwino, iye nthaŵi zonse amachedwa akapangana ndi anzake. Kwa iye, sichachilendo kuchedwa ndi phindu 30 kapena kuposerapo kufika pamalo omwe wapangana ndi olengeza Ufumu anzake kuti akalalikire. Lisa sakuchita zinthu zomukomera. Kodi iye angaimbe mlandu anzakewo ngati iwo atopa nako kuwononga kwake nthaŵi yofunikayo ndiponso kusiya kupangana kuchita naye zinthu?

Munthu wongofuna zangwiro​—amene amadziikira miyezo yapamwamba mopambanitsa yochitira zinthu​—amadzichitiranso nkhanza yekha. Iye nthaŵi zonse amalimbana ndi kukwaniritsa zolinga zake zosathekazo ndipo amakhala woti angadzitopetse ndiponso kukhumudwa. Koma timadzichitira zokoma ngati tiika zolinga zabwino zomwe tingazikwanitse. Mwina mutu wathu sugwira zinthu msanga poyerekeza ndi ena. N’kuthekanso kuti mwina matenda kapena ukalamba zikutilepheretsa kuchita zinthu zina. Tisakhumudwe ndi mmene tikupitira patsogolo mwauzimu, koma tipitirize nthaŵi zonse kuchita mwanzeru ndi zofooka zathu. Tidzakhala achimwemwe ngati tichita changu malinga ndi mphamvu zathu​—2 Timoteo 2:15; Afilipi 4:5.

Popitiriza kulongosola mwatsatanetsatane mmene wolungama amadzipindulitsira ndiponso mmene wankhanza amadzivulazira, mfumu yanzeru ikuti: “Woipa alandira malipiro onyenga; koma wofesa chilungamo aonadi mphoto. Wolimbikira chilungamo alandira moyo; koma wolondola zoipa adzipha yekha. Okhota mtima anyansa Yehova; koma angwiro m’njira zawo am’sekeretsa. Zoonadi [“Ngakhale pakhale kugwirana chanza,” NW], wochimwa sadzapulumuka chilango; koma mbewu ya olungama idzalanditsidwa.”​Miyambo 11:18-21.

M’njira zosiyanasiyana mavesi ameneŵa akutsindika mfundo yaikulu yakuti: Bzalani chilungamo kuti mukolole mphoto yake. Munthu woipa angayambe chinyengo kapena kutchova njuga kuti apeze zinthu mosavutikira. Popeza malipiro oterowo ndi onyenga, iye angadzagwire mwala. Wogwira ntchito mokhulupirika amapeza malipiro enieni chifukwa amakhala wotetezeka. Pokhala woyanjidwa ndi Mulungu, wolungama adzapeza moyo. Nanga bwanji woipa? “Ngakhale pakhale kugwirana chanza” pokonza chinyengo, wochimwa sadzapulumuka chilango. (Miyambo 2:21, 22) Langizotu labwino kwambiri lakuti tichite chilungamo!

Kukongola Kwenikweni kwa Munthu Wanzeru

Solomo akupitiriza kuti: “Monga chipini chagolidi m’mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.” (Miyambo 11:22) Kuvala chipini pamphuno kunali njira yodzikongoletsera yotchuka kwambiri m’nthaŵi za m’Baibulo. Chipini chagolidi chomwe anaika mbali imodzi ya mphuno kapena pakati pa mphuno chinali kuoneka bwino kwambiri pankhope ya mkazi. Zinalidi zosayenera kuti mphete yokongola ngati imeneyo ikhale pamphuno pa nkhumba. N’chimodzimodzinso ndi munthu wokongola maonekedwe koma “wosasinkhasinkha bwino.” Kukongola sikumukhala munthu woteroyo, kaya ndi mkazi kapena mwamuna. Sikusangalatsanso.

N’zoona kuti mwachibadwa timaganiza za mmene timaonekera. Koma kodi n’kusamaliranji kwambiri mmene thupi lathu lilili? Sitingathe kusintha zinthu zambiri pathupi lathu. Ndipotu kaonekedwe ka thupi sindiko nkhani yaikulu ayi. Kodi si zoona kuti anthu ambiri amene timawakonda ndiponso kuwasirira ndi osakongola kwenikweni? Kukongola kwa thupi sindiko kumabweretsa chimwemwe ayi. Chofunika kwambiri ndicho kukongola kwa m’kati kwa makhalidwe osatha aumulungu. Chotero, tikhaletu anzeru ndiponso tikulitse makhalidwe ngati amenewo.

“Mtima wa Mataya Udzalemera”

Mfumu Solomo ikuti: “Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha; koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo.” Posonyeza mmene zimenezi zilili zoona, mfumuyi ikupitiriza kuti: “Alipo wogaŵira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka.”​Miyambo 11:23, 24.

Pamene tikugaŵa mwakhama​—kuphunzitsa ena​—kuti adziŵe Mawu a Mulungu, timawonjezera kumvetsa kwathu “kupingasa, ndi utali, ndi kukwera” kwa Mawuwo. (Aefeso 3:18) Koma amene amangokhala osauza ena zomwe akudziŵa, ali pangozi yoti atha kuiŵala zomwe akudziŵazo. Inde, “iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.”​—2 Akorinto 9:6.

Mfumuyi ikupitiriza kuti: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.” (Miyambo 11:25) Tikamagwiritsa ntchito nthaŵi ndi chuma chathu moolowa manja kupititsa patsogolo kulambira koona, Yehova amakondwera nafe kwambiri. (Ahebri 13:15, 16) Iye ‘adzatitsegulira mazenera a kumwamba, ndi kutitsanulira mdalitso wakuti tidzasoŵa malo akuulandirira.’ (Malaki 3:10) Tangoonani ulemerero wauzimu wa atumiki a Mulungu lerolino!

Solomo akuperekanso chitsanzo china cha kusiyana kwa zolinga za wolungama ndi za woipa. Iye akuti: “Womana tirigu anthu am’temberera; koma madalitso adzakhala pamutu pa wogulitsa.” (Miyambo 11:26) Kugula katundu wambiri mitengo ikadali yotsika, n’kudzamugulitsa m’tsogolo pamene katunduyo akusoŵa ndipo mitengo itakwera kungakhale kopindulitsa. Ngakhale kuti munthu angapindule ndithu mwa kuchepetsa katundu ndi kusunga wina, nthaŵi zambiri anthu amadana naye munthu woteroyo chifukwa cha dyera lake. Koma anthu amakonda munthu amene safuna kudyera masuku pamutu anzake nthaŵi ya mavuto kuti apeze phindu lalikulu.

Pofuna kutilimbikitsa kukhala ndi chilakolako cha zinthu zabwino, kapena kuti zolungama, mfumu ya Israyeli ikuti: “Wopwaira ubwino afunitsa chikondwerero; koma zoipa zidzam’fikira wozilondola. Wokhulupirira chuma chake adzagwa; koma olungama adzaphuka ngati tsamba.”​Miyambo 11:27, 28.

Wolungama Akola Mitima

Posonyeza mmene kuchita zinthu zopusa kumabweretsera mavuto, Solomo akuti: “Munthu wovuta nyumba yake adzangolandira mphepo.” (Miyambo 11:29a, Malembo Oyera) Akani ‘anasautsidwa’ chifukwa cha tchimo lake ndipo iye pamodzi ndi a m’banja lake anawaponya miyala mpaka kuwapha. (Yoswa, chaputala 7) Masiku ano, mutu wa banja lachikristu ndiponso ena m’banjalo angachite tchimo lomwe lingawachotsetse mumpingo wachikristu. Ngati mwamuna alephera kutsatira malamulo a Mulungu ndi kulekerera tchimo lalikulu m’banja lake, amabweretsa masautso pabanja lakelo. Iye ndipo mwinanso ena m’banja lake amachotsedwa mumpingo wachikristu chifukwa chosalapa machimo awo. (1 Akorinto 5:11-13) Kodi zikatero adzapeza chiyani? Adzangolandira mphepo​—chinthu chopanda phindu.

Vesili likupitiriza kuti: “Wopusa adzatumikira wanzeru.” (Miyambo 11:29b) Popeza wopusa alibe nzeru yeniyeni, iye sangapatsidwe udindo waukulu. Ndiponso kusadziŵa kwake kusamala zinthu zake kungam’chititse kudalira munthu wina. Motero munthu wopusa ngati ameneyu angakhaledi ‘mtumiki wa munthu wanzeru.’ Choncho, m’pofunika kukhala ndi luso la kulingalira ndiponso nzeru yeniyeni pa zochita zathu zonse.

Mfumu yanzeru ikutitsimikizira kuti: “Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo; ndipo wokola mtima ali wanzeru.” (Miyambo 11:30) Kodi zimenezi zimachitika bwanji? Eya, zolankhula ndi zochita za munthu wolungama zimalimbikitsa ena mwauzimu. Iwo amalimbikitsidwa kutumikira Yehova ndipo m’kupita kwa nthaŵi angalandire moyo umene umatheka chifukwa cha Mulungu.

‘Wochimwa Adzalandira Mphoto Yoposa’

Miyambi imene taitchula kale ikutilimbikitsatu kwambiri kubzala chilungamo. Pogwiritsa ntchito m’njira inanso mfundo yakuti “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta,” Solomo akuti: “Taonani, wolungama adzalandira mphoto kunja kuno; koposa kotani woipa ndi wochimwa?”​Miyambo 11:31.

Ngakhale kuti wolungama amayesetsa kuchita zabwino, iye nthaŵi zina amalakwa. (Mlaliki 7:20) Ndipo akalakwa amalandira chilango monga “mphoto” ya kulakwa kwakeko. Ngati wolungama amalandira chilango, nanga bwanji woipa amene amasankha dala njira zoipa ndipo safuna kusintha kutsatsa njira yachilungamo? Kodi woteroyo sayenera “mphoto” yoposerapo​—chilango chachikulu? Mtumwi Petro analemba kuti: “Ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?” (1 Petro 4:18) Choncho, tiyeni titsimikize mtima nthaŵi zonse kubzala mbewu zathu m’chilungamo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Dzinali si lake.

[Chithunzi patsamba 28]

Abigayeli anapatsidwa “ulemu” chifukwa cha ‘kudekha’

[Zithunzi patsamba 30]

‘Woipa alandira malipiro onyenga; koma wolungama aonadi mphoto’

[Chithunzi patsamba 31]

‘Fesani moolowa manja, tutani moolowa manja’