Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akusangalala Chifukwa Anaphunzira Kuŵerenga!

Akusangalala Chifukwa Anaphunzira Kuŵerenga!

Akusangalala Chifukwa Anaphunzira Kuŵerenga!

M’MADERA ena a pa chilumba cha Solomon, ambiri mwa anthu omwe tsopano ndi Mboni za Yehova anali ndi vuto losadziŵa kulemba ndi kuŵerenga. Zimenezi zinkawachititsa kuti asamatenge nawo mbali mokwanira pamisonkhano yampingo ya mlungu ndi mlungu ndiponso kuti azivutika kuphunzitsa ena choonadi cha Ufumu. Kodi n’zothekadi kuti anthu achikulire omwe sanagwirepo cholembera adziŵe kulemba ndi kuŵerenga?

Buku lakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, aligwiritsa ntchito m’makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga m’mipingo yonse ya Mboni za Yehova pachilumba cha Solomon. Zitsanzo zotsatirazi zisonyeza mmene pulogalamuyi yathandizira anthu ambiri kuwonjezera luso lawo. Chofunika kwambiri n’chakuti kuphunzira kuŵerenga kwawathandiza kuti azilalikira bwino chikhulupiriro chawo.​—1 Petro 3:15.

Mmishonale wina yemwe anamutumiza ku mpingo womwe unali ndi ofalitsa Ufumu opitirira 100 anaona kuti pa phunziro la Baibulo la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu, anthu ochepa okha ndiwo anali ndi magazini ndipo oŵerengeka ndiwo ankayankha. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti sankadziŵa kuŵerenga. Mpingowo utalengeza kuti wakhazikitsa sukulu yophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga, mmishonaleyo mokondwera anadzipereka kukhala mphunzitsi. Poyamba, kunabwera anthu ochepa, koma posakhalitsa anthu amisinkhu yonse oposa 40 anayamba kuphunzira nawo.

Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mmishonaleyo anasimba kuti: “Titangoyamba sukuluyo, ndinapita kumsika 6 koloko mmamaŵa kukagula zakudya za kunyumba ya amishonale. Kumeneko ndinaona ophunzira ena, ngakhale ana ang’onoang’ono, akugulitsa ngole ndiponso ndiwo zamasamba. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ankafuna kupeza ndalama zogulira makope ndi zolembera zokagwiritsa ntchito kusukulu yophunzitsa kulemba ndi kuŵerengayi. Ndiponso kupita kusukuluyo kunawalimbikitsa kukhala ndi magazini awoawo a Nsanja ya Olonda.” Mmishonaleyo ananenanso kuti: “Tsopano, pa Phunziro la Nsanja ya Olonda, ana ndiponso achikulire amayankha ndipo zimenezi zimachititsa phunzirolo kukhala losangalatsa.” Mmishonaleyo anasangalala kwambiri makamaka pamene ophunzira anayi anapempha ngati angapite kukalalikira kwa anthu ena, chifukwa iwo anati, “tsopano sakuopa wina aliyense.”

Ophunzirawo apindula zambiri kuposa kungodziŵa kulemba ndi kuŵerenga chabe. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri mkazi wina wosakhulupirira yemwe mwamuna wake ndi Mboni anali kudetsa nkhaŵa mpingo kwambiri. Iye ankaponya miyala anthu akangosemphana nawo mawu pang’ono chabe ndiponso ankamenya akazi ena ndi mtengo. Nthaŵi zina mkaziyu akapita nawo kumisonkhano yachikristu ndi mwamuna wake, ankam’chitira nsanje kwambiri kotero kuti mwamunayo anaganiza zomavala magalasi akuda kuti mkaziyo asamamuimbe mlandu woti amaona akazi ena.

Komabe, sukulu yophunzitsa kulemba ndi kuŵerengayo itayamba, mayiyo anapempha kuti: “Kodi ndingaloŵe nawo sukuluyi?” Anamuvomera. Kuchokera nthaŵi imeneyo sanaphonyepo kalasi kapena msonkhano wampingo. Analimbikira kwambiri maphunziro ake oŵerenga ndipo anapita patsogolo mofulumira ndipo zimenezi zinam’sangalatsa kwambiri. Kenako anapempha kuti: “Kodi ndingamaphunzire Baibulo?” Mwamuna wake mokondwera anayamba kuphunzira naye Baibulo ndipo akupitirizabe kuwonjezera luso lake la kulemba ndi kuŵerenga ndiponso kudziŵa kwake Baibulo.

Kwa munthu wa zaka 50 yemwe sanagwirepo cholembera, chingakhale chinthu chovuta kwambiri kugwira cholembera kuti alembe zilembo. Ena mpake kuti amatuluka matuza m’zala chifukwa chokanikiza kwambiri cholembera poyamba kuphunzira kulemba. Akavutika ndi kuphunzira kugwira cholembera kwa milungu ingapo, ophunzira ena amanena akumwetulira kuti: “Ndingathe kuyendetsa dzanja langa papepalali!” Ophunzira akamakwanitsa kuchita zomwe akuphunzirazo mphunzitsi nayenso amasangalala kwambiri. Mphunzitsi wina anati: “Kuphunzitsa m’kalasi n’kosangalatsa kwambiri ndipo nthaŵi zambiri ophunzira amayamikira ndi mtima wonse dongosolo la Yehova limeneli mwa kuwomba m’manja tikamaliza kuphunzira.”

Tsopano Mboni zodziŵa kulemba ndi kuŵerenga zimenezi pamodzi ndi amishonale zikusangalala kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti tsopano atha kugwiritsa ntchito luso lawo la kulemba ndi kuŵerenga polemekeza Yehova.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Ana ndiponso achikulire akuyamikira kwambiri sukulu yophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga