Kodi Mayesero Tiziwaona Bwanji?
Kodi Mayesero Tiziwaona Bwanji?
MAYESERO! Aliyense amakumana nawo. Angabwere chifukwa cha kusiyana maganizo, mavuto a zachuma, matenda, zokopa, anzathu kutisonkhezera kuti tichite zoipa, chizunzo, kusaloŵerera kwathu m’nkhani za ndale ndi kulambira mafano, ndi zina zambiri. Kaya ndi mayesero otani amene tingakumane nawo, nthaŵi zambiri amayambitsa nkhaŵa yaikulu. Kodi tingatani kuti tithane nawo bwinobwino? Kodi pali njira iliyonse imene timapindula ndi mayesero?
Thandizo Labwino Kwambiri
Mfumu Davide yakale inakumana ndi mayesero m’moyo wake wonse, koma inamwalira ili yokhulupirika. Inatha bwanji kupirira? Iyo inatchula amene anali kuipatsa mphamvu pamene inati: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasoŵa.” Ndiyeno inapitiriza kuti: “Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine: chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.” (Salmo 23:1, 4) Inde, Yehova ndiye amene angapereke thandizo lopanda malire. Iye anatsogolera Davide m’nthaŵi zovuta kwambiri, ndipo ndiwokonzeka kutichitira ifenso chimodzimodzi pakafunika kutero.
Kodi tingatani kuti Yehova atithandize? Baibulo likufotokoza zimene tingachite pamene likuti: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” (Salmo 34:8) Ndi pempho labwinotu limenelo, koma kodi limatanthauza chiyani? Likutilimbikitsa kutumikira Yehova ndi kutsatira chifuniro chake ndi mtima wonse. Kuchita zimenezi kumafuna kusiya ufulu wathu wina, kudzimana zinthu zina. Nthaŵi zina, zimenezi zingatichititse kukumana ndi mayesero, monga chizunzo ndi mavuto ena. Komabe, amene amavomera pempho la Yehova limeneli ndi mtima wonse sadzadandaula kuti analakwitsa posankha kuchita zimenezo. Yehova adzawachitira zabwino kwambiri. Adzawatsogolera ndi kuwasamalira mwauzimu. Adzawathandiza m’mayesero awo pogwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake woyera, ndi mpingo wachikristu. Ndipo kenako adzawapatsa mphoto ya moyo wosatha.—Salmo 23:6; 25:9; Yesaya 30:21; Aroma 15:5.
Anthu amene amasankha kusintha moyo wawo kuti atumikire Yehova ndiponso amene amapitirizabe kuchita zimenezo amaona kuti Yoswa 21:44, 45) Zimenezi zingatichitikirenso ife ngati tidalira Yehova ndi mtima wonse pamene tili m’mayesero ndiponso m’nthaŵi zina zonse.
Yehova amakwaniritsa malonjezo ake onse. N’zimene anaona Aisrayeli amene anatsatira Yoswa kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Ataoloka mtsinje wa Yordano, anapirira mayesero, anamenya nkhondo, ndiponso anaphunzira maphunziro opweteka. Koma mbadwo umenewo unali wokhulupirika kwambiri kusiyana ndi makolo awo amene anatuluka mu Igupto ndi kufa m’chipululu. Motero, Yehova anathandiza anthu okhulupirikawo, ndipo pofotokoza mmene iwo analili Yoswa atatsala pang’ono kumwalira, Baibulo limati: “Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo awo . . . Sikadasoŵa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.” (Kodi n’chiyani chingafooketse kudalira kwathu Yehova? Yesu anatchula chinthu chimodzi pamene anati: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri . . . Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” (Mateyu 6:24) Ngati tikhulupirira Yehova, sitidzatanganidwa kufunafuna chuma kuti tikhale ndi moyo wabwino monga mmene amachitira anthu ambiri m’dzikoli. Yesu analangiza otsatira ake kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo [zinthu zofunika] zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Mkristu amene amaona chuma moyenera ndi kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo m’moyo wake amachita bwino. (Mlaliki 7:12) N’zoona kuti zingam’chititse kusoŵa zinthu zina. Angadzimane zinthu zina zakuthupi. Koma adzapeza mphoto yaikulu. Ndipo Yehova adzamuthandiza.—Yesaya 48:17, 18.
Zimene Mayesero Amatiphunzitsa
Komabe, kusankha ‘kulaŵa ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino,’ sikumateteza munthu pa zochitika zina zadzidzidzi m’moyo. Ndiponso sikumatiteteza kotheratu ku mavuto amene Satana ndi anthu amene amawagwiritsa ntchito amabweretsa. (Mlaliki 9:11) Chifukwa cha zimenezi, kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwa Mkristu kungayesedwe. N’chifukwa chiyani Yehova amalola anthu amene amamulambira kukumana ndi mayesero oterowo? Mtumwi Petro anapereka chifukwa chimodzi pamene anati: “Tsopano kanthaŵi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu, kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo amtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Kristu.” (1 Petro 1:6, 7) Inde, mayesero amatithandiza kusonyeza mmene chikhulupiro chathu chilili ndiponso mmene timakondera Yehova. Ndiponso mayesero amathandiza kuyankha kutonza ndi kuneneza kwa Satana Mdyerekezi.—Miyambo 27:11; Chivumbulutso 12:10.
Mayesero amatithandizanso kukhala ndi makhalidwe ena achikristu. Mwachitsanzo, taonani mawu a wamasalmo aŵa: “[Yehova] apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza am’dziŵira kutali.” (Salmo 138:6) Ambirife mwachibadwa sindife odzichepetsa, koma mayesero angatithandize kukhala ndi khalidwe lofunika kwambiri limeneli. Takumbukirani zimene zinachitika kalelo m’nthaŵi ya Mose pamene ena mu Israyeli anatopa ndi kudya mana mlungu ndi mlungu, mwezi ndi mwezi. Mwachionekere, chimenecho chinali chiyeso kwa iwo, ngakhale kuti anali kulandira manawo mozizwitsa. Kodi cholinga cha chiyesochi chinali chiyani? Mose anawauza kuti: “[Yehova] anakudyetsani m’chipululu ndi mana, . . . kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni.”—Deuteronomo 8:16.
Kudzichepetsa kwathu kungayesedwenso chimodzimodzi. Motani? Chabwino, kodi timatani gulu likasintha momwe limachitira zinthu? Yesaya 60:17) Kodi timathandizira ndi mtima wonse ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa? (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kodi timavomereza ndi mtima wonse mmene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amafotokozera mfundo za choonadi za m’Baibulo? (Mateyu 24:45-47; Miyambo 4:18) Kodi timakana kusonkhezeredwa kuti tikhale ndi chipangizo chimene changopangidwa kumene, zovala zimene zili mu fashoni, kapena mtundu wa galimoto umene wangotuluka kumene? Munthu wodzichepetsa angayankhe mafunso ameneŵa kuti inde.—1 Petro 1:14-16; 2 Petro 3:11.
(Mayesero amatithandizanso kukhala ndi khalidwe lina labwino kwambiri, la kupirira. Wophunzira Yakobo anati: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.” (Yakobo 1:2, 3) Kupirira bwinobwino mayesero osiyanasiyana ndi kudalira Yehova ndi mtima wonse kumachititsa munthu kukhala wosasunthika, wodalirika, ndiponso wokhulupirika. Kumatilimbikitsa kuti tidzathane ndi mavuto ena amene Satana, mulungu wamkwiyo wa dziko lino, angabweretse m’tsogolo.—1 Petro 5:8-10; 1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:12.
Pitirizani Kuwaona Mayesero Moyenera
Mwana wangwiro wa Mulungu, Yesu Kristu, anakumana ndi mayesero ambiri pamene anali padziko lapansi ndipo anapindula kwambiri chifukwa chopirira mayesero ameneŵa. Paulo analemba kuti Yesu “anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo.” (Ahebri 5:8) Kukhulupiririka kwake mpaka imfa kunalemekeza dzina la Yehova ndipo zinathandiza kuti iye apereke mtengo wa moyo wake wangwiro waumunthu monga dipo la anthu onse. Zimenezo zinatsegula mpata woti amene angakhulupirire Yesu ayembekezere kudzakhala ndi moyo wosatha. (Yohane 3:16) Yesu pakalipano ndi Mkulu wa Ansembe wathu ndiponso Mfumu yathu chifukwa chakuti anakhulupirikabe pa nthaŵi ya mayesero.—Ahebri 7:26-28; 12:2.
Bwanji nanga ifeyo? Kukhulupirika kwathu pamene tili m’mayesero kumatibweretseranso madalitso ambiri. Kwa amene adzapita kumwamba, Baibulo limati: “Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akum’konda Iye.” (Yakobo 1:12) Amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi akuwatsimikizira kuti ngati apirira mokhulupirika, adzakhala ndi moyo wosatha m’dziko la paradaiso. (Chivumbulutso 21:3-6) Ndiponso kuposa zonsezi, kupirira kwawo mokhulupirika kumalemekeza dzina la Yehova.
Pamene tikutsatira mapazi a Yesu, tikhale ndi chikhulupiriro kuti mayesero onse amene timakumana nawo m’dongosolo la zinthu lino tingathe kuwapirira bwinobwino. (1 Akorinto 10:13; 1 Petro 2:21) Motani? Mwa kudalira kwathu Yehova, amene amapereka “mphamvu zoposa zachibadwa” kwa amene amamudalira. (2 Akorinto 4:7, NW) Tiyenitu tikhale ndi chikhulupiriro monga cha Yobu, yemwe ngakhale pamene anali m’mayesero opweteka kwambiri, ananena mtima uli m’malo kuti: “Atandiyesa ndidzatuluka ngati golidi.”—Yobu 23:10.
[Chithunzi patsamba 31]
Kukhulupirika kwa Yesu pamene anali kuyesedwa kunalemekeza dzina la Yehova. Kukhulupirika kwathu kungachitenso chimodzimodzi