Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomwe Tingaphunzire ku Mbalame Yotchedwa Dokowe

Zomwe Tingaphunzire ku Mbalame Yotchedwa Dokowe

Zomwe Tingaphunzire ku Mbalame Yotchedwa Dokowe

“Chumba [“dokowe,” NW] cha mlengalenga chidziŵa nyengo zake . . . koma anthu anga sadziŵa chiweruziro cha Yehova.” (Yeremiya 8:7) Ndi mawu ameneŵa, mneneri Yeremiya analengeza chiweruzo cha Yehova kwa anthu opanduka a mtundu wa Yuda, amene anasiya Yehova Mulungu wawo n’kumalambira milungu ina. (Yeremiya 7:18, 31) N’chifukwa chiyani Yeremiya anasankha dokowe monga chinthu chomwe chingapatse phunziro Ayuda osakhulupirikawo?

Aisrayeli ankaona adokowe pafupipafupi, makamaka oyera, chifukwa mbalamezi zinkangoyendayenda m’madera otchulidwa m’Baibulo. Dzina la Chihebri la mbalame zazikulu, zazitali miyendo zimenezi, lomwe ndi liwu losonyeza chinthu chachikazi, limatanthauza “wokhulupirika; wokoma mtima.” Dzinali n’loyenera kwambiri chifukwa chakuti, mosiyana ndi mbalame zina, adokowe oyera amakhala kwa moyo wawo wonse ali aŵiri monga banja, wamwamuna ndi wamkazi. Chaka chilichonse pa nyengo yozizira, mbalamezi zimapita kumadera otentha ndipo nyengo yozizira ikatha zambiri mwa izo zimabwereranso pachisa chawo chakale chomwe zinachisiya.

Zomwe adokowe amachita mwachibadwa zimasonyeza kukhulupirika kwawo m’njira inanso yapadera. Adokowe onse aŵiri, wamwamuna ndi wamkazi amathandizana kukhalira mazira ndiponso kudyetsa anapiye. Buku lakuti Our Magnificent Wildlife limafotokoza kuti: “Monga makolo, adokowe amakhala okhulupirika kwambiri kwa wina ndi mzake. Dokowe wina wamwamuna ku Germany anatera pa waya wamphamvu kwambiri wamagetsi ndipo anafa. Dokowe wamkazi anapitiriza yekha kukhalira mazira kwa masiku atatu ndipo panthaŵiyo ankangochoka pachisa kwa nthaŵi yochepa chabe kuti akafune chakudya. . . . Nthaŵi ina, pamene dokowe wina wamkazi anamuwombera, dokowe wamwamuna analera yekha anapiye.”

Inde, dokowe mwachibadwa amasonyeza kukhulupirika kwa mkazi kapena mwamuna wake pa moyo wake wonse ndiponso amasamalira anapiye mwachikondi. Izi zimasonyeza kuti amachitadi mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake lomwe limatanthauza kuti “wokhulupirika.” Chotero, mpake kuti adokowe anali chitsanzo chabwino kwambiri kwa Aisrayeli osakhulupirika ndiponso osamverawo.

Kwa anthu ambiri lerolino, kukhulupirika amati ndi khalidwe lachikale. Ambiri amangonena chabe kuti n’labwino koma safuna kulitsatira. Kuchuluka kwa mabanja amene akusudzulana, kunyanyalana, ndiponso kukhala osakhulupirika, komanso mitundu ina ya chinyengo, kukusonyeza kuti anthu amaona kukhulupirika kukhala kosafunika. Koma Baibulo limanena kuti kukhulupirika komwe maziko ake ndi chikondi ndiponso kukoma mtima n’kofunika kwambiri. Limalimbikitsa Akristu “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwa chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.” (Aefeso 4:24, NW) N’zoona kuti umunthu watsopano umatithandiza kukhala okhulupirika, koma tikhoza kuphunziranso za kukhulupirika ku mbalame yotchedwa dokowe.