Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Yesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:
• Kodi chisoni n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani Akristu ayenera kukulitsa khalidwe limeneli?
Chisoni ndicho kutha kudziyerekeza uli m’mavuto amene akuchitikira munthu wina. Akristu amalangizidwa kukhala “ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni.” (1 Petro 3:8) Yehova anatipatsa chitsanzo kuti ife titsatire pankhani yosonyeza chisoni. (Salmo 103:14; Zekariya 2:8) Tingakulitse chisoni chathu mwa kumvetsera, kuona, ndiponso kuyerekezera.—4/15, masamba 24-26.
• Kuti tipeze chimwemwe chenicheni, n’chifukwa chiyani kuchiritsa kwauzimu kuyenera kuchitika kaye kuchiritsa kwenikweni kusanachitike?
Anthu ambiri amene ali ndi thanzi labwino sakusangalala, ali ndi mavuto osaneneka. Mosiyana ndi ameneŵa, Akristu ambiri olumala mwakuthupi lerolino akusangalala kwambiri kutumikira Yehova. Amene akupindula ndi kuchiritsa kwauzimu kumeneku adzakhala ndi mwayi wodzachiritsidwa mwakuthupi m’dziko lapansi latsopano.—5/1, masamba 6-7.
• N’chifukwa chiyani Ahebri 12:16 amagwirizanitsa Esau ndi munthu wachigololo?
Nkhani ya m’Baibulo imasonyeza kuti Esau anaika mtima kwambiri pa phindu la nthaŵi yomweyo ndipo sanaone zinthu zopatulika kukhala zofunika kwambiri. Ngati wina lerolino atakhala ndi mtima ngati umenewu, angachite tchimo lalikulu, monga chigololo.—5/1, masamba 10-11.
• Kodi Tertullian anali ndani, ndipo amatchuka ndi chiyani?
Tertullian anali wolemba mabuku ndiponso wamaphunziro apamwamba a zaumulungu yemwe anakhalako m’zaka za m’ma 100 ndi 200 C.E. Iye amatchuka chifukwa cholemba mabuku ambiri olimbikitsa Chikristu cha dzina lokha. Polemba mfundo zakezo, iye anayambitsa maganizo a nzeru ya dziko omwe anayambitsa ziphunzitso zopotoka, monga Utatu.—5/15, masamba 29-31.
• N’chifukwa chiyani sitingaimbe mlandu chibadwa chathu chokha kuti ndicho chimachititsa matenda, khalidwe lathu, ndiponso imfa?
Akatswiri asayansi akunena kuti matenda ambiri a anthu amayamba chifukwa cha chibadwa chathu, ndipo ena akukhulupirira kuti khalidwe la munthu limadalira chibadwa chake. Komabe, Baibulo limapereka mfundo zotsegula maso zokhudza chiyambi cha munthu ndiponso mmene uchimo ndi kupanda ungwiro zinayambira. Ngakhale kuti chibadwa chathu chingasonkhezere khalidwe lathu, kupanda ungwiro kwathu ndiponso malo omwe tikukhala n’zimene zimasonkhezera kwambiri khalidwe lathu.—6/1, masamba 9-11.
• Kodi chidutswa cha mpukutu chimene anachipeza ku Oxyrhynchus, ku Egypt, chikutitsegula maso motani pankhani yogwiritsa ntchito dzina la Mulungu?
Chidutswa chimenechi chomwe chili ndi ndime ya pa Yobu 42:11, 12 yochokera m’Baibulo lachigiriki la Septuagint chili ndi zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu. Umenewu ndi umboni winanso wosonyeza kuti dzina la Mulungu la m’Chihebri linali kupezeka m’Baibulo la Septuagint lomwe olemba Malemba Achigiriki Achikristu analigwira mawu kwambiri.—6/1, tsamba 30.
• Kodi maseŵera omenyana achiwawa ndiponso ophetsa munthu omwe ankachitika mu Ufumu wa Roma ali ngati maseŵera ati a masiku ano?
Chionetsero chaposachedwapa ku bwalo lalikulu la maseŵera la Colosseum ku Rome, Italy, chinasonyeza maseŵera a masiku ano ofanana ndi akalewo mwa kuonetsa mbali zina za vidiyo yosonyeza ng’ombe zikumenyana, anyamata a nkhonya ophunzitsidwa bwino, mpikisano wa magalimoto ndi njinga zamoto, ndiponso zipolowe za oonerera maseŵera a masiku ano m’mabwalo ena azamaseŵera. Akristu oyambirira ankadziŵa bwino kuti Yehova sakonda chiwawa kapena anthu achiwawa, choncho Akristunso lerolino sayenera kukonda chiwawa. (Salmo 11:5)—6/15, tsamba 29.
• Pamene tikuyesetsa kukhala aphunzitsi ogwira mtima, kodi tingaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Ezara?
Ezara 7:10 amatsindika zinthu zinayi zimene Ezara anachita zimenenso ifeyo tingatsatire. Lembali limati: “Ezara [1] adaikiratu [“anakonzekeretsa,” NW ] mtima wake [2] kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi [3] kuchichita, ndi [4] kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.”—7/1, tsamba 20.
• Kodi ndi pa zochitika za mitundu iŵiri ziti pamene mkazi wachikristu ayenera kuvala chophimba kumutu?
Choyamba n’chokhudza kutsogolera pa zochitika zauzimu kunyumba. Kuvala kwake chophimba kumutu kumasonyeza kuzindikira kuti mwamuna wake ndiye ali ndi udindo wopemphera ndiponso kutsogolera phunziro la Baibulo. Chochitika chachiŵiri n’chokhudza kutsogolera pa zochitika za mpingo, pamene amasonyeza kuzindikira kuti abale obatizidwa ndiwo ali oyenera mwa Malemba kuphunzitsa ndiponso kutsogolera. (1 Akorinto 11:3-10)—7/15, masamba 26-7.
• N’chifukwa chiyani Akristu amazindikira kuti maseŵera a yoga si olimbitsa thupi chabe koma kuti pali zinanso ndiponso kuti ndi oopsa?
Cholinga cha maseŵera a yoga ndicho kugwirizanitsa munthu ndi mzimu winawake waukulu. Mosemphana ndi malangizo a Mulungu, maseŵera a yoga amaimitsa luso lachibadwa la kuganiza. (Aroma 12:1, 2) Maseŵera a yoga angaike munthu pangozi yokhulupirira mizimu ndi matsenga. (Deuteronomo 18:10, 11)—8/1, masamba 20-22.