Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Malemba amapereka malangizo otani pankhani yophunzitsa ana ngati kholo lina ndi la Mboni za Yehova ndipo linalo si Mboni?

Pali mfundo za m’Malemba zofunika kwambiri ziŵiri zomwe zingathandize kholo lomwe ndi Mboni pankhani yophunzitsa ana ngati kholo linalo si Mboni. Mfundo yoyamba ndi iyi: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Ndipo yachiŵiri ndi iyi: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia [“mpingo,” NW].” (Aefeso 5:23) Mfundo yachiŵiriyi imagwira ntchito kwa akazi amene amuna awo ndi Mboni komanso kwa akazi amene amuna awo si Mboni. (1 Petro 3:1) Kodi kholo lomwe ndi Mboni lingatsatire bwanji mfundo ziŵirizi nthaŵi imodzi pophunzitsa ana ake?

Ngati mwamuna ndiye wa Mboni za Yehova, ali ndi udindo wopezera banja lake zinthu zofunika pa moyo ndiponso zinthu zauzimu. (1 Timoteo 5:8) Ngakhale kuti mayi wosakhulupirirayo angamakhale nthaŵi yaitali ndi anawo, bambo wa Mboniyo ayenera kuphunzitsa ana ake zinthu zauzimu kunyumba ndiponso kuwatengera kumisonkhano yachikristu, komwe adzapindula ndi malangizo amakhalidwe abwino ndiponso kusangalala ndi macheza abwino.

Nanga bwanji ngati mkazi wosakhulupirirayo akulimbikira zopita ndi anawo ku chipembedzo chake ndiponso kuwaphunzitsa zikhulupiriro zake? Malamulo a m’dzikolo angamupatse ufulu wochita zimenezo. Kaya anawo amakopeka kumalambira nawo akafika kumene amalambirirako, zimenezo mbali yaikulu zingadalire pa kaphunzitsidwe ka zinthu zauzimu ka bamboyo. Pamene anawo akukula, zinthu za m’Malemba zomwe anaphunzira kwa bambo awo ziyenera kuwathandiza kutsatira choonadi cha Mawu a Mulungu. Zingakhaletu zosangalatsa kwambiri kwa mwamuna wokhulupirira ngati ana ake atasankha kutsatira choonadi!

Ngati mayi ndiye wa Mboni za Yehova, iye ayenera kulemekeza mfundo yoti mwamuna ndiye mutu wabanja kwinaku akuganiziranso za tsogolo losatha la ana ake. (1 Akorinto 11:3) Nthaŵi zambiri, mwamuna wosakhulupirirayo sangaletse ngati mkazi wake wa Mboni akuphunzitsa ana makhalidwe abwino ndiponso zinthu zauzimu ngakhalenso kukaphunzira zimenezo kumisonkhano ya anthu a Yehova. Mayiyo angathandize mwamuna wake wosakhulupirirayo kuona phindu la maphunziro abwino omwe anawo akulandira kudzera m’gulu la Yehova. Iye mwanzeru angagogomezere ubwino wophunzitsa anawo mfundo zamakhalidwe abwino za m’Baibulo pamene akukhala m’dziko lopanda khalidweli.

Komabe, mwina mwamuna wosakhulupirirayo angalimbikire zoti anawo azipita ku chipembedzo chake ndiponso kuwaphunzitsa ziphunzitso zake. Kapenanso mwamunayo anganene kuti anawo asaloŵe chipembedzo chilichonse ndiponso asaphunzire chilichonse chokhudza chipembedzo. Monga mutu wabanja, iye ndiye ali ndi mlandu waukulu chifukwa chosankha zimenezo. *

Pamene akulemekeza mwamuna wake monga mutu wabanja, mkazi wokhulupirira monga Mkristu wodzipatulira ayenera kukumbukira maganizo a mtumwi Petro ndiponso mtumwi Yohane omwe ananena kuti: “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Machitidwe 4:19, 20) Poganizira za tsogolo lauzimu la ana ake, mayi wa Mboniyo adzapezabe mipata yolangiza anawo makhalidwe abwino. Iye ali ndi udindo kwa Yehova wophunzitsa anthu kuphatikizapo ana ake zomwe akudziŵa kuti n’zoona. (Miyambo 1:8; Mateyu 28:19, 20) Kodi mayi yemwe ndi Mboni angatani kuti athane ndi vuto lothetsa nzeru limeneli?

Mwachitsanzo, titenge nkhani yokhudza kukhulupirira Mulungu. Mwina mayi yemwe ndi Mboni sangathe kuchititsa phunziro la Baibulo ndi ana ake chifukwa chakuti mwamuna wake amaletsa zimenezo. Kodi iye pachifukwa chimenechi ayenera kusiya kuuza ana akewo chilichonse chokhudza Yehova? Ayi. Zomwe amalankhula ndiponso zochita zake ziyenera kusonyeza kuti amakhulupirira Mlengi. Mosakayika ana akewo adzakhala ndi mafunso pankhaniyi. Iye ayenera kukhala womasuka kukwaniritsa ufulu wake wachipembedzo mwa kulankhula za chikhulupiriro chake mwa Mlengi kwa ena, kuphatikizapo kwa ana ake. Ngakhale kuti sangachititse phunziro la Baibulo ndi anawo kapena kuwatengera kumisonkhano nthaŵi zonse, iye angawaphunzitse za Yehova Mulungu.​—Deuteronomo 6:7.

Ponena za ukwati wa mwamuna yemwe si Mboni ndi mkazi yemwe ndi Mboni kapena mkazi yemwe si Mboni ndi mwamuna yemwe ndi Mboni, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.” (1 Akorinto 7:14) Yehova amaona ukwati ndiponso ana a anthu otereŵa kukhala zoyera chifukwa cha mwamuna kapena mkazi wokhulupirirayo. Mkazi yemwe ndi Mboni ayenera kuchita zonse zomwe angathe kuthandiza ana ake kudziŵa choonadi, n’kusiya zotsatira zake m’manja mwa Yehova.

Anawo akamakula, adzasankha okha zomwe adzatsatire malinga ndi zomwe makolo aŵiriwo anawaphunzitsa. Iwo angasankhe kuchita mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine.” (Mateyu 10:37) Iwo amalamulidwanso kuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye.” (Aefeso 6:1) Ana ambiri asankha ‘kumvera Mulungu monga wolamulira,’ m’malo momvera kholo lawo lomwe si Mboni, ngakhale kuti khololo lingawavutitse kwambiri. Zingakhaletu zosangalatsa zedi kwa kholo lomwe ndi Mboni kuona ana akusankha kutumikira Yehova ngakhale kuti akutsutsidwa!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Ufulu wachipembedzo wa mkazi wake umaphatikizapo kupita kumisonkhano yachikristu. Nthaŵi zina, mwamuna safuna kusamalira ana aang’ono panthaŵi yomwe mkazi wake wapita kumisonkhano, choncho ndi udindo wa mayi wachikondi kupita ndi anawo kumisonkhano.