Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Luso la Kulingalira Lingakutetezeni Bwanji?

Kodi Luso la Kulingalira Lingakutetezeni Bwanji?

Kodi Luso la Kulingalira Lingakutetezeni Bwanji?

MAFUNDE aakulu amasangalatsa kwambiri kuwaona, koma ndi oopsa kwa oyenda panyanja. Mafundewo akhoza kuwapha.

Mofanana ndi mafunde, atumiki a Mulungu angakumane ndi mavuto ambirimbiri amene angawaike pangozi. Mwina mwaonapo kuti mayesero ndi zokopa zotsatizanatsatizana zimagwera Akristu. Mosakayika, mumafuna kugonjetsa zimenezi kotheratu, muli wotsimikiza mtima kupeŵa kusweka mwauzimu ngati chombo. (1 Timoteo 1:19) Luso la kulingalira lingakuthandizeni kwambiri kuti mudziteteze. Kodi luso la kulingalira n’chiyani, ndipo munthu amalipeza bwanji?

Liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “kulingalira,” mezim·mahʹ, linachokera ku liwu limene limatanthauza “kulinganiza kapena kukonza.” (Miyambo 1:4) Motero, mabaibulo ena anamasulira liwu lakuti mezim·mahʹ kukhala “nzeru” kapena “kuoneratu za m’tsogolo.” Akatswiri a maphunziro a Baibulo aŵa: Jamieson, Fausset, ndi Brown, anafotokoza kuti mezim·mahʹ ndiko “kusamala kuti upeŵe choipa ndi kupeza chabwino.” Zimenezi zikutanthauza kuganizira zotsatira za zimene tingachite kaya zimene zingatenge nthaŵi yaitali kapena zosakhalitsa. Ngati tili ndi luso la kulingalira, tidzapenda njira zosiyanasiyana zimene tingatsatire tisanasankhe kuti ndi njira iti imene titsatire, makamaka ngati tikufuna kusankha chochita pankhani yofunika kwambiri.

Munthu amene ali ndi luso la kulingalira, posankha zoti achite zokhuza m’tsogolo kapena zokhudza mmene zinthu zilili kwa iye pakalipano, amayamba kaye wapenda ngozi ndi mbuna zimene zingakhalepo. Akaona kuti ndi ngozi zotani zimene zingakhalepo, amapeza mmene angapeŵere zimenezo, akumaganizira mmene malo omwe iye ali ndiponso anzake zingawakhudzire. Ndiyeno angatsatire njira imene ingabweretse zotsatira zabwino, ngakhalenso madalitso a Mulungu. Tiyeni tikambirane zina mwa zitsanzo zothandiza mmene munthu angachitire zimenezi.

Peŵani Msampha wa Chiwerewere

Mphepo ikamakankha mafunde amphamvu mowombana ndi kutsogolo kwa boti, amawatcha mafunde a kutsogolo. Oyenda panyanjawo amakhala pangozi yakuti botilo likhodza kutembenuzika ngati sakudutsa mafundewo mwaluso.

Timakumana ndi zinthu zofanana ndi zimenezi pamene tikukhala m’dziko lino lodzaza ndi nkhani za kugonana. Tsiku lililonse timamva mawu ndi kuona zithunzi zosonyeza kugonana. Sitiyenera kunyalanyaza mmene zimenezi zingakhudzire chilakolako chathu chachibadwa chofuna kugonana. Tiyenera kugwiritsira ntchito luso la kulingalira ndi kuthana ndi zokopa zimenezi kotheratu, mmalo mochita zinthu zimene zingatibweretsere mavuto.

Mwachitsanzo, amuna achikristu nthaŵi zambiri amagwira ntchito limodzi ndi amuna ena amene salemekeza kwambiri akazi, ndipo amangowaona ngati zinthu zogonana nazo basi. Anthu ogwira nawo ntchitowo angamakambe nkhani zolaula ndiponso mawu oipa onena za kugonana. M’kupita kwa nthaŵi, zimenezi zingachititse Mkristu kuganizira zinthu zoipa.

Mkazi wachikristu wotinso ali pa ntchito angakumane ndi mavuto kuntchitoko. Angamagwire ntchito ndi amuna ndiponso akazi amene makhalidwe awo ndi osiyana ndi ake. Mwina mmodzi mwa amuna amene akugwira naye ntchito limodzi angasonyeze kuti akumufuna. Poyamba, mwamunayo angamamukomere mtima mlongoyo, ngakhalenso kulemekeza zikhulupiriro zake zachipembedzo. Khama lake ndi kulankhula kapena kuchita naye zinthu zina pafupipafupi kungachititse mlongoyo kufuna kuti azicheza naye kwambiri.

Ife monga Akristu, kodi luso la kulingalira lingatithandize bwanji zinthu zikatere? Choyamba, lingatichenjeze za ngozi zauzimu, ndipo chachiŵiri, lingatilimbikitse kutsatira njira yoyenera. (Miyambo 3:21-23) M’zochitika ngati zimenezi, pangafunike kuwauza amene tikugwira nawo ntchitowo mosapita m’mbali kuti makhalidwe athu ndi osiyana chifukwa cha zikhulupiriro zathu za m’Malemba. (1 Akorinto 6:18) Kalankhulidwe kathu ndi khalidwe lathu zingalimbikitse uthengawo. Ndiponso, pangafunike kuchepetsa kuchita zinthu ndi ena mwa amene tikugwira nawo ntchito.

Komabe, zinthu zimene zingasonkhezere munthu kuchita zoipa sizimangopezeka kuntchito kokha. Zingabukenso ngati anthu okwatirana alola kuti mavuto afooketse mgwirizano wawo. Mtumiki wina woyendayenda anati: “Kutha kwa ukwati sikumangochitika mwadzidzidzi. Anthu okwatiranawo angamapatukane m’maganizo pang’onopang’ono, kumangolankhulana mwa apa ndi apo kapena nthaŵi zambiri osachezera limodzi. Ndiyeno angamafunefune zinthu zakuthupi kuti apeze chimwemwe chimene chikukanika m’banjamo. Ndipo popeza kaŵirikaŵiri sakhalira limodzi, mwamunayo angakopeke ndi akazi ena ndipo mkaziyo angakopeke ndi amuna ena.”

Mtumikiyu yemwe watumikira kwa nthaŵi yaitali anapitiriza kuti: “Anthu okwatirana ayenera kukhala pansi nthaŵi zambiri n’kukambirana ngati pali chinachake chimene chikuwononga ukwati wawo. Ayenera kukonza mmene angamaphunzirire, kupemphera ndi kulalikira limodzi. Angapindule kwambiri ngati alankhulana ‘m’nyumba, poyenda panjira, pogona, ndiponso pouka,’ monga mmene makolo ayenera kuchitira ndi ana awo.”​—Deuteronomo 6:7-9.

Kulimbana ndi Khalidwe Lotsutsana ndi Chikristu

Kuwonjezera pa kutithandiza kuthana bwinobwino ndi zokopa zoipa, luso la kulingalira lingatithandizenso kulimbana ndi mavuto okhudza Akristu anzathu. Mphepo ikamakankha mafunde omenya kumbuyo kwa boti, amatchedwa mafunde a m’mbuyo. Mafundewo anganyamule mbali ya kumbuyo ya botilo n’kulikankhira cha m’mbali. Zimenezi zingachititse mafundewo kumamenya m’mbali mwa botilo ndipo likhoza kuwonongeka.

Ifenso tingakumane ndi ngozi imene ingachokere kumene sitinali kuyembekezera. Timatumikira Yehova “ndi mtima umodzi” pamodzi ndi abale ndi alongo athu achikristu ambiri okhulupirika. (Zefaniya 3:9) Wina akachita zinthu zotsutsana ndi Chikristu, zingaoneke ngati kusakhulupirika ndipo zingativutitse maganizo kwambiri. Kodi luso la kulingalira lingatithandize bwanji kupeŵa kusasamala ndiponso kuipidwa monkitsa?

Kumbukirani kuti “palibe munthu wosachimwa.” (1 Mafumu 8:46) Motero, tisadabwe ngati nthaŵi zina mbale wachikristu atikhumudwitsa kapena kutilakwira. Podziŵa zimenezi, tingakonzekere kuti zoterezi zitha kuchitika ndipo tingasinkhesinkhe mmene tingachitire. Kodi mtumwi Paulo anatani pamene abale ake ena achikristu analankhula za iye mom’pweteketsa mtima ndiponso mwachipongwe? Iye m’malo mosiya kuchita zinthu zauzimu, anaona kuti kuyanjidwa ndi Yehova kunali kofunika kwambiri kuposa kuyanjidwa ndi anthu. (2 Akorinto 10:10-18) Maganizo otero angatithandize kupeŵa kuchita zinthu mwaphuma wina akatilakwira.

Zimenezi zikufanana ndi kuphunthwa chala. Tikaphunthwa, mtima ungakhale m’malere kwa mphindi imodzi kapena ziŵiri. Koma kuwawako kukacheperapo, tingaganize mwanzeru ndi kuchita zinthu moyenera. Mofananamo, musachite zinthu mopupuluma wina akakulankhulani mokhadzula kapena kukuchitirani zinthu zina zolakwika. M’malo mwake, khazikani mtima pansi ndi kulingalira zomwe zingachitike mukabwezera mosaganizira bwino.

Malcolm, yemwe wachita umishonale kwa zaka zambiri, anafotokoza zimene amachita wina akamulakwira. “Choyamba ndimadzifunsa mafunso amene ndinawakonza kale: Kodi ndamukwiyira mbaleyu chifukwa chakuti tasiyana maganizo? Kodi zimene ananena n’zodetsa nkhaŵa kwambiri? Kodi mphamvu ya matenda a malungo m’thupi langa ndi imene yawonjezera mkwiyo wanga? Kodi ndidzaganiza mosiyana ndi mmene ndikuganizira pakalipano pakapita maola angapo?” Nthaŵi zambiri, monga mmene Malcolm anaonera, kusagwirizanako kungakhale kosadetsa nkhaŵa kwenikweni ndipo munthu akhoza kungokunyalanyaza. *

Malcolm anawonjezera kuti: “Nthaŵi zina, ngakhale nditayesetsa kuthetsa vutolo, mbale winayo amakhalabe ndi mkwiyo. Ndimayesetsa kusalola zimenezi kundisokoneza. Ndikachita zonse zomwe ndingathe, ndimaiona nkhaniyo mwa njira ina. M’maganizo mwanga ndimaika nkhaniyo pambali monga yoti idzatha m’kupita kwa nthaŵi m’malo moganiza kuti ndiithetse ndekha. Sindingalole kuti indivulaze mwauzimu kapena kusokoneza ubwenzi wanga ndi Yehova ndiponso ndi abale anga.”

Mofanana ndi Malcolm, tisalole khalidwe loipa la munthu wina kutisokoneza mopambanitsa. Mumpingo uliwonse muli abale ndi alongo ambiri osangalatsa ndiponso okhulupirika. Zimasangalatsa kuyenda m’njira yachikristu “ndi moyo umodzi” ndi abale otereŵa. (Afilipi 1:27) Kukumbukira thandizo lachikondi la Atate wathu wakumwamba kungatithandizenso kuona zinthu moyenera.​—Salmo 23:1-3; Miyambo 5:1, 2; 8:12.

Osakonda Zinthu za Dziko

Luso la kulingalira lingatithandize kulimbana ndi zosonkhezera zina zazing’ono. Mphepo ikamakankha mafunde n’kumamenya m’mbali mwa boti, amawatcha mafunde a m’mbali. Ngati mphepo yake si ya namondwe, mafunde otereŵa angakankhe pang’onopang’ono botilo n’kulichititsa kuti lisalondole kumene likufuna kupita. Koma kukakhala namondwe, mafunde a m’mbali ameneŵa angatembenuze boti.

Mofananamo, ngati tikopeka kuti tikhale ndi zinthu zonse zimene dziko loipali limapereka, moyo wokondetsa chuma umenewu ungatisocheretse mwauzimu. (2 Timoteo 4:10) Ngati sitisamala, m’kupita kwa nthaŵi kukonda dziko kungatichotseretu pa njira yachikristu. (1 Yohane 2:15) Kodi luso la kulingalira lingatithandize bwanji?

Choyamba, lidzatithandiza kuona ngozi zimene tingakumane nazo. Dziko likugwiritsa ntchito kutsatsa malonda konyengerera kwa mtundu uliwonse kuti tikopeke. Limalimbikitsa mosalekeza moyo wooneka ngati aliyense ayenera kukhala nawo​—moyo wa kutapa kutaya wa anthu olemera, anthu otsogola, ndiponso anthu “opambana.” (1 Yohane 2:16) Limatilonjeza kuti aliyense adzatiyamikira ndi kutikonda, makamaka anzathu ndi anthu amene tikukhala nawo pafupi. Luso la kulingalira lidzatithandiza kuthana ndi bodza limeneli, kutikumbutsa kufunika ‘kosakonda chuma,’ popeza Yehova watilonjeza kuti ‘sadzatisiya.’​—Ahebri 13:5.

Chachiŵiri, luso la kulingalira lidzatithandiza kupeŵa kutsatira anthu amene “adasokera kunena za choonadi.” (2 Timoteo 2:18) N’zovuta kutsutsa anthu amene tinali kuwakonda ndi kuwakhulupirira. (1 Akorinto 15:12, 32-34) Ngakhale zochita za anthu amene anachoka m’chikristu zitamatikhudza pang’ono chabe, zingasokoneze kupita kwathu patsogolo mwauzimu ndipo m’kupita kwa nthaŵi zingatiike pangozi. Tingakhale ngati ngalawa imene yangopatuka pang’ono pa njira imene inayenera kutsatira. Ikayenda ulendo wautali, ngalawa yoteroyo ingasokere ndi mtunda wautali pa malo amene imafuna kupita.​—Ahebri 3:12.

Luso la kulingalira lingatithandize kuzindikira malo amene tili mwauzimu ndi kumene tikupita. Mwina tingazindikire kuti tifunika kugwira nawo ntchito zachikristu mokulira. (Ahebri 6:11, 12) Taonani mmene mnyamata wina wa Mboni anagwiritsira ntchito luso la kulingalira kuti alondole zolinga zauzimu: “Ndinali ndi mwayi wodzagwira ntchito ya utolankhani. Ntchito imeneyi inali kundisangalatsa kwambiri, koma ndinakumbukira vesi la m’Baibulo limene limati ‘dziko lapansi lipita,’ koma ‘iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.’ (1 Yohane 2:17) Ndinaganiza kuti zochita zanga m’moyo ziyenera kusonyeza zikhulupiriro zanga. Makolo anga anali atachoka m’chikristu ndipo sindinafune kutsatira chitsanzo chawo. Motero, ndinaganiza zokhala ndi cholinga pa moyo wanga ndipo ndinalembetsa utumiki wa nthaŵi zonse n’kukhala mpainiya wokhazikika. Papita zaka zinayi tsopano, ndipo ndikuona kuti ndinasankha bwino.”

Kukwanitsa Kulimbana ndi Namondwe Wauzimu

N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kukhala ndi luso la kulingalira masiku ano? Oyenda panyanja amayenera kukhala tcheru ndi zizindikiro zosonyeza kuti ngozi ikhoza kuchitika, makamaka namondwe akamayamba. Kukamazizira kwambiri ndiponso mphepo ikamalimbikira, iwo amakunga chinsalu choteteza ngalawayo ndi kukonzekera nyengo yoipa kwambiri. Mofananamo, tiyenera kukonzekera kukumana ndi mavuto aakulu pamene dongosolo la zinthu loipa lino likuyandikira mapeto ake. Makhalidwe abwino akuchepa ndipo ‘anthu oipa akuipa chiipire.’ (2 Timoteo 3:13) Monga mmene oyenda panyanja nthaŵi zonse amamvetsera odziŵa za nyengo akamafotokoza mmene nyengo ikhalire, tiyenera kumvera machenjezo aulosi a Mawu ouziridwa a Mulungu.​—Salmo 19:7-11.

Tikamagwiritsa ntchito luso la kulingalira, timatsatira chidziŵitso chimene chingatithandize kudzapeza moyo wosatha. (Yohane 17:3) Tingaganizire za mavuto amene angabwere ndi kuona mmene tingawathetsere. Motero, tidzatsimikiza mtima kuti tisapatutsidwe pa njira yachikristu, ndipo tingaike “maziko okoma ku nyengo ikudzayi” mwa kukonza ndi kutsatira zolinga zauzimu.​—1 Timoteo 6:19.

Ngati titeteza nzeru yeniyeni ndi luso la kulingalira, sitidzafunika ‘kuopa zoopsa zodzidzimutsa.’ (Miyambo 3:21, 25, 26) M’malo mwake, tingasangalale ndi lonjezo la Mulungu lakuti: “Nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira.”​—Miyambo 2:10, 11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Akristu ayenera kuyesetsa kulimbikitsa mtendere, mogwirizana ndi malangizo amene ali pa Mateyu 5:23, 24. Ngati nkhaniyo ndi yokhudza machimo aakulu, Mkristu ayenera kuyesetsa kubweza mbale wake, monga mmene akufotokozera pa Mateyu 18:15-17. Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1999 masamba 17-22.

[Chithunzi patsamba 23]

Kulankhulana nthaŵi zonse kumalimbitsa ukwati