Maseŵero a Yoga—Kodi Ndi Ongolimbitsa Thupi Chabe Kapena Pali Zinanso?
Maseŵero a Yoga—Kodi Ndi Ongolimbitsa Thupi Chabe Kapena Pali Zinanso?
ANTHU ambiri masiku ano amafuna kukhala ochepa thupi ndiponso a thanzi labwino. Zimenezi zachititsa ena kupita ku nyumba zochitira maseŵero olimbitsa thupi kapena ku magulu a zaumoyo kuti akawathandize. Anthu ambirimbiri a ku mayiko a Azungu akuchita nawo maseŵero a ku Asia a yoga pa chifukwa chomwechi.
Anthu amene ali ndi nkhaŵa, amene akuvutika maganizo, ndiponso amene akhumudwa amachitanso maseŵero a yoga kuti apeze mpumulo ndi kuthetsa vuto lawo. Makamaka kuyambira m’zaka za m’ma 1960, nthaŵi imene kunabuka gulu la achinyamata otayirira, kukonda zipembedzo za ku Asia ndi miyambo yawo ya kukhulupirira mizimu zinafalikira m’mayiko a Azungu. Anthu otchuka a m’mafilimu ndi oimba nyimbo za rock atchukitsa kusinkhasinkha kumene kumachitika pa maseŵero a yoga. Poona mmene anthu ochuluka akukondera maseŵeroŵa, tingafunse kuti: ‘Kodi maseŵero a yoga ndi ongolimbitsa thupi chabe amene angathandize woseŵerayo kukhala ndi thanzi labwino, kuchepetsa thupi ndi kupeza mtendere wa maganizo? Kodi munthu angachite maseŵeroŵa popanda kukhudzidwa ndi zachipembedzo? Kodi Akristu angachite maseŵero ameneŵa?’
Chiyambi cha Maseŵero a Yoga
Liwu loyambirira m’chinenero chakale cha ku India cha Chisansikiriti, lakuti ‘yoga’ lingatanthauze kugwirizanitsa pamodzi kapena kuika m’goli limodzi kapena kukoloŵeka m’goli, kumangirira pamodzi kapena kulamulira. Kwa Ahindu, maseŵero a yoga ndiwo luso kapena njira yolamulira thupi imene ingathandize munthu kugwirizana ndi mphamvu yaikulu yoposa yachibadwa kapena mizimu. Amati maseŵero a yoga ndiwo “kumangirira m’goli mphamvu zonse za thupi, maganizo, ndi moyo kwa Mulungu.”
Kodi maseŵero a yoga anayamba liti kalelo? Zithunzi za anthu okhala mosiyanasiyana posonyeza mmene amachitira maseŵero a yoga zimaonekera m’zidindo zokhala ndi zizindikiro zogoba zimene azipeza m’chigwa cha Indase, kumene lerolino amati ku Pakistan. Ofukula za m’mabwinja amati anthu otukuka oyambirira kukhala ku chigwa cha Indase anakhalako pakati pa zaka za m’ma 3,000 ndi 1,000 B.C.E., pafupi kwambiri ndi Genesis 10:8, 9) Ahindu amati anthu okhala mosonyeza mmene amachitira maseŵero a yoga amenewo ndiwo zithunzi za mulungu wotchedwa Siva, mbuye wa zinyama ndiponso mbuye wa yoga. Mulungu ameneyu nthaŵi zambiri amamulambira kudzera m’chizindikiro chosonyeza maliseche achimuna. N’chifukwa chake buku lakuti Hindu World limati yoga ndi “malangizo a kudzimana konkitsa, makamaka amene anayamba Aariyani asanakhaleko. Maseŵeroŵa ali ndi zizindikiro za zikhulupiriro ndi miyambo yambiri yachikale.”
nthaŵi imene anthu oyamba a ku Mesopotamiya anakhalako. Zinthu zofukula m’mabwinja za malo onse aŵiriŵa zimasonyeza munthu, woimira mulungu, wokhala ndi nyanga za nyama ndiponso atazunguliridwa ndi zinyama, yemwe ayenera kukhala Nimrode, “mpalu wamphamvu.” (Poyamba, anthu ankauzidwa pakamwa kachitidwe ka maseŵero a yoga. Ndiyeno Mmwenye wina wanzeru wochita maseŵeroŵa dzina lake Patañjali analemba mwatsatanetsatane kachitidwe ka maseŵeroŵa m’buku lakuti Yoga Sutra, limene mpaka pano likadali buku la malangizo a yoga. Patañjali anati, maseŵero a yoga ndiwo “kuyesetsa mwakhama kuti munthu ukhale wangwiro, mwa kulamulira mbali zosiyanasiyana za umunthu, thupi ndi maganizo.” Kuyambira pachiyambi mpaka lero, maseŵero a yoga akhala mbali yaikulu m’zipembedzo za ku Asia, masiku ano makamaka m’Chihindu, Chijaini, ndi Chibuda. Anthu ambiri amene amachita maseŵero a yoga amakhulupirira kuti kudzawachititsa kupeza moksha, kapena kuti kupeza ufulu, mwa kugwirizana ndi mzimu.
Ndiyeno tikubwerezanso kufunsa kuti: ‘Kodi munthu angachite maseŵero a yoga n’cholinga cholimbitsa thupi chabe kuti akhale ndi thupi labwino ndi mtendere wa maganizo, popanda kukhudzidwa ndi zachipembedzo?’ Poona mmene maseŵeraŵa anayambira, tingayankhe kuti ayi.
Kodi Maseŵero a Yoga Angakutsogolereni Kuti?
Cholinga cha yoga chomwe ndi kulamulira thupi chimatsogolera munthu ku zinthu zauzimu “n’kumangidwa m’goli” kapena kugwirizana ndi mzimu. Koma kodi ungakhale mzimu wanji umenewo?
M’buku lake lakuti Hindu World, Benjamin Walker anafotokoza za maseŵero a yoga kuti: “Iyenera kuti inali miyambo yoyambirira ya zamatsenga, ndipo tanthauzo la yoga lomwe limakhudza zamizimu ndi zamatsenga likadapitirirabe.” Anzeru za dziko a Chihindu amavomereza kuti kuchita maseŵero a yoga kungam’chititse munthu kukhala ndi mphamvu za mizimu, ngakhale kuti nthaŵi zambiri amati chimenechi si cholinga chachikulu cha maseŵeroŵa. Mwachitsanzo, m’buku lakuti Indian Philosophy, pulezidenti wakale wa dziko la India, Dr. S. Radhakrishnan anafotokoza za munthu wochita maseŵero a yoga kuti “kulamulira thupi mwa kaimidwe kumam’pangitsa kusamva kutentha kapena kuzizira ngakhale kutatentha kwambiri kapena kuzizira kwambiri. . . . Wochita maseŵeroŵa angamve kapena kuona patali kwambiri . . . Angathe kulankhulana wina ndi mnzake popanda kugwiritsa ntchito njira zachibadwa zolankhulirana. . . . Wochita maseŵeroŵa angachititse thupi lake kusaoneka.”
Kuona wochita maseŵeroŵa atagona pa bedi la misomali kapena kuyenda pa makala a moto kungaoneke ngati zabodza kwa anthu ena pamene kwa ena zingakhale zoseketsa. Komatu zimenezi zimachitikachitika ku India, monganso mmene chilili chizoloŵezi choima ndi mwendo umodzi pamene akuyang’anitsitsa dzuŵa kwa maola ambiri ndiponso kubanika mwadala kumene kumachititsa munthu kumukwirira mumchenga kwanthaŵi yaitali. Mu June 1995, nyuzipepala ya The Times of India inasimba kuti mwana wina wamkazi wa zaka zitatu ndi theka anagona pansi akuoneka ngati wakomoka ndiyeno galimoto ya makilogalamu 750 inayendetsedwa pamimba pake. Khamu la anthu limene linali kuonerera linadabwa pamene iye anadzuka osavulala pena paliponse. Nkhaniyo inapitiriza kuti: “Inali mphamvu ya yoga yeniyeni.”
Mosakayika, munthu wabwinobwino sangathe kuchita zimenezi. Motero, Akristu ayenera kufunsa kuti: Kodi zinthu zodabwitsa zimenezi zimachokera kuti? Kodi zimachokera kwa Yehova Mulungu, “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” kapena zimachokera kumagwero ena? (Salmo 83:18) Baibulo limafotokoza mosapita m’mbali mfundo imeneyi. Pamene Aisrayeli anatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, mmene munkakhala Akanani, Yehova anauza ana a Israyeli kudzera mwa Mose kuti: “Musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja.” Kodi “zonyansa” zake ziti? Mose anawachenjeza kuti apeŵe ‘kusamalira mitambo, kusamalira kulira kwa mbalame, kapena nyanga.’ (Deuteronomo 18:9, 10) Zimenezi zimanyansa Mulungu chifukwa ndi ntchito za ziwanda ndiponso za thupi lochimwa.—Agalatiya 5:19-21.
Akristu Sangasankhe Kuchita Zimenezi
Ngakhale mlangizi wa zaumoyo atanena zosiyana ndi zimene zili pamwambazi, maseŵero a yoga si ongolimbitsa thupi chabe. Buku lakuti Hindu Manners, Customs and Ceremonies linasimba zimene anaona ophunzira yoga aŵiri amene aphunzitsi awo anali kuwatsogolera. Bukuli linanena kuti wophunzira wina anati: “Ndinayesetsa mwapadera kubanika kwanthaŵi yaitali, ndipo ndinapuma nditangotsala pang’ono kukomoka. . . . Tsiku lina dzuŵa lili paliwombo, ndinaganiza kuti ndinaona mwezi wowala kwambiri, umene unaoneka ngati umayenda uku ndi uku. Nthaŵi ina ndinaona ngati ndinali m’kati mwa mtambo wakuda bii masana dzuŵa likuswa mtengo. Mphunzitsi wangayo. . . anasangalala kwambiri nditamuuza masomphenya ameneŵa. . . . Iye ananditsimikizira kuti sipapita nthaŵi yaitali kuti ndione zodabwitsa zina zambiri chifukwa cha kudzilanga kwanga.” Mwamuna winayo anati: “Iye anandiuza kuti ndiziyang’ana kuthambo tsiku ndi tsiku popanda kuphethira kapena kusintha malo amene ndaima. . . . Nthaŵi zina ndinaganiza kuti ndinaona malaŵi a moto mumlengalenga: nthaŵi zina ndinkakhala ngati ndikuona zinthu zikuluzikulu zozungulira za moto ndi miyala ina ikuluikulu yowala. Mphunzitsi wanga anali kusangalala ndi kupambana kwa khama langa.”
Mwachionekere, kuona zinthu zachilendozo n’kumene aphunzitsiwo anaganiza kuti ndizo zinali zotsatira zabwino zimene zidzawathandiza kupeza cholinga chenicheni cha maseŵero a yoga. Inde, cholinga chachikulu cha yoga ndicho moksha, imene imatanthauza kugwirizana ndi mzimu winawake waukulu. Amati maseŵero a yoga ndiwo “kuimitsa (dala) luso lachibadwa la kuganiza.” Zimenezi n’zosemphana ndi cholinga cha Akristu, amene alamulidwa kuti: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”—Aroma 12:1, 2.
Kusankha maseŵero olimbitsa thupi amene munthu angachite ndi nkhani ya aliyense payekha. Komabe, Akristu sangalole kuwononga ubwenzi wawo ndi Yehova Mulungu chifukwa cha maseŵero olimbitsa thupi, kudya, kumwa, kuvala, zosangalatsa, kapena china chilichonse. (1 Akorinto 10:31) Kwa amene amachita maseŵero olimbitsa thupi n’cholinga choti angokhala ndi thanzi labwino, pali maseŵero ambiri amene sangawaike pangozi yokhulupirira mizimu ndi matsenga. Mwa kupeŵa zochitika ndi zikhulupiriro zomwe n’zachipembedzo chonyenga, tingayembekezere madalitso a Mulungu a dongosolo la zinthu latsopano mmene tidzakhala ndi thanzi langwiro m’thupi ndiponso m’maganizo kwamuyaya.—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.
[Zithunzi patsamba 22]
Anthu ambiri amachita maseŵera olimbitsa thupi amene sawaika pa ngozi yokhulupirira mizimu