Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Onjezerani Kudzipereka kwa Mulungu pa Chipiriro Chanu

Onjezerani Kudzipereka kwa Mulungu pa Chipiriro Chanu

Onjezerani Kudzipereka kwa Mulungu pa Chipiriro Chanu

‘Muwonjezere pa chikhulupiriro chanu chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo [“kudzipereka kwa Mulungu,” NW].’​—2 PETRO 1:5-7.

1, 2. (a) Kodi mwana amafunika kukula kotani? (b) N’chifukwa chiyani kukula mwauzimu n’kofunika kwambiri?

MWANA amafunika kukula, koma osati msinkhu wokha. Amafunikanso kukula m’nzeru. M’kupita kwa nthaŵi, amasiya chibwana n’kukhala mwamuna kapena mkazi wamkulu ndithu. Mtumwi Paulo anafotokoza zimenezi pamene analemba kuti: “Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana., ndinaŵerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.”​—1 Akorinto 13:11.

2 Zimene Paulo ananenazi zikukhudza mfundo yofunika kwambiri pa kukula mwauzimu. Akristu afunika kukula kuchoka pa ukhanda wauzimu n’kukhala ‘akulu misinkhu m’chidziŵitso.’ (1 Akorinto 14:20) Ayenera kuvala zilimbe ndi kuyesetsa kupeza “muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.” Akatero, sadzakhala “makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso.”​—Aefeso 4:13, 14.

3, 4. (a) Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tikule msinkhu mwauzimu? (b) Kodi tiyenera kuonetsa makhalidwe ati okondweretsa Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani ali ofunika?

3 Kodi tingatani kuti tikhale akulu msinkhu mwauzimu? Pamene kusinkhuka kwa thupi kumangochitika mwachibadwa, kukula msinkhu mwauzimu kumafuna kuyesetsa zolimba. Kumayamba kaye ndi kudziŵa molondola Mawu a Mulungu ndi kutsatira zimene tikuphunzira. (Ahebri 5:14; 2 Petro 1:3) Ndiyeno, zimenezi zimatithandiza kuonetsa makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu. Mofanana ndi kusinkhuka kwa thupi ndi mbali zina pa kukula kwa munthu, makhalidwe osiyanasiyana okondweretsa Mulungu amakulira limodzi. Mtumwi Petro analemba kuti: “Mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muwonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo [“kudzipereka kwa Mulungu,”]; ndi pachipembedzo [“kudzipereka kwa Mulungu,”] chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.”​—2 Petro 1:5-7.

4 Khalidwe lililonse limene Petro walitchula apa n’lofunika, ndipo palibe limene tingalisiye. Iye akuwonjeza kuti: “Izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Kristu.” (2 Petro 1:8) Tiyeni tione kufunika kowonjezera kudzipereka kwa Mulungu pa chipiriro chathu.

Kufunika Kopirira

5. N’chifukwa chiyani tifunika kupirira?

5 Petro ndi Paulo akusonyeza kuti kudzipereka kwa Mulungu kumayendera limodzi ndi kupirira. (1 Timoteo 6:11) Kupirira sikungotanthauza kulimbika tikakumana ndi mavuto ndi kusasunthika ayi. Kumatanthauzanso kuleza mtima, kulimba mtima, ndi kutsimikiza mtima, osataya chiyembekezo tikakumana ndi mayesero, zopinga, zokopa, ndi chizunzo. Pokhala “opembedza [“odzipereka kwa Mulungu,” NW] m’moyo mwa Kristu Yesu,” timayembekeza kuzunzidwa. (2 Timoteo 3:12) Tiyenera kupirira ngati tikufuna kutsimikizira kuti timakondadi Yehova ndiponso kukhala ndi makhalidwe amene akufunika kuti tidzapulumuke. (Aroma 5:3-5; 2 Timoteo 4:7, 8; Yakobo 1:3, 4, 12) Ngati sitipirira, sitidzapeza moyo wosatha.​—Aroma 2:6, 7; Ahebri 10:36.

6. Kodi tingatani kuti tipirire mpaka mapeto?

6 Ngakhale kuti tinayamba bwino, chofunika kwambiri ndi kupirira. Yesu anati: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Inde, tiyenera kupirira mpaka mapeto, kaya adzakhala mapeto a moyo wathu uno kapena mapeto a dongosolo la zinthu loipa lino. Mulimonse mmene zikhalire, tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu. Komabe, popanda kuwonjezera kudzipereka kwa Mulungu pa chipiriro chathu, sitingasangalatse Yehova ndipo sitidzapeza moyo wosatha. Koma kodi kudzipereka kwa Mulungu n’kutani?

Tanthauzo la Kudzipereka kwa Mulungu

7. Kodi kudzipereka kwa Mulungu n’kutani, nanga kumatilimbikitsa kuchita chiyani?

7 Kudzipereka kwa Mulungu ndiko kulemekeza, kulambira, ndi kutumikira Yehova Mulungu ndipo munthu amachita zimenezi chifukwa cha kukhulupirika kwake ku ulamuliro wa Mulungu m’chilengedwe chonse. Kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu, tifunika kudziŵa Yehova ndi njira zake molondola. Tifunika kum’dziŵa bwino kwambiri Mulungu. Tikatero, tidzamukonda ndi mtima wonse ndipo zimenezo zidzaonekera mwa zochita zathu ndiponso mmene tikukhalira pa moyo wathu. Tiyenera kulakalaka kufanana ndi Yehova mmene tingathere, kutanthauza kutsanzira njira zake ndi kusonyeza makhalidwe ndi mtima wake. (Aefeso 5:1) Inde, kudzipereka kwa Mulungu kumatilimbikitsa kufuna kumukondweretsa pa chilichonse chimene tikuchita.​—1 Akorinto 10:31.

8. Kodi kudzipereka kwa Mulungu kumagwirizana bwanji ndi kulambira iye yekha?

8 Kuti tikhale odziperekadi kwa Mulungu, tiyenera kulambira Yehova yekha basi, osalola china chilichonse kutenga malo ake mumtima mwathu. Iye amafuna kuti tizimulambira iye yekhayo basi popeza ndiye Mlengi wathu, ndipo m’pake. (Deuteronomo 4:24; Yesaya 42:8) Komabe, Yehova satiumiriza kumulambira. Amafuna kuti tidzipereke mwaufulu. Kukonda kwathu Mulungu chifukwa chakuti tikum’dziŵa molondola n’kumene kumatilimbikitsa kuyeretsa miyoyo yathu ndi kudzipatulira kotheratu kwa iye ndiyeno kuchita zimenezo nthaŵi zonse.

Tilimbitse Ubwenzi Wathu ndi Mulungu

9, 10. Kodi tingachite chiyani kuti tikhale ndi ubwenzi wolimba ndi Mulungu ndi kuusunga?

9 Tikasonyeza kudzipatulira kwathu kwa Mulungu mwa kubatizidwa, tifunikabe kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye nthaŵi zonse. Ndiye, pofuna kuchita zimenezi ndi kutumikira Yehova mokhulupirika, timapitiriza kuphunzira Mawu ake ndi kuwasinkhasinkha. Tikamalola mzimu wa Mulungu kugwira ntchito m’maganizo ndi mumtima mwathu, chikondi chathu pa Yehova chimakula. Ubwenzi wathu ndi iye umakhalabe chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu. Yehova amakhala Bwenzi lathu lapamtima ndipo timafuna kumukondweretsa nthaŵi zonse. (1 Yohane 5:3) Chimwemwe chathu chimakula chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, ndipo timayamikira kuti amatilangiza mwachikondi ndiponso kutiwongolera pakafunika kutero.​—Deuteronomo 8:5.

10 Ubwenzi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova ungazilale ngati sitiyesetsa kuulimbitsa nthaŵi zonse. Zimenezo zitati zachitika, silingakhale vuto la Mulungu, chifukwa iye “sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Ndife okondwa kuti Yehova si wovuta kulankhula naye. (1 Yohane 5:14, 15) Inde, tiyenera kulimbikira kuti Yehova akhalebe bwenzi lathu lapamtima. Komabe, iye amatithandiza kuti timuyandikire mwa kutipatsa zonse zofunika kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu ndi kupitiriza kutero. (Yakobo 4:8) Kodi tingachite chiyani kuti tigwiritse ntchito mokwanira zinthu zabwino zonse zimene akutipatsa?

Tikhale Olimba Mwauzimu

11. Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere kudzipereka kwathu kwa Mulungu?

11 Kukonda kwathu Mulungu ndi mtima wonse kudzatilimbikitsa kuonetsa kukula kwake kwa kudzipereka kwathu. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Paulo ananena kuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Kuti tichite zimenezi tifunika kukhala ndi chizoloŵezi chabwino choŵerenga Baibulo nthaŵi zonse, kupita ku misonkhano, ndi kuchita nawo utumiki wakumunda. Tingakhalenso pafupi ndi Yehova mwa ‘kupemphera kosaleka.’ (1 Atesalonika 5:17) Zimenezi ndi njira zabwino zimene tingasonyezere kudzipereka kwathu kwa Mulungu. Ngati tinyalanyaza imodzi mwa njira zimenezi, tidzadwala mwauzimu ndipo sikudzakhala kovuta kuti Satana atikole.​—1 Petro 5:8.

12. Kodi tingathe bwanji kulimbana ndi mayesero?

12 Kukhalabe olimba mwauzimu ndi kukangalika kumatithandizanso kulimbana ndi mayesero ambiri amene timakumana nawo. Mayesero angachokere kwa anthu ena amene angatiyese kwadzaoneni. Kungakhale kovutirapo kupirira ngati a pabanja pathu, achibale, kapena anansi athu salabadira, akutitsutsa ndi kutizunza. Kuntchito kapena kusukulu kungakhale zinthu zina zovuta kuzindikira zimene zingatikope pang’onopang’ono kuswa mfundo za makhalidwe abwino achikristu. Kukhumudwa, matenda, ndi kuvutika maganizo zingatifooketse ndipo kungakhale kovuta kupirira chikhulupiriro chathu chikamayesedwa. Komabe, tingathe kulimbana ndi mayesero onse ngati tilimbikabe “m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo [“kudzipereka kwa Mulungu,” NW], akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:11, 12) Ndipo tingakhalebe ndi chimwemwe pochita zimenezo, tikukhulupirira kuti Mulungu atidalitsa.​—Miyambo 10:22.

13. Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tikhalebe odzipereka kwa Mulungu?

13 Ngakhale kuti Satana amalimbana ndi anthu odzipereka kwa Mulungu, sitifunika kuopa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.” (2 Petro 2:9) Kuti tipirire mayesero ndiponso kuti atilanditse, tiyenera ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, n’kukhala ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.’ (Tito 2:12) Ife monga Akristu, tiyenera kukhala tcheru kuti tisafooke chifukwa cha zilakolako ndi ntchito za thupi zimene zingasokoneze ndi kuwononga kudzipereka kwathu kwa Mulungu. Tiyeni tsopano tikambirane zina mwa zinthu zimenezi zomwe zingawononge kudzipereka kwathu.

Tisamale ndi Zinthu Zowononga Kudzipereka Kwathu kwa Mulungu

14. Kodi tizikumbukira chiyani tikakopeka ndi msampha wokondetsa chuma?

14 Kukondetsa chuma ndi msampha wa anthu ambiri. Tingadzinyenge tokha ndi “kuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa [kuthupi].” Motero, tingalimbe mtima n’kuganiza zodyera masuku pa mutu abale athu chifukwa chakuti amatikhulupirira. (1 Timoteo 6:5) Tingafike poganiza molakwika kuti palibe vuto ngati tiumiriza Mkristu wochita bwino kuti atibwereke ndalama zomwe n’zokayikitsa ngati tingathe kubweza. (Salmo 37:21) Komatu, kudzipereka kwa Mulungu n’kumene ‘kuli nalo lonjezano la ku moyo uno ndi la moyo ulinkudza,’ osati kukundika chuma. (1 Timoteo 4:8) Popeza “sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano,” tiyeni titsimikize mtima ‘kupembedza [“kudzipereka kwa Mulungu,” NW] pamodzi ndi kudekha’ ndiponso tikhutire ndi “zakudya ndi zofunda.”​—1 Timoteo 6:6-11.

15. Kodi tingatani ngati kukondetsa zosangalatsa kukufuna kulanda malo a kudzipereka kwathu kwa Mulungu?

15 Kukondetsa zosangalatsa kungalande malo a kudzipereka kwathu kwa Mulungu. Kodi n’kutheka kuti tifunika kusintha mwamsanga pa nkhani imeneyi? N’zoona kuti maseŵero olimbitsa thupi ndi zosangalatsa n’zothandiza. Komabe, phindu limene tingapeze pochita zimenezi n’lochepa zedi poyerekeza ndi moyo wosatha. (1 Yohane 2:25) Masiku ano, anthu ambiri ndi “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana,” ndipo tiyenera kupeŵa anthu oterowo. (2 Timoteo 3:4, 5) Amene amaika patsogolo kudzipereka kwa Mulungu ‘akudzikundikira okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.’​—1 Timoteo 6:19.

16. Kodi ndi zilakolako zoipa ziti zimene zimalepheretsa ena kutsatira malamulo olungama a Mulungu, nanga tingazigonjetse bwanji?

16 Mowa ndi mankhwala osokoneza bongo, chiwerewere, ndi zilakolako zoipa zingawononge kudzipereka kwathu kwa Mulungu. Tikagonja ku zimenezi zingatilepheretse kutsatira malamulo olungama a Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1) Ngakhalenso Paulo anali kulimbanabe ndi thupi la uchimo. (Aroma 7:21-25) M’pofunika kulimba kuti tithetse zilakolako zoipa. Chofunika ndi kuyesetsa kukhalabe ndi makhalidwe abwino. Paulo akutiuza kuti: “Fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.” (Akolose 3:5) Kuti tifetse ziwalo zathu pa zinthu zoipa zimenezi tifunika kutsimikiza mtima kuzipeŵa. Tidzatha kukana zilakolako zoipa ndi kuchita zolungama ndiponso kudzipereka kwa Mulungu m’dongosolo loipa lino ngati tipemphera ndi mtima wonse kuti Mulungu atithandize.

17. Kodi chilango tizichiona bwanji?

17 Zokhumudwitsa zingatifooketse kuti tisapirire ndipo zingawononge kudzipereka kwathu kwa Mulungu. Atumiki a Yehova ambiri akhumudwapo. (Numeri 11:11-15; Ezara 4:4; Yona 4:3) Ngati tiipidwa chifukwa chakuti ena atilakwira kapena atidzudzula mwamphamvu kapena kutilanga pamene ndife okhumudwa kale, zinthu zingatiipire kwambiri. Komabe, chidzudzulo ndi chilango ndi umboni wakuti Mulungu amatiganizira ndiponso amatikonda. (Ahebri 12:5-7, 10, 11) Chilango tiyenera kuchiona kukhala njira yotiphunzitsira m’chilungamo osati kutikhaulitsa. Ngati tili odzichepetsa, tidzayamikira ndi kulandira uphungu, pozindikira kuti “zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.” (Miyambo 6:23) Zimenezi zingatithandize kupita bwino patsogolo mwauzimu pofuna kukhala odzipereka kwa Mulungu.

18. Kodi tili ndi udindo wotani tikasiyana maganizo ndi ena?

18 Kusamvetsetsana ndi kulakwirana kungayese kudzipereka kwathu kwa Mulungu. Zimenezi zingayambitse nkhaŵa. Zingasonkhezerenso ena kuchita zopanda nzeru monga kudzipatula kwa abale ndi alongo awo auzimu. (Miyambo 18:1) Koma ndi bwino kukumbukira kuti kusunga mkwiyo kapena kungoipidwabe ndi anthu ena kungawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. (Levitiko 19:18) Ndipotu, “iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.” (1 Yohane 4:20) Yesu pa Ulaliki wake wa pa Phiri, anatsindika kuti m’pofunika kuchitapo kanthu mwamsanga kuti muthetse kusamvana. Anauza omvera ake kuti: “Ngati ulikupereka mtulo wako paguwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.” (Mateyu 5:23, 24) Kupepesa kungathandize kuziziritsa mtima wa mnzako amene wam’puta chifukwa chakuti walankhula kapena kuchita zinthu mosaganizira. Ubwenzi uja umene unafuna kusokonezeka ungakonzeke kukhalanso wabwinobwino tikapempha kuti atikhululukire ndi kuvomereza kuti tinalakwitsa. Yesu anaperekanso malangizo ena a mmene tingachitire tikasiyana maganizo. (Mateyu 18:15-17) Timasangalala ngati takhoza kuthetsa mavuto.​—Aroma 12:18; Aefeso 4:26, 27.

Tsanzirani Chitsanzo cha Yesu

19. N’chifukwa chiyani kutsanzira chitsanzo cha Yesu kuli kofunika kwambiri?

19 Inde, mayesero tikhala nawobe, komabe asatichewukitse pa liŵiro lathu lokapeza moyo wosatha. Kumbukirani kuti Yehova atha kutilanditsa tikamakumana ndi mayesero. Pamene ‘titaya cholemetsa chilichonse’ ndi ‘kuthamanga mwachipiriro makaniwo adatiikira,’ tiyeni ‘tipenyerere woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu.’ (Ahebri 12:1-3) Kupenda mosamala chitsanzo cha Yesu ndi kuyesetsa kumutsanzira m’kalankhulidwe kathu ndi zochita zathu kudzatithandiza kukhala odzipereka kwa Mulungu ndi kuchita zimenezi mokulirapo.

20. Kodi tingapindule chiyani ngati tipirira ndi kudzipereka kwa Mulungu?

20 Chipiriro ndi kudzipereka kwa Mulungu zimagwirizana kuthandiza kuti chipulumutso chathu chikhale chodalirika. Mwa kusonyeza makhalidwe abwino kwambiri ameneŵa, tingapitirize kuchita utumiki wathu wopatulika kwa Mulungu mokhulupirika. Ngakhale pamene tikuyesedwa, tidzasangalala poona chikondi cha Yehova ndi madalitso ake chifukwa chakuti tapirira ndiponso ndife odzipereka kwa Mulungu. (Yakobo 5:11) Ndiponso, Yesu akutilimbitsa mtima kuti: “Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiriro.”​—Luka 21:19.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani chipiriro chili chofunika?

• Kodi kudzipereka kwa Mulungu n’kutani, ndipo timakusonyeza bwanji?

• Kodi tingachite chiyani kuti tikhale ndi ubwenzi wolimba ndi Mulungu ndi kuusunga?

• Kodi zinthu zina zimene zingasokoneze kudzipereka kwathu kwa Mulungu ndi ziti, nanga tingatani kuti tizipeŵe?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Timasonyeza kudzipereka kwa Mulungu m’njira zambiri

[Zithunzi patsamba 14]

Samalani ndi zinthu zimene zingasokoneze kudzipereka kwanu kwa Mulungu