Kodi Mumakhulupirira Malodza pa Moyo Wanu?
Kodi Mumakhulupirira Malodza pa Moyo Wanu?
KUKHULUPIRIRA malodza kumachitika padziko lonse. Nthaŵi zina, anthu amati kukhulupirira malodza n’kofunika kwambiri monga mbali yachikhalidwe chawo. Nthaŵi zinanso amati ndi kungofuna kudziŵa zinthu ndiponso kumachititsa moyo kukhala wosangalatsa kwambiri. Ku mayiko a Azungu, kukhulupirira malodza amati si nkhani yaikulu. Koma kumadera ena, mwachitsanzo kuno ku Africa, kukhulupirira malodza kungakhudze kwambiri miyoyo ya anthu.
Kukhulupirira malodza ndiko maziko a mbali yaikulu yachikhalidwe cha kuno ku Africa. Mafilimu, mapulogalamu a pa wailesi, ndiponso mabuku zopangidwa ku Africa kuno, nthaŵi zambiri zimafotokoza za kukhulupirira malodza komanso zinthu zamizimu monga matsenga, kulambira makolo, ndiponso zithumwa. N’chifukwa chiyani anthu amakopeka ndi kukhulupirira malodza, ndipo kodi kunayambira kuti?
Kodi Kukhulupirira Malodza Kunayamba Bwanji?
Kukhulupirira malodza kunayamba chifukwa choopa mizimu ya anthu akufa kapena mizimu yamtundu wina uliwonse. Mizimu imeneyi amati ndiyo imachititsa zinthu zina n’cholinga chofuna kuuza anthu za ngozi, chenjezo, kapena mphoto.
Kukhulupirira malodza kumagwirizananso kwambiri ndi kuchiritsa ndiponso mankhwala. Kwa anthu ambiri m’mayiko amene akutukuka kumene, mankhwala achizungu ndi odula kwambiri ndipo nthaŵi zambiri sangawapeze n’komwe. Choncho, ambiri amafuna mankhwala kapena njira zodzitetezera potsatira miyambo yamakolo, kukhulupirira mizimu, ndiponso kukhulupirira malodza. Iwo amamasuka kulankhula ndi sing’anga chifukwa amadziŵa miyambo yawo ndiponso chinenero chawo kusiyana ndi dokotala wamankhwala achizungu. Chifukwa cha zimenezi, kukhulupirira malodza kukupitirizabe kufala.
Anthu okhulupirira malodza amakhulupirira kuti matenda ndiponso ngozi sizimangochitika mwadzidzidzi chabe, koma zimachitika chifukwa cha mphamvu ya mizimu. Asing’anga amizimu anganene kuti kholo lina limene linamwalira kale silikukondwa ndi zina zake. Kapenanso wobwebweta angauze munthu amene akudwala kapena amene wachita ngozi kuti zimenezo zachitika chifukwa chakuti wina wamulodza.
Malodza amene anthu amakhulupirira amasiyanasiyana padziko lonse ndipo kufala kwa zikhulupirirozi kumadalira miyambo ndi nthano za m’deralo komanso mmene zinthu zilili. Koma kulikonseko anthu amakhulupirira kuti mzimu wina wake ufunika kuusangalatsa.
Kodi N’koopsa Kapena N’kosaopsa?
Mabanja ambiri amasangalala kukabadwa ana amapasa. Koma kwa okhulupirira malodza, amati
ndi chizindikiro. M’madera ena akumadzulo kwa Africa, kukabadwa ana amapasa anthu ambiri amati kwabadwa milungu ndipo amalambira anawo. Ngati mmodzi kapena aŵiri onsewo amwalira, amapanga timafano ta ana amapasawo, ndipo banjalo limayenera kupatsa timafanoto chakudya. M’madera ena, kubadwa kwa ana amapasa amati ndi temberero, moti mpaka makolo amapha mmodzi mwa anawo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amakhulupirira kuti ngati ana onsewo atakula ndiye kuti tsiku lina adzapha makolo awo.Zitsanzo ngati zimenezi zimasonyeza kuti ngakhale zikhulupiriro zina zingaoneke ngati zosangalatsa ndiponso zabwino, zina n’zoopsa ndiponso zakupha. Zinthu zabwinobwino atha kuzimasulira molakwa kuti n’zoopsa.
Inde, kukhulupirira malodza n’chipembedzo. Popeza taona kuopsa kwa kukhulupirira malodza, tifunse kuti: Ndani kwenikweni amapindula ndi kukhulupirira malodza ndi miyambo yake?
Gwero la Kukhulupirira Malodza
Ngakhale pali umboni wotsimikiza kuti Satana ndiponso mizimu yoipa ziliko, anthu ena masiku ano amakana zimenezi. Komabe, kukana zoti adani oopsa aliko panthaŵi yankhondo kungangokuthetsani psiti. N’chimodzimodzinso ndi nkhondo yolimbana ndi zolengedwa zauzimu. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Kulimbana kwathu tilimbana nawo a uzimu a choipa.”—Aefeso 6:12.
Ngakhale kuti mizimu yoipa sitingaione, iyo iliko. Baibulo limanena kuti cholengedwa china chauzimu chosaoneka chinagwiritsa ntchito njoka polankhula kwa mkazi woyamba Hava, ndi kumuchititsa kupandukira Mulungu. (Genesis 3:1-5) Baibulo limatcha cholengedwa chauzimu chimenechi kuti “njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Satanayo ananyenganso angelo ena kuti apanduke. (Yuda 6) Angelo oipaŵa anakhala ziwanda, adani a Mulungu.
Yesu ndi ophunzira ake anatulutsa ziwanda mwa anthu. (Marko 1:34; Machitidwe 16:18) Mizimu imeneyi si makolo omwe anamwalira kale ayi, chifukwa akufa “sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Koma ameneŵa ndi angelo opanduka amene Satana ananyenga. Kulankhula nawo kapena kulola mphamvu yawo kutilamulira si nkhani yamaseŵera chifukwa iwo pamodzi ndi mtsogoleri wawo, Satana Mdyerekezi, akufuna kutilikwira. (1 Petro 5:8) Cholinga chawo n’chakuti tisakhulupirire Ufumu wa Mulungu womwe udzathetse mavuto a anthu.
Baibulo limavumbula imodzi mwa njira zomwe Satana ndi ziwanda zake amagwiritsa ntchito. Limati: “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 11:14) Satana akufuna kutinyenga kuti tikhulupirire kuti iye atha kutipatsa moyo wabwinopo. Chotero, pangakhale zinthu zina zabwino zosakhalitsa zomwe zingaoneke ngati zimachitika chifukwa cha mphamvu ya mizimu yoipa. Komabe mizimu singathetse mavuto athu kwamuyaya. (2 Petro 2:4) Iyo siingapereke moyo wosatha kwa wina aliyense. Ndiponsotu mizimuyi idzawonongedwa posachedwapa. (Aroma 16:20) Mlengi wathu ndiye gwero la moyo ndi chimwemwe chenicheni komanso ndiye yekha amene angatiteteze ku mphamvu ya mizimu yoipa.—Yakobo 4:7.
Mulungu amadana ndi kufunafuna thandizo pogwiritsa ntchito mizimu. (Deuteronomo 18:10-12; 2 Mafumu 21:6) Kuchita zimenezo n’kugwirizana ndi adani a Mulungu. Ngati mukhulupirira nyenyezi, kufunsira kwa asing’anga kapena kuchita zina zilizonse zokhudza kukhulupirira malodza, ndiye kuti mukulola mizimu yoipa kukusankhirani zochita pa moyo wanu. Kuchita zimenezi n’chimodzimodzi ndi kupandukira Mulungu.
Kodi Munthu Angatetezeke ku Mizimu Yoipa?
Ade, * mwamuna yemwe akukhala ku Niger, ankaphunzira Baibulo ndi mlaliki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Ade anafotokoza chifukwa chimene ankasungira chithumwa m’sitolo yake. Anati: “Ndili ndi adani ambiri.” Amene ankaphunzira Baibulo ndi Ade anamuuza kuti, Yehova yekha ndi amene tingamudalire kuti atiteteze. Anamuŵerengera Salmo 34:7, lomwe limati: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.” Ndiyeno Ade anati: “Ngati Yehova anganditetezedi, ndiye kuti ndidzataya chithumwachi.” Tsopano patha zaka zambiri, ndipo iye ndi mkulu ndiponso mtumiki wanthaŵi zonse. Palibe mdani ndi mmodzi yemwe amene anamulodza.
Baibulo limanena kuti nthaŵi ndiponso zochitika Mlaliki 9:11) Koma Yehova satiyesa ndi zinthu zoipa. (Yakobo 1:13) Timafa ndiponso ndife opanda ungwiro chifukwa cha tchimo lomwe tinatengera kwa Adamu. (Aroma 5:12) Pachifukwa chimenechi, aliyense amadwala komanso amalakwitsa nthaŵi ndi nthaŵi ndipo zolakwazo zingam’bweretsere mavuto. Choncho, n’kulakwa kunena kuti mizimu yoipa ndiyo imachititsa matenda onse kapena mavuto onse. Kukhulupirira zimenezi kungatichititse kugwa m’chiyeso chofuna kukondweretsa mizimu m’njira ina yake. * Tikadwala, tizifuna mankhwala oyenera osati kufunsira malangizo kwa Satana Mdyerekezi, “wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Ziŵerengero zimasonyeza kuti anthu amene amakhala m’mayiko amene kukhulupirira malodza kuli kofala kwambiri sakhala ndi moyo wautali kapena wabwinopo powayerekezera ndi amene amakhala m’mayiko ena. Choncho, n’zodziŵikiratu kuti kukhulupirira malodza sikungathandize munthu kukhala ndi umoyo wabwino.
zadzidzidzi zimatigwera tonse, kaya timakhulupirira malodza kapena ayi. (Mulungu ndi wamphamvu kwambiri kuposa mzimu woipa uliwonse, ndipo Iye amatisamalira. “Maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.” (1 Petro 3:12) Pempherani kwa iye kuti akutetezeni ndiponso kuti akupatseni nzeru. (Miyambo 15:29; 18:10) Yesetsani kumvetsa Mawu ake Opatulika, Baibulo. Kudziŵa zolondola zomwe Baibulo limanena ndiko chitetezo chabwino kwambiri chomwe tingapeze. Kudzatithandiza kuzindikira chifukwa chake zinthu zoipa zikuchitika komanso zimene tingachite kuti Mulungu Wamphamvuyonse atiyanje.
Phindu la Kudziŵa Mulungu
Kudziŵa Yehova ndi zolinga zake molondola ndiko chinsinsi cha chitetezo chenicheni, kusiyana ndi kusamudziŵa ndiponso kukhulupirira malodza. Izi n’zimene anaona mwamuna wina wa ku Benin dzina lake Jean. Banja la Jean linkakhulupirira malodza kwambiri. Malinga ndi miyambo yawo, mkazi amene wabereka kumene mwana wamwamuna ayenera kubindikira m’kanyumba kapadera kwa masiku asanu ndi anayi. Ngati wabereka mwana wamkazi ndiye kuti ayenera kubindikira m’kanyumbako kwa masiku asanu ndi aŵiri.
Mu 1975, mkazi wa Jean anabereka mwana wamwamuna wokongola kwambiri ndipo anamutcha dzina loti Marc. Mogwirizana ndi zomwe akudziŵa kuchokera m’Baibulo, Jean ndi mkazi wake sanafune kuchita chilichonse chokhudza mizimu yoipa. Kodi akanagonja chifukwa cha mantha ndiponso kuumirizidwa kuti atsatire mwambowo ndi kulolera mayiyo kukabindikira m’kanyumbako? Ayi, iwo anakana kuchita zimenezo.—Aroma 6:16; 2 Akorinto 6:14, 15.
Kodi banja la Jean linapeza vuto lililonse? Zaka zambirimbiri zapita tsopano, ndipo Marc ndi mtumiki wotumikira mumpingo wa Mboni za Yehova wakwawo. Banja lonse likuthokoza kuti iwo sanalole kukhulupirira malodza pa moyo wawo ndi kuika moyo wauzimu pangozi.—1 Akorinto 10:21, 22.
Akristu oona ayenera kupeŵa kukhulupirira malodza pa moyo wawo, koma ayenera kulandira kuwala kwauzimu kumene Mlengi, Yehova, ndi Mwana wake, Yesu Kristu anapereka. Akatero adzasangalala ndi mtendere weniweni wamumtima umene umadza chifukwa chodziŵa kuti akuchita zoyenera pamaso pa Mulungu.—Yohane 8:32.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 20 Mayina tasintha.
^ ndime 21 Onani nkhani yakuti “Kodi Mdyerekezi Ndiye Amatidwalitsa?” mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1999.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]
Zikhulupiriro Zina Zamalodza Zofala Padziko Lonse
• Timitengo todyela tikaimirira m’mbale ya mpunga n’chizindikiro choti kuchitika maliro
• Kuona kadzidzi masana dzuŵa likuswa mtengo kumabweretsa masoka
• Kandulo ikazima pa mwambo wina wake ndiye kuti mizimu yoipa ili pafupi
• Kugwetsa ambulera pansi m’nyumba n’chizindikiro choti wina m’nyumbamo aphedwa
• Kuika chisoti pa bedi kumabweretsa masoka
• Kulira kwa belu kumathamangitsa ziŵanda
• Kuzima makandulo kamodzinkamodzi pa keke ya tsiku lobadwa kumatanthauza kuti zofuna za munthuyo zidzachitikadi
• Kuyedzeka tsache ku bedi kumachititsa mizimu yoipa yomwe ili ku tsachero kuti iike nyanga pa bedilo
• Mphaka wakuda akadutsa kutsogolo kwanu ndiye kuti ndi masoka amenewo
• Munthu akagwetsa foloko pansi ndiye kuti kubwera mlendo wamwamuna kudzacheza
• Chithunzi cha njovu chimabweretsa mwayi ngati njovuzo zitayang’ana kukhomo
• Nsapato ya hatchi ikakhala pakhomo la nyumba imabweretsa mwayi
• Maluŵa akayanga pamwamba pa nyumba amateteza zoipa
• Kuyenda kunsi kwa makwerero kumabweretsa masoka
• Munthu akaswa galasi ndiye kuti aona masoka kwa zaka zisanu ndi ziŵiri
• Munthu akamwaza tsabola ndiye kuti akangana ndi bwenzi lake lapamtima
• Kumwaza mchere pansi kumabweretsa masoka, koma ngati kam’bulu ka mchere kokwanira pachala angakaponye kudutsa paphewa lakumanzere, masokawo sangachitike.
• Mitundu ina ya mipando imene anaipanga kuti izitha kugwedera payokha, ingaitane ziŵanda kuti zikhalepo ngati munthu ataisiya ikugwedera popanda kanthu
• Kusiya nsapato itavundikirika kumabweretsa masoka
• Munthu akamwalira mawindo a nyumba ya womwalirayo ayenera kukhala otsekula kuti mzimu utulukemo
[Bokosi patsamba 6]
Anasiya Kukhulupirira Malodza
Mboni za Yehova zinali kulalikira m’dera lina ku South Africa. Zitagogoda pakhomo lina, mkazi wina anatuluka atavala zovala zonse za Sangoma (sing’anga wamizimu). Mbonizo zinafuna kuchoka, koma mkaziyo anaziumiriza kuti zinene uthenga wawo. Mboni ina inaŵerenga Deuteronomo 18:10-12 kuti imusonyeze mkaziyo zomwe Mulungu amanena pankhani ya zamizimu. Sing’anga wamizimuyo analandira uthengawo ndipo anavomera kuphunzira Baibulo. Iye ananena kuti ngati pophunzira Baibulo adzaonedi kuti kukhala Sangoma n’kosemphanadi ndi zomwe Yehova amafuna, adzasiya using’angawo.
Ataphunzira chaputala 10 m’buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi pogwiritsa ntchito Baibulo, iye anatentha zinthu zonse zaufiti ndipo anayamba kupita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Komanso, anabwererana ndi mwamuna wake ndi kulembetsa ukwati wawo ku boma ngakhale kuti anali atapatukana kwa zaka 17. Tsopano, onse aŵiri ndi Mboni za Yehova zodzipatulira ndiponso zobatizidwa.
[Chithunzi patsamba 6]
“Sangoma” akuponya mafupa kuti mizimu imuuze chomwe chinayambitsa matenda a wodwala
[Zithunzi patsamba 7]
Kudziŵa zolondola zokhudza Mulungu kumadzetsa chitetezo ndi chimwemwe chenicheni