“Kodi Mukudziŵa Chifukwa Chomwe Ndikukubwezerani Ndalama Zanu?”
“Kodi Mukudziŵa Chifukwa Chomwe Ndikukubwezerani Ndalama Zanu?”
‘HA, N’TANGOPEZA ndalama ine!’ anatero Nana, mayi wa ana atatu, yemwenso alibe mwamuna. Mayiyu akukhala ku Kaspi m’dziko la Republic of Georgia. Tsiku lina m’mawa, ndalama zomwe ankazifuna zija anazipeza. Iye anatola ndalama zokwana 300 lari (madola 150 a ku United States) pafupi ndi maofesi apolisi. Anatola ndalamazo ali yekha. Zinalitu ndalama zambiri. Ndiponsotu Nana anali asanaionepo 100 lari yapepala chiikhazikitsireni zaka zisanu zapitazo kukhala ndalama yadzikolo. Amalonda a m’dzikolo sangapeze ndalama zochuluka ngati zimenezo atagwira ntchito kwa zaka zingapo.
Nana anadzifunsa kuti: ‘Kodi ndalamazi n’zaphindu lanji ngati n’tataya chikhulupiriro changa, mantha anga aumulungu, ndiponso khalidwe langa lauzimu?’ Iye anali atakulitsa mikhalidwe yachikristu imeneyi moti anapirirapo chizunzo choopsa ngakhale kumenyedwa kumene chifukwa cha chikhulupiriro chake.
Nana atapita kupolisiko, anaona maofesala asanu akufunafuna chinachake. Iye anazindikira kuti akufunafuna ndalama ndipo anawayandikira n’kuwafunsa kuti: “Kodi mwataya chinachake?”
“Tataya ndalama,” iwo anatero.
“Zingati?”
“300 lari!”
Nana anati: “Ndatola ndine ndalama zanu.” Kenako anawafunsa kuti: “Kodi mukudziŵa chifukwa chomwe ndikukubwezerani ndalama zanu?” Iwo sanadziŵe.
Nana anapitiriza kuti, “chifukwa chakuti ndine wa Mboni za Yehova. N’kanakhala kuti si ndine wa Mboni, sindikanakubwezerani ndalama zanu.”
Mkulu wa apolisi amene anataya ndalamazo anam’patsa Nana chionamaso chandalama zokwana 20 lari pom’thokoza chifukwa cha kuona mtima kwake.
Nkhaniyi inafala mofulumira m’chigawo chonse cha Kaspi. Tsiku lotsatira, mayi wina yemwe amagwira ntchito yokonza m’maofesi akupolisiko anauza Nana kuti: “[Mkulu wa apolisi] amakhala ndi mabuku anu nthaŵi zonse muofesi yake. Mwina tsopano adzaona ubwino wake.” Ofesala wapolisi wina mpaka ananena kuti: “Anthu onse akanakhala a Mboni za Yehova, ndani akanaswa malamulo?”