Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mudzakhalabe Wokhulupirika?

Kodi Mudzakhalabe Wokhulupirika?

Kodi Mudzakhalabe Wokhulupirika?

KODI ndi mpheta zingati zimene zafa dzulo? Palibe akudziŵa, ndipo mwina ndi ochepa amene angakhale ndi chidwi chofuna kudziŵa chifukwa pali mbalame zambirimbiri. Komatu, Yehova amaikirapo mtima kwambiri. Yesu pofotokoza za mbalame zing’onozing’ono zimenezi, anauza ophunzira ake kuti: “Imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziŵa, NW].” Anapitiriza kuti: “Musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.”​—Mateyu 10:29, 31.

Patapita nthaŵi, ophunzirawo anamvetsa bwino mmene Yehova anali kuwaonera kukhala ofunika kwambiri. Mmodzi mwa iwo, mtumwi Yohane, analemba kuti: “Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anam’tuma Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.” (1 Yohane 4:9) Yehova anapereka dipo ndiponso amatsimikizira mtumiki wake aliyense kuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”​—Ahebri 13:5.

Inde, chikondi cha Yehova kwa anthu ake n’chosagwedera. Koma funso n’lakuti: ‘Kodi ife timakonda kwambiri Yehova moti sitidzamusiya?

Zimene Satana Amachita Kuti Aswe Kukhulupirika Kwathu

Yehova atauza Satana kuti Yobu anali wokhulupirika, Satana anayankha kuti: “Kodi Yobu akanakulambirani inu ngati akanakhala kuti sakupindulapo kanthu?” (Yobu 1:9, Today’s English Version) Iye anasonyeza kuti kukhulupirika kwa anthu kwa Mulungu kumadalira ‘zimene iwo angapindulepo.’ Ngati zimenezi zikanakhala zoona, Mkristu aliyense akanaleka kukhulupirika ngati zimene anapatsidwa kuti aswe kukhulupirikako zinali zabwino kwambiri.

Pa nkhani ya Yobu, Satana poyamba ananena kuti Yobu akanaleka kukhulupirika kwa Mulungu ngati katundu wake amene anali kum’dalira akanawonongeka. (Yobu 1:10, 11) Kuneneza kumeneku kutapezeka kuti kunali kwabodza, Satana anati: “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Ngakhale kuti zimene Satana ananenazi zingakhale zoona kwa ena, Yobu anakana kutaya kukhulupirika kwake. Nkhani yake imatsimikizira zimenezo. (Yobu 27:5; 42:10-17) Kodi ndinu wokhulupirira mofanana ndi iye? Kapena kodi mudzalola kuti Satana aswe kukhulupirika kwanu? Dziganizireni nokha pamene tikukambirana mfundo za choonadi zotsatirazi zimene zikukhudza Mkristu aliyense.

Mtumwi Paulo anakhulupirira kuti kukhulupirika kwenikweni kwachikristu kungakhale kwamphamvu kwambiri. Analemba kuti: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, . . . ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, . . . ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:38, 39) Tingakhalenso ndi chikhulupiriro chonga chimenechi ngati timakonda kwambiri Yehova. Chikondi choterocho n’cholimba kwambiri moti ngakhale imfa siingachithetse.

Ngati tili ndi ubwenzi woterowo ndi Mulungu, sitidzafunsa kuti: ‘Kodi ndidzakhala ndikutumikirabe Yehova m’zaka zingapo zikubwerazi?’ Kukayikira koteroko kungasonyeze kuti kukhulupirika kwathu kwa Mulungu kukudalira zimene zingatichitikire m’moyo wathu. Kukhulupirika kwenikweni sikukhudzidwa ndi zimene zingatichitikire. Kumadalira mmene tilili m’kati mwathu. (2 Akorinto 4:16-18) Ngati timakonda Yehova ndi mtima wathu wonse, sitidzam’khumudwitsa.​—Mateyu 22:37; 1 Akorinto 13:8.

Komabe, tizikumbukira kuti Satana nthaŵi zonse amafuna kuti aswe kukhulupirika kwathu. Iye angatikope kuti titsatire zilakolako za thupi, kugonjera zimene anzathu akutilimbikitsa kuchita, kapena kulola mavuto ena kutisiyitsa choonadi. Dziko losaopa Mulunguli ndi chinthu china chachikulu chimene chimathandizira Satana kuti tiswe kukhulupirika kwathu, ngakhale kuti kupanda ungwiro kwathunso kumachititsa kuti iye asavutike kuchita ntchito yakeyi. (Aroma 7:19, 20; 1 Yohane 2:16) Komabe, tili ndi zinthu zambiri zimene zingatithandize pomenya nkhondo imeneyi, ndipo chachikulu kwambiri mwa zinthu zimenezi ndicho mfundo yakuti timadziŵa machenjerero a Satana.​—2 Akorinto 2:11.

Kodi machenjerero a Satana ndi otani? Paulo anafotokoza m’kalata yake kwa Aefeso za “machenjerero” ameneŵa. (Aefeso 6:11) Satana amagwiritsa ntchito machenjerero ake kuti tiswe kukhulupirika kwathu. N’zokondweretsa kuti tingadziŵe machenjerero ameneŵa, popeza njira za Mdyerekezi zinalembedwa m’Mawu a Mulungu kuti zitithandize. Zimene Satana anachita kuti aswe kukhulupirika kwa Yesu ndi Yobu zikupereka chitsanzo cha njira zina zimene amagwiritsa ntchito kuti aswe kukhulupirika kwathu kwachikristu.

Analephera Kuswa Kukhulupirika kwa Yesu

Kuchiyambi kwa utumiki wa Yesu, Satana analimba mtima kuyesa Mwana wa Mulungu ameneyu mwa kumuuza kuti asandutse mwala ukhale mkate. Kuchenjera kwakeko inu! Yesu anali asanadye kwa masiku 40, motero n’zosakayikitsa kuti anali ndi njala zedi. (Luka 4:2, 3) Satana anafuna kuti Yesu akhutiritse chilakolako chake chachibadwa mwamsanga, mwa njira yotsutsana ndi chifuniro cha Yehova. N’chimodzimodzinso masiku ano. Zonyengerera za dzikoli zimalimbikitsa kukwaniritsa zilakolako zathu nthaŵi yomweyo, osaganizira kwenikweni zotsatira zake. Uthenga wake umakhala wakuti: ‘Ukuyenerera zimenezi pakalipano,’ kapena, ‘Ingochita!’

Ngati Yesu akanathetsa njala yake popanda kuganizira zimene zingachitike, Satana akanapambana pom’chititsa Yesu kuswa kukhulupirika kwake. Yesu anaiona nkhaniyo mwauzimu, ndipo anayankha molimba mtima kuti: “Kwalembedwa, kuti, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.”​—Luka 4:4; Mateyu 4:4.

Ndiyeno Satana anasintha machenjera ake. Pogwiritsa ntchito Malemba molakwika, omwenso Yesu anawagwira mawu, Mdyerekezi anauza Yesu kuti adziponye kuchokera pamwamba pa chimbudzi cha kachisi. ‘Mngelo akutchinjiriza,’ anatero Satana. Yesu sanafune kulamula Atate wake kuti amutetezere mozizwitsa n’cholinga choti angodzionetsera ayi. Yesu anati: “Usamuyese Ambuye Mulungu wako.”​—Mateyu 4:5-7; Luka 4:9-12.

Machenjera omaliza amene Satana anagwiritsa ntchito anali osapita m’mbali. Anafuna kusinthana zinthu ndi Yesu mwa kumuuza kuti am’patsa dziko lonse ndi ulemerero wake ngati atangom’gwadira chabe posonyeza kum’lambira. Satana anafuna kupereka pafupifupi chilichonse. Koma kodi Yesu akanalambira bwanji mdani wamkulu wa Atate wake? Sakanayerekeza! “Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekhayekha udzam’lambira,” anayankha motero Yesu.​—Mateyu 4:8-11; Luka 4:5-8.

Mayesero atatu onsewo atakanika, Satana ‘anam’leka Yesu kufikira nthaŵi ina.’ (Luka 4:13) Zimenezi zikusonyeza kuti Satana nthaŵi zonse anali maso psuu, kufunafuna mpata woti ayese kukhulupirika kwa Yesu. Nthaŵi inayo inapezeka patapita zaka ziŵiri ndi theka pamene Yesu anayamba kukonzekeretsa ophunzira ake za imfa yake imene inatsala pang’ono. Mtumwi Petro anati: “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ayi.”​—Mateyu 16:21, 22.

Kodi n’kutheka kuti malangizo ameneŵa omwe anali n’cholinga chabwino koma olakwika anam’sangalatsa Yesu popeza anachokera kwa mmodzi mwa ophunzira ake? Yesu anazindikira mwamsanga kuti mawu amenewo anasonyeza maganizo a Satana osati a Yehova. Kristu anayankha mwamphamvu kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.”​—Mateyu 16:23.

Yesu anakonda kwambiri Yehova ndipo chifukwa cha zimenezi, Satana analephera kuswa kukhulupirika kwake. Palibe chimene Mdyerekezi akanapereka, kaya akhale mayesero oopsa bwanji, chimene chikanafooketsa kukhulupirika kwa Yesu kwa Atate wake wakumwamba. Kodi ifenso tidzatsimikiza mtima chimodzimodzi ngati zinthu zitathina n’kukhala kovuta kuti tikhulupirikebe? Chitsanzo cha Yobu chingatithandize kudziŵa bwino mavuto amene tingakumane nawo.

Kukhulupirika Polimbana ndi Mavuto

Monga mmene Yobu anaonera, tingakumane ndi mavuto nthaŵi ina iliyonse. Yobu anali ndi banja lachimwemwe, ana khumi, ndiponso anali ndi chizoloŵezi chabwino chochita zinthu zauzimu. (Yobu 1:5) Koma Yobu sanadziŵe kuti panali kusagwirizana ku mabwalo akumwamba pankhani ya kukhulupirika kwake kwa Mulungu, ndipo Satana anatsimikiza mtima kuti aswe kukhulupirika kwa Yobu mwa njira iliyonse imene akanatha.

Posakhalitsa, chuma cha Yobu chinawonongeka. (Yobu 1:14-17) Komabe, kukhulupirika kwa Yobu kunagonjetsa mayesero ameneŵa chifukwa mtima wake sunali pa ndalama. Poganizira za nthaŵi imene anali wolemera, Yobu anati: “Ngati ndayesa golidi chiyembekezo changa, . . . ngati ndinakondwera popeza chuma changa n’chachikulu, . . . ichinso ndi mphulupulu . . . pakuti ndikadakana Mulungu ali m’mwamba.”​—Yobu 31:24, 25, 28.

Masiku ano n’zothekanso kuti katundu wathu yense awonongeke m’kanthaŵi kochepa chabe. Mwamuna wina wabizinesi yemwe ndi Mboni ya Yehova anam’bera mwachinyengo ndalama zambiri, ndipo zimenezi zinam’chititsa kukhala wopanda kalikonse. Iye anavomereza mosabisa mawu kuti: “Ndinatsala pang’ono kudwala nthenda ya mtima. Ndipo, pakanapanda ubwenzi wanga ndi Mulungu, ndikuganiza kuti ndikanadwala nthendayi. Komabe, zimenezi zandithandiza kuzindikira kuti zinthu zauzimu sizinali pa malo oyamba m’moyo wanga. Kufuna kupeza ndalama kunali patsogolo kuposa china chilichonse.” Mboni imeneyi kuyambira nthaŵi imeneyo yachepetsa bizinesi yake, ndipo imachita upainiya wothandiza nthaŵi zambiri, kuthera maola 50 kapena kuposerapo pa mwezi mu utumiki wachikristu. Komabe, mavuto ena angakhale opweteka kwambiri kuposa kuwonongeka kwa katundu.

Yobu atangolandira kumene uthenga wa kuwonongeka kwa chuma chake, analandiranso uthenga wakuti ana ake khumi amwalira. Iye analimbikirabe kuti: “Lidalitsike dzina la Yehova.” (Yobu 1:18-21) Kodi tidzakhulupirikabe ngati mwadzidzidzi achibale athu angapo amwalira? Ana aŵiri a Francisco, woyang’anira wachikristu ku Spain, anamwalira pa ngozi ya basi yomvetsa chisoni. Anapeza chilimbikitso mwa kuyandikira kwambiri kwa Yehova ndi kuwonjezera zochita zake mu utumiki wachikristu.

Ngakhale pamene ana a Yobu anali atamwalira momvetsa chisoni, mavuto ake anali asanathe. Satana anakantha Yobu ndi nthenda yoipa, yopweteka kwambiri. Zitatero, Yobu analandira malangizo oipa kwa mkazi wake. Mkaziyo anati: “Chitira Mulungu mwano, ufe.” Yobu sanamvere malangizo amenewo, ndipo iye “sanachimwa ndi milomo yake.” (Yobu 2:9, 10) Kukhulupirika kwake kunadalira ubwenzi wake ndi Yehova, osati zimene a m’banja mwake akanamuuza.

Flora, yemwe mwamuna wake ndi mwana wake wamwamuna wamkulu anachoka m’Chikristu zaka zoposa khumi zapitazo, akumvetsa mmene Yobu ayenera kuti anavutikira maganizo. Iye anati: “Zimapweteka kwambiri a m’banja lako akaleka kukulimbikitsa. Koma ndinadziŵa kuti sindikanapeza chimwemwe kunja kwa gulu la Yehova. Motero, ndinachirimika ndi kuika Yehova pamalo oyamba uku ndikuyesetsa kukhalabe mkazi ndiponso mayi wabwino. Ndinali kupemphera mosalekeza, ndipo Yehova anandilimbitsa. Ndine wosangalala chifukwa ngakhale kuti mwamuna wanga amanditsutsa kwambiri, ndaphunzira kudalira Yehova kotheratu.”

Kenako machenjera amene Satana anagwiritsa ntchito pofuna kuswa kukhulupirika kwa Yobu anadzera mwa anzake atatu. (Yobu 2:11-13) Ziyenera kuti zinali zopweteka pamene anayamba kum’dzudzula. Ngati akanatsatira mfundo zawo, akanaleka kukhulupirira Yehova Mulungu. Malangizo awo ofooketsa akanamukhumudwitsa ndi kuswa kukhulupirika kwake ndipo machenjera a Satana akanapambana.

M’malo mwake, Yobu analimbikira kuti: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga [“kukhulupirika kwanga,” NW].” (Yobu 27:5) Iye sananene kuti, ‘Sindilola kuti anthu inu munditayire kukhulupirika kwanga.’ Yobu anadziŵa kuti kukhulupirika kwake kunadalira iyeyo ndi kukonda kwake Yehova.

Kugwiritsa Ntchito Machenjera Akale Pofuna Kunyenga Anthu Masiku Ano

Satana akugwiritsabe ntchito malangizo olakwika kapena mawu opanda nzeru a mabwenzi athu kapena okhulupirira anzathu. Zokhumudwitsa zochokera mumpingo zingafooketse kukhulupirika kwathu mosavuta kusiyana ndi chizunzo chochokera kunja kwa mpingo. Mkulu wina wachikristu amene anamenyapo nkhondo monga msilikali anasiyanitsa kupweteka kwa nkhondo ndi kupweteka kumene anamva chifukwa cha mawu ndi zochita zosaganizira ena za Akristu anzake. Pofotokoza za zokhumudwitsa zochokera kwa Akristu anzake, iye anati: “N’zopweteka kwambiri kuposa zina zilizonse zimene ndakumana nazo.”

Komanso, tingakhumudwe kwambiri ndi kupanda ungwiro kwa okhulupirira anzathu mpaka kusiya kulankhula ndi ena mwa iwo kapena ngakhale kuyamba kujomba kumisonkhano yachikristu. Kuthetsa kupwetekedwa mtima kumene tili nako kungaoneke ngati nkhani yaikulu kwambiri. Koma zingakhaletu zomvetsa chisoni kwambiri ngati tikhala ndi maganizo opanda nzeru oterowo ndi kulola kuti ubwenzi wathu ndi Yehova womwe ndi wamtengo wapatali kuposa china chilichonse, uwonongeke chifukwa cha zimene ena akuchita kapena kunena. Ngati tilola zimenezo kuchitika, ndiye kuti tikunyengedwa ndi machenjera a Satana amene anali kuwagwiritsanso ntchito kale.

N’zoona kuti timayembekezera makhalidwe apamwamba mumpingo wachikristu. Koma ngati tiyembekeza kuti okhulupirira anzathu, omwe ndi opanda ungwiro, azichita zoposa zimene angathe, mosakayika tidzakhumudwa. Mosiyana ndi zimenezo, Yehova sayembekezera atumiki ake kuchita zimene sangathe. Ngati titsanzira chitsanzo chake, tidzakhala okonzeka kupirira kupanda ungwiro kwawo. (Aefeso 4:2, 32) Mtumwi Paulo anapereka malangizo aŵa: “Ngati mwakwiya, musalole kuti mkwiyowo ukuchimwitseni; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire; musam’patse danga mdyerekezi.”​—Aefeso 4:26, 27, The New English Bible.

Monga mmene Baibulo likusonyezera, Satana amagwiritsa ntchito machenjera osiyanasiyana kuti apeze njira yoswera kukhulupirira kwa Mkristu ngati angathe kutero. Machenjera ake ena amasangalatsa thupi lochimwali pamene ena ndi obweretsa mavuto. Malinga ndi zimene takambiranazi, mungaone chifukwa chake simuyenera kugwidwa mosadziŵa. Mwa kukonda kwanu Mulungu ndi mtima wonse, tsimikizani kusonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza ndipo sangalatsani mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11; Yohane 8:44) Kumbukirani kuti kukhulupirika kwachikristu kwenikweni sikuyenera kusweka, ngakhale titakumana ndi mayesero otani.