Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Helo N’chiyani Kwenikweni?

Kodi Helo N’chiyani Kwenikweni?

Kodi Helo N’chiyani Kwenikweni?

KAYA mumaganiza za chiyani mukamva mawu akuti “helo,” mfundo n’njakuti, ambiri amaganiza kuti helo ndi malo olangilako anthu ochimwa. Pa za uchimo ndi zotsatira zake, Baibulo limati: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Malemba amanenanso kuti: “Mphoto yake ya uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Popeza chilango cha uchimo ndi imfa, kuti tipeze tanthauzo lenileni la helo funso lofunika kwambiri ndi lakuti: Kodi chimachitika kwa ife n’chiyani tikamwalira?

Kodi munthu akamwalira amakhalabe ndi moyo wamtundu wina? Kodi helo n’chiyani ndipo ndi anthu otani amene amapitako? Kodi amene ali kuhelo zinthu zidzawakhalira bwino m’tsogolo? Baibulo limayankha mafunso ameneŵa molondola ndiponso mogwira mtima.

Kodi Munthu Akamwalira Amakakhalanso ndi Moyo Kwinakwake?

Kodi m’thupi lathu muli mbali ina, kapena kuti mzimu, imene imapulumuka imfa? Talingalirani mmene munthu woyamba Adamu anakhalira wamoyo. Baibulo limati: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) Ngakhale kuti kupuma kunam’thandiza kukhala wamoyo, kuuzira “mpweya wa moyo” m’mphuno mwake kunatanthauza zambiri m’malo mongouzira chabe mpweya m’mapapu ake. Kunatanthauza kuti Mulungu anaika m’thupi lopanda moyo la Adamu mphamvu ya moyo​—“mpweya wa moyo,” womwe umagwira ntchito m’zamoyo zonse zomwe analenga padziko lapansi. (Genesis 6:17; 7:22) Baibulo limatcha mphamvu ya moyo imeneyi kuti “mzimu.” (Yakobo 2:26) Mzimu tingauyerekezere ndi mphamvu yamagetsi imene imayendetsa makina kapena kuchititsa kuti chipangizo chamagetsi chigwire ntchito yake. Mphamvu yamagetsi siitengera khalidwe la chipangizo chamagetsi chomwe imagwiritsa ntchito. N’chimodzimodzinso ndi mphamvu ya moyo. Siikhala ndi makhalidwe a zinthu zamoyo. Ilibe umunthu ndipo siitha kuganiza.

Kodi chimachitikira mzimu munthu akamwalira n’chiyani? Salmo 146:4 limati: “Mpweya [“mzimu,” NW] wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” Munthu akamwalira, mzimu wake sukhala ndi moyo kwinakwake ayi. ‘Umabwerera kwa Mulungu amene anaupereka.’ (Mlaliki 12:7) Izi zikutanthauza kuti chiyembekezo chakuti munthuyo adzakhalanso ndi moyo m’tsogolo chimadalira Mulungu yekha basi.

Nanga bwanji za anthu akufa? Yehova popereka chilango kwa Adamu anati: “Ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Kodi Adamu anali kuti Mulungu asanamupange ndi dothi ndi kum’patsa moyo? Iye kunalibe! Choncho, Adamu atamwalira, iye anasiya kukhalako. Pa Mlaliki 9:5, 10 pamalongosola bwino kwambiri za anthu akufa. Pamenepo timaŵerenga kuti: ‘Akufa sadziŵa kanthu bi . . . kulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.’ Chotero, Malemba amati munthu akafa ndiye kuti iye kulibe. Akufa sadziŵa kanthu, sakumva chilichonse, ndiponso saganiza.

Kodi Ndi Malo Ozunzirako Kwamuyaya Kapena Ndi Manda a Onse?

Popeza kuti akufa sadziŵa kanthu, helo sangakhale malo amoto ozunzirako oipa akamwalira. Nangano helo n’chiyani? Kupenda zomwe zinachitikira Yesu atamwalira kutithandiza kuyankha funso limeneli. Wolemba Baibulo Luka anasimba kuti: “[Yesu] sanasiyidwa m’Hade, [“m’helo,” King James Version] ndipo thupi lake silinaona chivunde.” * (Machitidwe 2:31) Kodi kuhelo kumene ngakhale Yesu anapitako kunali kuti? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndinapereka kwa inu . . . kuti Kristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo.” (1 Akorinto 15:3, 4) Yesu anali kuhelo, kumanda, koma sanasiyidwe kumeneko, chifukwa anaukitsidwa.

Talingaliraninso za Yobu munthu wolungama amene anavutika kwambiri. Iye pofuna kuthaŵa mavuto ake, anapempha kuti: “Mukadandibisa kumanda, [“kuhelo,” Douay Version] mukadandisunga m’seri, mpaka wapita mkwiyo wanu.” * (Yobu 14:13) N’kupandatu nzeru kuganiza kuti Yobu anafuna kupita ku malo amoto kuti akapeze chitetezo. Kwa Yobu, “helo” anali manda kumene sakanavutika ayi. Choncho, helo amene Baibulo limanena ndi manda komwe anthu onse abwino ndi oipa amapita.

Kodi Moto wa Helo N’chiwonongeko Chotheratu?

Kodi n’kutheka kuti mwina moto wa helo umatanthauza chiwonongeko chotheratu? Posiyanitsa moto ndi Hade, kapena kuti helo, Malemba amati: “Imfa ndi Hade zinaponyedwa m’nyanja yamoto.” “Nyanja” imene aitchula pano ndi yophiphiritsa chifukwa chakuti imfa ndi helo (Hade) zomwe aziponya m’nyanjayo sizingapse ndi moto weniweni. “Iyo [nyanja yamoto] ndiyo imfa yachiŵiri”​—imfa imene wakufayo sangayembekezere kudzakhalanso ndi moyo m’tsogolo.​—Chivumbulutso 20:14.

Tanthauzo la nyanja yamoto n’lofanana ndi la “gehena wamoto [“moto wa helo,” King James Version]” amene Yesu anatchula. (Mateyu 5:22; Marko 9:47, 48) Liwu lakuti Gehena limapezeka nthaŵi 12 m’Malemba Achigiriki Achikristu ndipo limatanthauza chigwa cha Hinomu chomwe chinali kunja kwa malinga a mzinda wa Yerusalemu. Yesu ali padziko lapansi, chigwa chimenechi anali kuchigwiritsa ntchito monga dzala lotayako zinyalala, komanso “mitembo ya anthu ambanda, ndiponso nyama zakufa ndi zinyalala zina zonse amazitaya komweko.” (Smith’s Dictionary of the Bible) Moto kumeneko sunali kuzima chifukwa ankaponyako miyala ya sulfure kuti izitentha zinyalalazo. Yesu anagwiritsa ntchito chigwa chimenecho monga chizindikiro choyenera cha chiwonongeko chotheratu.

Nyanja ya moto ndiponso Gehena zonse zimaimira chiwonongeko chotheratu. Imfa ndi Hade ‘akuziponya’ m’nyanja imeneyi kutanthauza kuti adzaziwononga kotheratu anthu akadzawamasula ku uchimo ndi chilango cha imfa. Ochimwa dala osalapa nawonso “cholandira chawo” chidzakhala nyanja imeneyi. (Chivumbulutso 21:8) Izi zikutanthauza kuti nawonso adzawonongedwa kotheratu. Koma anthu amene Mulungu akuwakumbukira amene ali m’helo, kapena kuti manda a onse, ali ndi tsogolo labwino.

Helo Akhala Wopanda Kanthu!

Pa Chivumbulutso 20:13 pamanena kuti: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali mmenemo.” Inde, helo amene Baibulo limanena adzakhala wopanda kanthu. Yesu analonjeza kuti: ‘Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu a [Yesu], nadzatuluka.’ (Yohane 5:28, 29) Ngakhale kuti panopa anthu miyandamiyanda amene anamwalira kulibeko, Yehova Mulungu akuwakumbukira ndipo adzawaukitsa, kapena kuti kuwapatsanso moyo, m’dziko lapansi lokonzedwanso la paradaiso.​—Luka 23:43; Machitidwe 24:15.

M’dziko latsopano la Mulungu, anthu oukitsidwa amene adzatsatire malamulo ake olungama sadzamwaliranso mpaka kalekale. (Yesaya 25:8) Yehova “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” Ndipotu ‘zoyambazo zidzakhala zitapita.’ (Chivumbulutso 21:4) Zimenezi ndi zinthu zabwinotu kwambiri zomwe zikudikira anthu amene ali m’helo, kapena kuti “m’manda achikumbukiro”! Ndithudi, chifukwa cha zinthu zabwino kwambiri ngati zimenezi, m’pofunikadi kudziŵa zambiri zokhudza Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu.​—Yohane 17:3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 M’Baibulo la King James Version liwu lachigiriki lakuti Hade analimasulira kuti “helo” m’malo khumi omwe liwuli limapezeka m’Malemba Achigiriki Achikristu. Pa Luka 16:19-31 pamatchula za malo a mazunzo, koma nkhani yonseyo ndi yophiphiritsa. Onani chaputala 88 cha buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 10 Liwu lachihebri lakuti Sheol limapezeka nthaŵi 65 m’Malemba Achihebri ndipo m’Baibulo la King James Version analimasulira kuti “helo,” “manda,” ndiponso “dzenje.”

[Chithunzi patsamba 5]

Yobu anapemphera kuti akapeze chitetezo m’helo

[Chithunzi patsamba 6]

Gehena wamoto ndi chizindikiro cha chiwonongeko chotheratu

[Chithunzi patsamba 7]

‘Amene ali m’manda achikumbukiro adzatuluka’