Anthu Abwino Okhala Nawo Pafupi Ndi Ofunika Kwambiri
Anthu Abwino Okhala Nawo Pafupi Ndi Ofunika Kwambiri
“Mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.”—Miyambo 27:10.
M’ZAKA 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, katswiri wina wamaphunziro anafunsa Yesu kuti: “Mnansi wanga ndani?” Poyankha, Yesu sanamuuze amene anali mnansi wake, koma chimene chimapangitsa munthu kukhala mnansi weniweni. Mosakayikira, fanizo la Yesu limeneli si lachilendo kwa inu. Limatchedwa fanizo la Msamariya wachifundo ndipo linalembedwa mu Uthenga Wabwino wa Luka. Yesu anasimba nkhaniyo motere:
“Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja a achifwamba amene anam’vula zovala, nam’kwapula, nachoka atam’siya wofuna kufa. Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina. Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina. Koma Msamariya wina ali paulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo, nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, nam’sungira. Ndipo mmaŵa mwake anatulutsa malupiya atheka aŵiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse um’patsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe. Uti wa aŵa atatu, uyesa iwe, Luka 10:29-36.
anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?”—Mosakayikira, katswiri wa maphunziroyo anamvetsa mfundo ya fanizolo. Mofulumira anatchula molondola yemwe anali mnansi wa amene anavulazidwa uja, anati: “Iye wakum’chitira chifundo.” Ndiyeno Yesu anati kwa iye: “Pita, nuchite iwe momwemo.” (Luka 10:37) Limeneli ndi fanizo lamphamvu kwambiri losonyeza chimene chimapangitsa munthu kukhala mnansi weniweni. Fanizo la Yesu lingatipangitse kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine mnansi wa mtundu wanji? Kodi mtundu kapena fuko langa limandipangitsa kusankha anansi anga? Kodi zinthu zimenezi zimandilepheretsa kuchita ntchito yanga yothandiza munthu aliyense amene ndaona akuvutika? Kodi ndimayesetsa kukhala mnansi wabwino?’
Kodi Tingayambire Pati?
Ngati tikuona kuti tikufunika kuwongolera pankhani imeneyi, tiyenera kuyamba tawongolera maganizo athu. Nkhaŵa yathu izigona pa kukhala mnansi wabwino. Izi zingatithandizenso kukhala ndi anansi abwino. Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, Yesu pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri ananena motsindika mfundo yofunika pa moyo wa anthu imeneyi. Anati: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Kulemekeza anthu ena ndi kuwakomera mtima kumawalimbikitsa kuti akuchitireni zomwezo.
M’nkhani yakuti “Kukonda Anthu Amene Mumakhala Nawo Pafupi,” imene inatuluka m’magazini ya The Nation Since 1865, Lise Funderburg yemwe ndi mtolankhani komanso wolemba nkhani anatchula zina mwa zinthu zing’onozing’ono zimene tingachitire ena polimbikitsa ubwenzi. Anati: “Ndikufuna . . . tigwirizane pochita zinthu zing’onozing’ono zambiri zabwino zimene anthu oyandikana nyumba amachitirana monga . . . kusungirana ana, kukagulirana zinthu. Ndikufuna kuti pakhale ubale umenewu m’dziko lino limene kusagwirizana kukukulirakulira , ndiponso anthu si otetezeka chifukwa cha mantha ndi upandu.” Ndiyeno anapitiriza kuti: “Muyenera kuyambira penapake. Ndipo mwina mungayambire kwa amene mumakhala nawo pafupi.”
Magazini ya Canadian Geographic inanenanso mfundo imene ingathandize anthu oyandikana nyumba kukhala okomerana mtima. Mlembi wina, Marni Jackson, anati: “Pamoyo wanu, simusankha anthu okhala nawo pafupi monga mmene simusankhira achibale anu. Choncho ubwenzi wake umafuna kuganizirana, kukomerana mtima pa zinthu zina ndiponso kulolerana.”
Anthu Abwino Okhala Nawo Pafupi Amafuna Kupatsa
N’zoona kuti ambirife zimativuta kulankhula anthu amene timakhala nawo pafupi moti kusawalankhula ndiponso kudzipatula n’zomwe zingaoneke zosavuta. Koma, Baibulo limati “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Choncho, mnansi wabwino amayesetsa kuzoloŵerana ndi anthu amene amakhala nawo pafupi. Ngakhale kuti sizikutanthauza kupanga nawo ubwenzi wa ponda apa nane mpondepo, amayesetsa kuwalankhula kaŵirikaŵiri, mwina mwa kungowamwetulira mwaubwenzi kapena kuwatukulira mkono mwansangala.
Monga tanenera, pali “zinthu zing’onozing’ono zambiri zabwino” zimene anthu oyandikana nyumba amachitirana zomwe n’zofunika kwambiri poyambitsa ndi kupitiriza ubwenzi. Choncho ndi bwino kuona zinthu zing’onozing’ono zabwino zimene mungachitire anthu amene mumakhala nawo pafupi, popeza nthaŵi zambiri zimenezi zimalimbikitsa kugwirizana ndi kulemekezana. Komanso, mwa kuchita zimenezi, timatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.”—Miyambo 3:27; Yakobo 2:14-17.
Anthu Abwino Okhala Nawo Pafupi Amathokoza Akapatsidwa Kanthu
Bwenzi zikoma chikhala kuti aliyense amene wathandizidwa ndiponso wapatsidwa mphatso amayamikira. Tsoka lake, si mmene zimakhalira nthaŵi zonse. Ambiri amene amathandizidwa ndiponso amapatsidwa mphatso zabwino
sayamikira moti munthu wopereka ndi mtima wonseyo angamunene chamumtima munthu wopatsidwa mphatsoyo kuti, ‘Watsekereza mafulufute kuuna!’ Nthaŵi zina, kuyesetsa kwanu kuwapatsa moni mwansangala ndiponso kuwatukulira mkono anthu amene mumakhala nawo pafupi, kungawapangitse kungokugwedezerani mutu mokokeka basi.Komabe, nthaŵi zambiri amene amachitiridwa zinthu zimenezi amayamikira, ngakhale kuti pamaso angaoneke ngati sayamikira. Mwina chikhalidwe chake chimam’pangitsa kugwa mphwayi kapena kumangika ndiponso kusaganizira ena kwenikweni, kuoneka ngati wosachezeka. Komano m’dziko la anthu osayamika lino, anthu ena angadabwe nazo nsangala zanu, kapena angakayikire zolinga zanu. Angafunike kuwatsimikizira. Choncho, kupanga ubwenzi kumatenga nthaŵi komanso pamafunika kuleza mtima. Komabe, anthu okhala nawo pafupi amene amaphunzira kukhala opatsa ndiponso oyamikira akalandira zinthu amalimbikitsa mzimu wamtendere ndiponso wachimwemwe.
Pakagwa Masoka
Anthu abwino okhala nawo pafupi amafunika kwambiri pakagwa masoka. Pa mavuto, mpamene pamaoneka mzimu weniweni wa unansi. Pali nkhani zambiri zonena za ntchito zopanda dyera zimene anthu oyandikana nyumba achitira anzawo panthaŵi zoterezi. Tsoka limene lakhudza anthu onse okhala moyandikana limawapangitsa kugwirizana mosayembekezeka ndiponso kuyesetsa kuthandizana. Nthaŵi zambiri ngakhale adani amagwirira ntchito pamodzi.
Mwachitsanzo, The New York Times inanena kuti ku Turkey kutachitika chivomezi mu 1999, anthu odziŵika kuti ankadana anagwirizana. Wolemba nkhani wina wachigiriki, Anna Stergiou, analemba mu nyuzipepala ya ku Athens kuti: “Kwa zaka zambiri takhala tikuuzidwa kuti tizidana ndi anthu a ku Turkey. Koma pamene anali kuvutika kwambiri, sitinasangalale. Tinamva chisoni kwambiri, ndipo titaona mitembo ya ana tinalira ngati kuti chidani chakalekale chomwe chinalipocho chinali chitatha.” Opulumutsa anthu atawauza kuti asapitirize ntchito yawo, magulu a ku Girisi anakana.
Kugwira ntchito yopulumutsa anthu patagwa masoka ndi ntchitodi yabwino ndiponso yaikulu imene anthu okhala moyandikana amagwira. Ngakhale zili choncho, kupulumutsa moyo wa mnzanu wokhala naye pafupi mwa kum’chenjeza tsoka lisanachitike kungakhalenso ntchito yabwino kwambiri imene anthu okhala nawo pafupi angachite. Tsoka lake, zochitika zikusonyeza kuti nthaŵi zambiri anthu amene amachenjeza anzawo zatsoka limene likudza sasamalidwa, popeza panthaŵiyo tsoka limene likubweralo silioneka. Nthaŵi zambiri anthu amene amachenjezawo amatsutsidwa. Aliyense amene akuyesetsa kuthandiza anthu amene sakudziŵa kuti ali pangozi, amafunika kulimbikira ndiponso kudzipereka.
Ntchito Yaikulu Imene Ena Akuchitira Anzawo Okhala Nawo Pafupi
Masiku ano, chinthu china choopsa kwambiri kuposa masoka achilengedwe chichitikira anthu posachedwapa. Ndi chimene Mulungu Wamphamvuyonse adzachite chomwe chinanenedweratu, chimene chidzachotsa upandu, kuipa, ndi mavuto obwera chifukwa cha zimenezi padziko lapansi. (Chivumbulutso 16:16; 21:3, 4) Zimenezi si zokayikitsa kuti mwina zidzachitika kapena ayi, koma kuti n’zotsimikizika kuti zidzachitikadi. Mboni za Yehova n’zachangu kuuza anthu ochuluka zimene afunika kudziŵa kuti adzapulumuke zochitika zogwedeza dziko zimenezi, zomwe zichitike posachedwapa. N’chifukwa chake amagwira molimbika ntchito yawo yolalikira yodziŵika kwambiri padziko lonse. (Mateyu 24:14) Amachita modzifunira, chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu ndi anansi awo.
Choncho, musalole kuti tsankho kapena kukhumudwa zikulepheretseni kumvera Mboni zikafika panyumba panu kapena zikakupezani kulikonse. Akuyesetsa kukhala anthu abwino okhala nawo pafupi. Choncho vomerani pempho lawo lakuti aziphunzira nanu Baibulo. Phunzirani zimene Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti nthaŵi imene anthu okhala nawo pafupi adzakhale mwamtendere yayandikira. Nthaŵi imeneyo mtundu, chipembedzo, kapena maphunziro a munthu sadzawononga mayanjano abwino amene ambirife timafuna.
[Zithunzi pamasamba 6, 7]
Ndi bwino kuwachitira zabwino anthu amene mumakhala nawo pafupi
[Mawu a Chithunzi]
Dziko lapansi: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.