Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Abele anadziŵa kuti nyama ndi imene inafunika popereka nsembe kuti Mulungu amuyanje?

Nkhani ya m’Baibulo yosimba za kupereka nsembe kwa Kaini ndi Abele ndi yaifupi. Pa Genesis 4:3-5 timaŵerenga kuti: “Panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova. Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang’anira Abele ndi nsembe yake: koma sanayang’anira Kaini ndi nsembe yake.”

Palibe paliponse m’Baibulo pamene akunena kuti zimenezi zisanachitike, Yehova anafotokoza mwachindunji za kupereka nsembe kapena nsembe zimene iye angazilandire. Motero, Kaini ndi Abele mwachionekere anangofuna okha kupereka nsembe. Iwo analetsedwa kupita ku malo oyambirira a Paradaiso a makolo awo. Anayamba kuona zotsatira za uchimo; ndiponso analekanitsidwa ndi Mulungu. Pamene anali m’vuto lawo la uchimo ndiponso lomvetsa chisoni limeneli, iwo ayenera kuti anaona kufunika kotembenukira kwa Mulungu kuti awathandize. Mwachionekere, kupereka mphatso kwa Mulungu mofuna okha ndiyo anaona kuti ndi njira yoti iye awayanje.

Ndiyeno zinachitika n’zakuti Mulungu analandira nsembe ya Abele koma ya Kaini anaikana. Chifukwa chiyani? Kodi chinali chifukwa chakuti Abele anapereka nsembe zinthu zoyenera pamene za Kaini zinali zosayenera? Sitingatsimikize kuti mtundu wa zimene anapereka nsembe sizinakhudze mmene Mulungu anaonera nsembeyo, chifukwa palibe m’modzi wa iwo anauzidwa nsembe imene inali yovomerezeka ndi yosavomerezeka. Komabe, ziyenera kuti zinthu zonse zimene anapereka nsembezo zinali zovomerezeka. M’Chilamulo chimene Yehova anapereka ku mtundu wa Israyeli patapita nthaŵi, nsembe zimene zinali zovomerezeka sizinali nyama zokha kapena ziwalo za nyama zokha ayi. Analinso kuvomereza nsembe za tirigu wokazinga, mtolo wa balere, ufa wosalala, zinthu zowotcha, ndiponso vinyo. (Levitiko 6:19-23; 7:11-13; 23:10-13) Mwachionekere, si mtundu wa zinthu zimene Kaini ndi Abele anapereka nsembe zimene zinachititsa Mulungu kuvomereza nsembe ina n’kukana inayo.​—Yerekezerani ndi Yesaya 1:11; Amosi 5:22.

Patapita zaka zikwi zingapo, mtumwi Paulo anati: “Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, amene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake.” (Ahebri 11:4) Motero, Mulungu anaona Abele kukhala wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake. Koma kodi anali kukhulupirira chiyani? Anali kukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti adzapereka Mbewu, imene ‘idzalalira mutu wa njoka’ ndi kubwezeretsa mtendere ndi ungwiro umene anthu anali nawo poyamba. Mawu akuti Mbewu ‘idzalaliridwa chitende,’ ayenera kuti anachititsa Abele kuganiza kuti panafunika nsembe yokhetsa mwazi. (Genesis 3:15) Kaya anatero kapena ayi, mfundo ndi yakuti chikhulupiriro cha Abele n’chimene chinachititsa nsembe yake kukhala “nsembe yoposa ija ya Kaini.”

Mofananamo, Kaini anakanidwa, osati chifukwa chakuti zimene anapereka nsembe zinali zolakwika, koma chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro, monga mmene zochita zake zinasonyezera. Yehova anauza Kaini momveka bwino kuti: “Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi?” (Genesis 4:7) Mulungu anakana Kaini osati chifukwa chakuti sanasangalale nayo nsembe yake ayi. M’malo mwake, Mulungu anakana Kaini chifukwa chakuti “ntchito zake zinali zoipa,” zimene anasonyeza mwa kuchita nsanje, udani, ndipo kenako kupha.​—1 Yohane 3:12.