Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Wokhulupirira Malodza

Moyo Wokhulupirira Malodza

Moyo Wokhulupirira Malodza

MWAKUMANA maso ndi maso ndi munthu wina potuluka m’nyumba yanu. Mwaphunthwa pamwala. Mbalame yamtundu winawake ikulira usiku. Mwalota maloto amodzimodzi mobwerezabwereza. Kwa anthu ambiri, zimenezi ndi zinthu zosaopsa m’pang’ono pomwe. Koma kwa anthu ena, mwachitsanzo kumadzulo kwa Africa, zimenezi amati n’zizindikiro, malodza, kapena mauthenga ochokera kudziko lamizimu. Kaya ukhale mwayi kapena tsoka, iwo amakhulupirira kuti zichitikadi mogwirizana ndi chizindikirocho komanso kumasulira kwake.

Komabe, si kuno kokha ku Africa komwe anthu amakhulupirira malodza. Anthu a ku China ndiponso a m’mayiko omwe kale anali m’manja mwa Soviet Union amakhulupiriranso malodza ngakhale kuti kwanthaŵi yaitali akhala akutsatira chikhulupiriro chovomerezeka ndi boma choti kulibe milungu. M’mayiko a Azungu, anthu ambiri amakhulupirira nyenyezi, ndiponso kuti tsiku lachisanu lomwe deti lake ndi 13 ndi tsiku latsoka. Amapeŵanso kukumana ndi amphaka akuda. Anthu ena m’mayiko a ku Far North amakhulupirira kuti kuwala kwapadera komwe kumachitika kumeneko kumalosera nkhondo kapena masoka. Ku India, madiraivala a magalimoto akuluakulu akufalitsa Edzi (AIDS) kwambiri chifukwa chakuti amakhulupirira kuti amafunika kugonana kuti thupi lawo lizikhala lozizira bwino masiku otentha. Ku Japan, ogwira ntchito yokonza ngalande zapansi, amakhulupirira kuti ndi tsoka ngati mkazi ataloŵa m’ngalande yosamaliza. Anthu ochita maseŵera otchuka amakhulupiriranso malodza. Woseŵera mpira wa volleyball wina ananena kuti anapambana motsatizanatsatizana chifukwa chovala sokosi zakuda m’malo mwa zoyera. Zikhulupiriro zoterezi n’zambiri moti sitingathe kutchula zonse.

Koma bwanji inuyo? Kodi m’maopa china chake chosadziŵika bwino? Kodi mumakhulupirira kwambiri chinthu china ngakhale pang’ono chabe, kapena kuopa mwambo winawake womwe ukuoneka kuti ulibe maziko enieni? Popeza kuti kumeneku ndiko kukhulupirira malodza, yankho lanu pafunsoli ndilo lingasonyeze ngati mumakhulupirira malodza kapena ayi.

Munthu amene amakhulupirira malodza pa zosankha zake ndiponso pamoyo wake watsiku ndi tsiku ndiye kuti akulola chinthu chimene sakuchidziŵa kuti chizimulamulira. Kodi zimenezi n’zanzeru? Kodi tiyenera kulola mphamvu yosadziŵika ndiponso yoipa ngati imeneyi kulamulira moyo wathu? Kodi kukhulupirira malodza n’kufooka chabe kosavulaza kapena n’koopsa kwambiri?